Chiukiriro
Tanthauzo: A·naʹsta·sis, liwu Lachigiriki lotembenuzidwa kukhala “chiukiriro,” kwenikweni limatanthauza “kuimiriranso” ndipo limanena za kuuka kuchokera ku imfa. Kulongosoledwa kokwanira kwambiri kwa “chiukiriro (kuchokera kwa) akufa” kumagwiritsiridwa ntchito mobwerezabwereza m’Malemba. (Mat. 22:31; Mac. 4:2; 1 Akor. 15:12) Kwachihebri ndiko techi·yathʹ ham·me·thimʹ, limene limatanthauza “kutsitsimuka kwa wakufa.” (Mat. 22:23, mawu amtsinde, a kope la NW la Malifrensi) Chiukiriro chimaloŵetsamo kuyambiranso kugwira ntchito kwa mkhalidwe wa moyo wa munthu, mkhalidwe wa moyo umene Mulungu wausunga m’chikumbukiro chake. Mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu kwa munthuyo, munthuyo amabwezeretsedwa kaya m’thupi laumunthu kapena lauzimu ndipo komabe amakhala ndi kudziŵika kwake monga munthu, wokhala ndi umunthu umodzimodziwo ndi zikumbukiro zimene anali nazo pamene anafa. Makonzedwe a chiukiriro cha akufa ali chisonyezero chabwino kopambana cha kukoma mtima kwapadera kwa Yehova; chimasonyeza nzeru zake ndi mphamvu ndipo ndicho njira yochititsira chifuno chake choyambirira ponena za dziko lapansi kuchitika.
Kodi chiukiriro ndicho kugwirizanitsidwanso kwa moyo wauzimu ndi thupi lanyama?
Ndithudi, kuti zimenezi zikhale zotheka, anthu akafunikira kukhala ndi moyo wauzimu umene ukatha kulekana ndi thupi lanyama. Baibulo silimaphunzitsa chinthu chotero. Lingaliro limenelo linabwerekedwa kunthanthi Yachigiriki. Chiphunzitso Chabaibulo chonena za moyo chafotokozedwa patsamba 294-297. Kaamba ka umboni ponena za magwero a chikhulupiriro cha Dziko Lachikristu cha moyo wosiyana ndi thupi, wosakhoza kufa, wonani tsamba 298, 299.
Kodi Yesu anaukitsidwa m’thupi lanyama, ndipo kodi iye ali ndi thupi lotero kumwamba patsopano lino?
1 Pet. 3:18: “Kristunso adamva zoŵaŵa kamodzi chifukwa cha machimo, wolungama mmalo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m’thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu [“mwa Mzimu,” KJ; “mumzimu,” RS, NE, Dy, JB].” (Pachiukiriro chake kuchokera kwa akufa, Yesu anaukitsidwa ndi thupi lauzimu. M’malemba Achigiriki mawu akutiwo “thupi” ndi “mzimu” amaikidwa molekana lina ndi linzake, ndipo onse aŵiri ali mumpangidwe wagaramala wofanana; chotero, ngati womasulira agwiritsira ntchito kumasulira kwakuti “mwa mzimu” ayeneranso kunena mosaphonyetsa kuti “mwa thupi,” kapena ngati agwiritsira ntchito “mu thupi” ayenera kunenanso kuti “mu mzimu.”)
Mac. 10:40, 41: “Ameneyo [Yesu Kristu] Mulungu anamuukitsa tsiku lachitatu, nalola kuti awonetsedwe, si kwa anthu onse ayi, koma kwa mboni zosankhidwiratu ndi Mulungu.” (Kodi nchifukwa ninji ena nawonso sanamuwone? Chifukwa chakuti anali cholengedwa chamzimu ndipo pamene, monga momwe angelo adachitira kalero, anavala thupi lanyama kudzichititsa kuwoneka, iye anatero kokha pamaso pa ophunzira ake.)
1 Akor. 15:45: “Koteronso kwalembedwa, Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. Adamu wotsirizayo [Yesu Kristu, amene anali wangwiro monga momwe analiri Adamu polengedwa] anakhala mzimu wa kulenga moyo.”
