‘Khalanibe M’mawu Anga’
‘Ngati mukhalabe inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu.’—YOHANE 8:31.
1. (a) Nthaŵi imene Yesu anabwerera kumwamba, kodi anasiya chiyani padziko lapansi? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?
NTHAŴI imene Yesu Kristu, woyambitsa Chikristu, anabwerera kumwamba, sanalembe mabuku kumanga zipilala kapena kupeza chuma n’kuzisiya padziko lapansi. Iye anasiya ophunzira ndiponso mfundo zenizeni zofunika kuti munthu akhale wophunzira. Ndipotu, mu Uthenga Wabwino wa Yohane, timapeza kuti Yesu anatchula mfundo zofunika zitatu zomwe aliyense wofuna kukhala wotsatira wake afunika kukwaniritsa. Kodi mfundo zofunika zimenezi n’ziti? Kodi tingachite chiyani kuti tizikwaniritse? Ndipo kodi tingatani kuti tionetsetse kuti tikuyenerera kukhala ophunzira a Kristu masiku ano?a
2. Kodi mfundo yofunika ndi iti kuti munthu akhale wophunzira, monga mmene Uthenga Wabwino wa Yohane ukunenera?
2 Pafupifupi miyezi isanu ndi umodzi imfa yake isanachitike, Yesu anapita ku Yerusalemu. Ndipo analalikira kwa makamu omwe anasonkhana kumeneko kukondwerera Madyerero a Misasa omwe ankachitika kwa mlungu umodzi. Chifukwa cha zimenezi, madyerero ali pakati, “ambiri a m’khamu la anthu anakhulupirira Iye.” Yesu anapitiriza kulalikira moti patsiku lomaliza la madyererowo, anthu enanso “ambiri anakhulupirira iye.” (Yohane 7:10, 14, 31, 37; 8:30) Panthaŵi imeneyi, Yesu analankhula kwa okhulupirira atsopano ndipo anawauza chinthu chofunika kuti munthu akhale wophunzira, monga mmene mtumwi Yohane analemba kuti: ‘Ngati mukhalabe inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu.’—Yohane 8:31.
3. Kodi ndi khalidwe liti limene munthu afunika kukhala nalo kuti ‘akhalebe m’mawu a [Yesu]’?
3 Ponena mawu ameneŵa, Yesu sanali kutanthauza kuti okhulupirira atsopanowo analibe chikhulupiriro chokwanira. Komano, iye amasonyeza kuti iwo anali ndi mwayi wokhala ophunzira ake oona ngati akanakhalabe m’mawu ake ndiponso ngati akanapirira. Iwo anali atalandira mawu ake, koma tsopano amafunika kukhalabe m’mawuwo. (Yohane 4:34; Ahebri 3:14) Ndithudi, Yesu anaona kupirira kukhala khalidwe lofunika kwa otsatira ake moti pokambirana komaliza ndi atumwi ake, komwe kwalembedwa mu Uthenga Wabwino wa Yohane, Yesu anawauza kaŵiri konse kuti: ‘Nditsateni ine.’ (Yohane 21:19, 22) Akristu oyambirira ambiri anachitadi zimenezi. (2 Yohane 4) Kodi n’chiyani chinawathandiza kupirira?
4. Kodi n’chiyani chinathandiza Akristu oyambirira kupirira?
4 Mtumwi Yohane, yemwe anali wophunzira wokhulupirika wa Kristu pafupifupi zaka 70, anatchula chinthu chimodzi chofunika. Iye anayamikira Akristu okhulupirika kuti: “Muli amphamvu, ndi mawu a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwam’laka woipayo.” Ophunzira a Kristu ameneŵa anapirira, kapena kuti anakhalabe m’mawu a Mulungu, chifukwa choti mawu a Mulungu anakhalabe mwa iwo. Iwo anawaona kukhala amtengo wapatali. (1 Yohane 2:14, 24) Mofananamo masiku ano, kuti ‘tilimbike chilimbikire kufikira kuchimaliziro,’ tifunika kutsimikiza kuti mawu a Mulungu akhalebe mwa ife. (Mateyu 24:13) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Fanizo limene Yesu anasimba likupereka yankho.
