Deuteronomo
33 Tsopano awa ndi madalitso amene Mose, munthu wa Mulungu woona, ananena asanafe kuti Aisiraeli adzalandira.+ 2 Iye anati:
“Yehova anabwera kuchokera ku Sinai,+
Anawala pa iwo kuchokera ku Seiri.
Anawala mwa ulemerero kuchokera kudera lamapiri la Parana,+
Ndipo anali ndi angelo ake ambirimbiri,*+
Kudzanja lake lamanja kunali asilikali ake.+
5 Mulungu anakhala mfumu mu Yesuruni,*+
Pamene atsogoleri a anthu anasonkhana pamodzi,+
Limodzi ndi mafuko onse a Isiraeli.+
7 Iye ananena kuti Yuda adzalandira madalitso otsatirawa:+
“Inu Yehova, imvani mawu a Yuda,+
Ndipo mumubwezere kwa anthu ake.
Munayamba kulimbana naye pafupi ndi madzi a ku Meriba.+
9 Munthu amene anauza bambo ndi mayi ake kuti, ‘Sindinasonyeze kuti ndikuwalabadira.’
Ngakhale abale ake sanawasamale,+
Ndipo ana ake anakhala ngati sakuwadziwa.
Chifukwa anatsatira mawu anu,
Ndipo anasunga pangano lanu.+
Azipereka nsembe zofukiza kuti zikhale kafungo kosangalatsa kwa inu,*+
Ndi nsembe yathunthu paguwa lanu lansembe.+
11 Inu Yehova dalitsani mphamvu zake,
Ndipo mukondwere ndi ntchito ya manja ake.
Muphwanye miyendo ya* amene akumuukira,
Kuti amene amadana naye asathenso kuimirira.”
12 Ponena za Benjamini anati:+
“Wokondedwa wa Yehova azikhala wotetezedwa ndi iye,
Pamene akumuteteza tsiku lonse,
Iye adzakhala pakati pa mapewa ake.”
“Dziko lake lidalitsidwe ndi Yehova.+
Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino kwambiri zakumwamba,
Ndi mame komanso madzi ochokera mu akasupe a pansi pa nthaka.+
14 Lidalitsidwenso ndi zinthu zabwino kwambiri, zochokera ku dzuwa,
Ndi zokolola zabwino kwambiri mwezi uliwonse,+
15 Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino koposa zamʼmapiri akale,*+
Ndi zinthu zabwino kwambiri zamʼmapiri amene adzakhalapo mpaka kalekale.
16 Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino kwambiri za padziko lapansi, ndi chuma chake chonse,+
Komanso movomerezedwa ndi Iye amene anaonekera mʼchitsamba chaminga.+
Madalitso amenewa akhale pamutu pa Yosefe,
Paliwombo pa munthu amene anasankhidwa pakati pa abale ake.+
17 Ulemerero wake ndi wofanana ndi wa mwana wa ngʼombe wamphongo woyamba kubadwa,
Ndipo nyanga zake ndi nyanga za ngʼombe yamphongo yamʼtchire.
Nyanga zimenezo adzakankha* nazo anthu.
Adzakankha nazo anthu onse pamodzi mpaka kukafika kumalekezero a dziko lapansi.
Nyanga zimenezo ndi anthu masauzande makumimakumi a fuko la Efuraimu,+
Ndiponso anthu masauzande a fuko la Manase.”
“Kondwera Zebuloni iwe, pa maulendo ako,
Ndiponso iwe Isakara, mʼmatenti ako.+
19 Adzaitanira mitundu ya anthu kuphiri.
Kumeneko adzapereka nsembe zachilungamo.
Chifukwa adzatenga chuma* kuchokera pa chuma chochuluka cha mʼnyanja,
Ndi chuma chobisika chamumchenga.”
“Wofutukula malire a dera la Gadi ndi wodala.+
Iye adzagona kumeneko ngati mkango,
Wokonzeka kukhadzula dzanja, komanso kungʼamba mutu paliwombo.
21 Iye adzasankha gawo labwino kwambiri kuti likhale lake,+
Chifukwa gawo loperekedwa ndi wopereka malamulo linasungidwa kumeneko.+
Atsogoleri a anthu adzasonkhana pamodzi.
Iye adzachita chilungamo cha Yehova,
Ndi zigamulo zake zokhudza Isiraeli.”
“Dani ndi mwana wa mkango.+
Adzadumpha kuchokera ku Basana.”+
“Nafitali wakhutira chifukwa chovomerezedwa,
Ndipo madalitso a Yehova amuchulukira.
Tenga chigawo chakumadzulo ndi kumʼmwera.”
“Aseri anamudalitsa ndi ana aamuna.
Abale ake amukomere mtima,
Ndipo apondetse* mapazi ake mʼmafuta.
25 Chitsulo komanso kopa* ndi zokhomera geti lako,+
Ndipo udzakhala wotetezeka masiku onse a moyo wako.*
26 Palibe amene angafanane ndi Mulungu woona+ wa Yesuruni,+
Amene amayenda mumlengalenga kuti akuthandize,
Amene amayenda pamitambo mu ulemerero wake.+
27 Mulungu ndi malo ako othawirapo kuyambira kalekale,+
Iye wakunyamula mʼmanja ake omwe adzakhalapo mpaka kalekale.+
28 Isiraeli adzakhala motetezeka,
Kasupe wa Yakobo adzakhala motetezeka,
Mʼdziko lokhala ndi chakudya komanso vinyo watsopano,+
Limene kumwamba kwake kudzagwetsa mame.+