Ana Opanda Kokhala—Kodi Pali Yankho?
ANTHU amene amasamaladi anthu anzawo sangafune kulefuka ngati kuti palibe chirichonse chowonjezereka chomwe chingachitidwe kaamba ka ana opanda kokhala. Iwo amazindikira kuti ana a m’makwalala amafuna zoposa pa kukhala ndi nyumba yokha. Ana amapambana atakhala ndi mtendere wamaganizo, ntchito yosangalatsa, umoyo wabwino, ndi kudzidalira. Amuna ndi akazi opanda dyera amadzipereka iwo eni mofunitsitsa m’zikondwerero za opanda kokhala, ndipo chimenecho nchoyamikirika. Koma mosasamala kanthu za kuyesayesa kwawo, vuto la ana a m’khwalala likuwumirirabe.
Chifukwa chiri chakuti dongosolo lomwe liripoli lomwe likupitiriza ndi mikhalidwe imene ikuturutsa ana opanda kokhala silingakonzedwe. Iyo liri ngati galimoto yowonongeka ku mlingo wosakonzekanso. Titayang’anizana ndi nsonga, kodi sitiyenera kuzindikira kuti kuyesayesa kwa munthu kokha sikungabweretse nkomwe chitaganya cholungama cha anthu?
Ngakhale ndi tero, mosangalatsa, kusintha kuli kothekera—koma osati ndi manja a anthu. Kokha Mulungu Wamphamvuyonse ndi amene ali ndi kuthekera ndi nzeru za kuchotserapotu chimene chiri chovulaza padziko lapansi. Mawu Ake, Baibulo, amatiuza ponena za kulamulira kochitidwa ndi Ufumu wake wakumwamba ndi mmene udzakwaniritsira zikhumbo za anthu kaamba ka mikhalidwe yolungama pompano padziko lapansi.—Danieli 2:44.
Mulungu Amasamala
Kodi mukuganiza kuti nchothekera kwa Mulungu kuchotsa dongosolo lamakonoli ndi kuyambitsa njira yatsopano ya moyo? Ngati ndi tero, kumbukirani kuti osati kokha chipulumuko cha anthu koma, pamwamba pa zonse, dzina la Yehova Mulungu likuphatikizadwapo. Pokhala Mlengi, chitsanzo chokwezeka kwenikweni cha dongosolo ndi kusunga nthaŵi, akutitsimikizira kuti adzachitapo kanthu m’nthaŵi yake ndi njira, ndipo ichi adzachichita kupyolera mu Ufumu wake. M’chenicheni, Ufumu umenewo suli chinachake chosatsimikizirika ndi chongopeka koma liri boma lakumwamba, lokhoza kupereka uyang’aniro ndi malangizo opita patsogolo ochita ndi zosowa zenizeni za anthu.—Yesaya 48:17, 18.
Mwana wopanda kokhala angaike mumtima mawu a Davide pa Salmo 27:10: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amai wanga, koma Yehova anditola.” Chirinso cholimbikitsa kudziwa kuti mkhalidwe wapansi m’dziko sumaletsa winawake kuphunzira ponena za chifuno cha Mulungu. Miyambo 22:2 ikunena kuti: “Wolemera ndi wosauka akumana, Wolenga onsewo ndiye Yehova.” Inde, osauka, atakhala owona mtima, angakhale otsimikiziridwa kuti Yehova Mulungu ali wofunitsitsa kuwathandiza.—Salmo 10:14, 17.
