Kodi Mumayamikira Zimene Mulungu Wachita?
“Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha nanyamule mtengo wozunzirapo wake tsiku ndi tsiku nanditsate ine.”—LUKA 9:23, “NW.”
1. Kodi ndi mphatso zina zodabwitsa ziti zimene Mulungu wapereka?
MIYOYO yathu njoŵerengera kwa Mulungu. Ngati iye sanalenge anthu, ife sitikanabadwa. Koma Mulungu analenga zambiri osati moyo chabe. Iye anatipanga kotero kuti tisangalale ndi zinthu zambiri: kukoma kwa zakudya, kutentha kwa dzuŵa, kumveka kwa nyimbo, ubwino wa tsiku la nyengo yangululu, kusamalira kwachikondi. Kuposa apa, Mulungu anatipatsa maganizo ndi chikhumbo cha kumphunzira. Iye anauzira Baibulo, limene limatipatsa chitsogozo chabwino, kutisonyeza mmene tingakhalire ndi moyo mwachimwemwe, ndi kupereka chiyembekezo chakukhala kosatha m’dziko lake latsopano lolungama. Mulungu amaperekanso mzimu wake woyera, wochilikiza mpingo wakumaloko, ndi amuna ndi akazi achimwemwe omwe angatithandize kukhala olimba nji mu utumiki wake.—Genesis 1:1, 26-28; 2 Timoteo 3:15-17; Ahebri 10:24, 25; Yakobo 5:14, 15.
2. (a) Kodi n’chinthu chapadera kwenikweni chiti chimene Mulungu watichitira? (b) Kodi tingachipeze chipulumuko kupyolera m’ntchito?
2 Kuwonjezera pa zonsezo, Mulungu anatumiza Mwana wake woyamba kubadwa kudzatiuza zambiri ponena za chimene Atateyo amatiyembekezera ndi kupereka “dipo” lowombola aliyense amene adzalivomereza. (Aefeso 1:7, NW; Aroma 5:18) Mwanayo, Yesu Kristu, anati: “Mulungu anakondadi dziko, kwakuti iye anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womkhulupirira asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16, King James Version) Chipulumuko chotheketsedwa ndi dipo limenelo nchamtengo wapatali kwenikweni kwakuti palibiretu njira imene aliyense angagwirire nayo ntchito kuchipeza, kunena mwantheradi osati ngakhale ntchito zochitidwa kalekale pansi pa Chilamulo cha Mose. Chotero, Paulo analemba motere: ‘Munthu sayesedwa wolungama pa ntchito ya lamulo, koma mwa chikhulupiriro cha Yesu Kristu.’—Agalatiya 2:16; Aroma 3:20-24.
Chikhulupiriro ndi Ntchito
3. Kodi nchiyani chimene Yakobo ananena ponena za chikhulupiriro ndi ntchito?
3 Chipulumuko chimabwera ndi chikhulupiriro, koma chikhulupiriro ndi chiyamikiro cha zonse zimene Mulungu wachita chiyenera kutifulumiza kuchita ntchito. Icho chiyenera kutisonkhezera kuchita zinthu zomwe zimasonyeza chikhulupiriro chathu. Yakobo, mbale wa Yesu mwa bambo wina, analemba motere: ‘Chikhulupiriro, chikapanda kukhala nazo ntchito, chikhala chakufa mkati mwakemo.’ Iye ananenanso kuti: ‘Undionetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m’ntchito zanga.’ Yakobo anasonyeza kuti ngakhale ziŵanda ‘zikhulupiranso ndipo zinthunthumira,’ koma mwachionekere ziŵanda sizimachita ntchito zaumulungu. Abrahamu, kumbali ina, anali ndi zonse ziŵiri chikhulupiriro ndi ntchito. ‘Chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro.’ Yakobo akubwereza kuti: ‘Chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa.’—Yakobo 2:17-26.
