Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kuwoneratu Ulemerero wa Ufumu wa Kristu
YESU waima panjira kuyenda ku Kaisareya wa Filipi, ndipo iye akuphunzitsa khamu limodzi ndi atumwi ake. Iye akupanga chilengezo chochititsa mantha ichi kwa iwo: “Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzawona Mwana wa munthu atadza mu ufumu wake.”
‘Kodi nchiyani chimene Yesu akanatanthauza?’ ophunzirawo ayenera kudabwa. Chifupifupi mlungu umodzi pambuyo pake, Yesu akutenga Petro, Yakobo, ndi Yohane limodzi naye nakwera phiri lalitali. Mwinamwake uli usiku, popeza ophunzirawo ali ndi tulo. Pamene Yesu ali kupemphera, iye asandulika pamaso pawo. Nkhope yake iyamba kuwala monga dzuŵa, ndi zovala zake ziyera mbu monga ngati kuwala.
Kenaka, anthu aŵiri, ozindikiritsidwa monga “Mose ndi Eliya,” awonekera ndi kuyamba kulankhula kwa Yesu ponena za ‘kunyamuka kwake komwe kudzachitika ku Yerusalemu.’ Kunyamukako mwachiwonekere kukulozera ku imfa ya Yesu ndi chiukiriro chotsatira. Chotero, kukambitsirana kumeneku kukutsimikizira kuti imfa yake yomvetsa manyazi siiri chinachake choyenera kuchipewa, monga mmene Petro anakhumbira.
Ali ogalamuka kwambiri tsopano, ophunzirawo akuwona ndi kumvetsera ndi kudabwitsidwa. Ngakhale kuti awa ndi masomphenya, chikuwoneka ngati chenicheni kotero kuti Petro akuyamba kutengamo mbali m’chochitikacho, akumanena kuti: “Ambuye, kuli bwino kuti ife tikhale pano. Ngati mulola ndidzamanga pano misasa itatu, umodzi wa inu ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.”
Pamene Petro akulankhula, mtambo wowala unawaphimba iwo, ndipo mawu kuchokera mumtambo akunena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani iye.” Pamene anamva mawuwo, ophunzirawo agwa pansi pa nkhope zawo. Koma Yesu anena kuti: “Ukani, musawopa.” Pamene iwo atero, sakuwonanso wina koma Yesu yekha.
Pa ulendo wawo kutsika phiri tsiku lotsatira, Yesu akulamulira kuti: “Musakauze munthu chowonekacho, kufikira Mwana wa munthu adadzauka kwa akufa.” Kuwoneka kwa Eliya m’masomphenyawo kukudzutsa funso m’maganizo a ophunzirawo. “Nchifukwa ninji,” iwo akufunsa, “alembi ananena kuti adzayamba kufika Eliya?”
“Eliya anadza kale,” Yesu akuyankha, “ndipo iwo sanamdziŵa iye.” Yesu, ngakhale kuli tero, akulankhula ponena za Yohane Mbatizi, yemwe anakwaniritsa mbali yofanana ndi ya Eliya. Yohane anakonza njira kaamba ka kudza kwa Kristu, monga momwe anachitira Eliya kaamba ka Elisa.
Ndi olimbikitsa chotani nanga mmene masomphenya amenewa atsimikizira kukhala, ponse paŵiri kwa Yesu ndi kwa ophunzira! Masomphenyawo ali, monga momwe kunaliri, kuwoneratu za ulemerero wa Ufumu wa Kristu. Ophunzirawo awona, m’chenicheni, “Mwana wa munthu akudza mu ufumu wake,” monga mmene Yesu analonjezera mlungu woyambirirawo. Pambuyo pa imfa ya Yesu, Petro analemba ponena za kukhala ‘mboni zowona ndi maso ukulu wa Kristu pokhala pamodzi ndi iye m’phiri lopatulika lija.’
Afarisi analamulira kuchokera kwa Yesu chizindikiro chotsimikizira kuti anali wolonjezedwa m’Malemba kukhala Mfumu yosankhidwa ya Mulungu. Iwo sanapatsidwe chizindikiro choterocho. Kumbali ina, ophunzira athithithi a Yesu avomerezedwa kuwona mawalitsidwe a Yesu monga chitsimikiziro cha maulosi a Ufumu. Chotero, Petro pambuyo pake analemba kuti: “Ndipo tiri nawo mawu achinenero okhazikika koposa.” Mateyu 16:28–17:13; Marko 9:1-13; Luka 9:27-37; 2 Petro 1:16-19.
◆ Ndimotani mmene ena anawonera Kristu akubwera mu Ufumu wake asanalawe imfa?
◆ M’masomphenya, Mose ndi Eliya analankhula ponena za chiyani ndi Yesu?
◆ Nchifukwa ninji masomphenyawa anali thandizo lolimbikitsa chotero kwa ophunzira?
[Chithunzi chachikulu patsamba 9]