Moyo ndi Uminisitala za Yesu
‘Zowonadi, Munthu Uyu anali Mwana Wa Mulungu’
YESU sanakhale pamtengopo kwa nthaŵi yaitali, pamene pakati pamasana, mdima wachilendo wautali kwa maola atatu ukuchitika. Siukuchititsidwa ndi kuphimbana kwa dzuŵa ndi mwezi, popeza kuti izi zimachitika kokha nthaŵi ya mwezi watsopano, ndipo mwezi ngwaukulu kale panthaŵi ya Paskha. Kuwonjezera apa, kuphimbana kwa dzuŵa ndi mwezi kumatenga mphindi zochepa zokha. Chotero mdimawo ngochititsidwa ndi Mulungu! Mwinamwake ukuletsako anthu amene akumseka Yesu, kupangitsadi zitonzo zawo kulekeka.
Ngati mdima wachilendowo ukuchitika wolakwa winayo asanadzudzule bwenzi lake ndikupempha Yesu kuti amkumbukire, ungakhale womwe wampangitsa kulapa. Mwinamwake munali mumdimamo mmene akazi anayi, iwo ndiwo, amayi a Yesu ndi mchemwali wawo Salome, Mariya wa Magadala, ndi Mariya amayi wa mtumwi Yakobo Wamng’ono, akunka pafupi ndi mtengo wozunzirapowo. Yohane, mtumwi wokondeka wa Yesu, ali nawo.
Mtima wa amake a Yesu ‘ukupyozedwa’ motani nanga pamene akuwona mwana amene anamlera ndi kumsamalira akulenjekeka pamenepo m’nsautso! Komabe, Yesu sakulingalira za kupweteka kwake, koma ubwino wa amake. Ndi kuyesayesa kwamphamvu, iye akupukusa mutu kulinga kwa Yohane nati kwa amake: “Mkazi, taonani, mwana wanu!” Kenaka, akumapukusa mutu kulinga kwa Mariya, akuti kwa Yohane: ‘Tawona, amayi wako.’
Mwakutero Yesu akuikizira chisamaliro cha amake, omwe mwachiwonekere tsopano ali mkazi wamasiye, kwa mtumwi wake wokondedwa mwapadera. Iye akuchita zimenezo chifukwa chakuti ana ena a Mariya sanasonyezebe chikhulupiriro mwa iye. Chotero akukhazikitsa chitsanzo chabwino chakupereka osati zosoŵa zakuthupi zokha za amake komanso zauzimu.
Pafupifupi 3 koloko masana, Yesu akuti: “Ndimva ludzu.” Kenaka, akumazindikira kuti Atate wake wachotsa chitetezo kwa iye, kunena kwake titero, kotero kuti umphumphu wake uyesedwe ku mlingo womalizira, iye akuitana ndi mawu ofuula kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?” Atamva zimenezi, ena amene aimirira pafupi akudzuma kuti: ‘Tawonani, aitana Eliya.’ Panthaŵi yomweyo mmodzi wa iwo akuthamanga ndipo, akumagwiritsira ntchito chinkhupule choviikidwa m’vinyo wosasa choikidwa paphesi la hisope, anampatsa kuti amwe. Koma ena akuti: ‘Lekani; tiwone ngati Eliya adza kudzamtsitsa.’
Pamene Yesu walandira vinyo wosasayo, akulira nati: “Kwatha.” Inde, iye wamaliza zonse zimene Atate wake anamtumira padziko lapansi kudzachita. Pomalizira pake, iye akuti: “Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu wanga.” Mwakutero Yesu akupereka kwa Mulungu mphamvu yamoyo wake ndichidaliro chakuti Mulungu adzaibwezeretsanso kwa iye. Kenaka akuweramitsa mutu wake pansi namwalira.
Mphindi imene Yesu wapuma komalizira, chivomezi champhamvu chikuchitika, chikumaswa matanthwe. Chivomezicho nchamphamvu kwakuti manda okhala kunja kwa Yerusalemu akutseguka, ndipo mitembo yaponyedwa kunja. Odutsa m’njira, omwe akuwona mitembo yomwe yavumbulidwayo, akuloŵa mumzinda nasimba zinthuzi.
Kuwonjezerapo, pamphindi imene Yesu wamwalira, chinsalu chochinga chachikulu chomwe chinalekanitsa Malo Opatulika ndi Malo Opatulikitsa m’kachisi wa Mulungu chang’ambika pakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Mwachiwonekere chinsalu chochinga chokometseredwa mokongolachi nchautali wa mamita 18 ndipo ncholemera kwambiri! Chozizwitsa chochititsa manthachi sichikusonyeza kokha mkwiyo wa Mulungu motsutsana ndi akupha Mwana Wake koma chikusonyezanso kuti kuloŵa m’Malo Opatulikitsa, kumwamba kwenikweniko, kwatheketsedwa tsopano ndi imfa ya Yesu.
Eya, pamene anthu amva chivomezi ndikuwona zinthu zimene zikuchitika, akuchita mantha kwambiri. Mkulu wa asirikali yemwe amayang’anira kuphedwako akupereka ulemerero kwa Mulungu. ‘Zowonadi, munthu uyu anali Mwana wa Mulungu,’ iye akulengeza motero. Mwachidziŵikire iye analipo pamene kukhala mwana wa Mulungu kunatchulidwa pa kuzengedwa milandu kwa Yesu pamaso pa Pilato. Ndipo tsopano iye wakhutiritsidwa kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, inde, kuti iye alidi munthu wamkulu koposa yemwe anakhalapo.
Anthu enanso akuchita mantha ndi zochitika zozizwitsa zimenezi, ndipo akuyamba kubwerera kwawo akudziguguda pachifuwa, monga chisonyezero cha chisoni chawo chachikulu ndi manyazi. Omwe akuwonera patali zochitikazi ndi ophunzira aakazi ambiri a Yesu omwe akhudzidwa kwenikweni ndi zochitika zodabwitsazi. Mtumwi Yohane aliponso. Mateyu 27:45-56; Marko 15:33-41; Luka 23:44-49; 2:34, 35; Yohane 19:25-30.
◆ Kodi nchifukwa ninji kuphimbana kwa dzuŵa ndi mwezi sikungakhale kumene kwachititsa mdima wa maola atatuwo?
◆ Nthaŵi pang’ono asanafe, kodi nchitsanzo chabwino chotani chimene Yesu akupereka kwa awo okhala ndi makolo okalamba?
◆ Kodi nziti zimene ziri ndemanga zinayi zomalizira za Yesu asanamwalire?
◆ Kodi chivomezi chikuchitanji, ndipo kodi kung’ambika kwa chinsalu chochinga kukutanthauzanji?
◆ Kodi mkulu wa asirikali woyang’anira kuphedwako wayambukiridwa motani ndi zozizwitsazo?