Yehova ali wokondweretsedwa m’kakhalidwe kathu kabwino ndipo amadziwa mokhutiritsira zikhumbo zathu zolondola. Panthawi ina iye anafunsa Aisraeli kupyolera mwa mneneri Yesaya kuti: “Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha? . . . Kodi sindiko kupatsa chakudya chako kwa anjala, ndikuti ubwere nawo kunyumba kwako aumphawi [anthu opanda kokhala, NW]? Pakuwona wamaliseche kuti umuveke?” (Yesaya 58:6, 7) Uku ndiko kulinganiza ndi chilungamo zimene Mulungu adzabweretsa kupyolera m’boma lake la Ufumu. Palibe aliyense amene adzanyalanyazidwa kapena kuchitiridwa ngati kuti sanali kanthu. Chotero, Salmo 145:19 ikutidziŵitsa kuti: “Adzachita chokhumba iwo akumuwopa; nadzamva kufuula kwawo, nadzawapulumutsa.” Chikondi cha pa Mulungu ndi anthu anzathu chidzakhala magwero aakulu ogwirizanitsa banja la munthu. Monga choturukapo, vuto la ana opanda kokhala lidzathetsedwa. Palibe aliyense amene adzasiidwa yekha!
Kodi Kupanda Ungwiro Kwa Munthu Kudzatsekereza Chifuno cha Mulungu?
Ayi, zikhoterero zoipa za munthu sizidzaloledwa kutsekereza chifuno cha Yehova cha kusintha dziko lapansi kukhala paradaiso ya chisangalalo. Awo amene ali ndi mwaŵi wa kukhala mu dongosolo latsopano la Mulungu, kaya chifukwa chopulumuka Armagedo, monga mmene zalongosoledwera m’Baibulo, kapena chifukwa cha kuwukitsidwa kuchokera kwa akufa kukhalanso ndi moyo padziko lapansi, adzalimbikitsidwa kuchita zabwino zawo zothekera.—Yohane 5:28, 29; Chibvumbulutso 16:14, 16.
Palibe aliyense amene akuvomereza amene adzapeza ntchito yake kukhala yachabe. Ntchito yake idzafupidwa mofananamo. Chonde, mvanitu lonjezo la Mulungu: “Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo. Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka; pakuti iwo ndiwo mbewu ya odalitsidwa a Yehova, ndi obadwa awo adzakhala pamodzi ndi iwo.” (Yesaya 65:22, 23) Kodi inu ndi banja lanu simungakonde kuwona kukwaniritsidwa kwa mawu amenewa? Ndipo ndi chisangalalo chotani nanga kudziŵa kuti panthawiyo simudzawona njala kulikonse, kusauka, kusalembedwa ntchito, kapena ana opanda kokhala!
Mosakaikira, awo omwe pakali pano adakavutikabe ndi kutsekerezedwa, monga mmene amachitira ana opanda kokhala, adzapindula mokwanira ndi madalitso a banja lachimwemwe ndi nyumba yodzetsa mpumulo. Monga mmene timaŵerengera pa Yesaya 65:17 kuti: “Zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.” Anthu amene ali ndi mwaŵi wa kudzakhala ndi moyo nthaŵiyo adzapeza kuti mikhalidwe yoipa idzakhala itatheratu ndikuti anthu a mitundu yonse, zinenero, ndi mafuko adzakhala akugwirira ntchito pamodzi mu ubale wachikondi. Magulu a mabanja amene adzapulumuka kulowa m’nthawi imeneyo mosakaikira adzapitiriza kupereka ulemerero kwa Mulungu. Salmo 37:11 ikunena za Paradaiso ya padziko lapansi limenelo kuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuruka.”
Kodi Mungadzikonzekere Motani Inueni Kaamba ka Mtsogolo?
Ngakhale tsopano lino, chiri chothekera kupeza chidziŵitso chopatsa moyo ndi kulimirira mikhalidwe yofunikira, yonga ngati chikondi ndi chifundo. Tero motani? Yehova amakonda banja la anthu, ndipo kupyolera mwa Mwana wake, Yesu Kristu, Iye ‘amakokera anthu kwa Kristu’ mwa kukumana ndi Mawu Ake ndi anthu Ake. (Yohane 6:44) Iye alinso ndi gulu pa dziko lapansi yomwe iri ndi programu yophunzitsa imene ingakuthandizeni kuchita chifuniro cha Mulungu kotero kuti mungayang’ane kutsogolo ku moyo wachimwewe ndi watanthauzo kosatha. Chotero, uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ukulalikidwa kwa amene ali m’kusowa. (Mateyu 24:14) Mawu a Mulungu akunena kuti: “Wonyoza anzake achimwa; koma wochitira osauka chifundo adala.” (Miyambo 14:21) Nchosangalatsa mtima kudziŵa kuti ngakhale amphaŵi angafikire Mulungu ngati zolinga zawo ziri zolondola. Wamasalmo analemba kuti: “Koma ine ndine wozunzika ndi waumphawi; mundifulumirire, Mulungu; Inu ndinu mthandizi wanga ndi mpulumutsi wanga; musachedwe, Yehova.”—Salmo 70:5.
