Kodi Yesu Amasonyeza Bwanji Chilungamo cha Mulungu?
“Mulungu anapereka [Khristu] monga nsembe ya chiyanjanitso, chochitika mwa kukhala ndi chikhulupiriro m’magazi ake. Mulungu anachita izi pofuna kuonetsa chilungamo chake.”—AROMA 3:25.
1, 2. (a) Kodi Baibulo limatiphunzitsa kuti anthu onse ndi otani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati m’nkhani ino?
NKHANI ya m’Baibulo yonena za kupanduka kwa anthu oyamba m’munda wa Edene, ndi yodziwika kwambiri. Uchimo wa Adamu umatikhudza tonsefe monga mawu awa akunenera kuti: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo, imfayo nifalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’ (Aroma 5:12) Ngakhale titayesetsa kwambiri kuchita zabwino timalakwitsabe zinthu zina ndipo timafuna kuti Mulungu atikhululukire. Ngakhale mtumwi Paulo anadandaula kuti: “Chinthu chabwino chimene ndimafuna kuchita sindichita, koma choipa chimene sindifuna kuchita ndi chimene ndimachita. Munthu wovutika ine!”—Aroma 7:19, 24.
2 Popeza ndife anthu ochimwa timadzifunsa kuti: Zinatheka bwanji kuti Yesu abadwe opanda uchimo ndipo n’chifukwa chiyani anabatizidwa? Kodi zimene Yesu anachita pa moyo wake zinasonyeza bwanji chilungamo cha Yehova? Ndipo funso lina lofunika kwambiri ndi lakuti, kodi imfa ya Yesu inakwaniritsa chiyani?
Chilungamo cha Mulungu Chinatsutsidwa
3. Fotokozani zimene Satana anachita kuti anyenge Hava.
3 Makolo athu oyamba Adamu ndi Hava anachita zinthu mopusa pokana ulamuliro wa Mulungu. Iwo anasankha ulamuliro wa “njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana.” (Chiv. 12:9) Taganizirani mmene zimenezi zinachitikira. Satana anakayikira zoti Mulungu amalamulira mwachilungamo. Anachita zimenezi pofunsa Hava kuti: “Kodi anatitu Mulungu, usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” Poyankha Hava anabwereza lamulo lomveka bwino la Mulungu lakuti asadye zipatso za mtengo umodzi wokha chifukwa ngati atadya, adzafa. Ndiyeno Satana ananena kuti Mulungu ndi wabodza. Iye anati: “Kufa simudzafa ayi.” Ndiyeno Satana anapitiriza kunamiza Hava kuti akhulupirire kuti Mulungu ankawamana china chake chabwino ndipo ngati atadya chipatsocho adzakhala ngati Mulungu n’kumasankha okha zochita.—Gen. 3:1-5.
4. Kodi chinachitika n’chiyani kuti anthu ayambe kulamulidwa ndi Satana yemwe ndi wotsutsa?
4 Kwenikweni, Satana ankatanthauza kuti anthu akhoza kukhala osangalala kwambiri ngati sakulamulidwa ndi Mulungu. M’malo mosonyeza kuti Mulungu amalamulira mwachilungamo, Adamu anamvera mkazi wake n’kudya nawo chipatso choletsedwa. Motero Adamu anataya mwayi wokhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo anachititsa kuti tikhale akapolo a uchimo ndi imfa. Pa nthawi imodzimodziyo, mtundu wonse wa anthu unayamba kulamuliridwa ndi Satana yemwe ndi wotsutsa ndiponso “mulungu wa dziko lino lapansi.”—2 Akor. 4:4. Chipangano Chatsopano Cholembedwa mu Chichewa cha Lero.
5. (a) Kodi Yehova anakwaniritsa bwanji mawu ake? (b) Kodi Mulungu anapereka chiyembekezo chotani kwa mbadwa za Adamu ndi Hava?
