NKHANI YOPHUNZIRA 40
Tingakhalebe Okhulupirika Ngati Petulo
“Ambuye, chokani pali ine pano, chifukwa ndine munthu wochimwa.”—LUKA 5:8.
NYIMBO NA. 38 Mulungu Adzakulimbitsa
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Kodi Petulo anatani Yesu atamuthandiza kupha nsomba zambiri modabwitsa?
PETULO anagwira ntchito yosodza usiku wonse koma sanaphe nsomba iliyonse. Kenako Yesu anamuuza kuti: “Palasira kwakuya, ndipo muponye maukonde anu kuti muphe nsomba.” (Luka 5:4) Petulo ankakayikira kuti angaphe nsomba komabe anachita zomwe anauzidwa. Maukonde anaponya aja anayamba kung’ambika chifukwa cha kuchuluka kwa nsomba. Atazindikira kuti Yesu wachita chozizwitsa, Petulo ndi anthu omwe ankagwira nawo ntchito “anadabwa kwambiri.” Petulo anati: “Ambuye, chokani pali ine pano, chifukwa ndine munthu wochimwa.” (Luka 5:6-9) Apatu Petulo ankadziona kuti sanali woyenera kukhala pafupi ndi Yesu.
2. N’chifukwa chiyani n’zofunika kuganizira chitsanzo cha Petulo?
2 Petulo ankanena zoona, chifukwa iye analidi “munthu wochimwa.” Malemba amasonyeza kuti nthawi zina, iye ankalankhula komanso kuchita zinthu zomwe pambuyo pake ankadzimvera nazo chisoni. Kodi inunso nthawi zina mumamva ngati mmene Petulo ankamvera? Kodi pali khalidwe linalake lomwe mukulimbana nalo kapena mtima winawake wofuna kuchita zoipa? Ngati ndi choncho, chitsanzo cha Petulo chingakuthandizeni. N’chifukwa chiyani tikutero? Taganizirani izi: Yehova akanatha kusankha kuti zimene Petulo ankalakwitsa zisalembedwe m’Baibulo. Koma Mulungu anauzira anthu kuti alembe zimenezo kuti tiziphunzirapo kanthu. (2 Tim. 3:16, 17) Kuphunzira za Petulo, yemwe ankalakwitsa zinthu komanso anali munthu ngati ifeyo, kumatithandiza kuona kuti Yehova sayembekezera kuti tizichita zinthu osalakwitsa kalikonse. Yehova amafuna kuti tizipitiriza kumutumikira ngakhale kuti timalakwitsa zinthu zina.
3. N’chifukwa chiyani sitiyenera kufooka?
3 N’chifukwa chiyani tiyenera kupitirizabe kuchita khama? Paja pali mawu akuti, khama lipindula. Tiyerekezere motere: Munthu woimba akhoza kutenga zaka zambiri kuti afike podziwa bwino chida chake choimbira. Pa nthawi imeneyi akhoza kumalakwitsa zinthu zambiri koma akapitiriza kuchita khama, angafike pochidziwa bwino chidacho. Ngakhale atafika pokhala katswiri, nthawi zina angathe kulakwitsabe zinthu zina. Komabe iye samataya mtima, amapitirizabe kuwonjezera luso lake. Mofanana ndi zimenezi, ngakhale zitaoneka kuti tayesetsa kulimbana ndi vuto linalake, nthawi zina zingapezeke kuti talakwitsanso. Koma tiyenera kupitilizabe kuchita khama, osagwa ulesi. Tonsefe timalankhula kapena kuchita zinthu zimene pambuyo pake timadzimvera nazo chisoni. Komabe tikapanda kutaya mtima, Yehova amatithandiza kuti tikonze zomwe zalakwikazo. (1 Pet. 5:10) Tiyeni tikambirane chitsanzo cha Petulo chosonyeza kufunika kochita khama. Chifundo chomwe Yesu ankamusonyeza ngakhale kuti ankalakwitsa zinthu, chingatilimbikitse kuti tipitirize kutumikira Yehova.
