Yehova Amapereka “Mzimu Woyera kwa Amene Akum’pempha”
“Ngati inu, ngakhale muli oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.”—LUKA 11:13.
1. Kodi ndi liti makamaka pamene timafunikira thandizo la mzimu woyera?
‘SINDINGATHE kupirira zimenezi pandekha. Pokhapokha ngati mzimu woyera utandithandiza, m’pamene ndingathe kupirira chiyeso chimenechi.’ Kodi munayamba mwalankhulapo mawu ochokera pansi pamtima ngati amenewa? Akhristu ochuluka alankhulapo mawu otero. Mwina munalankhula zimenezo mutadziwa kuti mwapezeka ndi matenda oopsa. Kapena mwina inali nthawi imene mnzanu amene mwakhala naye muukwati kwa nthawi yaitali anamwalira. Kapena pamene munayamba kuvutika maganizo, wosakhalanso wosangalala ngati kale. Panthawi zovuta m’moyo, mwina munamva kuti mukupirira chifukwa mzimu woyera wa Yehova unakupatsani “mphamvu yoposa yachibadwa.”—2 Akorinto 4:7-9; Salmo 40:1, 2.
2. (a) Kodi Akhristu oona amakumana ndi zovuta ziti? (b) Kodi mu nkhani ino tikambirana mafunso ati?
2 Akhristu oona ayenera kulimbana ndi zovuta ndiponso zitsutso, zinthu zomwe zikuchulukirachulukirabe m’dziko losaopa Mulungu limene tikukhalamoli. (1 Yohane 5:19) Kuphatikiza pa zimenezo, otsatira a Khristu amaukiridwa ndi Satana Mdyerekezi, amene ali pa nkhondo yoopsa ndi anthu omwe ‘akusunga malamulo a Mulungu, ndi amene ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.’ (Chivumbulutso 12:12, 17) Choncho, n’zosadabwitsa kuti tikufunikira thandizo la mzimu wa Mulungu tsopano kuposa kale. Kodi tingatani kuti tipitirizebe kulandira mokwanira mzimu woyera wa Mulungu? Ndipo kodi n’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yehova ndi wofunitsitsa kutipatsa chilimbikitso chofunikira pa nthawi za chiyeso? Timapeza mayankho a mafunso amenewa mu mafanizo awiri a Yesu.
Limbikirani Kupemphera
3, 4. Kodi ndi fanizo liti limene Yesu anasimba, ndipo likugwirizana motani ndi kupemphera?
3 Mmodzi mwa ophunzira a Yesu anapemphapo kuti: “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera.” (Luka 11:1) Poyankha, Yesu anawasimbira ophunzira akewo mafanizo awiri. Loyamba ndi lonena za munthu amene walandira mlendo, ndipo lachiwiri ndi lonena za atate amene akumvetsera zopempha za mwana wake. Tiyeni tikambirane mafanizo awiri amenewa, lililonse palokha.
4 Yesu anati: “Ndani wa inu amene ali ndi bwenzi lake kumene angapite pakati pa usiku kukam’pempha kuti, ‘Bwanawe, ndibwerekeko mitanda itatu ya mkate, chifukwa mnzanga wangofika kumene kuchokera ku ulendo ndipo ndilibe chom’patsa’? Ndiyeno ali m’nyumbayo n’kuyankha kuti, ‘Usandivutitse ine. Takhoma kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga aang’ono tagona kale; sindingadzukenso kuti ndikupatse kanthu.’ Ndithu ndikukuuzani, Adzadzuka ndi kum’patsa zonse zimene akufuna, osati chifukwa chakuti ndi bwenzi lake, komatu chifukwa cha kulimbikira kwake mwankhakamira.” Kenako, Yesu anafotokoza mmene fanizoli likugwirizanira ndi kupemphera, anati: “Choncho ndikukuuzani, Pemphanibe, ndipo adzakupatsani; funafunanibe, ndipo mudzapeza; gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani. Pakuti aliyense wopempha amalandira, aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzam’tsegulira.”—Luka 11:5-10.
5. Kodi fanizo lonena za munthu wolimbikira kupempha likutiphunzitsa kuti pamene tikupemphera tiyenera kukhala ndi mtima wotani?