Kodi nchiyani chimene Luka 24:36-39 amatanthauza ponena za thupi limene Yesu anaukitsidwa nalo?
Luka 24:36-39: “Pakulankhula izi iwowa [ophunzirawo], Iye anaimira pakati pawo; nanena nawo, Mtendere ukhale nanu. Koma anawopsedwa ndi kuchita mantha, nayesa ali kuwona mzimu. Ndipo anati kwa iwo, Mukhala bwanji ovutika? Ndipo matsutsano amawuka bwanji m’mitima mwanu? Penyani manja anga ndi mapazi anga, kuti ine ndine mwini: ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu ulibe mnofu ndi mafupa, monga muwona ndiri nazo ine.”
Anthu sangathe kuwona mizimu, chotero mwachiwonekere ophunzirawo analingalira kuti anali kuwona mzukwa kapena masomphenya. (Yerekezerani ndi Marko 6:49, 50.) Yesu anawauza motsimikizira kuti iye sanali mzukwa; iwo anakhoza kuwona thupi lake lanyama ndipo anakhoza kumkhudza, kugunda mafupa; iye anadyanso pamaso pawo. Mofananamo, kalero, angelo anavala matupi kuti awonedwe ndi anthu; iwo anadya, ndipo ena anafikira ngakhale pa kukwatira ndi kubala ana. (Gen. 6:4; 19:1-3) Pambuyo pa chiukiriro chake, Yesu sanawonekere nthaŵi zonse m’thupi lofananalo laumunthu (mwinamwake kukhomereza m’maganizo mwawo chenicheni chakuti iye panthaŵiyo anali mzimu), ndipo chotero sanazindikiridwe mwamsanga ngakhale ndi atsamwali ake apafupi. (Yoh. 20:14, 15; 21:4-7) Komabe, mwa kuwonekera kwake kwa iwo mobwerezabwereza m’matupi ovalidwawo ndiyeno kunena ndi kuchita zinthu zimene zikamdziŵikitsa kukhala Yesu amene iwo anamdziŵa, analimbikitsa chikhulupiriro chawo m’chenicheni chakuti iye anaukitsidwadi kwa akufa.
Ngati ophunzirawo anali atawonadi Yesu m’thupi limene iye tsopano ali nalo kumwamba, Paulo pambuyo pake sakanatchula Kristu wolemekezedwayo kukhala “chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe [cha Mulungu],” chifukwa chakuti Mulungu ndiye Mzimu ndipo sanakhalepo konse m’thupi.—Aheb. 1:3; yerekezerani ndi 1 Timoteo 6:16.
Pamene tiŵerenga mbiri ya kuwonekera kwa Yesu pambuyo pa chiukiriro, timathandizidwa kuizindikira bwino lomwe ngati tikumbukira 1 Petro 3:18 ndi 1 Akorinto 15:45, wogwidwa mawu patsamba 107, 108.
Wonaninso tsamba 431, 432, pamutu wakuti “Yesu Kristu.”
Kodi ndani amene adzaukitsidwa kuti akakhale ndi moyo wakumwamba limodzi ndi Kristu, ndipo kodi iwo akachitanji kumeneko?
Luka 12:32: “Musawopa, kagulu kankhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani ufumu.” (Amenewa sakuphatikizapo onse amene asonyeza chikhulupiriro; chiŵerengerocho nchochepa. Kukhala kwawo kumwamba kuli ndi chifuno.)
Chiv. 20:4, 6: “Ndinawona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiŵeruziro; . . . wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nawo pakuuka koyamba; pa iwoŵa imfa yachiŵiri iribe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi iye zaka chikwizo.”
Wonaninso tsamba 203-210, pamutu wakuti “Kumwamba.”
Kodi oukitsidwira kumoyo wakumwambawo potsirizira pake adzakhala ndi matupi anyama ovekedwa ulemerero kumeneko?
Afil. 3:20, 21: “Ambuye Yesu Kristu . . . adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake laulemerero monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nawo zinthu zonse.” (Kodi zimenezi zitanthauza kuti liri thupi lawo lanyama limene potsirizira pake lidzapangidwa kukhala laulemerero kumwamba? Kapena kodi kumatanthauza kuti, mmalo mwa kukhala ndi thupi lanyama lopepulidwa, iwo adzavekedwa thupi laulemerero lauzimu pamene aukitsidwira kumoyo wakumwamba? Imani lemba lotsatirali liyankhe.)