MAVUTO OMWE PETULO ANKALIMBANA NAWO KOMANSO MADALITSO AMENE ANAPEZA
4. Mogwirizana ndi Luka 5:5-10, kodi Petulo ankadziona bwanji, nanga Yesu anamutsimikizira za chiyani?
4 Malemba safotokoza chifukwa chake Petulo ananena kuti anali “munthu wochimwa” kapenanso machimo omwe ankatanthauza. (Werengani Luka 5:5-10.) Koma n’kutheka kuti pali zinthu zina zomwe analakwitsa kwambiri. Yesu anaona kuti Petulo ankachita mantha mwina chifukwa choti ankadziona kuti anali munthu wosayenera. Yesu ankadziwanso kuti Petulo akhoza kupitiriza kukhala wokhulupirika. Choncho, iye anauza Petulo mokoma mtima kuti: “Usachite mantha.” Zimene Yesu anachita posonyeza kuti ankakhulupirira Petulo, zinamuthandiza kwa moyo wake wonse. Pambuyo pake Petulo ndi m’bale wake Andireya, anasiya ntchito yawo yausodzi n’kukhala otsatira a Mesiya, zomwe zinachititsa kuti apeze madalitso ambiri.—Maliko 1:16-18.
5. Kodi Petulo anadalitsidwa bwanji atasiya kuchita mantha n’kupitiriza kutsatira Yesu?
5 Petulo anaona zinthu zambiri zosangalatsa chifukwa chokhala wotsatira wa Khristu. Mwachitsanzo, iye anaona Yesu akuchiritsa odwala, kutulutsa ziwanda komanso kuukitsa akufa.b (Mat. 8:14-17; Maliko 5:37, 41, 42) Petulo anaonanso masomphenya osonyeza ulemerero womwe Yesu adzakhale nawo monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo mosakayikira zimenezi zinamulimbikitsa. (Maliko 9:1-8; 2 Pet. 1:16-18) Petulo akanapanda kutsatira Yesu, sakanaona zinthu zimenezi. Iyetu ayenera kuti anasangalala chifukwa chosalola kuti maganizo ofooketsa amulepheretse kupeza madalitso amenewa.
6. Kodi zinali zosavuta kuti Petulo athane ndi mavuto ake? Fotokozani.
6 Ngakhale kuti anaona komanso kumva zinthu zambiri, Petulo ankalakwitsabe zinthu zina. Taganizirani zitsanzo zochepa izi. Pa nthawi ina, iye anadzudzula Yesu atafotokoza kuti adzavutika komanso kufa kuti akwaniritse ulosi wa m’Baibulo. (Maliko 8:31-33) Petulo ndi atumwi ena ankakangananso mobwerezabwereza pa nkhani yakuti wamkulu ndani. (Maliko 9:33, 34) Pa usiku womaliza Yesu asanaphedwe, Petulo anadula khutu la munthu wina. (Yoh. 18:10) Usiku womwewo, iye anachita mantha ndipo anakana Yesu katatu. (Maliko 14:66-72) Zimenezi zinachititsa kuti Petulo alire mopwetekedwa mtima kwambiri.—Mat. 26:75.
7. Kodi Petulo anapatsidwa mwayi wotani Yesu ataukitsidwa?
7 Yesu sanasiye kukonda mtumwi wakeyu, yemwe anafooka kwambiri chifukwa cha zimene analakwitsa. Ataukitsidwa, iye anapereka mwayi kwa Petulo woti asonyeze kuti amamukondabe. Yesu anapempha Petulo kuti akhale wodzichepetsa n’kumaweta nkhosa zake. (Yoh. 21:15-17) Petulo anavomera kuchita zimenezi. Choncho pa tsiku la Pentekosite, iye anali ku Yerusalemu ndipo anali pagulu la anthu oyambirira kudzozedwa ndi mzimu woyera.
