Lingaliro la Baibulo
Kodi Mdyerekezi Alikodi?
PAMENE mudali mwana, kodi mudawopapo mdima? Mwinamwake munkalingalira kuti chirombo chinabisala panja pa zenera lanu, chikumadikirira kukutsompholani kwa makolo anu. Tsopano monga mkulu, wokhoza kuŵerenga chidziŵitso chenicheni ndi kulingalira mwaufulu, mantha anu apaubwana amakhala opanda pake. “Chotero,” osuliza ena amatero, “bwanji osapita patsogolo pang’ono ndi kuika Mdyerekezi mu mkhalidwe umodzimodziwo—kusakhala weniweni monga chirombo cha m’malingaliro a mwana?”
Kulibe Mdyerekezi weniweni? Chimenecho ndicho chimene kabukhu kena kachipembedzo kakukutsimikizirani kuti: “Baibulo silimadziŵa chirichonse ponena za chirombo choterocho cha kuipa” ndipo, “M’mawu akuti Mdyerekezi ndi Satana tiri ndi . . . lingaliro la chimo ndi kuipa zimene munthu amabadwa nazo monga cholowa.” Kapena monga mmene mphunzitsi wa Sande sukulu mu United States akuchiikira icho kuti: “Anthu ndiwo ali ziwanda.” Kodi zonsezi zikuwoneka zopepuka kwambiri—kapena zopepuka mopambanitsa?
Kulongosola Mkhalidwe wa Anthu
Ngati anthufe ndife ziwanda, pamenepo kodi nchifukwa ninji chifupifupi tonsefe timasonyeza kudera nkhaŵa kaamba ka ubwino wa banja lathu? Mwachitsanzo, anthu ambiri yense payekha amapereka chakudya kaamba ka mabanja awo; iwo samadziikira paizoni mwadala, ndipo amapewa ngozi zowopsyeza moyo. Palibe chauchiwanda ponena za zimenezo! Komabe, pamene anthu amodzimodziwa achita mogwirizana monga mitundu, chinachake chimatsekereza kawonedwe kawo ka ubwino wa onse. Monga mitundu, iwo amalola chakudya chotsala kuola m‘malo modyetsa anthu awo anjala. Iwo amaipitsa malo ozungulira a dziko lapansi. Iwo amadzikonzekeretsa ndi zida kaamba ka chiwonongeko cha onse—nkhondo ya nyukiliya. Kachitidwe ka kudziwononga kwaumwini, nchachilendo chotani nanga!
Kodi n’chisonkhezero chiti chomwe chiri ndi liwongo la mbali yoipa imeneyi ya mkhalidwe wa munthu? Malingaliro aunyinji? Atsogoleri osalingalira oŵerengeka? Ndithudi choposa apa chikuloŵetsedwamo. Baibulo lokha limazindikiritsa winawake amene “wachititsa khungu maganizo” a “dongosolo la zinthu” la dziko lonse lapansi losakhulupirira. Ndani? “Iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse.” Iye akuyendetsa mtundu wa anthu wolinganizidwa mwachipambano kotero kuti Baibulo limamutcha “mulungu” wa dongosolo iri lazinthu.—2 Akorinto 4:4; Chibvumbulutso 12:9.
“Mulungu” ameneyu sali chirombo chowopsya chobisala panja pa zenera lanu. Koma iye ali wandale zadziko wochenjera ndi wamphamvu, cholengedwa chauzimu chosawoneka ndi maso, amene, m’kuyesera kopanda chipambano kuti apeze chiyanjo cha Yesu, anakhoza kumpatsa Yesu ufumu uliwonse wa dziko. (Luka 4:6, 7) Mwachiwonekere, Satana adapatsapo mphamvu yoteroyo kwa ena asadaipatse kwa Yesu, popeza kuti bukhu la Baibulo la Danieli limavumbula kuti monga nduna zazikulu, angelo achipanduko analandira ulamuliro pa maufumu a dziko—ndi maina aulemu onga “kalonga wa Perisiya,” ndi “kalonga wa Helene.”—Danieli 10:20, 21.
Chotero, Satana wapanga gulu lalikulu—monga ponse paŵiri “wolamulira wa dziko [lowoneka]” ndi “wolamulira wa ziwanda [zosawoneka].” (Yohane 14:30; 16:11; Mateyu 12:24) Chidziŵitso chimenechi, chakuti Mdyerekezi akutsogolera gulu la dziko lonse, chimalongosola zambiri.