1 Akor. 15:40, 42-44, 47-50: “Palinso matupi a m’mwamba, ndi matupi apadziko: koma ulemerero wa lam’mwamba ndiwina, ndi ulemerero wa lapadziko ndiwinanso. Chomwechonso kudzakhala kuuka kwa akufa. . . . Lifesedwa thupi lachibadidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. . . . Munthu woyambayo [Adamu] ali wapansi, wanthaka. Munthu wachiŵiri [Yesu Kristu] ali wakumwamba. Monga wanthakayo, ateronso anthaka; ndi monga wakumwamba, ateronso akumwamba. Ndipo monga tavala fanizo la wanthakayo, tidzavalanso fanizo la wakumwambayo. Koma ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kuloŵa ufumu wa Mulungu.” (Panopa palibe kuthekera kwa kusanganikirana kulikonse kwa mitundu iŵiri ya matupi kapena kumka ndi thupi lanyama kumwamba.)
Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera chimene chiukiriro chidzatanthauza kwa anthu onse?
Yohane 11:11, 14-44: “[Yesu anati kwa ophunzira ake:] Lazaro bwenzi lathu ali mtulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take. . . . Yesu anati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira. . . . Pamene Yesu anadza, anapeza kuti [Lazaro] pamenepo atakhala m’manda masiku anayi. . . . Yesu anati kwa iye [Marita, mlongo wake wa Lazaro] ine ndine kuuka ndi moyo. . . . Anafuula ndi mawu aakulu, Lazaro, tuluka. Ndipo womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu zakumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nawo, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.” (Ngati Yesu anali ataitana Lazaro kuchoka m’mkhalidwe wadalitso m’moyo wina, zimenezo sizikanakhala kusonyeza chifundo. Koma kuukitsa Lazaro kwa Yesu kuchokera kumkhalidwe wopanda moyo kunali kusonyeza chifundo kwa onse aŵiri iye ndi alongo ake. Kachiŵirinso Lazaro anakhala munthu wamoyo.)
Marko 5:35-42: “Anafika a kunyumba yamkulu wa sunagoge, nanena, kuti, Mwana wako wafa; uvutiranjinso mphunzitsi? Koma Yesu wosasamala mawu olankhulidwawo, ananena kwa mkulu wa sunagoge, Usawope, khulupirira kokha. . . . Natenga atate wa mwana ndi amake, ndi ajawo anali naye, naloŵa mmene munali mwanayo. Ndipo anagwira dzanja lake la mwana, nanena kwa iye, Talita koumi; ndiko kunena kosandulika, Buthu, ndinena ndi iwe, Uka. Ndipo pomwepo buthulo linauka, niliyenda; pakuti linali lazaka khumi ndi ziŵiri. Ndipo anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukulu.” (Pamene chiukiriro cha anthu onse chichitika padziko lapansi mkati mwa Kulamulira kwa Kristu kwa Zaka Chikwi, mosakaikira mamiliyoni ambiri a makolo ndi ana awo adzasangalala kwambiri pamene agwirizanitsidwanso.)
Kodi nziyembekezo zotani zimene zidzayembekezera oukitsidwira kumoyo padziko lapansi?
Luka 23:43, NW: “Ndinena ndi iwe lerolino, Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Dziko lonse lapansi lidzasandulizidwa kukhala paradaiso mu ulamuliro wa Kristu monga Mfumu.)
Chiv. 20:12, 13: “Ndinawona akufa, aakulu ndi aang’ono alinkuima kumpando wachifumu; ndipo mabukhu anatsegulidwa; ndipo bukhu lina linatsegulidwa, ndiro la moyo; ndipo akufa anaŵeruzidwa mwazolembedwa m’mabukhu, monga mwa ntchito zawo. . . . Ndipo anaŵeruzidwa yense monga mwa ntchito zake.” (Mwachiwonekere kutsegulidwa kwa mipukutuyo kumasonya kunthaŵi ya kuphunzira chifuniro cha Mulungu, mogwirizana ndi kunena kwa Yesaya 26:9. Chenicheni chakuti “mpukutu wa moyo” ukutsegulidwa chikusonyeza kuti pali mpata kaamba ka awo olabadira maphunzirowo kuchititsa maina awo kulembedwa mu mpukutuwo. Patsogolo pawo pali chiyembekezo cha moyo wamuyaya mu ungwiro waumunthu.)