Inde, Mawu a Mulungu angakupatseni chiyembekezo chenicheni kaamba ka m’tsogolo. Komabe, kugwiritsiridwa kofala kwa liwu lakuti “chiyembekezo” kaŵirikaŵiri sikumatanthauza zenizeni. Mu Brazil kaŵirikaŵiri mumamveka mawu akuti: “A esperança é a última que morre” (ofanana ndi Chicheŵa chakuti “Chiyembekezo chimabweretsa umuyaya”). Lingaliro ndilo lakukhalabe woyembekeza ngakhale patawoneka kukhala popanda maziko a iko. Mosiyanako, Malemba amapereka malingaliro amphamvu a kusungilira chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu ndi kuyembekeza m’malonjezano ake. Timawerenga pa Aroma 10:11 kuti: “Amene aliyense akhulupirira Iye, sadzachita manyazi.” Chiyembekezo chozikidwa m’Baibulo choterocho sichidzatsogolera ku kugwiritsiridwa mwala. Mongadi mmene zozizwitsa za dziko lathu lapansi ziriri zenizeni, zikumachitira umboni nzeru ndi chikondi cha Yehova, choteronso kukwaniritsidwa kwa maulosi a Baibulo kumakulolani inu kukhala ndi kapenyedwe kotsimikizirika, chiyembekezo chenicheni kaamba ka mtsogolo.—Aroma 15:13.
Ufumu wa Mulungu uli yankho lenileni la ana opanda kokhala, inde, kaamba ka onse amene amakonda zabwino. Kupeza chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo tsopano kudzakutheketsani kusangalala ndi chimwemwe ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. Kuyembekezera malonjezano amenewa sikuli kokha maloto. Monga mmene Miyambo 11:19 ikulengezera kuti: “Wolimbikira chilungamo alandira moyo.”
[Bokosi patsamba 11]
Yankho Losakhalitsa?
Dzanja lotambasulidwa la wopanda kokhala wa mawonekedwe osowa chochita lingakhale lonyansa ku mtima. Koma anthu odera nkhawa akuvutika ponena za mmene angathandizire mwana wopanda kokhala. Ndi cholinga cha kufuna kukhala wodzimva waliwongo mocheperako, anthu ena amaponyamo makobiri oŵerengeka m’zikhato za mwanayo ndi kuchokapo mofulumira. Komabe, mwaŵi ulidi wochepera kuti mphatsozo zidzagulidwa zakudya kapena chofunda. Mmalo mwake, izo zingangothera m’kugwiritsiridwa ntchito kugula mankhawala ogodomalitsa kapena zakumwa zoledzeretsa. Chotero, achikulire ena owoloŵa manja akupereka chisamaliro chawo ndi ndalama ku maprogramu ochilikizidwa ndi boma la kumaloko omwe akulingalira kuti adzathandiza ana opanda kokhala. Anthu ena amakhulupirira kuti kachitidwe kaphindu kwenikweni kali kutsogoza mwana wopanda kokhala ku gulu loyenerera kuti akathandizidwe. Mwanjirayi, nzika zodera nkhawazo zikudzimva kuti zikuyesera kupanga chitaganya chawo kukhala chaumunthu kwenikweni.
[Chithunzi patsamba 9]
“Iwo sadzawoka, ndi wina kudya.”—Yesaya 65:22
[Mawu a Chithunzi]
FAO photo
[Chithunzi patsamba 10]
“Pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga.”—Yesaya 65:22