4. Kodi nchiyani chimene Yesu ananena kuti omwe amafuna kumtsatira ayenera kuchita?
4 Yesu anasonyezanso kufunika kwa ntchito zabwino, nati: ‘Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa kumwamba.’ “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha nanyamule mtengo wozunzirapo wake tsiku ndi tsiku nanditsate ine.”a Ngati ‘tidzikana’ tokha, timasiya zosankha zathu zambiri. Timazindikira kuti timaŵerengera zonse kwa Mulungu, chotero timadzipereka tokha kwa iye monga akapolo, kufuna kuphunzira ndi kuchita chifuniro chake, monga mmene Yesu anachitira.—Mateyu 5:16; Luka 9:23, NW; Yohane 6:38.
Miyoyo Njoyambukiridwa
5. (a) Kodi nchiyani chimene Petro anasonyeza kuti chiyenera kuyambukira njira yathu yonse yamoyo? (b) Kodi ndi ntchito zabwino zotani zimene iye anayamikira?
5 Petro anasonyeza kuti ‘mwazi wa mtengo wake wapatali’ wa Kristu, woperekedwa m’malo mwathu, ngwamtengo wapatali kwenikweni kwakuti kuuyamikira kwathu kuyenera kuwonekera m’njira yathu yonse yamoyo. Mtumwiyo anandandalitsa zinthu zambiri zimene chiyamikiro chathu chiyenera kutifulumiza kuchita. Iye analangiza kuti: ‘Tayani choipa chonse.’ “Lirani monga makanda alero mkaka woyenera.” ‘Mukalalikire zoposazo za iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, muloŵe kuunika kwake kodabwitsa.’ ‘Ndipo apatuke pa choipa, nachite chabwino.’ ‘Okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chiri mwa inu.’ ‘Kuti nthaŵi [yanu] yotsalira simukakhalenso ndi moyo m’thupi kutsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu.’—1 Petro 1:19; 2:1, 2, 9; 3:11, 15; 4:2.
6. (a) Kodi ndimotani mmene Akristu a m’zaka za zana loyamba anasonyezera chikhulupiriro chawo? (b) Kodi nchitsanzo chiti chimene ichi chiyenera kutikhazikitsira?
6 Akristu a m’zaka za zana loyamba anakhalira moyo chikhulupiriro chawo. Icho chinasintha kapenyedwe kawo ndi maumunthu awo, kuwafulumiza kubweretsa miyoyo yawo mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Iwo anavutika ndi ukapolo, kuponyedwa miyala, kupandidwa, kuikidwa m’ndende, ndipo ngakhale imfa m’malo mwa kupotoza chikhulupiriro chawo. (Machitidwe 7:58-60; 8:1; 14:19; 16:22; 1 Akorinto 6:9-11; Aefeso 4:22-24; Akolose 4:3; Filemoni 9, 10) Katswiri wa mbiri yakale Wachiroma wotchuka Tacitus, yemwe anabadwa pafupifupi 56 C.E., anati Akristu “anaponyedwa m’malaŵi a moto ndi kuotchedwa, kutumikira monga miuni ya usiku, pamene dzuŵa linaloŵa.” Komatu iwo sanagwedezeke!—The Annals, Bukhu XV, ndime 44.
7. Kodi ndi mumkhalidwe wotani umene anthu ena amadzipeza okha?
7 M’mipingo ina inu mungapeze anthu omwe akhala akupezeka pamisonkhano kwazaka zambiri. Iwo amakonda gulu la Yehova, kuganizira kuti anthu ake ndi anthu abwino kwambiri omwe sanakumanepo nawo, kuthirira ndemanga zabwino ponena za chowonadi, ndi kuchilikiza chowonadi kwa akunja. Koma chinachake chimawatsekerezera m’njira yawo, chinachake chimawaletsa. Iwo sanatengebe njira yabwino imene anthu 3,000 anachita pa tsiku la Pentekoste, chimene wokhulupirira wa ku Aitiopiya anafunsa, kapena chimene Hananiya anafulumiza Saulo kuchita mwamsanga pamene wozunza wakaleyu anazindikira kuti Yesu analidi Mesiya. (Machitidwe 2:41; 8:36; 22:16) Kodi chikusoŵeka nchiyani mwa oterewa lerolino? Kodi nchifukwa ninji sanatengebe sitepe limene Baibulo limatcha ‘funso lake lachikumbumtima chokoma kwa Mulungu’? (1 Petro 3:21) Ngati inuyo mudzipeza mumkhalidwe uwu—wakudziŵa chowonadi koma wozengeleza kuchita chinachake—lingalirani nkhaniyi kukhala itakonzekeredwera ndi chikondi chapadera kaamba ka inu.