‘Kumva Mawu’
5. (a) Kodi ndi nthaka zosiyanasiyana zotani zomwe Yesu anatchula mu limodzi la mafanizo ake? (b) M’fanizo la Yesu, kodi mbewu ndi nthaka zimaimira chiyani?
5 Yesu anafotokoza fanizo la wofesa yemwe anafesa mbewu, ndipo linalembedwa m’Mauthenga Abwino a Mateyu, Marko ndi Luka. (Mateyu 13:1-9, 18-23; Marko 4:1-9, 14-20; Luka 8:4-8, 11-15) Pamene mukuŵerenga nkhanizi, mudzaona kuti chinthu chachikulu m’fanizoli n’chakuti mbewu za mtundu umodzi zinagwera pa nthaka zosiyanasiyana ndipo zinakula mosiyana. Nthaka yoyamba inali yolimba, yachiŵiri inalibe nthaka yambiri ndipo yachitatu inamera minga yambiri. Mosiyana ndi nthaka zitatuzi, yachinayi inali “yabwino.” Malinga ndi mmene Yesu anafotokozera, mbewu ndiyo uthenga wa Ufumu wopezeka m’Mawu a Mulungu, ndipo nthaka imaimira anthu a mitima yosiyana. Ngakhale kuti anthu omwe akuimiridwa ndi nthaka zosiyanasiyana ali ndi zinthu zina zofanana, amene akuimiridwa ndi nthaka yabwino ali ndi khalidwe lina lomwe likuwasiyanitsa ndi enawo.
6. (a) Kodi nthaka yachinayi m’fanizo la Yesu ikusiyana bwanji ndi nthaka zina zitatu zija, ndipo zimenezi zikutanthauzanji? (b) Kodi n’chiyani chikufunika kuti tisonyeze kupirira monga ophunzira a Kristu?
6 Nkhani ya pa Luka 8:12-15 ikusonyeza kuti m’zochitika zonse zinayi, anthu ‘akumva mawu.’ Komabe, amene ali ndi “mtima woona ndi wabwino” akuchita zoposa ‘kumva mawu.’ Iwo ‘akuwasunga ndi kubala zipatso mopirira.’ Nthaka yabwino popeza ndi yofewa ndiponso yakuya, ikulola mizu ya mbewu kupita pansi ndipo chifukwa cha zimenezi, mbewu zikumera ndi kubala zipatso. (Luka 8:8) Mofananamo, amene ali ndi mtima wabwino amamvetsa mawu a Mulungu, amawaona kukhala ofunika ndipo amawaphunzira mawuwo. (Aroma 10:10; 2 Timoteo 2:7) Mawu a Mulungu amakhalabe mwa iwo. Motero, amabala zipatso mopirira. Chotero, kuona Mawu a Mulungu kukhala amtengo wapatali n’kofunika kuti tisonyeze kupirira monga ophunzira a Kristu. (1 Timoteo 4:15) Komano, kodi tingachite chiyani kuti tiziona Mawu a Mulungu kukhala amtengo wapatali?
Mmene Mtima Ulili Ndiponso Kusinkhasinkha Kopindulitsa
7. Kodi mtima wabwino umagwirizana kwambiri ndi chiyani?
7 Onani zimene Baibulo likugwirizanitsa mobwerezabwereza ndi mtima wabwino. ‘Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe.’ (Miyambo 15:28) ‘Mawu a m’kamwa mwanga ndi maganizo a m’mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova.’ (Salmo 19:14) ‘Ndipo chilingiriro cha mtima wanga chidzakhala cha chidziŵitso.’—Salmo 49:3.
8. (a) Tikamaŵerenga Baibulo, kodi tiyenera kupeŵa chiyani koma tizichita chiyani? (b) Kodi ndi phindu lotani limene timapeza posinkhasinkha mwapemphero Mawu a Mulungu? (Onaninso bokosi lakuti “Okhazikika M’choonadi.”)