5 Mogwirizana ndi zimene ananena, Yehova anaweruza Adamu ndi Hava kuti afa. (Gen. 3:16-19) Koma zimenezi sizinatanthauze kuti cholinga cha Mulungu chalephereka. Popereka chilango kwa Adamu ndi Hava, Yehova anaperekanso chiyembekezo kwa mbadwa zawo. Iye anachita zimenezi potchula cholinga chake kuti adzaukitsa “mbewu” imene Satanayo adzailalire chitende. Koma Mbewu yolonjezedwa imeneyo inali yoti idzachira, ndipo “idzalalira mutu” wa Satana. (Gen. 3:15) Baibulo limafotokoza momveka bwino nkhani imeneyi. Limanena za Yesu Khristu kuti: “Choncho, Mwana wa Mulungu anaonekera, kuti awononge ntchito za Mdyerekezi.” (1 Yoh. 3:8) Kodi khalidwe ndiponso imfa ya Yesu inasonyeza bwanji chilungamo cha Mulungu?
Zimene Ubatizo wa Yesu Unatanthauza
6. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu sanatengere uchimo wa Adamu?
6 Yesu ali munthu wamkulu, anali wofanana ndendende ndi mmene Adamu analili poyamba ali wangwiro. (Aroma 5:14; 1 Akor. 15:45) Zimenezi zikutanthauza kuti Yesu anafunika kubadwa ali wangwiro. Kodi zimenezi zikanatheka bwanji? Mngelo Gabrieli anauza Mariya, mayi a Yesu, momveka bwino kuti: “Mzimu woyera udzafika pa iwe, ndipo mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba. Pa chifukwa chimenechinso, wodzabadwayo adzatchedwa woyera, Mwana wa Mulungu.” (Luka 1:35) Mosakayikira, Yesu ali mwana, Mariya anamuuza zinthu zina zokhudza kubadwa kwake. N’chifukwa chake nthawi ina Mariya ndi bambo a Yesu omulera Yosefe, atapeza Yesu m’kachisi wa Mulungu, Yesuyo anawafunsa kuti: “Simunadziwe kodi kuti ndiyenera kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?” (Luka 2:49) Zimenezi zikusonyezeratu kuti kuyambira ali mwana, Yesu ankadziwa kuti iye ndi Mwana wa Mulungu. Choncho kusonyeza chilungamo cha Mulungu inali nkhani yofunika kwambiri kwa Yesu.
7. Kodi Yesu anali ndi chiyani chomwe chinali chamtengo wapatali?
7 Yesu anasonyeza kuti ankakonda kwambiri zinthu zauzimu, chifukwa nthawi zonse ankapita ku misonkhano yolambira Mulungu. Popeza anali ndi maganizo angwiro, iye anamvetsa bwino chilichonse chimene anamva ndiponso kuwerenga m’Malemba Achiheberi. (Luka 4:16) Iye analinso ndi chinthu china cha mtengo wapatali. Anali ndi thupi langwiro limene akanatha kulipereka nsembe m’malo mwa anthu onse. Pa ubatizo wake, Yesu ankapemphera ndipo n’kutheka kuti ankaganizira mawu aulosi a pa Salmo 40:6-8.—Luka 3:21; werengani Aheberi 10:5-10.a
8. N’chifukwa chiyani Yohane M’batizi ankakana kubatiza Yesu?
8 Poyamba, Yohane M’batizi sankafuna kubatiza Yesu. Kodi n’chifukwa chiyani sankafuna? Yohane ankabatiza Ayuda monga chizindikiro chakuti alapa machimo awo chifukwa chophwanya Chilamulo. Popeza Yohane anali m’bale wake wa Yesu, ayenera kuti ankadziwa kuti Yesuyo anali munthu wolungama ndipo sankafunikira kulapa. Koma Yesu anauza Yohane kuti n’koyenera kuti iye abatizidwe. Yesu anafotokoza kuti: “N’koyenera kwa ife kutero kuti tikwaniritse chilungamo chonse.”—Mat. 3:15.
9. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anabatizidwa?
