Pewani Kuyendera Maganizo a Anthu Ena
ZINTHU zimene anthu amati ndi zabwino kapena zoipa, zolemekezeka kapena zolakwika zimasiyana malinga ndi madera amene anthuwo akukhala. Anthu amasintha mmene amaonera zinthu zimenezi pakapita nthawi. Choncho tikamawerenga nkhani zosiyanasiyana za m’Malemba, zimene zinachitika kale tiyenera kuganiziranso mmene anthu ankaonera zinthu pa nthawi ya m’Baibulo m’malo mongoika maganizo athu pa zimene tikuwerenga.
Mwachitsanzo, taganizirani mfundo ziwiri zonena za ulemu ndi manyazi zomwe zimatchulidwa mobwerezabwereza m’Malemba Achigiriki Achikhristu. Kuti timvetse bwino nkhani zimene zimafotokoza za ulemu ndi manyazi, tiyenera kuganizira mmene anthu ankaonera zinthu zimenezi pa nthawiyo.
Mfundo Zimene Anthu Ankayendera M’nthawi ya Atumwi
Katswiri wina wamaphunziro a Baibulo ananena kuti: “Agiriki, Aroma ndiponso Ayuda ankaona ulemu ndi manyazi kuti ndi nkhani zofunika kwambiri pa chikhalidwe chawo. Amuna ankayesetsa kwambiri pa moyo wawo wonse kuti apeze ulemu, adzipangire mbiri yabwino, atchuke, azikondedwa ndiponso kuti azilemekezedwa.” Izi zinkachititsa kuti azingotsatira maganizo a anthu ena.
Kutchuka, udindo komanso ulemu zinali zofunika kwambiri pakati pa anthu amene anazolowera kupereka ulemu kwa munthu malinga ndi udindo wake, kaya ndi wolemekezeka kapena kapolo. Munthu ankati ndi wolemekezeka osati kokha chifukwa cha mmene amadzionera koma mmene anthu enanso amamuonera. Kuti munthu azilemekezedwa, anthu ena ankafunika kuona kuti khalidwe lake ndi labwino. Chuma kapena udindo wa munthu zinkachititsanso kuti anthu azimupatsa ulemu. Anthu ena ankapatsidwa ulemu chifukwa cha ntchito yotamandika imene agwira kapena ngati achita zinthu zoposa anthu ena. Koma munthu wosalemekezedwa ankanyozedwa kapena kuchititsidwa manyazi pagulu. Choncho munthu ankachita manyazi kwambiri osati chifukwa cha mmene akumvera mumtima mwake, koma chifukwa cha mmene anthu ankamuonera.
Pamene Yesu ankanena zokhala “pa malo olemekezeka koposa” kapena “pa malo otsika koposa” pa phwando, kwenikweni ankanena za ulemu ndi manyazi malinga ndi chikhalidwe cha pa nthawiyo. (Luka 14:8-10) Ophunzira a Yesu anakangana kawiri konse pa nkhani yofuna “kudziwa amene ali wamkulu koposa pakati pawo.” (Luka 9:46; 22:24) Zochita zawozi zikusonyezeratu maganizo amene anali ndi anthu ambiri pa nthawiyo. Atsogoleri a chipembedzo achiyuda anali odzikuza ndipo ankafuna malo apamwamba, choncho ankaona kuti ntchito ya Yesu yolalikira iwachotsera ulemu wawo. Iwo ankayesetsa kutsutsana naye pagulu n’cholinga chakuti aoneke kuti ndi apamwamba koma analephera mochititsa manyazi.—Luka 13:11-17.
Ayuda, Agiriki ndi Aroma ankaonanso kuti “kumangidwa n’kuimbidwa mlandu pa gulu” chinali chinthu chochititsa manyazi kwambiri. Kumangidwa n’kutsekeredwa m’ndende chinalinso chinthu chochititsa manyazi kwambiri. Munthu amene izi zamuchitikira, ankachititsa manyazi anzake, anthu a m’banja lake ndiponso anthu ena onse, kaya amupezadi ndi mlandu kapena ayi. Ngakhale patapita nthawi munthu wotereyu sankapatsidwanso ulemu ndipo ubwenzi wake ndi anthu ena unkasokonekera. Chinthu china chomwe chinali chochititsa manyazi kwambiri kuposa kumangidwa chinali kuvulidwa n’kukwapulidwa. Munthu amene izi zamuchitikira ankanyozedwa kwambiri ndipo sankapatsidwa ulemu.