Kulaka Zopinga Kubatizidwa
8. Ngati inu simunakhalepo wophunzira wabwino, kodi ndi iti imene ingakhale njira yanzeru yotengapo?
8 Kodi nchiyani chimene chingakutsekerezereni njira yanu? Nkhani yomwe yapitayo yasonyeza kuti ena angapeze phunziro laumwini kukhala vuto. Mulungu anatipatsa malingaliro odabwitsa, ndipo amatiyembekezera kuwagwiritsira ntchito m’kumtumikira. Anthu ena omwe sanaphunzirepo kuŵerenga anadzipereka okha kuntchitoyi ndi cholinga cha kuphunzira zambiri ponena za Mulungu ndi zifuno zake. Bwanji ponena za inu? Ngati inu mumadziŵa kale kuŵerenga, kodi mumaphunziradi, monga mmene Abereya anachitira, ‘kusanthula Malemba masiku onse’ kuwona ngati zinthu izi zinali tere? Kodi inuyo mwasanthula “kupingasa, ndi utali, ndi kukwera” kwa chowonadi? Kodi mwakumba mwakuya mokwanira Mawu a Mulungu? Kodi mwapeza mmene kuliridi kochititsa chidwi? Kodi mwakulitsa chikhumbo chenicheni cha kudziŵa chifuniro cha Mulungu? Kodi muli ndi njala yeniyeni ya chowonadi?—Machitidwe 17:10, 11; Aefeso 3:18.
9. Kodi nchiyani chomwe chiri chinthu chabwino kuchichita ngati muli ndi vuto ndi winawake mu mpingo?
9 Nthaŵi zina anthu amazengereza chifukwa cha vuto lenileni kapena longoganizira limene iwo anakhala nalo ndi winawake mu mpingo. Kodi munthu wina wakulakwirani mwamphamvu? Pamenepo tsatirani chitsogozo chosonyezedwa ndi mawu a Yesu awa: “Pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye.” (Mateyu 18:15) Inu mungadabwitsidwe kupeza kuti munthuyo sanadziŵedi kuti anakulakwirani. Ngakhale ngati iye akudziŵadi, inuyo ‘mungabweze mbale wanu,’ monga mmene ananenera Yesu. Inu mungamthandizenso kupeŵa kukhumudwitsa winawakenso. Ndiponso, pamene muganiza za icho, kodi inu mukutumikiradi yani—munthuyo kapena Mulungu? Kodi chikondi chanu cha Mulungu nchaching’ono motero chakuti mungalole zophophonya za anthu opanda ungwiro kudodometsa chikondi chanu kwa Iye?
10, 11. Kodi muyenera kuchitanji ngati machimo ena amseri akhala akukuzengerezetsani?
10 Chimo lamseri lingaletse munthu kubatizidwa. Ili lingakhale chinachake chomwe chinachitika kumbuyo, kapena kungakhale kulakwa kopitirizidwabe. Ngati ili ndilo vuto lanu, kodi ino sinthaŵi ya kuliongolera? (1 Akorinto 7:29-31) Anthu ambiri a Yehova anafunikira kupanga zosintha m’miyoyo yawo. Baibulo limati: ‘Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera ku nkhope ya [Yehova, NW].’—Machitidwe 3:19.
