Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Onyada ndi Odzichepetsa
PAMBUYO potchula maubwino a Yohane Mbatizi, Yesu atembenukira kwa onyada, anthu akavuwevuwe omwe amazinga iye. “Mbadwo uwu,” iye akulengeza, “uli wofanana ndi ana akukhala m’mabwalo a malonda amene alikuitana anzawo, ndi kuti, ‘tinakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simunavina; tinabuma maliro, inu simunalira.’”
Kodi nchiyani chimene Yesu akutanthauza? lye akulongosola: “Yohane anadza wosadya ndiponso wosamwa, koma anthu akuti, ‘iye ali ndi chiwanda’; mwana wa munthu anadza wakudya, ndi wakumwa, ndipo iwo amati, ‘Onani munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa.’”
Chiri chosathekera kuwakhutiritsa anthu. Palibe chirichonse chowasangalatsa iwo. Yohane anakhala moyo wabwino wa kudzikana yekha monga Mnaziri, m’kusunga ulaliki wa m’ngelo wakuti “sayenera kumwa vinyo kapena chakumwa chaukali chiri chonse.” Koma anthu akunena kuti iye ali wogwidwa ndi ziwanda. Kumbali ina, Yesu amakhala ndi moyo monga anthu ena onse, wosadziletsa, ndipo iye akuimbidwa mlandu wakumwerekera.
Ha ndi anthu ovuta kusangalatsa chotani nanga! Iwo ali monga osewera nawo ena omwe anakana kuvomereza mwa kuvina pamene ana ena anayimba zitoliro kapena kukana kulira pamene anzawo analira maliro. Komabe, Yesu akunena kuti: “Nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.” Inde, chitsimikiziro—ntchito—zimatitsimikizira kuti kusinjiriridwa kwa onse awiri Yohane ndi Yesu kuli kwabodza.
Yesu akupitirira kutchula chimodzi ndi chimodzi cha chitonzo cha mizinda ya Korazini, Betsaida, ndi Kapernao, kumene anachita zambiri zantchito zake zamphamvu. Ngati akanazichita izomu mizinda yaku Foinike ya Turo ndi Sino, Yesu akuti, mizinda imeneyi ikanatembenuka mtima m’ziguduli ndi m’phulusa. Kudzudzula Kapernao, amene mwachiwonekere wakhala mudzi wake wa maziko mkati mwa utumiki wake, Yesu akulengeza: “Kudzakhala kopiririka pa dziko la Sodomy pa Tsiku la Chiweruzo kuposa iwe.”
Kodi nchiyani chimene Yesu akutanthauza ponena ichi? Mwachiwonekere iye akusonyeza kuti, mkati mwa Tsiku Lachiweruzo pamene onyada a ku Kapernao adzaukitsidwa, chidzakhala chovuta kwambiri kaamba ka iwo kuvomereza zolakwa zawo ndi kulandira Kristu kuposa mmene kudzakhalira kwa oukitsidwa a Sodomu wakale kulapa modzichepetsa ndi kuphunzira chilungamo.
Kenaka mwapoyera Yesu alemekeza Atate wake Wakumwamba. lye wafulumizidwa kuchita choncho chifukwa chakuti Mulungu amabisa chowonadi chauzimu chamtengo wapatali kuchokera kwa anzeru ndi aluntha, amavumbula zinthu zozizwitsa zimenezi kwa odzichepetsa, makanda, monga mmene kunaliri.
Pomalizira, Yesu akupereka chiitano chachitokoso: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo ine ndizakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa liri lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.”
Ndimotani mmene Yesu anaperekera mpumulo? lye amachita choncho mwakupereka ufulu kuchokera ku ukapolo ku miyambo imene atsogoleri achipembedzo asenzetsa anthu, kuphatikizapo, mwachitsanzo, lamulo lokakamiza la kusunga Sabata. Ndiponso, iye akusonyeza njira yathandizo kwa awo amene amadzimva kukhala olemedwa chifukwa cha ulamuliro wa olamulira andale zadziko ndi kwa awo omwe amadzimva kukhala olemedwa chifukwa cha machimo awo kudzera mu chikumbumtima chasautsidwa. lye akuvumbulutsa kwa anthu osautsidwa amenewa kuti ndimotani mmene machimo awo angakhululukidwire ndipo ndimotani mmene iwo angasangalalire ndi unansi wamtengo waptali ndi Mulungu.
Goli lokoma mtima limene Yesu akupereka liri kudzipereka kotheratu kwa Mulungu, kukhala okhoza kutumikira Atate wathu Wakumwamba wachikondi; ndi wachifundo. Ndipo katundu wopepuka amene Yesu akupereka kwa awo omwe akudza kwa iye kuli kumvera ziyeneretso za Mulungu kaamba ka moyo, malamulo ake, omwesiali othodwetsa. Mateyu 11:16-30; Luka 1:15; 7:31-35; 1 Yohane 5:3.
◆ Kodi ndimotani mmene mbadwo wa Yesu uliri monga ana?
◆ Kodi ndimotani mmene chikakhalira chopiririka kaamba ka Sodomu kuposa ndi Kapernao?
◆ Kodi ndi mwanjira zotani mmene anthu amazilemetsedwera, ndipo ndi thandizo lotani limene Yesu akupereka?