Kodi Yehova Amafunanji kwa Ife Lerolino?
“Mawu . . . mumtambo [anati], Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.”—MATEYU 17:5.
1. Kodi Chilamulo chinakwaniritsa liti cholinga chake?
YEHOVA anapatsa mtundu wa Israyeli Chilamulo, chimenenso chinali ndi malamulo ambiri. Ponena za malamulo amenewo, mtumwi Paulo analemba kuti: “Akhala zoikika za thupi zokha, . . . oikidwa kufikira nthaŵi yakukonzanso.” (Ahebri 9:10) Chilamulo chinakwaniritsa cholinga chake chitatsogolera Aisrayeli kufika pa kukhulupirira kuti Yesu ndiye Mesiya, kapena kuti Kristu. Ndiye chifukwa chake Paulo anati: “Kristu ali chimaliziro cha lamulo [“Chilamulo,” NW].”—Aroma 10:4; Agalatiya 3:19-25; 4:4, 5.
2. Kodi ndi ayani amene ankatsogozedwa ndi Chilamulo, ndipo ndi liti pamene sanafunikirenso kuchitsatira?
2 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Chilamulo chilibe mphamvu pa ife lerolino? Kwenikweni, ochuluka mwa anthu a padziko lapansi sanali kutsogozedwa ndi Chilamulo, monga momwe wamasalmo anafotokozera kuti: “[Yehova] aonetsa mawu ake kwa Yakobo; malemba ake, ndi maweruzo ake kwa Israyeli. Sanatero nawo anthu a mtundu wina; ndipo za maweruzo ake, sanaŵadziŵa.” (Salmo 147:19, 20) Mulungu atakhazikitsa pangano latsopano pamaziko a nsembe ya Yesu, ngakhale mtundu wa Israyeli weniweniwo sunayenerenso kutsatira Chilamulo. (Agalatiya 3:13; Aefeso 2:15; Akolose 2:13, 14, 16) Tsono ngati Chilamulo sichikugwiranso ntchito, kodi n’chiyani chimene Yehova akufuna kwa awo amene akufuna kum’tumikira lerolino?
Zimene Yehova Akufuna
3, 4. (a) Kodi n’chiyani kwenikweni chimene Yehova akufuna kwa ife lerolino? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira mapazi a Yesu mosamalitsa?
3 M’chaka chomaliza cha utumiki wa Yesu, atumwi ake Petro, Yakobo, ndi Yohane anatsagana naye pa phiri lalitali, mwinamwake pansonga ina ya pa Phiri la Hermoni. Kumeneko anaona masomphenya olosera ulemerero waukulu wa Yesu ndipo anamva Mawu a Mulungu weniweniyo akunena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani iye.” (Mateyu 17:1-5) Kwenikweni, ndizo zimene Yehova akufuna kwa ife—kuti timvere Mwana wake ndi kutsatira chitsanzo chake ndi ziphunzitso zake. (Mateyu 16:24) Chotero, mtumwi Petro analemba kuti: “Kristu anamva zoŵaŵa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake.”—1 Petro 2:21.
4 N’chifukwa chiyani tiyenera kulondola mapazi a Yesu mosamalitsa? Chifukwa chakuti mwa kum’tsanzira, timatsanziranso Yehova Mulungu. Yesu anali kuwadziŵa bwino kwambiri Atate wake, popeza kuti anakhala nawo zaka mabiliyoni osaŵerengeka kumwamba asanabwere padziko lapansi. (Miyambo 8:22-31; Yohane 8:23; 17:5; Akolose 1:15-17) Pamene anali padziko lapansi, Yesu anaimira Atate wake mokhulupirika. Anafotokoza kuti: “Monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.” Kwenikweni, Yesu anatsanzira Yehova mosamalitsa kwambiri moti anati: “Iye amene wandiona Ine waona Atate.”—Yohane 8:28; 14:9.
5. Kodi ndi lamulo lotani limene Akristu ayenera kutsatira, ndipo lamulo limenelo linayamba liti kugwira ntchito?
5 Kodi kumvera Yesu ndi kum’tsanzira kumaphatikizapo chiyani? Kodi kumafuna kuti tizitsatira lamulo linalake? Paulo analemba kuti: ‘Sindili womvera lamulo.’ Pamenepa anali kunena za “pangano lakale,” pangano la Chilamulo limene Mulungu anachita ndi Aisrayeli. Koma Paulo anavomereza kuti anali “womvera lamulo kwa Kristu.” (1 Akorinto 9:20, 21; 2 Akorinto 3:14) Pangano lakale la Chilamulo litatha, “pangano latsopano” lophatikana ndi “chilamulo cha Kristu” linayamba kugwira ntchito ndipo atumiki onse a Yehova lerolino ayenera kumvera chilamulocho.—Luka 22:20; Agalatiya 6:2; Ahebri 8:7-13.
