Wolembedwa ndi Luka
5 Nthawi inayake, gulu la anthu linkamvetsera pamene Yesu ankaphunzitsa mawu a Mulungu mʼmphepete mwa nyanja ya Genesarete*+ ndipo anthuwo ankamupanikiza. 2 Ndiyeno iye anaona ngalawa ziwiri ataziimika mʼmphepete mwa nyanjayo, koma asodzi anali atatsikamo ndipo ankachapa maukonde awo.+ 3 Choncho iye analowa mʼngalawa imodzi, imene inali ya Simoni ndipo anamupempha kuti aisunthire mʼmadzi pangʼono. Kenako anakhala pansi mʼngalawamo nʼkuyamba kuphunzitsa gulu la anthulo. 4 Atamaliza kulankhula, anauza Simoni kuti: “Palasira kwakuya, ndipo muponye maukonde anu kuti muphe nsomba.” 5 Koma poyankha Simoni anati: “Mlangizi, ife tagwira ntchito usiku wonse koma osapha kalikonse.+ Koma popeza mwanena ndinu, ndiponya maukondewa.” 6 Atachita zimenezo, anagwira nsomba zochuluka kwambiri. Ndipo maukonde awo anayamba kungʼambika.+ 7 Choncho anakodola anzawo amene anali mʼngalawa ina kuti adzawathandize. Iwo anabweradi, ndipo nsombazo zinadzaza ngalawa zonse ziwiri, moti ngalawazo zinayamba kumira. 8 Ataona zimenezi, Simoni Petulo anagwada pamaso pa Yesu ndipo anamuuza kuti: “Ambuye, chokani pali ine pano chifukwa ndine munthu wochimwa.” 9 Simoni komanso amene anali naye limodzi anadabwa kwambiri ndi nsomba zimene anaphazo. 10 Komanso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo,+ amene ankapha nsomba limodzi ndi Simoni anadabwa kwambiri. Koma Yesu anauza Simoni kuti: “Usachite mantha. Kuyambira lero uzisodza anthu amoyo.”+ 11 Choncho ngalawazo anafika nazo kumtunda, ndipo iwo anasiya chilichonse nʼkumutsatira.+
12 Nthawi inanso pamene anali mumzinda wina, anakumana ndi munthu wakhate thupi lonse. Munthuyo ataona Yesu, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi ndipo anamupempha kuti: “Ambuye, ndikudziwa kuti ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”+ 13 Choncho Yesu anatambasula dzanja lake nʼkumukhudza ndipo ananena kuti: “Inde ndikufuna. Khala woyera.” Nthawi yomweyo khate lakelo linatha.+ 14 Kenako analamula munthuyo kuti asauze aliyense. Ndiyeno anamuuza kuti: “Koma upite ukadzionetse kwa wansembe, ndipo ukapereke nsembe ya kuyeretsedwa kwako, monga mmene Mose analamulira,+ kuti ikhale umboni kwa iwo.”+ 15 Koma mbiri yake inafalikira kwambiri ndipo magulu a anthu ankasonkhana pamodzi kudzamumvetsera komanso kudzachiritsidwa matenda awo.+ 16 Komabe nthawi zambiri iye ankapita kumalo kwayekha kukapemphera.