8 Mofanana ndi olemba Baibulo awa, ifenso tifunika kuganizira kapena kuti kusinkhasinkha moyamikira ndiponso mwapemphero Mawu a Mulungu ndi zochita zake. Tikamaŵerenga Baibulo kapena zofalitsa zothandiza kuphunzira Baibulo, tisamakhale ngati alendo oona malo amene akuona malo mothamanga ndipo akuyang’ana malo okongola ambirimbiri n’kumajambula chilichonse koma kuona zochepa. M’malo mwake, pamene tikuphunzira Baibulo, tifunika kuima kaye kuti tione malowo bwinobwino, kunena kwake titero.b Pamene tisinkhasinkha mofatsa zimene tikuŵerenga, mawu a Mulungu amakhudza mtima wathu ndipo amaumba maganizo athu. Amatichititsanso kuuza Mulungu zakukhosi kwathu popemphera. Chifukwa cha zimenezi, ubwenzi wathu ndi Yehova umalimba, ndipo kukonda kwathu Mulungu kumatichititsa kupitiriza kutsatira Yesu ngakhale pamene zinthu zili zovuta. (Mateyu 10:22) Mwachionekere, kusinkhasinkha zimene Mulungu amanena n’kofunika ngati tikufuna kukhalabe okhulupirika mpaka mapeto.—Luka 21:19.
9. Kodi tingatani kuti tionetsetse kuti mtima wathu ukhalebe womvera mawu a Mulungu?
9 Fanizo la Yesu likusonyezanso kuti pali zopinga kuti mbewu, mawu a Mulungu, zikule. N’chifukwa chake, kuti tikhalebe ophunzira okhulupirika tingachite bwino (1) kuzindikira zopinga zomwe nthaka yomwe sinali bwino ikuimira zotchulidwa m’fanizolo ndipo (2) kuchitapo kanthu kuzikonza kapena kuzipeŵa. Mwa njira imeneyo, tidzatsimikizira kuti mtima wathu ukhalebe womvera mbewu za Ufumu ndipo upitirizebe kubala zipatso.
“M’mbali Mwa Njira” Mukutanthauza Anthu Amene Ali Otanganidwa
10. Fotokozani nthaka yoyamba m’fanizo la Yesu ndi tanthauzo lake.
10 Nthaka yoyamba pamene mbewu zinagwera ndi ya “m’mbali mwa njira” mmene mbewu “zinapondedwa.” (Luka 8:5) Nthaka ya m’mbali mwa njira yodutsa m’munda wa dzinthu imakhala yolimba kwambiri chifukwa cha kupondedwa ndi anthu oyenda m’njirayo. (Marko 2:23) Mofananamo, amene amalola zinthu zotangwanitsa za dziko kuwachititsa kuwononga kwambiri nthaŵi ndi mphamvu zawo angapeze kuti ali otanganidwa kwambiri moti n’kulephera kuyamikira kwambiri mawu a Mulungu. Iwo amamva mawuwo, koma amalephera kuwasinkhasinkha. Chotero mtima wawo umakhalabe wosakhudzidwa. Iwo asanayambe kuwakonda mawuwo, ‘amadza Mdyerekezi, nachotsa mawu m’mitima yawo, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.’ (Luka 8:12) Kodi tingapeŵe zimenezi?
11. Kodi tingachite bwanji kuti mtima wathu usakhale monga nthaka yolimba?
11 Pali zambiri zimene tingachite kuti mtima usakhale monga nthaka yosabala ya m’mbali mwa njira. Nthaka yopondedwa ndiponso yolimba ingakhale yofeŵa ndi yobala zipatso ngati ilimidwa ndipo anthu aletsedwa kuyendapo. Mofananamo, kupeza nthaŵi ya kuphunzira ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu kungapangitse mtima kukhala ngati nthaka yabwino, yobala zipatso. Chofunika ndicho kusatanganidwa kwambiri ndi zinthu wamba pa moyo. (Luka 12:13-15) M’malo mwake, tiyenera kuonetsetsa kuti tili ndi nthaŵi yosinkhasinkha “zinthu zosiyana [“zofunika kwambiri,” NW]” pa moyo.—Afilipi 1:9-11.
