Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi Mariya amene anakhala mayi wa Yesu anali kale ndi pakati pamene anakachezera Elisabeti wachibale wake?
Inde, malinga ndi umboni umene ulipo.
Mu Luka chaputala 1, choyamba timaŵerenga za pathupi pa Elisabeti, mkazi wa Zekariya wansembe, amene anabala Yohane (Mbatizi). Pamene Elisabeti anali mu “mwezi wachisanu ndi chimodzi mngelo Gabrieli” anafika kwa Mariya kukamuuza kuti adzakhala ndi pakati nadzabala “Mwana wa Wamkulukulu.” (Luka 1:26, 30-33) Koma kodi Mariya anakhala liti ndi pakati?
Nkhani ya Luka imapitiriza kusimba kuti zitatha zimenezo Mariya anapita ku Yuda kukacheza kwa Elisabeti wachibale wake yemwe anali ndi pakati. Pamene akazi aŵiriwo anakumana, khanda (Yohane) m’mimba mwa Elisabeti linatsalima. Elisabeti anatchula ‘chipatso cha mimba ya Mariya,’ natcha Mariya “amake wa Ambuye wanga.” (Luka 1:39-44) Chifukwa chake moyenerera tinena kuti Mariya anali ataima kale, kuti anali ndi pakati pamene anapita kukaona Elisabeti.
Luka 1:56 amati: “Ndipo Mariya anakhala ndi iye ngati miyezi itatu, nabweranso kunyumba kwake.” Vesi limeneli silikusonyeza kuŵerengera kwenikweni kumene kungatipatse tsiku lenileni pa kalenda. Ilo likuti “ngati miyezi itatu,” zimene zikutanthauza kuti Elisabeti ayenera kuti anali m’mwezi wachisanu ndi chinayi wa pathupi pake.
Atathandiza Elisabeti mkati mwa nyengo yomaliza ya pathupi pake, Mariya anabwerera kwawo ku Nazarete. Mwinamwake Mariya anazindikira kuti Elisabeti atangobala (Yohane), mwinamwake padzakhala alendo ambiri, amene ena a iwo adzakhala achibale ake. Zimenezo zikanakhala zovuta kapena zamanyazi kwa mkazi wosakwatiwa amenenso anali ndi pakati. Kodi Mariya anali ndi pathupi pa miyezi ingati pamene anachoka kubwerera ku Nazarete? Popeza kuti anakhala ndi Elisabeti “ngati miyezi itatu,” mwinamwake pathupi pa Mariyapo panali kumapeto kwa mwezi wake wachitatu kapena kuchiyambi kwa mwezi wake wachinayi pamene iye anabwerera ku Nazarete.