Mafunso Ochokera kwa Owerenga
N’chifukwa chiyani Yesu anauza mayi amene anali kudziwika monga wochimwa kuti machimo ake akhululukidwa?—Luka 7:37, 48.
Pamene Yesu ankalandira chakudya kunyumba kwa Mfarisi wina dzina lake Simoni, mayi wina ‘anagwada kumapazi a Yesu.’ Mayiyu anayamba kunyowetsa mapazi a Yesu ndi misozi yake n’kumawapukuta ndi tsitsi lake. Kenako anayamba kupsompsona mapazi akewo mwachikondi ndi kuwapaka mafuta onunkhira. Uthenga wabwino wa Luka umati, mayiyu anali “wodziwika mu mzindawo monga wochimwa.” N’zoona kuti munthu aliyense ndi wopanda ungwiro ndiponso wochimwa, koma Malemba nthawi zambiri amagwiritsa ntchito mawu amenewa pofotokoza munthu amene ali ndi mbiri yoti amachita machimo oipa kwambiri. N’kutheka kuti mayiyu anali hule. Ndiyeno Yesu anauza mayi wotereyu kuti: “Machimo ako akhululukidwa.” (Luka 7:36-38, 48) Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani? Popeza nsembe ya dipo inali isanaperekedwe, zikanatheka bwanji kuti akhululukidwe?
Mayiyu atasambitsa mapazi a Yesu n’kuwadzoza mafuta koma asanamuuze kuti machimo ako akhululukidwa, Yesu anagwiritsa ntchito fanizo pofotokoza mfundo yofunika kwambiri kwa Simoni yemwe anali mwini wa nyumba imene izi zinachitikira. Yesu anayerekezera tchimo ndi ngongole yaikulu imene munthu akufunika kubweza. Iye anauza Simoni kuti: “Amuna awiri anatenga ngongole kwa wokongoza wina. Wina anali ndi ngongole ya madinari 500, koma winayo anali ndi ngongole ya madinari 50. Atasowa chopereka, kuti abweze ngongolezo, mwini wake uja anakhululukira onsewo ndi mtima wonse. Kodi ndani mwa awiriwo amene adzam’konda koposa?” Poyankha Simoni anati: “Ndiganiza ndi amene anamukhululukira zochulukayo.” Yesu anamuuza kuti: “Wayankha molondola.” (Luka 7:41-43) Tonsefe timafunika kumvera Mulungu, ndiye tikapanda kumumvera timakhala titachimwa ndiponso titalephera kumupatsa zinthu zoyenera, choncho timakhala naye ngongole. Koma Yehova ali ngati munthu wobwereketsa ndalama yemwe amakhala wokonzeka kukhululukira ngongole. Yesu anagwiritsa ntchito mawu otanthauza ngongole pamene analimbikitsa ophunzira ake kuti azipempha Mulungu kuti: “Mutikhululukire zolakwa zathu, pakuti ifenso takhululukira amene amatilakwira.”—Mat. 6:12.
Kodi ndi zinthu ziti zimene zinkachititsa kuti Mulungu azikhululukira machimo a anthu akale? Malinga ndi chilungamo cha Mulungu, chilango cha munthu wochimwa ndi imfa. Motero Adamu anafa chifukwa cha tchimo lake. Koma m’Chilamulo chimene Mulungu anapatsa mtundu wa Isiraeli chinkanena kuti munthu wochimwa angakhululukidwe ngati atapereka nsembe ya nyama kwa Yehova. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pafupifupi zinthu zonse ziyeretsedwa ndi magazi malinga ndi Chilamulo, ndipo popanda kukhetsa magazi chikhululukiro sichichitika.” (Aheb. 9:22) Ayuda sankadziwa njira ina iliyonse kupatulapo imeneyi yoti Mulungu angakhululukire munthu. Choncho, n’zosadabwitsa kuti anthu amene analipo pa nthawiyo sanagwirizane ndi zimene Yesu anauza mayi uja. Anthu amene ankadya ndi Yesu ankadzifunsa kuti: “Kodi munthu ameneyu n’ngotani wokhozanso ngakhale kukhululukira machimo?” (Luka 7:49) Ndiye kodi zikanatheka bwanji kuti mayi amene ankadziwika kuti ndi wochimwa kwambiriyo akhululukidwe machimo ake?