5 Fanizo losavuta kumva limeneli, la munthu wolimbikira, likusonyeza mtima umene tiyenera kukhala nawo tikamapemphera. Onani kuti Yesu ananena kuti mwamunayu anapeza zimene anali kufuna “chifukwa cha kulimbikira kwake mwankhakamira.” (Luka 11:8) Mawu akuti “kulimbikira mwankhakamira” amapezeka kamodzi kokha m’Baibulo. Mawuwa anamasuliridwa kuchokera ku mawu a Chigiriki amene kwenikweni amatanthauza “kupanda manyazi.” Kawirikawiri mawu akuti kupanda manyazi amasonyeza khalidwe loipa. Komabe, kupanda manyazi kapena kulimbikira kukasonyezedwa pa zinthu zabwino, lingakhale khalidwe lotamandika. Zinali choncho ndi wolandira mlendo wa m’fanizoli. Sanachite manyazi kupempha molimbikira zimene anali kufuna. Popeza kuti Yesu anafotokoza wolandira mlendo ameneyu ngati chitsanzo kwa ife, nafenso tiyenera kupemphera molimbikira. Yehova akufuna kuti ife ‘tizipemphabe, tizifunafunabe, tizigogodabe.’ Ndipo iye ‘adzapereka mzimu woyera kwa amene akum’pempha.’
6. M’nthawi ya Yesu, kodi anthu anali kuona bwanji mwambo wochereza alendo?
6 Yesu sanangotisonyeza kuti tiyenera kulimbikira mwankhakamira kupemphera ayi, koma anasonyezanso chifukwa chochitira zimenezi. Kuti timvetse bwino phunziro limeneli, tiyenera kuganizira mmene anthu amene ankamvetsera fanizo la Yesu lonena za wolandira mlendo wolimbikira ameneyo, ankaonera kufunika kwa mwambo wochereza alendo. Nkhani zambiri za m’Malemba zimasonyeza kuti m’nthawi za m’Baibulo, kusamalira alendo unali mwambo wofunika kwambiri, makamaka kwa atumiki a Mulungu. (Genesis 18:2-5; Aheberi 13:2) Kulephera kuchereza alendo chinali chinthu chochititsa manyazi. (Luka 7:36-38, 44-46) Poganizira zimenezo, tiyeni tionenso nkhani ya Yesu ija.
7. N’chifukwa chiyani wolandira mlendo wa mu fanizo la Yesu sanachite manyazi kudzutsa mnzake?
7 Wolandira mlendo wa mu fanizoli analandira mlendo pakati pa usiku. Wolandira mlendoyo anakakamizika kuti akonzere mlendoyo chakudya, koma ‘analibe chom’patsa.’ Kwa wolandira mlendoyo, limeneli linali vuto lofunika thandizo mwamsanga. Iye anayenera kupeza mkate, mosasamala kanthu za zovuta zimene akanakumana nazo. Choncho anapita kwa mnzake ndipo mopanda manyazi anam’dzutsa. Wolandira mlendoyo anati: “Bwanawe, ndibwerekeko mitanda itatu ya mkate.” Analimbikira kupempha mpaka anapeza chimene anali kufuna. Pambuyo popeza mitandayo, m’pamene anatha kukhala wolandira mlendo wabwino.
Tikazifuna Kwambiri M’pamenenso Timazipempha Kwambiri
8. N’chiyani chimene chidzatilimbikitsa kupempha mzimu woyera molimbika?
8 Kodi fanizoli likusonyeza chifukwa chiti chopempherera molimbika? Mwamunayo anapitirizabe kupempha mkate chifukwa ankadziwa kuti kukhala ndi mitandayo kunali kofunika kwambiri kuti athe kukwaniritsa udindo wake monga wolandira mlendo. (Yesaya 58:5-7) Popanda mkate, sakanakwanitsa udindo wakewo. Mofanana ndi zimenezi, chifukwa chakuti timazindikira kuti kukhala ndi mzimu wa Mulungu n’kofunika kwambiri kuti tithe kuchita utumiki wathu monga Akhristu oona, timapitirizabe kupempherera mzimu umenewu kwa Mulungu. (Zekariya 4:6) Popanda mzimuwo, sitingakwanitse utumiki wathu. (Mateyo 26:41) Kodi mukuona mfundo yofunika imene tikuphunzira mu fanizo limeneli? Ngati timaona mzimu wa Mulungu kukhala chinthu chinachake chimene timachifunikira kwambiri, ndiye kuti tidzalimbikira kuupempha.
