Anachita Chifuniro cha Yehova
Mariya anasankha “Dera Lokoma”
M’MASIKU a Yesu, akazi achiyuda anali oponderezedwa ndi chikhalidwe cha arabi. Chifukwa cha chimenecho, ankawaletsa kuphunzira Chilamulo. Ndithudi, Mishnah inafotokoza kuti: “Ngati mwamuna aliyense aphunzitsa mwana wake wamkazi za Chilamulo, zimakhala ngati wam’phunzitsa zachiwerewere.”—Sotah 3:4.
Zotsatira zake zinali zakuti, akazi ambiri a m’Yudeya m’zaka za zana loyamba anali osaphunzira. The Anchor Bible Dictionary inati: “Palibe umboni uliwonse wotsimikizira kuti Yesu asanayambe utumiki wake, akazi achiyuda ankaloledwa kukhala ophunzira a aphunzitsi akuluakulu, ndipo n’zachionekere kuti sankawalola kuyenda ndi aphunzitsi amenewo, kapena kulangiza wina aliyense kupatulapo ana.” Popitiriza kuwaona akazi ngati opanda phindu, atsogoleri ena achipembedzo anaika malamulo oletsa amuna kulankhula ndi akazi poyera!
Yesu sanasamale za mkhalidwe wopanda umulungu umenewo. Anaphunzitsa akazi ndi amuna omwe, ndipo om’tsatira ake anali amuna ndi akazi omwe. (Luka 8:1-3) Nthaŵi ina, Yesu anaitanidwa kuti akakhale mlendo wa Marita ndi Mariya. (Luka 10:38) Akazi aŵiri ameneŵa anali alongo ake a Lazaro, ndipo atatuwa anali ophunzira ndi mabwenzi abwino a Yesu. (Yohane 11:5) Banja limeneli liyenera kuti linali lodziŵika kwambiri, tikalingalira za kuchuluka kwa anthu amene anadza kudzatonthoza Marita ndi Mariya pamene Lazaro anamwalira. Komabe, chomwe chinachitika m’nyumba yawo pamene Yesu anali mlendo wawo, chinapereka phunziro lamtengo wapatali zedi kwa iwo ndi kwa ifenso lerolino.
Kuphunzira pa Mapazi a Yesu
Mosakayikira, Marita ndi Mariya anali achangu kukonzera Yesu chakudya chapamwamba, ndipo mwinamwake chinali chakudya chawo chamasiku onse. (Yerekezani ndi Yohane 12:1-3.) Komabe, pamene mlendo wawoyo anafika, Mariya ‘anakhala pamapazi a Ambuye namva mawu ake.’ (Luka 10:39) Miyambo ya anthu sikanaletsa Yesu kuphunzitsa mkazi woona mtima ameneyu yemwe anali wofunitsitsa kuphunzira! Tangoganizani Mariya atakhala kutsogolo kwa Yesu, monga wophunzira amene wafunitsitsa kumvetsera zimene Mbuyake akuphunzitsa.—Yerekezani ndi Deuteronomo 33:3; Machitidwe 22:3.
Mosiyana ndi Mariya, Marita “anatekeseka ndi kutumikira kwambiri.” Anali wotanganidwa ndi ntchito za panyumbapo pokonza chakudya chokoma. Pambuyo pake Marita anakhumudwa chifukwa mbale wakeyo samamuthandiza ntchitoyo ndipo anangokhala pa mapazi a Yesu! Choncho Yesu alikulankhulabe ndi Mariya, Marita anati: “Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga anandisiya nditumikire ndekha? Mumuuze tsono kuti andithandize.”—Luka 10:40.
Ndi iko komwe, panalibe cholakwika ndi pempho la Marita. N’zoona kuti kuphika chakudya cha anthu ambiri ndi ntchito yaikulu, kotero kuti sinali yoyenera kuchitidwa ndi munthu mmodzi. Komabe Yesu anapezerapo mwayi wopereka phunziro labwino pa mawu a Marita. Ndipo iye anati: “Marita, Marita, uda nkhaŵa nuvutika ndi zinthu zambiri. Koma chisoŵeka chinthu chimodzi. Pakuti Mariya anasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye.”—Luka 10:41, 42.
Yesu sanali kutanthauza kuti Marita analibe chidwi ndi zinthu zauzimu. Mosiyana ndi zimenezo, iye anali kudziŵa kuti Marita anali mkazi wodzipereka kwa Mulungu.a Ndiye chifukwa chake anaitanira Yesu kunyumba kwawo. Komabe, popereka chidzudzulo chofeŵacho, Yesu anali kuuza Marita kuti, mwa kupereka maganizo ake onse ku chakudyacho, akuphonya mwayi wosoŵa zedi wolandira malangizo mwachindunji ochokera kwa Mwana wa Mulugu.
N’zoona kuti chikhalidwe cham’nthaŵiyo chinalimbikitsa maganizo akuti mkazi wabwino amadziŵika ndi changu chake pantchito zapanyumba. Koma mawu a Yesu anasonyeza kuti akazi mofanana ndi amuna, angakhale pansi pa mapazi a Mwana wa Mulungu ndi kulandira mawu amoyo! (Yohane 4:7-15; Machitidwe 5:14) Chifukwa cha chimenecho, kukanakhala bwino ngati Marita akanapereka mbale zochepa za chakudya—ngakhale imodzi yokha—ngati akanafuna kukakhala pa mapazi a Mbuye wake ndi kuphunzira kuchokera kwa iye.—Yerekezani ndi Mateyu 6:25.
Phunziro kwa Ife
Lerolino, amuna ndi akazi ali m’gulu la anthu amene amamva kuitana kwa Yesu kwakuti ‘tengani madzi amoyo kwaulere.’ (Chivumbulutso 22:17) Posonkhezeredwa ndi chikondi, ena—ofanana ndi Marita—amayesetsa kuthandiza pa zosoŵa za okhulupirira anzawo. Amadzipereka kuchita chilichonse ndipo amakhala achangu kuchitapo kanthu, motero Yehova analonjeza kufupa ntchito zawo zachikondizo. (Ahebri 6:10; 13:16) Ena mwinamwake amafanana kwambiri ndi Mariya. Ali ofatsa ndi omvetsera kwambiri zinthu zauzimu. Changu chawo polingalira Mawu a Mulungu chimawathandiza kukhala ozikika mwamphamvu m’chikhulupiriro.—Aefeso 3:17-19.
Anthu a m’magulu onse aŵiriŵa amachita zofunika zedi mu mpingo wachikristu. Komabe, onse ayenera ‘kusankha dera lokoma’ mwa kuika zinthu zauzimu patsogolo. Mwa kuyesa zinthu zosiyana, tidzalandira chiyanjo ndi madalitso a Yehova.—Afilipi 1:9-11.
[Mawu a M’munsi]
a Umboni wakuti Marita anali mkazi wauzimu, wachikhulupiriro champhamvu, ukusonyezedwa pamene anali kukambirana ndi Yesu pambuyo pa imfa ya mlongo wake Lazaro. Pachochitikachi, anali Marita amene anachita changu pofuna kuonana ndi Mbuye wake.—Yohane 11:19-29.