Ulosi woyamba umene unanenedwa makolo athu oyambirira atangochimwa, unanena cholinga cha Mulungu kuti adzaukitsa “mbewu” imene idzalaliridwa chitende ndi Satana pamodzi ndi “mbewu” yake. (Gen. 3:15) Zimenezi zinachitika pamene Yesu anaphedwa ndi adani a Mulungu. (Agal. 3:13, 16) Magazi amene Yesu anakhetsa amagwira ntchito monga dipo lomasula anthu ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. Popeza kuti palibe chimene chingalepheretse Yehova kukwaniritsa cholinga chake, pamene anangonena mawu a pa Genesis 3:15, kwa Mulungu zinali ngati kuti dipo laperekedwa kale. Tsopano Mulungu akanatha kukhululukira anthu amene amakhulupirira malonjezo ake.
Chikhristu chisanayambe, Yehova ankaona kuti anthu ena anali okhulupirika. Ena mwa anthu amenewa ndi Enoke, Nowa, Abulahamu, Rahabi ndiponso Yobu. Iwo anali ndi chikhulupiriro ndipo ankayembekezera kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu. Yakobe yemwe anali wophunzira wa Yesu analemba kuti: “Abulahamu anakhulupirira mwa Yehova, ndipo anayesedwa wolungama.” Ponena za Rahabi, Yakobe anati: “Momwemonso, kodi Rahabi mkazi wachiwerewere uja, sanayesedwe wolungama chifukwa cha ntchito zake?”—Yak. 2:21-25.
Davide yemwe anali mfumu ya Isiraeli anachita machimo akuluakulu ambiri koma ankakhulupirira kwambiri Mulungu woona ndipo akachimwa ankalapa mochokera pansi pa mtima. Komanso Malemba amati: “Mulungu anam’pereka [Yesu] monga nsembe ya chiyanjanitso, chochitika mwa kukhala ndi chikhulupiriro m’magazi ake. Mulungu anachita izi pofuna kuonetsa chilungamo chake, chifukwa chakuti anali kukhululuka machimo amene anachitika kale, pamene iye anali kusonyeza khalidwe losakwiya msanga, pofuna kuonetsa chilungamo chake m’nyengo inoyo, kuti adzakhale wolungama ngakhale pakutcha munthu amene ali ndi chikhulupiriro mwa Yesu kukhala wolungama.” (Aroma 3:25, 26) Chifukwa cha nsembe ya dipo imene Yesu anali kudzapereka, Yehova anatha kukhululukira machimo a Davide popanda kuphwanya mfundo Zake zokhudza chilungamo.
Mosakayikira, umu ndi mmenenso zinalili ndi mkazi amene anadzoza mafuta mapazi a Yesu. Iye analidi wachiwerewere koma pa nthawiyi anali atalapa. Iye anazindikira kuti akufunika kuwomboledwa ku machimo ake ndipo zochita zake zinasonyeza kuti anadziwa kuti Yesu ndiye munthu amene Yehova wapereka kuti awombole anthu. Ngakhale kuti nsembeyo inali kudzaperekedwa m’tsogolo, zinali zosakayikitsa kuti idzaperekedwa, choncho anthu ngati mayiyu ankatha kukhululukidwa machimo awo pa maziko a nsembe imeneyo. N’chifukwa chake Yesu anauza mayiyu kuti: “Machimo ako akhululukidwa.”
Nkhaniyi ikusonyeza kuti Yesu sankasala anthu ochimwa. Iye ankawachitira zinthu zabwino. Komanso Yehova ndi wokonzeka kukhululukira anthu ochimwa amene alapa. Zimenezitu ndi zokhazika mtima pansi kwambiri kwa anthu opanda ungwirofe.
[Chithunzi patsamba 7]
Anthu awa anayesedwa olungama