9, 10. (a) Perekani chitsanzo chosonyeza chifukwa chimene tiyenera kulimbikira kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu wake. (b) Kodi ndi funso liti limene tingadzifunse, ndipo n’chifukwa chiyani?
9 Kuti phunziro limeneli tilione m’zochitika za masiku ano, taganizirani kuti mmodzi mwa anthu a m’banja mwanu wayamba kudwala pakati pa usiku. Kodi mungakadzutse dokotala n’kumupempha kuti akuthandizeni? Simungatero ngati wodwalayo sakudwala kwambiri. Komabe, ngati wodwalayo mtima wake wasiya kugwira bwino ntchito, simungachite manyazi kukadzutsa dokotala. N’chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mwakumana ndi matenda ofunika thandizo mwamsanga. Mukudziwa kuti thandizo la munthu waluso likufunikira kwambiri. Ngati simupempha thandizolo, mwina wodwalayo angamwalire. Mofananamo, Akhristu oona nthawi zonse amakumana ndi vuto lofunika thandizo mwamsanga. Ndipotu, Satana akuyendayenda uku ndi uku ngati “mkango wobangula,” kuyesayesa kuti atidye. (1 Petulo 5:8) Kuti ife tikhalebe amoyo mwauzimu, timafunikira kwambiri thandizo la mzimu wa Mulungu. Tingakhale pa ngozi yaikulu ngati sitipempha thandizo kwa Mulungu. Choncho, polimbikira mwankhakamira, timapempha mzimu woyera kwa Mulungu. (Aefeso 3:14-16) Pokhapokha ngati tichita zimenezi, tingakhalebe ndi mphamvu zimene tikufunikira kuti ‘tipirire mpaka mapeto.’—Mateyo 10:22; 24:13.
10 Choncho n’kofunika kwa ife kumadzifunsa nthawi zina kuti, ‘Kodi ndimalimbikira kwenikweni pa mapemphero anga?’ Kumbukirani kuti tikazindikira bwino kuti tikufunikira thandizo la Mulungu, tidzalimbikira kwambiri kupempherera mzimu woyera.
Kodi N’chiyani Chimatilimbikitsa Kupemphera ndi Chidaliro?
11. Kodi Yesu anafotokoza motani mmene fanizo la atate ndi mwana wake likugwirizanira ndi pemphero?
11 Fanizo la Yesu la wolandira mlendo wolimbikira likusonyeza khalidwe la munthu wokhulupirira amene amapempherayo. Fanizo lotsatira likusonyeza khalidwe la Yehova Mulungu amene amamva mapempherowo. Yesu anafunsa kuti: “Kodi alipo tate pakati panu kapena, amene mwana wake atam’pempha nsomba angam’patse njoka m’malo mwa nsomba? Kapena atam’pempha dzira iye n’kum’patsa chinkhanira?” Yesu anapitiriza kufotokoza fanizolo kuti: “Choncho ngati inu, ngakhale muli oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.”—Luka 11:11-13.
12. Ndi motani mmene fanizo la atate amene akumva pempho la mwana wake limasonyezera kuti Yehova amafuna kutiyankha mapemphero athu?
12 Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha atate amene anapereka kwa mwana wake chimene anali kufuna, Yesu anafotokoza bwino mmene Yehova amamvera ndi anthu amene amapemphera kwa iye. (Luka 10:22) Choyamba, taonani kusiyana pakati pa mafanizo awiriwa. Mosiyana ndi mwamuna wa mu fanizo loyamba lija amene ankanyinyirika kuthandiza mnzake, Yehova ali monga kholo laumunthu, limene lili tcheru kufuna kuyankha pempho la mwana wake. (Salmo 50:15) Yesu anasonyezanso kuti Yehova ali ndi mtima wofuna kutithandiza mwa kufotokoza za atate waumunthu n’kumuyerekezera ndi atate wakumwamba. Iye anati, ngati atate waumunthu, ngakhale ‘ali woipa’ chifukwa cha uchimo wobadwa nawo, amapatsa mwana wake mphatso yabwino, kuli bwanji Atate wathu wakumwamba, pokhala wokoma mtima, adzapereka mzimu woyera kwa banja lake la anthu omulambira.—Yakobe 1:17.