11 Mosasamala kanthu za chimene inuyo mungakhale munachita kumbuyoko, inu mungalape, kusintha, ndi kupempha chikhululukiro kwa Mulungu. ‘Chifukwa chake fetsani ziŵalozo ziri padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa . . . Vulani munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, ndipo munavala watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye.’ Inu mungabweretse moyo wanu mogwirizana ndi njira zake, kusangalala ndi chikumbumtima choyera, ndi kukhala ndi chiyembekezeo cha moyo wosatha m’dziko lake latsopano. Kodi ichi sichopindulitsa kuyesayesa kulikonse kumene kungachitidwe?—Akolose 3:5-10; Yesaya 1:16, 18; 1 Akorinto 6:9-11; Ahebri 9:14.
12. Kodi muyenera kuchitanji ngati fodya, kugwiritsira ntchito molakwa zoledzeretsa, kapena mankhwala ogodomalitsa kukhala pakati pa inu ndi chikumbumtima choyera?
12 Kodi kugwiritsira ntchito fodya, kugwiritsira ntchito molakwa zoledzeretsa, kapena kumwerekera ndi mankhwala ogodomalitsa kumakhala pakati pa inu ndi chikumbumtima choyera? Kodi zizoloŵezi zoopsya moyozi sizimasonyeza kusalemekeza mphatso yodabwitsa ya Mulungu yamoyo? Ngati zizoloŵezizi zimakutsekerezani, motsimikizirika iyi ndinthaŵi ya kuziongolera. Kodi zizoloŵezizi nzofunikira kuwononga moyo wanu? Paulo anati: ‘Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuopa Mulungu.’ Kodi mumayamikira kuyera kwa Mulungu ndi njira zake zolungama mokwanira kwakuti nanunso nkuchita tero?b—2 Akorinto 7:1.
Chuma Chakuthupi
13, 14. (a) Kodi nchiyani chimene Malemba amanena ponena za zonulirapo za chuma chakuthupi? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuika zinthu zakumwamba choyamba?
13 Dziko lalerolino limaika chipambano ndi “matamandidwe a moyo” pafupifupi patsogolo pa chirichonse. Koma Yesu anafanizitsa ‘malabadiro a dziko lapansi, ndi chinyengo chachuma’ ku “minga” zomwe zinatsamwitsa mawu a Mulungu. Iye anafunsanso kuti: ‘Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake?’—1 Yohane 2:16; Marko 4:2-8, 18, 19; Mateyu 16:26.
14 Yesu anasonyeza kuti Mulungu anakonzekera mbalame kupeza zakudya ndi maluŵa kumera modabwitsa. Pamenepo iye anafunsa kuti: “Nanga inu simuziposa mbalame kwambiri? . . . Nanga inu sadzakuninkhani [Mulungu] koposa!” Mwanzeru, Yesu anatiuza ‘kusada nkhaŵa’ ponena za chuma chakuthupi. Iye anati: ‘Tafunani Ufumu wa [Mulungu] ndipo izi adzakuonjezerani.’ Iye anasonyeza kuti tiyenera kuika zinthu zakumwamba poyamba chifukwa chakuti ‘kumene kuli chuma chathu, komweko kudzakhalanso mtima wathu.’—Luka 12:22-31; Mateyu 6:20, 21.