Chifukwa Chake Iye Akutsogolera Gulu
Monga mmene mkulu wa upandu wolinganizidwa angayang’anire machitidwe ochuluka osakhala alamulo—mankhwala ogodomalitsa, machitachita a chigololo, umbala, kutchova njuga, kuba, ndi zina zotero—popanda kudzivumbula iyemwini kwa atumiki ake onse, chimodzimodzinso Satana amagwiritsira ntchito gulu kulamulira anthu ochuluka kwambiri amene iye yekha sangakhoze. Cholinga chake? Pambali pa kuvutitsa anthu, iye ndi ziwandazo amachitira unyinji wa anthu monga ngati kuti anali gulu la ng’ombe. Palibe chifukwa cha kutsogozera aliyense payekha. Koma kungotembenuza oŵerengeka okhala kutsogolo kwa khamulo, ndipo unyinji wonse udzatsatira. Ndiyeno n’kusumika pa osokera.
Inde, Mdyerekezi alidi weniweni, koma mawonekedwe ake enieni sali ofananadi ndi zolembedwa zimene timawona m’zithunzi zoseketsa kapena nthanthi zosazindikirika bwino za akatswiri a maphunziro a zaumulungu. Zosazindikirika bwino? Inde, monga mmene bukhu lakuti Satan, A Portrait likudziŵitsira kuti: “Kukhulupirira mwa Satana kunakhala kosawonekera bwino” m’zaka za zana la 19, ndipo akatswiri a maphunziro a zaumulungu “anayesera kumlongosola Satana monga chinachake chosakhala munthu wauzimu.”
Kodi Ndani Amene Akunena Chowonadi Ponena za Mdyerekezi?
Kuchipeza kukhala chosavuta kukaikira chimene Baibulo limanena pa za Mdyerekezi kwa zipembedzo zamakono kwapanga chitaganya chokonda zinthu zakuthupi chimene chakhala chosatsimikiza ponena za Mulungu iyemwini. “Lerolino,” akutero Ruth Ansher m’bukhu lake lakuti The Reality of the Devil, “Mdyerekezi wazimiririka ndipo . . . Mulungu iyemwini wachoka m’malo a kuzindikiridwa.”
Mwakukaikira lingaliro la Baibulo, “akatswiri” achipembedzo amakono asuliza nsonga imodzi imene imaika mbiri yakale m’malo oyenera. Monga mmene wolemba maseŵero wa ku Romania Eugène Ionesco anavomerezera ku nyuzipepala ya ku Germany kuti: “Mbiri yakale ikanakhala yosakhoza kumveka ngati tinachotsamo zinthu zauchiwanda.”—Welt am Sonntag, September 2, 1979.
Kodi wina aliyense angalimbe mtima kuchirikiza chowonadi ponena za thayo la Mdyerekezi mkati mwa vuto la lerolino la dziko lonse? Momvekera, inde! Lingalirani “Chilengezo Chotsutsa Satana koma Choyanja Yehova” chotengedwa mwachivomerezo cha onse pa msonkhano wa mu 1928. Icho chinasonkhezera Mboni za Yehova kulengeza, monga kufuula kwa nkhondo motsutsana ndi mdani wa munthu, Satana, kuti nkhondo yaikulu yomadzayo ya Armagedo posachedwapa idzaimitsa Satana ndi gulu lake loipa.
Mowonadi, mbiri yakale imachitira umboni kuti Mdyerekezi ali mdani weniweni kwa aliyense wa ife. Komabe, momvekera, Yehova Mulungu sanatisiye tokha. Bwanji osaphunzira zowonjezereka? Zimapinduladi kudziŵa mdani wathu, “kuti asatichenjerere Satana; pakuti sitikhala osadziŵa machenjerero ake.”—2 Akorinto 2:11.
[Mawu Otsindika patsamba 13]
“Lerolino Mdyerekezi wazimiririka ndipo . . . Mulungu iyemwini wachoka m’malo a kuzindikiridwa.”
[Chithunzi patsamba 12]
Mdyerekezi weniweni sali wofananadi ndi zithunzi zachipembedzo kapena nthanthi zaumulungu zosamvekera bwino
[Mawu a Chithunzi]
Gustave Doré