9 Popeza Yesu anali munthu wangwiro, iye ankadziwa kuti mofanana ndi Adamu akanatha kubereka ana angwiro. Koma Yesu sanafune n’komwe kuchita zimenezo chifukwa ankadziwa kuti si zimene Yehova akanafuna kuti iye achite. Mulungu anatumiza Yesu padziko lapansi kuti adzakwaniritse udindo wa Mbewu yolonjezedwa kapena kuti Mesiya. Zimenezi zinaphatikizapo kuti Yesu anayenera kupereka nsembe moyo wake wangwiro. (Werengani Yesaya 53:5, 6, 12.) Tanthauzo la ubatizo wa Yesu linali losiyana ndi la ubatizo wathu. Ubatizo wake sunkatanthauza kuti iye akudzipereka kwa Mulungu, chifukwa chakuti anabadwira mu mtundu womwe unali kale wodzipereka kwa Mulungu. M’malomwake, unasonyeza kuti akufuna kuyamba kuchita chifuniro cha Mulungu mogwirizana ndi zimene Malemba analosera kuti Mesiya adzachita.
10. Kodi Mulungu ankafuna kuti Mesiya adzachite chiyani, nanga Yesu anamva bwanji ndi zimenezi?
10 Zina mwa zimene Yehova ankafuna kuti Yesu achite, ndi kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, kupanga ophunzira ndiponso kukonzekeretsa ophunzirawo kuti nawonso adzagwire ntchito yopanga ophunzira. Pamene Yesu anasonyeza kuti akufuna kuyamba kuchita chifuniro cha Mulungu, zinasonyezanso kuti ndi wokonzeka kupirira pozunzidwa ndiponso kuphedwa mwankhanza pofuna kuonetsa kuti ali ku mbali ya ulamuliro wolungama wa Yehova Mulungu. Chifukwa chakuti Yesu ankakonda Atate wake wakumwamba ndi mtima wonse, iye ankasangalala kuchita chifuniro cha Mulungu ndipo ankafunitsitsa kupereka thupi lake monga nsembe. (Yoh. 14:31) Iye ankasangalalanso kudziwa kuti angapereke moyo wake wangwiro kwa Mulungu monga dipo loombolera anthu ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. Yesu atasonyeza kuti akufuna kuchita chifuniro cha Mulungu, kodi Mulungu anavomereza kuti iye akhale ndi maudindo onsewa? Inde anavomereza.
11. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti akuvomereza kuti Yesu ndi Mesiya wolonjezedwa kapena kuti Khristu?
11 Anthu onse anayi amene analemba Mauthenga Abwino anapereka umboni wakuti Yehova Mulungu anavomereza Yesu pamene ankatuluka m’madzi a mu mtsinje wa Yorodano. Yohane M’batizi ananena kuti: “Ndinaona mzimu ukutsika ngati nkhunda kuchokera kumwamba, ndipo unakhalabe pa [Yesu] . . . Ndipo ine ndaonadi zimenezo, ndachitira umboni ndithu kuti iyeyu ndi Mwana wa Mulungu.” (Yoh. 1:32-34) Komanso pa nthawi imeneyi, Yehova analengeza kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.”—Mat. 3:17; Maliko 1:11; Luka 3:22.
Yesu Anakhala Wokhulupirika Mpaka Imfa
12. Kodi Yesu atabatizidwa anachita chiyani pa zaka zitatu ndi theka?
12 Kwa zaka zitatu ndi theka, Yesu anadzipereka kwambiri kuphunzitsa anthu za Atate ake ndiponso kuti ulamuliro wa Mulungu ndi wolungama. Iye anayenda Dziko Lolonjezedwa lonse wapansi ndipo mosakayikira ankatopa. Komabe palibe chimene chinamulepheretsa kuchitira umboni mokwanira choonadi. (Yoh. 4:6, 34; 18:37) Yesu anaphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu. Mwa kuchiritsa odwala, kudyetsa makamu a anthu anjala ndiponso kuukitsa akufa, Yesu anasonyeza zimene Ufumu udzachitire anthu.—Mat. 11:4, 5.