Utumiki wa Mulungu ndi Thandizo la Mulungu
15. Kodi ndi chilimbikitso chabwino chotani chimene chitsanzo cha Akristu a m’zaka za zana loyamba chimatipatsa?
15 Kodi kuchitira umboni kwa ena kumaonekera kubweretsa vuto kwa inu? Kodi manyazi amakupangitsani kuzengereza? Ngati ndi tero, nkofunika kukumbukira kuti Akristu a m’zaka za zana loyamba anali ndi mtundu wofananawo wamalingaliro womwe tiri nawo lerolino. Mulungu sanasankhe anthu ambiri anzeru ndi amphamvu, koma iye anasankha ‘zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru.’ (1 Akorinto 1:26-29) Atsogoleri amphamvu achipembedzo anatsutsa anthu “opulukira” amenewa ndi kuwalamulira kuleka kulalikira. Kodi Akristuwo anachitanji? Iwo anapemphera. Iwo anapempha Mulungu kaamba ka kulimba mtima, ndipo iye anawapatsa. Monga chotulukapo, uthenga wawo unadzala Yerusalemu ndipo pambuyo pake unagwedeza dziko lonse!—Machitidwe 4:1-4, 13, 17, 23, 24, 29-31; 5:28, 29; Akolose 1:23.
16. Kodi timaphunziranji kuchokera ku ‘mtambo waukulu wa mboni’ wofotokozedwa m’mutu 11 wa Ahebri?
16 Motero, kuopa anthu, sikuyenera kukhala pakati pathu ndi utumiki wa Mulungu. Ahebri mutu 11 amasimba za ‘mtambo waukulu wa mboni’ omwe anaopa, osati anthu, koma Mulungu. Tiyenera kusonyeza chikhulupiriro chofananacho. Mtumwiyo analemba kuti: ‘Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chirichonse, ndi chimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.’—Ahebri 12:1.
17. Kodi nchilimbikitso chotani chimene Mulungu anapereka kupyolera mwa Yesaya?
17 Mulungu angapatse atumiki ake thandizo lalikulu. Mlengi wa thambo anauza Yesaya kuti: “Koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.”—Yesaya 40:31.
18. Kodi ndimotani mmene mungalakire manyazi kotero kuti mukhale ndi phande m’kulalikira Ufumu?
18 Mboni zolimba mtima ndi zachimwemwe zimene mumaona mu mpingo wakwanuko ziri kokha mbali yaing’ono ya atumiki achangu oposa mamiliyoni atatu ndi theka padziko lonse. Iwo amasangalala kukhala ndi mbali m’ntchito imene Yesu Kristu iyemwini ananeneratu m’mawu awa: ‘Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.’ Ngati kugawanamo m’kulalikira Ufumu kumabweretsa vuto pa inu ngakhale pamene muyeneretsedwa kuchita tero, bwanji osafunsa Mboni imene imachita bwino mu uminisitala kuti ipite nanu kukakhala ndi phande mu ntchito yolalikirayo? Mulungu amaperekadi “ukulu woposa wamphamvu,” ndipo inuyo mungadabwitsidwe kupeza mmene utumiki waumulungu umenewu uliri wosangalatsa.—Mateyu 24:14; 2 Akorinto 4:7; onaninso Salmo 56:11; Mateyu 5:11, 12; Afilipi 4:13.
19. Kodi ndi ntchito yophunzitsa iti imene Yesu analamulira ophunzira ake kuichita?
19 Yesu amayembekezera anthu omwe amayamikira uthenga Waufumu kuchitapo kanthu. Iye anati: ‘Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.’—Mateyu 28:19, 20.
20. Ngati inu mukupita patsogolo mwauzimu, kodi ndi funso liti limene moyenerera lingafunsidwe mofulumira?
20 Kodi kuyamikira kwanu madalitso a Mulungu, kaamba ka ‘mwazi wa mtengo wake wapatali’ wa Yesu, ndi kaamba ka chiyembekezo chodabwitsa cha moyo wosatha kumakusonkhezerani kuchitapo kanthu? (1 Petro 1:19) Kodi mwabweretsa moyo wanu mogwirizana ndi ziyeneretso zolungama za Mulungu? Kodi mumakhala ndi phande mokhazikika m’kupanga ophunzira? Kodi mwadzikana inu eni ndi kupereka moyo wanu kwa Mulungu? Ngati yankho kumafunso onsewa ndi inde weniweni, iyi ingakhale nthaŵi ya kufunsa mmodzi wa akulu mu mpingo umene mumapezekapo funso limodzimodzi lija limene munthu wa ku Aitiopiya wokhulupirira anafunsa Filipo kuti: ‘Chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?’—Machitidwe 8:36.