17 Tsiku lina iye akuphunzitsa, Afarisi ndi aphunzitsi a Chilamulo amene anachokera mʼmidzi yonse ya Galileya, ku Yudeya ndi ku Yerusalemu anakhala pansi pamalo omwewo. Ndipo mphamvu ya Yehova* inali pa iye kuti athe kuchiritsa.+ 18 Kenako panafika anthu atanyamula munthu wakufa ziwalo pamachira. Iwo ankafunafuna njira yoti amulowetsere mʼnyumbamo nʼkukamuika pafupi ndi Yesu.+ 19 Koma atalephera kudutsa naye chifukwa cha kuchuluka kwa anthu, anakwera padenga. Ndipo kudzera pabowo limene anapanga padengapo, anamutsitsa limodzi ndi machirawo nʼkumufikitsa pakati pa anthu amene anali pamaso pa Yesu. 20 Ataona chikhulupiriro chawo anati: “Bwanawe, machimo ako akhululukidwa.”+ 21 Kenako alembi ndi Afarisi anayamba kudzifunsa kuti: “Kodi ameneyu ndi ndani kuti azinyoza Mulungu chonchi? Winanso ndi ndani amene angakhululukire machimo kupatulapo Mulungu?”+ 22 Koma Yesu atazindikira zimene ankaganiza anawafunsa kuti: “Kodi mukuganiza chiyani mʼmitima mwanu? 23 Chosavuta nʼchiti kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka uyendeʼ? 24 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali ndi mphamvu padziko lapansi zokhululukira machimo—” kenako anauza wakufa ziwalo uja kuti: “Ndikunena ndi iwe, Nyamuka, tenga machira akowa ndipo uzipita kwanu.”+ 25 Nthawi yomweyo anaimirira onse akuona, ndipo ananyamula machira ake aja nʼkumapita kwawo, akutamanda Mulungu. 26 Ndiyeno anthu onsewo anadabwa kwambiri ndipo anayamba kutamanda Mulungu, moti anagwidwa ndi mantha. Iwo ankanena kuti: “Komatu lero ndiye taona zodabwitsa!”
27 Zimenezi zitachitika, Yesu anachokako. Kenako anaona munthu wina wokhometsa msonkho dzina lake Levi atakhala mu ofesi yokhomeramo msonkho, ndipo anamuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.”+ 28 Leviyo anasiya chilichonse ndipo ananyamuka nʼkuyamba kumutsatira. 29 Kenako Levi anakonzera Yesu phwando lalikulu kunyumba kwake. Kumeneko kunabwera anthu ambiri okhometsa msonkho komanso ochimwa ndipo ankadya* limodzi ndi Yesu komanso ophunzira ake.+ 30 Afarisi ndi alembi awo ataona izi, anayamba kungʼungʼudza nʼkufunsa ophunzira ake kuti: “Nʼchifukwa chiyani inu mumadya ndi kumwa limodzi ndi okhometsa msonkho komanso anthu ochimwa?”+ 31 Yesu anawayankha kuti: “Anthu abwinobwino safunikira dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.+ 32 Ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa kuti alape.”+
33 Iwo anamuuza kuti: “Ophunzira a Yohane amasala kudya kawirikawiri ndipo amapemphera mopembedzera. Ophunzira a Afarisi amachitanso chimodzimodzi, koma anuwa amangodya ndi kumwa.”+ 34 Yesu anawayankha kuti: “Inu simungauze anzake a mkwati kuti asale kudya pamene mkwatiyo ali nawo limodzi, mungatero ngati? 35 Koma masiku adzafika pamene mkwati+ adzachotsedwa pakati pawo. Zikadzatero, iwo adzasala kudya masiku amenewo.”+
36 Komanso anawapatsa fanizo lakuti: “Palibe amene amadula chigamba pamalaya akunja atsopano nʼkuchisokerera pamalaya akunja akale. Munthu akachita zimenezo, chigamba chatsopanocho chimachoka pansalu yakaleyo. Ndiponso chigamba cha nsalu yatsopanocho sichigwirizana ndi malaya akalewo.+ 37 Komanso palibe amene amathira vinyo watsopano mʼmatumba achikopa akale. Munthu akachita zimenezo, vinyo watsopanoyo amaphulitsa matumba achikopawo ndipo amatayika. Ndiponso matumba achikopawo amawonongeka. 38 Koma vinyo watsopano akuyenera kuikidwa mʼmatumba achikopa atsopano. 39 Munthu akamwa vinyo wakale safunanso watsopano, chifukwa amanena kuti, ‘Wakaleyu ali bwino kwambiri.’”