MUTU 25
Yesu Anachitira Chifundo Munthu Wakhate N’kumuchiritsa
MATEYU 8:1-4 MALIKO 1:40-45 LUKA 5:12-16
YESU ANACHIRITSA MUNTHU WAKHATE
Pamene Yesu ndi ophunzira ake 4 ‘ankalalikira m’masunagoge a ku Galileya’ mbiri ya zimene ankachita inamveka m’madera akutali. (Maliko 1:39) Mbiriyi inafikanso mumzinda wina kumene kunali munthu amene ankadwala khate. Luka, yemwe anali dokotala, anafotokoza kuti munthuyu anali “wakhate thupi lonse.” (Luka 5:12) Matenda akhate akalowerera kwambiri m’thupi amawononga ziwalo za munthu.
Choncho munthu wakhate amene anakumana ndi Yesuyu anali womvetsa chisoni kwambiri moti sankaloledwa kukhala pafupi ndi anthu. Komanso ankafunika kufuula kuti “Wodetsedwa, wodetsedwa!” Zimenezi zinkathandiza kuti anthu asamuyandikire kuopera kuti angatengera matenda oopsawa. (Levitiko 13:45, 46) Kodi munthuyu anachita chiyani ataona Yesu? Anamuyandikira n’kugwada kenako anamupempha kuti: “Ambuye, ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”—Mateyu 8:2.
Munthuyu anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yesu. Zikuoneka kuti munthuyu ankaoneka womvetsa chisoni kwambiri chifukwa cha matendawo. Koma kodi Yesu anachita chiyani? Kodi inuyo mukanatani mukanakhala kuti munalipo? Yesu anamva chisoni moti anatambasula dzanja lake n’kukhudza munthuyo. Kenako ananena kuti: “Ndikufuna. Khala woyera.” (Mateyu 8:3) Anthu ena sanakhulupirire ataona kuti nthawi yomweyo munthu uja wachira ndipo khate lake latha.
Kodi inuyo mungakonde kukhala ndi mfumu yomvera ena chisoni komanso yofunitsitsa kuthandiza anthu ngati mmene ankachitira Yesu? Zimene Yesu anachita pothandiza munthu wakhateyu zimatitsimikizira kuti akadzayamba kulamulira monga Mfumu padzikoli, ulosi wa m’Baibulo udzakwaniritsidwa. Ulosi umenewu umati: “Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka, ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka.” (Salimo 72:13) Pa nthawi imeneyo, Yesu adzakwaniritsa cholinga chake chofuna kuthandiza anthu onse ovutika.
Kumbukirani kuti Yesu asanachiritse munthu wakhateyu, anthu ambiri ankasangalala ndi zimene Yesu ankachita atayamba kugwira ntchito yolalikira. Anthu ambiri ayenera kuti anamvanso nkhani yosangalatsa ya kuchiritsidwa kwa munthu wakhateyu. Koma Yesu sankafuna kuti anthu azimukhulupirira pongotengera zimene amva. Iye ankadziwa za ulosi umene unaneneratu kuti “mawu ake sadzamvedwa mumsewu” n’cholinga choti akope anthu. (Yesaya 42:1, 2) Chifukwa cha zimenezi, Yesu anauza munthu amene anamuchiritsa uja kuti: “Samala, usauze aliyense zimenezi, koma upite ukadzionetse kwa wansembe, ndipo ukapereke mphatso imene Mose analamula.”—Mateyu 8:4.
Koma chifukwa chakuti munthuyo anali wosangalala kwambiri kuti wachiritsidwa analephera kutsatira zimene Yesu anamuuza moti ankauza aliyense zimene zinamuchitikirazo. Zimenezi zinachititsa chidwi anthu ambiri ndipo ankafunitsitsa kudziwa zambiri za Yesu. Chifukwa cha zimenezi, Yesu anayamba kulowa mumzinda mobisa moti kwa kanthawi ndithu, ankakhala kwa yekha. Komabe, anthu ochokera m’madera osiyanasiyana ankabwerabe kuti adzawaphunzitse komanso kuwachiritsa.