[Mawu a M’munsi]
a The Jerusalem Bible imamasulira ichi motere “adzitaye yekha.” Matembenuzidwe olembedwa ndi J. B. Phillips amati “akane zomuyenerera zonse.” The New English Bible imati “adzisiye m’mbuyo.”
b Kaamba ka chidziŵitso pa kuleka zizoloŵezizi, onani Nsanja ya Olonda, August 1, 1981, masamba 3-13; June 1, 1973, (Chingelezi) masamba 336-43; ndi Galamukani! May 8, 1983, masamba 19-24; May 22, 1981, (Chingelezi) masamba 3-11. Awa angapezedwe pa laibulale ya pa Nyumba Yaufumu yakwanuko ya Mboni za Yehova.
Kodi Mumakumbukira?
◻ Kodi nzifukwa zapadera ziti zomwe tiri nazo zakukhalira oyamikira Mulungu?
◻ Kodi nchiyani chimene chikhulupiriro ndi chiyamikiro chingatisonkhezere kuchita?
◻ Kodi ndi mavuto ati omwe angaime pakati pa ife ndi chimvero kwa Mulungu, ndipo kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita nawo?
◻ Kodi ndi mafunso ati amene anthu osabatizidwa angadzifunse?
[Bokosi patsamba 18]
‘Kodi ndine “nthaka” ya mtundu wanji?’
Yesu anapereka fanizo la munthu yemwe anakafesa mbewu. Mbewu zina zinagwera m’mbali mwanjira ndipo zinadyedwa ndi mbalame. Zina zinagwera pamiyala popanda nthaka. Izi zinamera, koma pamene dzuŵa linawala, zinafota ndi kufa. Mbewu zinabe zinagwera pa minga ndipo zinatsamwitsidwa. Yesu anati magulu atatu amenewa amaimira: choyamba, munthu amene ‘amamva mawu a Ufumu, osawadziwitsai’; chachiŵiri, munthu amene amavomereza mawuwo koma amatembenuzidwa ndi mkuntho wa “nsautso kapena zunzo”; ndipo lachitatu, munthu amene ‘kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mawu.’
Koma Yesu anasimbanso za mbewu zina zomwe zinagwera pa nthaka yabwino. Iye anati: ‘Uyu ndiye wakumva mawu nawadziŵitsa; amene abaladi zipatso.’—Mateyu 13:3-8, 18-23.
Chingakhale chabwino kudzifunsa ife eni kuti: ‘Kodi ndine “nthaka” ya mtundu wanji?’
[Bokosi patsamba 19]
Iwo anafera chikhulupiriro chawo
Kodi mumadziŵa aliyense amene angakonde kufa m’malo mwakuswa chikhulupiriro chake? Zikwi zambiri za Mboni za Yehova zatero. Mu The Nazi State and the New Religions: Five Case Studies in Non-Conformity, Dr. Christine E. King analemba kuti: “Mmodzi mwa Mboni ziŵiri zirizonse Zachijeremani anaikidwa m’ndende, mmodzi mwa anayi anaphedwa.”
Pamene mavuto a m’misasa pomalizira pake anatha mu 1945, “chiŵerengero cha Mboni chinawonjezereka ndipo panalibe kugonja komwe kunapangidwa.” Mu The Nazi Persecution of the Churches, J. S. Conway analemba za Mboni motere: “Palibe mpatuko uliwonse womwe unasonyeza chirichonse chofanana ndi kugamula kofananako poyang’anizana ndi kukakamizidwa kokwanira kwa uchigawenga wa Gestapo.”
Mboni za Yehova sizinazunzidwe chifukwa cha ndale zawo zadziko kapena fuko. M’malomwake, izo zinavutika kotheratu chifukwa cha chikondi chawo cha Mulungu ndi kukana kwawo kuswa chikumbumtima chawo chophunzitsidwa ndi Baibulo.