13. Pa nkhani ya pemphero, kodi Yesu anaphunzitsa chiyani?
13 Ngakhale kuti Yesu ankaphunzitsa ndiponso kuchiritsa anthu, sankadziona kuti ndi wapamwamba. Iye anapereka chitsanzo chabwino kwambiri cha kudzichepetsa mwa kupereka ulemu wonse kwa Yehova. (Yoh. 5:19; 11:41-44) Yesu anatithandizanso kudziwa nkhani zofunika kwambiri kuzitchula m’mapemphero athu. M’mapemphero athu tiyenera kupempha kuti dzina la Mulungu lakuti Yehova “liyeretsedwe.” Tiyenera kupemphanso kuti ulamuliro wolungama wa Mulungu ulowe m’malo ulamuliro woipa wa Satana ndiponso kuti “chifuniro chake chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.” (Mat. 6:9, 10) Yesu ananenanso kuti tiyenera kuchita zinthu mogwirizananso ndi mapemphero athuwo mwa “kufuna ufumu choyamba ndi chilungamo” cha Mulungu.—Mat. 6:33.
14. Ngakhale kuti Yesu anali wangwiro, n’chifukwa chiyani anafunika kuchita khama kuti achite bwino pa udindo wake pokwaniritsa cholinga cha Mulungu?
14 Yesu atatsala pang’ono kufa kuti apereke moyo wake nsembe, anayamba kuvutika maganizo kwambiri chifukwa cha udindo waukulu umene anali nawo. Kuti chifuniro cha Atate wake chikwaniritsidwe ndiponso kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe, zinadalira kuti Yesu apirire pozunzidwa ndiponso kuphedwa mwankhanza. Kutatsala masiku asanu kuti afe, Yesu anapempera kuti: “Moyo wanga ukusautsika tsopano, ndinenenji kodi? Atate ndipulumutseni ku nthawi iyi. Komabe n’chifukwa chake ndinabwera ku nthawi imeneyi.” Apatu Yesu ankamva mmene munthu aliyense angamvere. Koma kenako anasiya kudziganizira kwambiri n’kuyamba kuganizira nkhani yofunika kwambiri ndipo anapemphera kuti: “Atate lemekezani dzina lanu.” Nthawi yomweyo Yehova anayankha kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.” (Yoh. 12:27, 28) Pamenepatu Yesu analolera kukumana ndi chiyeso chachikulu cha kukhala wokhulupirika chimene munthu wina aliyense sanakumanepo nacho. Koma n’zosakayikitsa kuti Yesu atamva mawu a Atate ake amenewa anakhala ndi chikhulupiriro kuti apambana pa nkhani yosonyeza kuti Yehova ndi woyenera kulamulira. Ndipo iye anapambanadi.
Zimene Imfa ya Yesu Inakwaniritsa
15. Atatsala pang’ono kufa, n’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti: “Zonse zakwaniritsidwa”?
15 Yesu atatsala pang’ono kufa pamtengo wozunzikirapo, ananena kuti: “Zonse zakwaniritsidwa!” (Yoh. 19:30) Kuchokera pamene Yesu anabatizidwa kukafika pamene anafa, panatenga zaka zitatu ndi theka. Kodi ndi zinthu zikuluzikulu ziti zimene iye mothandizidwa ndi Mulungu anakwaniritsa pa nthawi imeneyi? Pamene Yesu ankafa, kunachitika chivomezi chachikulu. Chifukwa cha zimenezi, kapitawo wa asilikali achiroma amene ankatsogolera kuti Yesu aphedwe, ananena kuti: “Ndithudi uyu analidi Mwana wa Mulungu.” (Mat. 27:54) N’kutheka kuti kapitawoyu anaona Yesu akunyozedwa chifukwa chonena kuti ndi Mwana wa Mulungu. Ngakhale kuti Yesu anakumana ndi mavuto ambirimbiri, iye anakhalabe wokhulupirika ndipo anasonyeza kuti Satana ndi wabodza lamkunkhuniza. Ponena za anthu amene ali kumbali ya ulamuliro wa Mulungu, Satana ananena kuti: “Munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.” (Yobu 2:4) Mwa kukhalabe wokhulupirika, Yesu anasonyeza kuti Adamu ndi Hava akanathanso kukhala okhulupirika pa nthawi imene anayesedwa. Chofunika kwambiri n’chakuti, zimene Yesu anachita ndiponso imfa yake zinasonyeza kuti ulamuliro wa Yehova ndi wolungama. (Werengani Miyambo 27:11.) Koma kodi palinso zimene imfa ya Yesu inakwaniritsa? Inde zilipo.