Wonaninso tsamba 376-380, pamutu wakuti “Ufumu.”
Kodi ena adzangoukitsidwira kuti apatsidwe chiŵeruzo ndiyeno nkuloŵa mu imfa yachiŵiri?
Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la Yohane 5:28, 29? Amati: “Onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, ku kuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa ku kuuka kwa kuŵeruza.” Zimene Yesu panopa adanena ziyenera kuzindikiridwa mothandizidwa ndi chivumbulutso chapambuyo pake chimene anapatsa Yohane. (Wonani Chivumbulutso 20:12, 13, chogwidwa mawu pamwambapa.) Ponse paŵiri awo amene poyamba anachita zabwino ndi awo amene poyamba anachita zinthu zoipa “adzaŵeruzidwa mogwirizana ndi ntchito zawo.” Ntchito zanji? Ngati titi titenge lingaliro lakuti anthu anatsutsidwa pamaziko antchito zawo za moyo wapapitapo, kumeneko kukakhala kosagwirizana ndi Aroma 6:7 amene amati: “Iye amene anafa anamasulidwa kuuchimo.” Kukakhalanso kopanda tanthauzo kuukitsa anthu kwa akufa kuchitira kokha kuti awonongedwe. Chotero, pa Yohane 5:28, 29a, Yesu anali kusonya mtsogolo ku chiukiriro; pamenepa, m’mbali yotsala ya vesi 29 iye anali kulongosola chotulukapo pambuyo pakufikitsidwa kuungwiro waumunthu ndi kukhala atapambana chiŵeruzo.
Kodi nchiyani chimene Chivumbulutso 20:4-6 chimasonyeza ponena za awo amene adzaukitsidwira padziko lapansi?
Chiv. 20:4-6: “Ndinawona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiŵeruziro; ndipo ndinawona mizimu ya iwo amene anawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mawu a Mulungu . . . anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Kristu zaka chikwi. (Otsala a akufa sanakhalanso ndi moyo kufikira kudzatha zaka chikwi.) Ndiko kuuka kwa akufa koyamba. Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nawo pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yachiŵiri iribe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi Akristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi iye zaka chikwizo.”
Mawu oyamba a vesi 5 mu NW ndi Mo aikidwa m’bokosi kuthandiza woŵerenga kugwirizanitsa zotsatira m’mawu oikidwa m’bokosiwo ndi apamwamba pawo. Monga momwe kwalongosoledwera momvekera bwino, saali “otsala a akufa” amene ali ndi mbali m’chiukiriro choyamba. Chiukiriro chimenecho ncha olamulira ndi Kristu kwazaka chikwi. Kodi zimenezi zitanthauza kuti palibe anthu ena amene adzakhala ndi moyo mkati mwa zaka chikwizo kusiyapo awo amene adzalamulira kumwamba ndi Kristu? Ayi; chifukwa chakuti, ngati zinali choncho, kukatanthauza kuti panalibe munthu amene iwo anali kutumikirako monga ansembe, ndipo ulamuliro wawo ukanakhala chiunda chapululu.
Pamenepa, kodi ndani, amene ali “otsala a akufa”? Ndiwo anthu onse amene anafa chifukwa cha imfa ya Adamu, ndi awo amene, ngakhale kuli kwakuti ali opulumuka chisautso chachikulu kapena amene angabadwe mkati mwa Zaka Chikwi, afunikira kumasulidwa ku ziyambukiro zodzetsa imfa za uchimo wotero.—Yerekezerani ndi Aefeso 2:1.
