Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kodi Ndani Amene Alidi Achimwemwe?
ALIYENSE amafuna kukhala wachimwemwe. Pozindikira chimenechi, phiri mwa kulongosola awo amene alidi achimwemwe. Monga momwe tingayerekezerere, chimenechi mwamsanga chikugwira chikondwerero cha omvetsera ake ambiriwo. Ndipo chikhalirechobe mawu ake oyambirira ayenera kuwonekera kukhala otsutsana kwa ambiri.
Akumalunjikitsa mawu ake kwa ophunzira ake, Yesu akuyamba mwa kumati: “Odala osauka inu; chifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu. Odala inu akumva njala tsopano; chifukwa mudzakhuta. Odala inu akulira tsopano; chifukwa mudzaseka. Odala inu, pamene anthu adzada inu, . . . kondwerani tsiku lomweli, dumphani ndi chimwemwe; pakuti wonani, mphotho zanu nzazikulu kumwamba.”
Chimenechi ndicho cholembedwa cha Luka mawu oyambirira a ulaliki wa Yesu. Koma mogwirizana ndi cholembedwa cha Mateyu, Yesu akunenanso kuti odekha mtima, achifundo, oyera mu mtima, ndi ochita mtendere ngachimwemwe. Yesu akuti, amenewa ngachimwemwe, chifukwa chakuti adzalandira dziko lapansi, adzasonyezedwa chifundo, adzawona Mulungu, ndipo adzatchedwa ana a Mulungu.
Komabe, chimene Yesu akutanthauza mwa kukhala achimwemwe, sindicho kokha kukhala osekaseka kapena ansangala, mofanana ndi pamene munthu akusewera. Chimwemwe chowona chiri chozamirapo, chiri ndi ganizo la kukhutira, lingaliro lachikhutiro ndi kukwaniritsidwa m’moyo. Chotero Yesu akusonyeza, kuti anthu amene alidi achimwemwe ali awo amene amazindikira chosowa chawo chauzimu, akumva chisoni ndi mkhalidwe wawo wa uchimo, ndi awo amene amafikira pakudziwa ndi kutumikira Mulungu. Pamenepo, ngati iwo adedwa kapena kuzunzidwa kaamba ka kuchita chifuniro cha Mulungu, ngachimwemwe chifukwa chakuti amadziwa kuti akukondweretsa Mulungu ndipo adzalandira mphotho yake ya moyo wosatha.
Komabe, unyinji wa omvetsera a Yesu, mofananadi ndi anthu ena lerolino, amakhulupirira kuti kukhala wolemera, kukhuphuka, ndi kukhala ndi zokondweretsa ndizo zimene zimapangitsa munthu kukhala wachimwemwe. Yesu amadziwa kuti siziri choncho. Posonyeza kusiyana kumene kuyenera kudabwitsa unyinji wa omvetsera ake, iye akuti:
“Tsoka inu eni chuma! Chifukwa mwalandira chisangalatso chanu. Tsoka inu okhuta tsopano! Chifukwa mudzamva njala. Tsoka inu, a kuseka tsopano! Chifukwa mudzachita maliro ndi kulira misozi. Tsoka inu, pamene anthu onse adzanenera inu zabwino! Pakuti makolo awo anawatero momwemo aneneri onama.”
Kodi Yesu akutanthauzanji? Kodi nchifukwa ninji kukhala ndi chuma, kulondola zikondwerero moseka, ndi kutamandidwa ndi anthu kumadzetsa tsoka? Chiri chifukwa chakuti pamene munthu ali nazo zinthu zimenezi ndi kuzitamandira pamenepo utumiki wa Mulungu, umene ndiwo wokha umene umabweretsa chimwemwe chowona, umasiyidwa m’moyo wake. Panthawi imodzimodziyo, Yesu sanatanthauze kuti kukhala osauka, kukhala wanjala ndi kulira mwa iko kokha kupangitsa mu nthu kukhala wachimwemwe. Komabe, kawirikawiri, anthu ovutika motero angalabadire ziphunzitso za Yesu, ndipo mwakutero angadalitsidwe mwa kukhala ndi chimwemwe chowona.
Kenako, polankhula kwa ophunzira ake, Yesu akuti: “Ndinu mchere wa dziko lapansi.” Ndithudi, iye sakutanthauza kuti, iwo ali mchere weniweni. Mmalo mwake, mchere umatetezera kuvunda. Mulu wake waukulu unaunjikidwa pafupi ndi guwa lansembe pakachisi wa Yehova, ndipo ansembe okhala pantchito anaugwiritsira ntchito kukoleretsa nsembe.
Ophunzira a Yesu ali “mchere wa dziko lapansi” nchakuti ali ndi chisonkhezero chotetezera pa anthu. Ndithudi, uthenga umene amanyamula udzatetezera miyoyo ya onse amene amaulabadira! Udzabweretsa m’miyoyo ya anthu otero mikhalidwe yokhalitsa, kudalirika ndi kukhulupirika, kutetezera kuvunda kulikonse kwauzimu ndi kwa makhalidwe mwa iwo
“Ndinu kuunika kwadziko,” Yesu akuuza ophunzira ake. Nyali simayatsidwa ndi kuikidwa mu mtanga koma imaikidwa pa choikapo nyali, chotero Yesu akuti: “Momwemonso lolani kuunika kwanu kuwale pamaso pa anthu.” Ophunzira a Yesu amachita zimenezi mwa kuchitira umboni kwawo kwapoyera, ndiponso mwa kutumikira monga zitsanzo zowala za khalidwe limene liri logwirizana ndi malamulo a makhalidwe abwino Abaibulo. Luka 6:20-26; Mateyu 5: 3-16, NW.
◆ Kodi ndani amene alidi achimwemwe, ndipo chifukwa ninji?
◆ Kodi amalandira tsoka ndani, ndipo chifukwa ninji?
◆ Kodi ophunzira a Yesu ali mchere wa dziko lapansi ndi kuunika kwa dziko motani?