13. Kodi tingakhale ndi chidaliro chotani tikamapemphera kwa Yehova?
13 Kodi ndi phunziro lanji limene tikupezapo? Tingakhale ndi chidaliro chakuti, tikapempha mzimu woyera kwa Atate wathu wakumwamba, iye ndi wofunitsitsa kutipatsa zopempha zathu. (1 Yohane 5:14) Tikamapemphera kwa iye nthawi ndi nthawi, Yehova sadzanena monga mmene ananenera munthu wa m’fanizo loyamba lija kuti: “Usandivutitse ine. Takhoma kale chitseko.” (Luka 11:7) Mosiyana ndi zimenezo, Yesu anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani; funafunanibe, ndipo mudzapeza; gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani.” (Luka 11:9, 10) Inde, Yehova adzatiyankha “tsiku lakuitana ife.”—Salmo 20:9; 145:18.
14. (a) Kodi ndi maganizo olakwika ati amene amavutitsa anthu ena akakumana ndi ziyeso? (b) Tikamakumana ndi ziyeso, n’chifukwa chiyani tingapemphere kwa Yehova ndi chidaliro?
14 Fanizo la Yesu la atate wachikondi likutsindikanso kuti, ubwino wa Yehova umaposa ubwino umene kholo lililonse laumunthu lingasonyeze. Choncho, sitiyenera kuganiza kuti ziyeso zimene timakumana nazo zikutanthauza kuti Mulungu sakukondwera nafe. Satana, yemwe ndi mdani wathu wamkulu, ndi amene amafuna kuti tiziganiza choncho. (Yobu 4:1, 7, 8; Yohane 8:44) Maganizo odziimba mlandu oterowo, sachokera m’Malemba. Yehova satiyesa “ndi zinthu zoipa.” (Yakobe 1:13) Satipatsa chiyeso chonga njoka kapena mayesero onga chinkhanira. Atate wathu wakumwamba amapereka “zinthu zabwino kwa onse om’pempha.” (Mateyo 7:11; Luka 11:13) Indedi, tikazindikira kwambiri za ubwino wa Yehova ndiponso kuti amafuna kutithandiza, tidzalimbikitsidwa kwambiri kuti tizipemphera ndi chidaliro. Tikamatero, ifenso tidzatha kulankhula mawu ofanana ndi a wamasalmo amene analemba akuti: “Koma Mulungu anamvadi; anamvera mawu a pemphero langa.”—Salmo 10:17; 66:19.
Mmene Mzimu Woyera Ulili Mthandizi Wathu
15. (a) Kodi Yesu analonjeza zotani ponena za mzimu woyera? (b) Ndi njira imodzi iti imene mzimu woyera umatithandizira?
15 Atatsala pang’ono kufa, Yesu anatsimikiziranso zimene ananena kale m’mafanizo ake. Ponena za mzimu woyera iye anauza atumwi ake kuti: “Ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani mthandizi wina kuti adzakhale nanu kosatha.” (Yohane 14:16) Choncho Yesu analonjeza kuti mthandizi, kapena mzimu woyera, udzakhala ndi otsatira ake m’tsogolo, kuphatikizapo m’masiku athu ano. Kodi ndi njira imodzi yaikulu iti imene mzimu woyera umatithandizira masiku ano? Mzimu woyera umatithandiza kupirira ziyeso zosiyanasiyana. Motani? Mtumwi Paulo, amene iye mwini anakumana ndi mayesero, anafotokoza m’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Korinto mmene mzimu wa Mulungu unam’thandizira. Tiyeni tikambirane mwachidule zimene iye analemba.