Kukhomedwa pamtengo wozunzikirapo ndiye anali mapeto a zinthu zochititsa manyazi. Katswiri wina wa maphunziro a Baibulo dzina lake Martin Hengel ananena kuti, “chilango chimenechi chinkaperekedwa kwa akapolo. Chinkasonyeza kuti munthuyo ndi wochititsa manyazi koopsa ndiponso woyenera kuzunzidwa.” Achibale ndiponso anzake a munthu wopachikidwayo ankakakamizika kumukana. Popeza Khristu anafa imfa yotereyi, Akhristu onse m’nthawi ya Atumwi anafunika kupirira kwambiri ponyozedwa. Anthu ambiri ankaona kuti si nzeru kunena kuti amatsatira munthu amene anaphedwa mwa kupachikidwa pamtengo wozunzikirapo. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ife timalalikira za Khristu amene anapachikidwa. Kwa Ayuda, ndi chinthu chokhumudwitsa ndipo kwa mitundu ina ndi kupusa.” (1 Akor. 1:23) Kodi Akhristu oyambirira anapirira bwanji vuto limeneli?
Ankayendera Mfundo Zawo
Akhristu oyambirira ankamvera malamulo ndipo ankayesetsa kupewa kuchita manyazi chifukwa chochita khalidwe loipa. Mtumwi Petulo analemba kuti: “Pasakhale wina wa inu wovutika chifukwa cha kupha munthu, kuba, kuchita choipa china kapena kulowerera nkhani za ena.” (1 Pet. 4:15) Koma Yesu ananena kuti otsatira ake adzazunzidwa chifukwa cha dzina lake. (Yoh. 15:20) Mtumwi Petulo analemba kuti: “Ngati [munthu] avutika chifukwa chokhala Mkhristu, asachite manyazi, koma apitirize kulemekeza Mulungu.” (1 Pet. 4:16) Kuti munthu asachite manyazi pozunzidwa chifukwa chotsatira Khristu ankayenera kusiya kuyendera mfundo zimene anthu ambiri ankayendera.
Akhristu sankalola kuti aziyendera mfundo za anthu ena. Pa nthawi ya atumwi, anthu ankaona kuti si nzeru kukhulupirira munthu amene anapachikidwa kuti ndi Mesiya. Maganizo amenewa akanatha kuchititsa Akhristu kutsatira mfundo zimene anthu onse ankayendera. Komabe chikhulupiriro chawo chakuti Yesu ndi Mesiya chinawalimbikitsa kumutsatira ngakhale kuti ankanyozedwa. Yesu ananena kuti: “Aliyense wochita manyazi ndi ine, komanso ndi mawu anga mu m’badwo wachigololo ndi wochimwa uno, Mwana wa munthu adzachitanso naye manyazi akadzafika mu ulemerero wa Atate wake limodzi ndi angelo oyera.”—Maliko 8:38.
Masiku ano tikhoza kukumana ndi mavuto amene angatichititse kusiya kutsatira Khristu. Nthawi zina anzathu a kusukulu, anthu oyandikana nawo nyumba, kapena anzathu a kuntchito angatikakamize kuti tichite chiwerewere, chinyengo kapena zinthu zina zokayikitsa. Anthu amenewa angatichititse kuganiza kuti kutsatira mfundo zabwino n’kochititsa manyazi. Kodi zikatere tiyenera kuchita chiyani?