“Pathanthwe” Pakutanthauza Kukhala Amantha
12. Kodi mbewu zomera panthaka yachiŵiri imene Yesu anafotokoza m’fanizo lake zinafota pa chifukwa chenicheni chiti?
12 Mosiyana ndi mbewu za panthaka yoyamba, mbewu zimene zinagwera pa nthaka yachiŵiri, sizinakhale chabe pamwamba panthaka. Zinakhala ndi mizu ndiponso zinamera. Komano pamene dzuŵa linakwera, mbewuzo zinapserera ndi kufota chifukwa cha kutentha kwa dzuŵa. Komabe, taonani mfundo yofunikayi. Chifukwa chenicheni chimene mbewuzo zinafotera si kutenthako. Ndipotu, mbewu zomwe zinamera panthaka yabwino zinawombedwanso ndi dzuŵa, koma sizinafote, zinakula bwino. Kodi kusiyana kunali pati? Yesu anati mbewuzo zinafota chifukwa chakuti “panalibe dothi lambiri” ndiponso “zinalibe mnyontho.” (Mateyu 13:5, 6; Luka 8:6) Thanthwe lomwe linali pansi padothilo, linachititsa mbewu kuti zisalowetse pansi kwambiri mizu yake kuti zipeze chinyontho ndi kukhazikika. Mbewuzo zinafota chifukwa chakuti dothi silinali lambiri.
13. Kodi ndi anthu otani amene ali ngati dothi losaya, ndipo zimene amachita, amatero pa chifukwa chachikulu chiti?
13 Mbali imeneyi ya fanizo ikunena za anthu amene “alandira mawu ndi kukondwera” ndiponso mwachangu amatsatira Yesu ‘kwa kanthaŵi.’ (Luka 8:13) Pamene dzuŵa lotentha la ‘nsautso kapena chizunzo’ liwaomba amakhala ndi mantha kwambiri moti amataya chimwemwe ndi mphamvu zawo ndiponso amasiya kutsatira Kristu. (Mateyu 13:21) Komabe, chifukwa chachikulu chimene amakhalira ndi mantha si chitsutso. Ndipotu, ophunzira ambiri a Kristu amapirira masautso osiyanasiyana, koma amakhalabe okhulupirika. (2 Akorinto 2:4; 7:5) Chifukwa chenicheni chimene ena amakhalira amantha ndiponso kusiya n’chakuti mtima wawo wangati thanthwe umawalepheretsa kusinkhasinkha mwakuya kwambiri zinthu zolimbikitsa ndiponso zauzimu. Chifukwa cha zimenezi, kuyamikira Yehova ndiponso mawu ake kumene amakhala nako n’kochepa kwambiri ndiponso kofooka kwambiri kuti apirire chitsutso. Kodi munthu angatani kuti zimenezi zisachitike?
14. Kodi munthu ayenera kuchita chiyani kuti mtima wake usakhale monga dothi la pathanthwe?
14 Munthu ayenera kuonetsetsa kuti alibe zopinga zangati thanthwe, monga kuwawidwa mtima kozika mizu, kudzikonda kosaonekera, kapena maganizo ena oipa koma obisika m’mtima wake. Ngati zopinga zimenezi zilipo kale, mphamvu ya mawu a Mulungu ingazichotse. (Yeremiya 23:29; Aefeso 4:22; Ahebri 4:12) Ndiyeno, kusinkhasinkha mwapemphero kudzachititsa kuti ‘mawu awokedwe’ kwambiri m’mtima wa munthu. (Yakobo 1:21) Zimenezi zidzatipatsa mphamvu yopirira zokhumudwitsa ndiponso kulimba mtima kuti tikhalebe okhulupirika mosasamala kanthu za mayesero.
“Paminga” Pakutanthauza Kukhala ndi Mitima Iŵiri
15. (a) N’chifukwa chiyani nthaka yachitatu imene Yesu anafotokoza makamaka ifunika kuipenda bwino kwambiri? (b) Kodi n’chiyani chikuchitikira nthaka yachitatuyo pomaliza pake, ndipo chifukwa chiyani?
15 Nthaka yachitatu, yokhala ndi minga, makamaka ifunika kuipenda bwino kwambiri chifukwa chakuti ndi yofanana ndi nthaka yabwino m’njira zina. Monga nthaka yabwino, nthaka yaminga inameretsa mbewu ndipo mizu yake inakhazikika. Poyamba, mbewu zomera kumene panthaka ziŵirizi sizinasiyane kakulidwe. Komabe, m’kupita kwanthaŵi zinthu zinasintha moti pomaliza pake mbewu zinatsamwitsidwa. Mosiyana ndi nthaka yabwino, nthaka imeneyi inamera minga yambiri. Pamene mbewu zazing’onozo zinali kukula panthaka imeneyi, zinalimbana ndi ‘minga yophuka pamodzi nazo.’ Kwa kanthaŵi ndithu minga ndi mbewuzo zinalimbirana chakudya, kuŵala ndi malo koma pomaliza pake minga inakula kwambiri kuposa mbewuzo ndipo ‘inazitsamwitsa.’—Luka 8:7.