16. Kodi tingakumane bwanji ndi zinthu zofanana ndi zimene Paulo anakumana nazo?
16 Choyamba, Paulo anauza okhulupirira anzake momasuka kuti anali kulimbana ndi “munga m’thupi,” mayesero a mtundu wina wake. Kenako anati: “Katatu konse ndinachonderera Ambuye [Yehova] kuti mungawu undichoke.” (2 Akorinto 12:7, 8) Ngakhale kuti Paulo anachonderera Mulungu kuti achotse mavuto akewo, sanachoke ayi. Mwina masiku ano mumakumananso ndi zinthu zofananazo. Monga Paulo, mungapemphere mwakhama ndiponso ndi chidaliro, kupempha Yehova kuti akuchotsereni mayesero. Komabe, mosasamala kanthu za kupempha kwanu mobwerezabwereza, mukupitirizabe kuvutika. Kodi zimenezi zimatanthauza kuti Yehova sakuyankha mapemphero anu ndiponso kuti mzimu wake sukukuthandizani? Ayi si choncho. (Salmo 10:1, 17) Onani zimene kenako mtumwi Paulo ananena.
17. Kodi ndi motani mmene Yehova anayankhira mapemphero a Paulo?
17 Poyankha mapemphero a Paulo, Mulungu anamuuza kuti: “Kukoma mtima kwa m’chisomo changa kwakukwanira; pakuti mphamvu yanga imakhala yokwanira m’kufooka.” Paulo anati: “Choncho, ndidzadzitama mosangalala kwambiri pa kufooka kwanga, kuti mphamvu ya Khristu ikhalebe pamutu panga ngati hema.” (2 Akorinto 12:9; Salmo 147:5) Chotero, Paulo anaona kuti kudzera mwa Khristu, Mulungu anamufunyululira chitetezo chake champhamvu monga hema. Leronso, Yehova amayankha mapemphero athu mwanjira yofananayo. Iye amafunyulula chitetezo chake kuti chitchingire atumiki ake.
18. N’chifukwa chiyani timatha kupirira ziyeso?
18 N’zoona kuti, hema saletsa mvula kuti isagwe kapena mphepo kuti isawombe, koma amangoteteza ku zinthu zimenezo. N’chimodzimodzinso chitetezo chimene chimaperekedwa ndi “mphamvu ya Khristu.” Siletsa ziyeso kuti zisatigwere kapena kuti tisakumane ndi mavuto ayi. Koma, imatiteteza mwauzimu ku zinthu zovulaza za m’dzikoli ndiponso kwa wolamulira wa dzikoli, Satana, akamatiukira. (Chivumbulutso 7:9, 15, 16) Choncho, ngakhale ngati mukulimbana ndi chiyeso chimene ‘sichikukuchokani,’ mungakhale ndi chikhulupiriro choti Yehova akudziwa za kuvutika kwanu ndiponso kuti wamva ‘kufuula kwanu.’ (Yesaya 30:19; 2 Akorinto 1:3, 4) Paulo analemba kuti: “Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire, koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.”—1 Akorinto 10:13; Afilipi 4:6, 7.
19. Kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?
19 Mwachidziwikire, ‘masiku otsiriza’ ano a dziko losaopa Mulungu ili, amadziwika ndi “nthawi yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Koma ngakhale zili choncho, kwa atumiki a Mulungu, nthawi imeneyi si yovuta kwambiri moti sitingapirire. N’chifukwa chiyani? Chifukwa cha thandizo ndi chitetezo cha mzimu woyera wa Mulungu, umene Yehova amapatsa mwakufuna kwake ndiponso mokwanira kwa onse amene amamupempha molimbika ndiponso mwachidaliro. Chotero, tiyeni titsimikize mtima kupitirizabe kupempherera mzimu woyera tsiku lililonse.—Salmo 34:6; 1 Yohane 5:14, 15.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi timayenera kuchita chiyani kuti tilandire mzimu woyera wa Mulungu?
• N’chifukwa chiyani tingakhale ndi chidaliro kuti tikamapempherera mzimu woyera, Yehova adzatiyankha?
• Ndi motani mmene mzimu woyera umatithandizira kupirira ziyeso?
[Chithunzi patsamba 21]
Kodi tingaphunzire chiyani pa fanizo la Yesu lonena za wolandira mlendo wolimbikira?
[Chithunzi patsamba 22]
Kodi mumapempherera mzimu woyera wa Mulungu molimbika?
[Chithunzi patsamba 23]
Kodi timaphunzira chiyani za Yehova mu fanizo la atate wachikondi?