Salimo
ל [Lamed]
10 Nʼchifukwa chiyani inu Yehova mukuima kutali?
Nʼchifukwa chiyani mukubisala pa nthawi ya mavuto?+
2 Modzikuza, munthu woipa amathamangitsa munthu wovutika,+
Koma adzakodwa mumsampha wa ziwembu zake.+
3 Chifukwa munthu woipa amanena za zolinga zake* zadyera modzitamandira,+
Ndipo amadalitsa munthu wadyera.
נ [Nun]
Iye amanyoza Yehova.
4 Chifukwa cha kudzikweza, munthu woipa safufuza kuti adziwe Mulungu.
Iye amangoganiza kuti: “Kulibe Mulungu.”+
5 Zochita zake zikupitiriza kumuyendera bwino,+
Koma zigamulo zanu sangathe kuzimvetsa.+
Iye amanyogodola adani ake onse.
פ [Pe]
7 Mʼkamwa mwake mwadzaza matemberero, mabodza ndi kuopseza ena.+
Pansi pa lilime lake pali mavuto ndi zopweteka ena.+
ע [Ayin]
Maso ake akuyangʼanayangʼana munthu woti amuchite chiwembu.+
9 Amadikirira anthu pamalo amene iye amabisala ngati mkango umene uli pamalo ake amene umabisala.*+
Amadikirira kuti agwire munthu wovutika.
Amagwira munthu wovutikayo pomukulunga ndi ukonde wake.+
10 Munthu wovutikayo amaponderezedwa ndipo amawerama ndi chisoni.
Anthu ovutikawo amagwidwa ndi dzanja lake lamphamvu.
11 Mumtima mwake amanena kuti: “Mulungu waiwala zoipa zimene ndimachita.+
Iye wayangʼana kumbali.
Sakuona chilichonse.”+
ק [Qoph]
12 Nyamukani, inu Yehova.+ Inu Mulungu, chitanipo kanthu.+
Musaiwale anthu ovutika.+
13 Nʼchifukwa chiyani munthu woipa wanyoza Mulungu?
Mumtima mwake amanena kuti: “Simudzandiimba mlandu.”
ר [Resh]
14 Koma inu mumaona mavuto ndi masautso.
Mumayangʼana nʼkuchitapo kanthu.+
ש [Shin]
16 Yehova ndi Mfumu mpaka kalekale.+
Mitundu ya anthu yawonongedwa, yachotsedwa padziko lapansi.+
ת [Taw]
17 Koma inu Yehova mudzamva pempho la anthu ofatsa.+
Mudzalimbitsa mitima yawo+ ndipo mudzawamvetsera mwatcheru.+