16. (a) Kodi ndi anthu otani amene amafanana ndi nthaka yaminga? (b) Malinga ndi nkhani za m’Mauthenga Abwino atatu, kodi minga imaimira chiyani?—Onani mawu a munsi.
16 Kodi ndi anthu otani amene amafanana ndi nthaka yaminga? Yesu akufotokoza kuti: “Ndiwo amene adamva, ndipo m’kupita kwawo atsamwitsidwa ndi nkhaŵa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.” (Luka 8:14) Monga mmene mbewu za wofesa ndiponso minga zimakulira m’nthaka panthaŵi imodzi, chotero anthu ena amayesa kutenga mawu a Mulungu ndiponso ‘zokondweretsa za moyo uno’ panthaŵi imodzi. Choonadi cha mawu a Mulungu chimafesedwa m’mitima yawo, koma chimalimbana ndi zinthu zina zimene zimafuna kuti iwo azisamalire. Mtima wawo wophiphiritsa umagaŵikana. (Luka 9:57-62) Zimenezi zimawalepheretsa kukhala ndi nthaŵi yokwanira yosinkhasinkha mawu a Mulungu mwapemphero ndiponso mopindulitsa. Iwo amalephera kuphunzira mokhazikika mawu a Mulungu ndipo motero sayamikira kuchokera pansi pamtima, chinthu chomwe n’chofunika kuti apirire. Pang’onopang’ono, zinthu zauzimu zimene amakonda zimaphimbidwa ndi zinthu zosakhala zauzimu moti zimafika ‘potsamwitsidwa’ kotheratu.c Ameneŵa amakhala mapeto omvetsa chisoni a anthu amene sakonda Yehova ndi mtima wonse.—Mateyu 6:24; 22:37.
17. Kodi tiyenera kuchita chiyani m’moyo kuti tisatsamwitsidwe ndi minga yophiphiritsa imene yatchulidwa m’fanizo la Yesu?
17 Mwa kukonda kwambiri zinthu zauzimu kuposa zakuthupi, timapeŵa kutsamwitsidwa ndi mavuto ndi zokondweretsa za dziko lino. (Mateyu 6:31-33; Luka 21:34-36) Sitiyenera kunyalanyaza kuŵerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha zimene taŵerengazo. Tidzapeza nthaŵi yochuluka ya kusinkhasinkha moyikirapo mtima ndi mwapemphero ngati tifeŵetsa moyo wathu mmene tingathere. (1 Timoteo 6:6-8) Yehova akudalitsa atumiki ake amene tinganene kuti, achotsa minga panthaka kuti apatse chakudya chambiri, kuŵala ndi malo ku mbewu yobala zipatso. Sandra wa zaka 26 anati: “Ndikasinkhasinkha madalitso anga m’choonadi, ndimazindikira kuti palibe chimene dziko lingapereke chimene chingafanane ndi choonadi.”—Salmo 84:11.
18. Kodi ndi motani mmene tingakhalirebe m’mawu a Mulungu ndi kupirira monga Akristu?
18 Mwachionekere, ife tonse, achichepere ndi achikulire, tidzakhalabe m’mawu a Mulungu ndi kupirira monga ophunzira a Kristu ngati mawu a Mulungu akhalabe mwa ife. Chotero, tiyeni tiyesetse kuti nthaka ya mtima wathu wophiphiritsa isakhale yolimba, yosaya kapena yoŵirira ndi zinthu zosafunika koma kuti ikhalebe yofewa ndi yakuya. Mwa njira imeneyi, tidzatha kuphunzira mokhazikika mawu a Mulungu ndi ‘kubala zipatso mopirira.’—Luka 8:15.