Kodi “sanakhalanso ndi moyo” kufikira kudzatha zaka chikwi mu lingaliro lotani? Zimenezi sizitanthauza chiukiriro chawo. ‘Kukhala kwawo ndi moyo’ kumeneko kumaphatikizapo zambiri koposa kukhalako kokha monga anthu. Kumatanthauza kupeza ungwiro waumunthu, kumasuka ku ziyambukiro zonse zauchimo wa Adamu. Wonani kuti kutchulidwa kwa mfundoyi m’vesi 5 kukuwonekera mwamsanga vesi lapamwambalo litangonena kuti awo amene adzakhala kumwamba “anakhala ndi moyo.” M’chochitika chawo kumatanthauza moyo wopanda ziyambukiro zonse zauchimo; iwo ayanjidwadi mwapadera ndi kusakhoza kufa. (1 Akor. 15:54) Pamenepa, ponena za “otsala a akufa,” kuyenera kutanthauza chidzalo cha moyo muungwiro waumunthu.
Kodi ndani amene adzaphatikizidwa m’chiukiriro chapadziko lapansi?
Yoh. 5:28, 29: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu [mawu a Yesu] nadzatulukira.” (Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “manda” siliri mu mpangidwe wa zochuluka wa liwulo taʹphos [lithinda, malo a munthu mmodzi oikira maliro] kapena haiʹdes [kumanda, manda onse a anthu akufa] koma liri mu mpangidwe wa zochuluka m’kalankhulidwe kagaramala ka mne·meiʹon [chikumbukiro, manda achikumbukiro]. Chigogomezero chikuikidwa pa kusunga chikumbukiro cha munthu wakufa. Osati awo amene chikumbukiro chawo chinafafanizidwa m’Gehena chifukwa cha machimo osakhoza kukhululukidwa koma anthu okumbukiridwa ndi Mulungu adzaukitsidwa ali ndi mwaŵi wa kukhala ndi moyo kosatha.—Mat. 10:28; Marko 3:29; Aheb. 10:26; Mal. 3:16.)
Mac. 24:15: “Ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Ponse paŵiri awo amene anakhala ndi moyo mogwirizana ndi njira zolungama za Mulungu ndi anthu amene, chifukwa cha kusadziŵa anachita zinthu zosalungama adzaukitsidwa. Baibulo silimayankha mafunso athu onse akuti kaya anthu enieni akutiakuti amene anafa adzaukitsidwa. Koma tingathe kukhala ndi chidaliro cha kuti Mulungu, amene amadziŵa maumboni onse, adzachita mosasankha, pamene chiŵeruzo cholungama chidzafeŵetsedwa ndi chifundo zimene sizimanyalanyaza miyezo yake yolungama. Yerekezerani ndi Genesis 18:25.)
Chiv. 20:13, 14: “Nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali m’menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake. Ndipo imfa ndi Hade zinaponyedwa m’nyanja ya moto. Iyo ndiyo imfa yachiŵiri, ndiyo nyanja ya moto.” (Chotero, awo amene imfa yawo inachititsidwa ndi uchimo wa Adamu adzaukitsidwa, kaya anakwiriridwa panyanja kapena m’Hade, manda a anthu onse akufa padziko lapansi.)
Wonaninso mutu waukulu wakuti “Chipulumutso.”
Ngati mabiliyoni ati adzaukitsidwe kwa akufa, kodi onsewo adzakhala kuti?
Kuyerekezera kokulira kwa chiŵerengero cha anthu amene anayamba akhala ndi moyo padziko lapansi ndiko 20 000 000 000. Monga momwe tawonera, sionse a amenewa adzaukitsidwa. Koma, ngakhale ngati tingayerekezere kuti iwo akatero, pakakhala malo okwanira. Panthaŵi ino, mtunda wa dziko lapansi uli pafupifupi masikweya mailo 57 000 000 (147 600 000 sq km). Ngati theka la malowo linapatulidwira zifuno zina, pakakhalabe yochepera pang’ono ekala imodzi (c. 0.37 ha) pamunthu mmodzi, imene ingagaŵire chakudya choposa chokwanira. Choputira kupereŵera kwa chakudya kulipoku sindicho kusakhoza kwa dziko lapansi kutulutsa zokwanira ayi koma, mmalo mwake, mikangano yandale zadziko ndi umbombo wa zamalonda.
Wonaninso tsamba 135 pamutu wakuti “Dziko Lapansi.”