Tsanzirani Anthu Amene Sanachite Manyazi
Kuti akhalebe wokhulupirika kwa Yehova, Yesu analolera kuphedwa mochititsa manyazi kwambiri. Iye “anapirira mtengo wozunzikirapo, nanyoza manyazi.” (Aheb. 12:2) Adani a Yesu anamumenya mbama, anamulavulira, anamuvula zovala, anamukwapula, anamupachika ndiponso anamunyoza. (Maliko 14:65; 15:29-32) Koma Yesu sanachite manyazi ndi zinthu zimenezi. N’chifukwa chiyani tikutero? Iye sanagonje ngakhale kuti anamuchitira zonsezi. Yesu ankadziwa kuti si wonyozeka pamaso pa Yehova ndipo sankafuna ulemu kuchokera kwa anthu. Ngakhale kuti Yesu anafa ngati kapolo, Yehova anamulemekeza mwa kumuukitsa n’kumupatsa malo aulemu kwambiri pafupi ndi Iye. Pa Afilipi 2:8-11, timawerenga kuti: “[Khristu Yesu] anadzichepetsa nakhala womvera mpaka imfa, inde, imfa ya pa mtengo wozunzikirapo. Pa chifukwa chimenechinso, Mulungu anam’kwezera pamalo apamwamba. Ndipo anam’komera mtima kum’patsa dzina loposa lina lililonse. Anatero kuti m’dzina la Yesu, onse apinde maondo awo, aja akumwamba, a padziko lapansi, ndi a pansi pa nthaka. Kutinso aliyense avomereze poyera ndi lilime lake kuti Yesu Khristu ndiye Ambuye, polemekeza Mulungu Atate.”
Sikuti Yesu sanakhudzidwe ndi zinthu zochititsa manyazi zimene anamuchitira asanaphedwe. Popeza Yesu ankaimbidwa mlandu wonyoza Mulungu, Mwana wa Mulunguyu ankaganizira mmene imfa yake yochititsa manyazi ingakhudzire dzina la Atate wake. Yesu anapempha Yehova kuti asalole iye kufa imfa yochititsa manyazi imeneyi. Iye anapemphera kuti: “Ndichotsereni chikho ichi.” Komabe Yesu ankafunitsitsa kuti chifuniro cha Mulungu chichitike ndipo analolera zimenezi. (Maliko 14:36) Koma kuti zimenezi zichitike, Yesu anapirira mavuto osiyanasiyana ndipo sanachite manyazi. Ndipotu amene akanachita manyazi ndi anthu amene ankangotsatira mfundo zimene anthu ambiri ankayendera pa nthawi imeneyo. Yesu sankayendera mfundo zoterozo.
Ophunzira a Yesu anamangidwa ndiponso kukwapulidwa. Zinthu zimenezi zinali zochititsa manyazi. Iwo ankanyozedwa koma zimenezi sizinawafooketse. Akhristu oona sankangotsatira zimene anthu ankafuna kuti iwo achite ndipo sanachite manyazi. (Mat. 10:17; Mac. 5:40; 2 Akor. 11:23-25) Iwo ankadziwa kuti ankayenera ‘kunyamula mtengo wawo wozunzikirapo ndi kutsatira Yesu mosalekeza.’—Luka 9:23, 26.
Nanga bwanji ifeyo masiku ano? Zinthu zimene anthu m’dzikoli amaziona kuti n’zopusa, zofooka ndiponso zopanda pake, Mulungu amaziona kuti ndi zanzeru, zamphamvu ndiponso zolemekezeka. (1 Akor. 1:25-28) Ndiyetu kungakhale kupusa ndiponso kupanda nzeru kumangotsatira maganizo a anthu ambiri.
Munthu aliyense amene amafuna kupatsidwa ulemu ndi dzikoli ayenera kuganizira zimene anthu m’dzikoli amafuna. Koma mofanana ndi Yesu ndiponso otsatira ake oyambirira, timafuna kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Choncho tipitiriza kulemekeza zinthu zimene iye amaziona kuti n’zolemekezeka ndipo tizichita manyazi ndi zinthu zimene iyenso amaziona kuti n’zochititsa manyazi.
[Chithunzi patsamba 4]
Yesu sankayendera maganizo a anthu pa nkhani ya zinthu zochititsa manyazi