Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kudya ndi Mfarisi
PAMBUYO pakuti Yesu wayankha osuliza omwe anafunsa magwero a mphamvu yake ya kuchiritsa munthu amene sanali kulankhula, Mfarisi akumuitana iye ku chakudya. Asanayambe kudya, Afarisi adzilowetsa m’mwambo wa kusamba manja awo kufikira m’chigongono. Iwo akuchita ichi pambuyo ndi pamapeto pa chakudya ndipo ngakhale pakati pa zakudya. Ngakhale kuti mwambowo sumanyalanyaza lamulo lolembedwa la Mulungu, iwo ukupita kupyola chimene Mulungu amafuna m’nkhani ya kuyera kwa mwambo.
Pamene Yesu akulephera kusunga mwambowo, wochereza wake wadabwitsidwa. Ngakhale kuti kudabwa kwake sikungakhale kunawonetsedwa mwapakamwa, Yesu akuzindikira iko ndi kunena kuti: “Tsopano inu Afarisi, muyeretsa kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma mkati mwanu mudzala zolanda ndi zoipa. Opusa inu! Kodi iye wopanga kunja kwake sanapanganso mkati mwake?”
Yesu mwakutero akuvumbulutsa chinyengo cha Afarisi omwe mwa mwambo amasamba manja awo koma amalephera kusambitsa mitima yawo kuchokera ku zoipa. Iye akuwalangiza kuti: “Patsani mphatso yachifundo za mkatimo, ndipo, onani! zonse ziri zoyera kwa inu.” Kupatsa kwawo kuyenera kusonkhezeredwa ndi mtima wachikondi, osati ndi chikhumbo chofuna kukondweretsa ena ndi chinyengo cha chilungamo.
“Tsoka inu Afarisi,” Yesu akupitiriza, “chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbewu tonunkhira ndi timbewu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo omwe amaleka chiŵeruziro ndi chikondi cha Mulungu! Mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo.” Lamulo la Mulungu kwa Aisrayeli limafuna kupereka chachikhumi, kapena gawo la khumi, la zokolola za m’munda. Mbewu zonunkhira ndi zokometsa chakudya ziri zomera zazing’ono kapena zitsamba zogwiritsiridwa ntchito m’kukometsera chakudya. Afarisi amapereka ngakhale chachikhumi cha zitsamba zosadziŵika zimenezi, koma Yesu akudzudzula iwo chifukwa cha kunyalanyaza chifuno chofunika koposa cha kusonyeza chikondi, kukoma mtima, ndi kukhala odzichepetsa.
Akumawatsutsa iwo mowonjezereka, Yesu akunena kuti: “Tsoka inu Afarisi, chifukwa mukonda mipando yaulemu mu masunagoge ndi kulankhulidwa m’misika! Tsoka inu, chifukwa muli ngati manda osawoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pawo sadziŵa!” Kudetsedwa kwawo sikuli kowonekera. Chipembedzo cha Afarisi chiri chodziwonetsera kunja koma chopanda zoyenerera mkati mwake! Icho chiri chozikidwa pa chinyengo.
Akumamvetsera ku chidzudzulo choterocho, wachilamulo, mmodzi wa awo odziŵa Lamulo la Mulungu, akudandaula: “Mpunzitsi, ndi kunena izi mutitonza ifenso.”
Yesu akuwapanga odziŵa Lamulo amenewa kukhalanso ndi thayo, akumanena kuti: “Tsoka inunso Achilamulo, chifukwa musenzetsa anthuwa katundu wosautsa kunyamula, ndipo inu nomwe simukhudza katunduyo ndi chala chanu chimodzi! Tsoka inu, chifukwa mumanga za pa manda a aneneri, ndipo makolo anu anawapha!”
Katundu amene Yesu akutchula ali miyambo ya pakamwa, koma achilamulo amenewo sangachotse lamulo ndi limodzi lonse kuchipangitsa icho kukhala chopepuka kwa anthu. Yesu akuvumbula kuti iwonso amavomereza ku kuphedwa kwa aneneri, ndipo akuchenjeza kuti: “‘Mwazi wa aneneri onse wokhetsedwa kuyambira kukhazika kwa dziko lapansi u[dz]afunidwa pa anthu a mbadwo uno, kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zakariya, amene anam’phera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya kachisi.’ Indetu, ndinena kwa inu, udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.”
Dziko la mtundu wa anthu wowomboleka linayambika ndi kudabwa kwa ana a Adamu ndi Hava; chotero, Abele anakhalako pa “kukhazika kwa dziko.” Kutsatira kuphedwa kwa Zakariya, mphamvu ya Siriya inasakaza Yuda. Koma Yesu akuneneratu za kusakazidwa koipa kwa mbadwo wake weniweni chifukwa cha kuipa kwake kokulirapo. Kusakaza kumeneko kukuwoneka chifupifupi zaka 38 pambuyo pake, mu 70 C.E.
Akumapitiriza kudzudzula kwake, Yesu akunena kuti: “Tsoka inu Achilamulo, chifukwa munachotsa chifungulo cha nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo ali nkulowa!” Akatswiri pa Lamulolo ali ndi thayo la kulongosola Mawu a Mulungu kwa anthu, kutsegula tanthauzo lake. Koma iwo akulephera kuchita ichi ndipo akufikira pa kuchotsa anthu ku mwaŵi wa kumvetsetsa.
Afarisi ndi akatswiri a lamulo akwiya ndi Yesu kaamba ka kuwavumbula iwo. Pamene iye akuchoka panyumbayo, iwo ayamba kutsutsa iye mwaukali ndi kumvutitsa ndi mafunso. Iwo akuyesera kumtchera msampha iye m’kunena chinachake kaamba ka chimene angampangitse iye kumangidwa. Luka 11:37-54; Deuteronomo 14:22; Mika 6:8; 2 Mbiri 24:20-25.
◆ Nchifukwa ninji Yesu akudzudzula Afarisi ndi akatswiri pa Lamulo?
◆ Ndi akatundu otani amene achilamulo amaika pa anthu?
◆ Ndi liti pamene panali “kukhazika kwa dziko?”