8. Kodi Petulo analakwitsa chiyani ku Antiokeya?
8 Ngakhale pambuyo podzozedwa, Petulo ankalakwitsabe zinthu zina. Mu 36 C.E., iye analipo pamene Koneliyo anadzozedwa ndi mzimu woyera. Umenewu unali umboni woonekeratu woti “Mulungu alibe tsankho” komanso kuti anthu a mitundu ina anali ndi mwayi wolowa mumpingo wa Chikhristu. (Mac. 10:34, 44, 45) Pambuyo pa zimenezi, Petulo ankamasuka kudya ndi anthu a mitundu ina, zinthu zomwe poyamba sakanachita. (Agal. 2:12) Komabe, Akhristu ena a Chiyuda sankaona kuti n’koyenera kuti Ayuda azidya ndi anthu a mitundu ina. Ayuda ena omwe anali ndi maganizo amenewa atabwera ku Antiokeya, Petulo anasiya kudya ndi abale ake a mitundu ina, mwina poopa kuti akhumudwitsa Ayudawo. Mtumwi Paulo ataona zachinyengo zomwe Petulo anachitazi, anamudzudzula pamaso pa anthu onse. (Agal. 2:13, 14) Ngakhale kuti iye analakwitsa zinthu, zimenezi sizinamufooketse. Ndiye n’chiyani chinamuthandiza?
KODI N’CHIYANI CHINATHANDIZA PETULO KUTI ASAFOOKE?
9. Kodi lemba la Yohane 6:68, 69, limasonyeza bwanji kuti Petulo anali wokhulupirika?
9 Petulo anali wokhulupirika ndipo sanalole kuti chilichonse chimulepheretse kutsatira Yesu. Iye anasonyeza kukhulupirika kwake pa nthawi ina pamene Yesu analankhula zinthu zimene ophunzira ake sanazimvetse. (Werengani Yohane 6:68, 69.) Anthu ambiri anasiya kutsatira Yesu popanda kudikira kuti awafotokozere zimene ankatanthauza. Koma Petulo ankadziwa kuti Yesu yekha, ndi yemwe ali ndi “mawu amoyo wosatha.”
10. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira Petulo? (Onaninso chithunzi.)
10 Yesu sanasiye kumukonda Petulo. Pa usiku wake womaliza, iye ankadziwa kuti Petulo ndi atumwi ena amusiya yekha. Komabe sankakayikira kuti Petulo adzabwerera n’kukhalabe wokhulupirika. (Luka 22:31, 32) Yesu ankadziwa kuti “mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” (Maliko 14:38). Choncho ngakhale kuti Petulo anamukana kuti sakumudziwa, iye sanasiye kukonda mtumwi wakeyu. Ataukitsidwa, Yesu anakumana ndi Petulo ndipo zikuoneka kuti Petuloyo anali yekha. (Maliko 16:7; Luka 24:34; 1 Akor. 15:5) Zimenezi ziyenera kuti zinalimbikitsa mtumwiyu, yemwe ankadzimvera chisoni kwambiri.
11. Kodi Yesu anamutsimikizira bwanji Petulo kuti Yehova adzamuthandiza?
11 Yesu anatsimikizira Petulo kuti Yehova adzamuthandiza. Iye ataukitsidwa anathandiza Petulo ndi atumwi anzake kuphanso nsomba m’njira yodabwitsa. (Yoh. 21:4-6) Mosakayikira zimenezi zinatsimikizira Petulo kuti Yehova angamuthandize kupeza zofunika pa moyo. N’kutheka kuti mtumwiyu anakumbukira zimene Yesu ananena kuti Yehova adzathandiza aliyense amene amapitiriza “kufunafuna Ufumu choyamba.” (Mat. 6:33) Zonsezi zinathandiza Petulo kuti aziona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri kuposa usodzi. Pa tsiku la Pentekosite mu 33 C.E., iye analalikira molimba mtima ndipo anathandiza anthu ambiri kuti amve uthenga wabwino. (Mac. 2:14, 37-41) Pambuyo pake anathandiza Asamariya komanso anthu amitundu ina kuti ayambe kukhulupirira Khristu. (Mac. 8:14-17; 10:44-48) Apatu Yehova anagwiritsa ntchito kwambiri Petulo kuti athandize anthu a mitundu yonse kuti abwere mumpingo wa Chikhristu.