16, 17. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Yehova ankaona atumiki ake amene anakhalako Chikhristu chisanayambe kuti ndi olungamana? (b) Kodi Yehova anapereka mphoto yotani kwa Mwana wake chifukwa cha kukhulupirika kwake, ndipo kodi Ambuye Yesu Khristu akupiritizabe kuchita chiyani?
16 Pali atumiki a Yehova ambirimbiri amene anakhalapo ndi moyo Yesu asanabwere padziko lapansi. Mulungu ankaona atumiki amenewa kuti ndi olungama ndipo iwo anali ndi chiyembekezo chakuti adzaukitsidwa. (Yes. 25:8; Dan. 12:13) Kodi zinatheka bwanji kuti Yehova Mulungu yemwe ndi woyera adalitse anthu ochimwa amenewa m’njira imeneyi? Baibulo limati: “Mulungu anapereka [Yesu Khristu] monga nsembe ya chiyanjanitso, chochitika mwa kukhala ndi chikhulupiriro m’magazi ake. Mulungu anachita izi pofuna kuonetsa chilungamo chake, chifukwa chakuti anali kukhululuka machimo amene anachitika kale, pamene iye anali kusonyeza khalidwe losakwiya msanga, pofuna kuonetsa chilungamo chake m’nyengo inoyo, kuti adzakhale wolungama ngakhale pakutcha munthu amene ali ndi chikhulupiriro mwa Yesu kukhala wolungama.”—Aroma 3:25, 26.b
17 Pamene Yehova anaukitsa Yesu, anamupatsa moyo wapamwamba kwambiri kuposa moyo umene anali nawo asanabwere padziko lapansi. Panopa, Yesu ali ndi moyo wosafa ndipo ndi cholengedwa chauzimu cha ulemerero wapamwamba kwambiri. (Aheb. 1:3) Monga Mkulu wa Ansembe ndiponso Mfumu, Ambuye Yesu Khristu akupitirizabe kuthandiza otsatira ake kusonyeza chilungamo cha Mulungu. Ndife oyamikira kwambiri kuti Atate wathu wakumwamba Yehova, amapereka mphoto kwa onse amene amasonyeza chilungamo chake ndiponso amamutumikira mokhulupirika potsanzira Mwana wake.—Werengani Salmo 34:3; Aheberi 11:6.
18. Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?
18 Kuyambira pa Abele, anthu onse okhulupirika anali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova chifukwa ankakhulupirira Mbewu yolonjezedwa. Yehova anadziwa kuti Mwana wake adzakhala wokhulupirika pa chilichonse ndipo anadziwanso kuti imfa yake idzaphimba “uchimo wa dziko.” (Yoh. 1:29) Imfa ya Yesu imapindulitsanso anthu amene ali ndi moyo panopa. (Aroma 3:26) Ndiye kodi dipo la Yesu lingakubweretsereni madalitso otani inuyo? M’nkhani yotsatira, tidzakambirana zimenezi?
[Mawu a M’munsi]
a Pa lemba la Aheberi 10:5-10, mtumwi Paulo anagwira mawu Salmo 40:6-8 kuchokera m’Baibulo la Greek Septuagint limene lili ndi mawu akuti, “munandikonzera thupi.” Mawu amenewa sapezeka m’mipukutu yakale yomasulira Malemba Achiheberi.
b Onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga,” tsamba 6 ndi 7.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi chilungamo cha Mulungu chinatsutsidwa bwanji?
• Kodi ubatizo wa Yesu unatanthauza chiyani?
• Kodi imfa ya Yesu inakwaniritsa chiyani?
[Chithunzi patsamba 9]
Kodi mukudziwa zimene ubatizo wa Yesu unkaimira?