[Mawu a M’munsi]
a M’nkhaniyi, tidzakambirana mfundo imodzi mwa mfundo zofunika zimenezi. Zina ziŵiri tidzakambirana m’nkhani zotsatira.
b Mwachitsanzo, kuti musinkhesinkhe mwapemphero chigawo cha m’Baibulo chimene mwaŵerenga, mungadzifunse kuti: ‘Kodi chikuonetsa khalidwe limodzi la Yehova kapena ambiri? Kodi zikugwirizana bwanji ndi mutu wa nkhani wa Baibulo? Kodi ndingachigwiritsire ntchito bwanji m’moyo wanga kapena pothandiza ena?’
c Malinga ndi nkhani za m’Mauthenga Abwino atatu za fanizo la Yesu, mbewu zinatsamwitsidwa ndi mavuto ndi zokondweretsa za dziko lino. Nkhanizo zimati zimenezi zinali: “Malabadiro a dziko lapansi,” “chinyengo cha chuma,” “kulakalaka kwa zinthu zina,” ndi “zokondweretsa za moyo.”—Marko 4:19; Mateyu 13:22; Luka 8:14; Yeremiya 4:3, 4.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• N’chifukwa chiyani tiyenera ‘kukhalabe m’mawu a Yesu’?
• Kodi tingalole bwanji mawu a Mulungu kukhalabe m’mtima wathu?
• Kodi nthaka zinayi zotchulidwa ndi Yesu zikuimira anthu otani?
• Kodi mungapeze bwanji nthaŵi yosinkhasinkha mawu a Mulungu?
[Bokosi/Chithunzi patsamba 10]
‘OKHAZIKIKA M’CHOONADI’
AMBIRI amene akhala ophunzira a Kristu kwanthaŵi yaitali amatsimikiza kuti ndi ‘okhazikika m’choonadi’ chaka chilichonse. (2 Petro 1:12) Kodi n’chiyani chimawathandiza kupirira? Taonani zina zimene iwo anena.
“Kumapeto kwa tsiku lililonse ndimaŵerenga chigawo cha Baibulo ndiponso kupemphera. Ndiyeno ndimaganizira zimene ndaŵerengazo.”—Anatero Jean, yemwe anabatizidwa mu 1939.
“Kusinkhasinkha mmene Yehova, munthu wapamwamba zedi, amatikondera kwambiri zimandipangitsa kuona kuti ndine wotetezeka ndipo zimandipatsa nyonga kuti ndikhalebe wokhulupirika.”—Anatero Patricia, yemwe anabatizidwa mu 1946.
“Mwa kukhala ndi zizoloŵezi zabwino za kuphunzira Baibulo nthaŵi zonse ndiponso kusinkhasinkha ‘zakuya za Mulungu,’ ndatha kupitirizabe kutumikira Yehova.”—1 Akorinto 2:10; anatero Anna, yemwe anabatizidwa mu 1939.
“Ndimaŵerenga Baibulo ndi zofalitsa zathu zothandiza kuphunzira Baibulo kuti ndipende mtima wanga ndi zolinga zanga.”—Anatero Zelda, yemwe anabatizidwa mu 1943.
“Nthaŵi yomwe ndimasangalala kwambiri ndi pamene ndimanyamuka kuti ndiwongole miyendo ndi kulankhula ndi Yehova m’pemphero ndi kungom’dziŵitsa mmene ndikumvera mu mtima.”—Anatero Ralph, yemwe anabatizidwa mu 1947.
“Ndimaŵerenga lemba latsiku ndiponso chigawo cha Baibulo m’maŵa uliwonse. Zimenezi zimandipatsa chinthu chatsopano choti ndisinkhesinkhe patsikulo.”—Anatero Marie, yemwe anabatizidwa mu 1935.
“Kwa ine, nkhani zofotokoza vesi ndi vesi la buku la m’Baibulo zimandilimbikitsa kwambiri.”—Anatero Daniel, yemwe anabatizidwa mu 1946.
Kodi ndi nthaŵi yanji imene mumasinkhasinkha mwapemphero mawu a Mulungu?—Danieli 6:10b; Marko 1:35; Machitidwe 10:9.
[Chithunzi patsamba 13]
Mwa kuika zinthu zauzimu pa malo oyamba, ‘tingabale zipatso mopirira’