KODI TIKUPHUNZIRA CHIYANI PA NKHANI YA PETULO?
12. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani ngati tikulimbana ndi vuto linalake lomwe likutenga nthawi yaitali?
12 Yehova angatithandize kuti tipitirizebe kumutumikira. Zimenezi zingakhale zovuta makamaka ngati tikulimbana ndi vuto linalake kwa nthawi yaitali. Nthawi zina zinthu zimene timalimbana nazo zingakhale zovuta kuposa zimene Petulo anakumana nazo. Komabe Yehova angatipatse mphamvu kuti tisafooke. (Sal. 94:17-19) Mwachitsanzo, m’bale wina asanaphunzire choonadi anakhala akugonana ndi amuna anzake kwa zaka zambiri. Koma iye anasinthiratu n’kusiya khalidwe loipali. Ngakhale zili choncho, nthawi zina amalimbanabe ndi mtima wofuna kuchita zoipa. Kodi n’chiyani chamuthandiza kuti asafooke? M’baleyu anati: “Yehova amatipatsa mphamvu.” Anawonjezera kuti: “Mothandizidwa ndi mzimu wa Yehova . . . ndaphunzira kuti n’zotheka kupitirizabe kuyenda m’njira ya choonadi . . . Yehova wakhala akundigwiritsa ntchito. Ndipo ngakhale kuti ndimalakwitsa zinthu zina, iye akupitirizabe kundipatsa mphamvu.”
13. Mogwirizana ndi Machitidwe 4:13, 29, 31, kodi tingatsanzire bwanji Petulo? (Onaninso chithunzi.)
13 Monga mmene taonera, maulendo angapo, Petulo analakwitsa zinthu chifukwa choopa anthu. Koma atapemphera kwa Mulungu kuti amuthandize, Petulo anachita zinthu molimba mtima. (Werengani Machitidwe 4:13, 29, 31.) Ifenso tingathe kuthetsa mantha. Taganizirani zimene zinachitikira m’bale wina wachinyamata dzina lake Horst yemwe ankakhala ku Germany pa nthawi ya ulamuliro wa Nazi. Maulendo angapo ali kusukulu, anachita mantha n’kunena nawo kuti “Hitler Mpulumutsi Wathu!” M’malo momukalipira, makolo ake anapemphera naye, kupempha Yehova kuti amuthandize kukhala wolimba mtima. Chifukwa chothandizidwa ndi makolo ake komanso kudalira Yehova, Horst anapeza mphamvu n’kupitiriza kukhala wolimba. Pambuyo pake iye anati: “Yehova sanandisiye ngakhale pang’ono.”c
14. Kodi abusa achikondi angalimbikitse bwanji anthu amene afooka?
14 Yehova ndi Yesu amatitsimikizira kuti sadzatisiya ngakhale pang’ono. Atakana Khristu, Petulo ankafunika kusankha zochita pa nkhani yofunika. Ankafunika kusankha pakati posiya kutsatira Khristu ndi kupitiriza kukhala wophunzira wake. Yesu anali atapempherera Petulo kuti chikhulupiriro chake chisathe. Yesu anauza Petulo kuti anamupempherera ndipo anasonyeza kuti sankakayikira kuti adzatha kulimbikitsa abale ake. (Luka 22:31, 32) Petulo ayenera kuti ankalimbikitsidwa akakumbukira zimene Yesu anamuuzazi. Ifenso tikafunika kusankha pa nkhani yofunika kwambiri, Yehova angagwiritse ntchito abusa achikondi kuti atitsimikizire kuti tingathe kukhalabe okhulupirika. (Aef. 4:8, 11) M’bale wina dzina lake Paul, yemwe wakhala mkulu kwa zaka zambiri amachita zimenezi polimbikitsa Akhristu anzake. Amafunsa Akhristu omwe akuoneka kuti akufooka kuti aganizire mmene poyamba Yehova anawathandizira kuti aphunzire choonadi. Kenako amawatsimikizira kuti Yehova sadzawasiya ngakhale pang’ono chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika. Iye anati: “Ndaona anthu ambiri omwe anafooka, Yehova akuwathandiza kupitiriza kumutumikira.”
15. Kodi chitsanzo cha Petulo ndi M’bale Horst chikusonyeza bwanji kuti mawu a pa Mateyu 6:33 ndi oona?
15 Yehova anathandiza Petulo ndi atumwi anzake kupeza zofunika pa moyo. Ifenso tikamaika utumiki pamalo oyamba pa moyo wathu, iye adzatithandiza kupeza zimene timafunikira. (Mat. 6:33) Nkhondo yachiwiri yapadziko lonse itatha, Horst yemwe tamutchula kale uja anaganiza zoyamba upainiya. Iye anali wosauka kwambiri ndipo ankakayikira ngati angamapeze ndalama zokwanira komanso kupitirizabe kuchita utumiki wa nthawi zonse. Ndiye kodi iye anachita chiyani? Iye anaganiza zoti amuyese Yehova polowa mu utumiki tsiku lililonse pa mlungu wapadera. Kumapeto kwa mlunguwo, iye anadabwa woyang’anira dera akumupatsa envelopu yomwe sanadziwe kumene yachokera. Mu envelopuyo munali ndalama zokwanira kumuthandiza kwa miyezi ingapo uku akuchita upainiya. Horst anaona kuti mphatso imeneyi unali umboni wakuti Yehova amusamalira. Choncho iye anakhala akuika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba kwa moyo wake wonse.—Mal. 3:10.
16. Kodi kuganizira chitsanzo cha Petulo komanso zimene analemba kungatithandize bwanji?
16 Petulo ayenera kuti ankasangalala akaganizira kuti Yesu sanamuchokere ngati mmene iye anamupemphera. Khristu anapitiriza kuphunzitsa Petulo kuti akhale mtumwi wokhulupirika komanso chitsanzo chabwino kwa Akhristu. Tikhoza kuphunzira zambiri pa zimene Petulo anaphunzitsidwa. Iye anafotokoza zimene anaphunzirazo m’makalata awiri ouziridwa omwe analembera mipingo ya m’nthawi yake. Munkhani yotsatira tidzakambirana mfundo zina zopezeka m’makalatawa komanso mmene tingazigwiritsire ntchito masiku ano.
NYIMBO NA. 126 Khalani Maso, Limbani M’chikhulupiriro, Khalani Amphamvu
a Nkhaniyi yakonzedwa kuti itsimikizire anthu amene akulimbana ndi mavuto enaake kuti akhoza kuthana nawo n’kupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika.
b Malemba ambiri munkhaniyi achokera mu Uthenga Wabwino wa Maliko. Zikuoneka kuti iye analemba zimene anauzidwa ndi Petulo, yemwe analipo pa nthawi yomwe zinthuzo zinkachitika.
c Onani mbiri ya moyo wa M’bale Horst Henschel munkhani yakuti, “Ndinalimbikitsidwa ndi Kukhulupirika kwa Banja Lathu kwa Mulungu,” mu Galamukani! ya March 8, 1998.
d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Chithunzi choyerekezerachi chikusonyeza kuti makolo a M’bale Horst Henschel ankapemphera naye komanso kumulimbikitsa kuti akhalebe wokhulupirika.