6. Kodi “chilamulo cha Kristu” tingachifotokoze motani, ndipo timachimvera mwa kuchita chiyani?
6 Yehova sanapereke “chilamulo cha Kristu” monga mpambo wa malamulo, kuchigaŵa m’magulumagulu, monga momwe anachitira ndi pangano lakale la Chilamulo. Chilamulo chatsopano chimenechi cha otsatira a Kristu chilibe mpambo wautali wa zinthu zomwe iwo ayenera kuchita ndi zomwe sayenera kuchita. Komabe, m’Mawu ake, Yehova anasunga nkhani zinayi zosimba mwatsatanetsatane moyo ndi ziphunzitso za Mwana wake. Ndiponso, Mulungu anauzira ena mwa otsatira oyambirira a Yesu kuti apereke malangizo olembedwa onena za khalidwe, nkhani zokhudza mpingo, khalidwe la m’banja, ndi nkhani zina. (1 Akorinto 6:18; 14:26-35; Aefeso 5:21-33; Ahebri 10:24, 25) Tikamatsanzira chitsanzo cha Yesu Kristu m’moyo wathu ndi kutsatira ziphunzitso zake ndi kumvera uphungu wa olemba Baibulo a m’zaka za zana loyamba ouziridwawo, ndiye kuti tikumvera “chilamulo cha Kristu.” N’zimene Yehova akufuna kwa atumiki ake lerolino.
Kufunika kwa Chikondi
7. Kodi Yesu anamveketsa bwino motani mfundo yaikulu ya chilamulo chake pa Paskha womaliza ndi atumwi ake?
7 Pamene kuli kwakuti chikondi chinali chofunika m’Chilamulo, ndicho tanthauzo lenileni, kapena kuti mfundo yaikulu koposa ya chilamulo cha Kristu. Yesu anaimveketsa bwino mfundo imeneyi atakumana ndi atumwi ake kuti achite Paskha wa 33 C.E. Malinga ndi mafotokozedwe achidule a Yohane a zimene zinachitika usikuwo, Yesu anatchula chikondi nthaŵi 28 m’mawu ake ochokera pansi pa mtima. Zimenezi zinamveketsa bwino kwa atumwi ake mfundo yaikulu, kapena kuti tanthauzo lenileni la chilamulo chake. Chotero, Yohane anayamba nkhani yake ya zimene zinachitika madzulo ofunika kwambiri amenewo mwa kunena kuti: “Podziŵa kuti nthaŵi yake idadza yakuchoka kutuluka m’dziko lino lapansi, kumka kwa Atate, mmene anakonda ake a Iye yekha a m’dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.”—Yohane 13:1.
8. (a) Kodi n’chiyani chinasonyeza kuti panali mkangano wosatha pakati pa atumwi? (b) Kodi Yesu anawaphunzitsa motani kudzichepetsa atumwi ake?
8 Yesu anawakonda atumwi ake, ngakhale zinaoneka ngati kuti kuyesetsa kwake kuti awathandize kuthetsa kukhumbitsa kwawo ulamuliro ndi malo apamwamba kunali kosaphula kanthu. Miyezi ingapo iwo asanapite ku Yerusalemu, ‘anatsutsana wina ndi mnzake kuti wamkulu ndani.’ Komanso kutangotsala pang’ono kuti apite kumzindawo kukachita Paskha, anakangananso zoti wamkulu ndani. (Marko 9:33-37; 10:35-45) Zimene zinachitika atumwiwo atangoloŵa m’chipinda chapamwamba kukachita Paskha amene anali womaliza kuchitira pamodzi zikusonyeza kuti vuto limeneli linali lisanathebe. Panthaŵiyo palibe amene anatenga mwayi woti achite mwambo wochezera alendo wosambitsa ena mapazi. Pofuna kuwaphunzitsa kudzichepetsa, Yesu iyemwini anawasambitsa mapazi.—Yohane 13:2-15; 1 Timoteo 5:9, 10.
9. Kodi Yesu anatani ndi zimene zinachitika atachita Paskha womaliza?
9 Mosasamala kanthu za phunziro limenelo, atachita Paskha ndipo Yesu atakhazikitsa Chikumbutso cha imfa yake yomwe inali pafupi, onani zimene zinachitikanso. Uthenga Wabwino wa Luka umati: “Kunakhala kutsutsana mwa iwo, ndani wa iwo ayesedwe wamkulu.” M’malo mokwiya ndi atumwi ake ndi kuwadzudzula, Yesu anawalangiza mokoma mtima za kufunika kwa kukhala osiyana ndi atsogoleri akudziko okondetsa ulamuliro. (Luka 22:24-27) Kenako anapereka amene tingawatche kuti maziko a chilamulo cha Kristu, nati: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.”—Yohane 13:34.
10. Ndi lamulo lotani limene Yesu anapatsa ophunzira ake, ndipo linaphatikizapo chiyani?
10 Pambuyo pake madzulo omwewo Yesu anafotokoza mlingo umene chikondi chonga chake chiyenera kufikapo. Anati: “Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu. Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.” (Yohane 15:12, 13) Kodi Yesu anali kutanthauza kuti otsatira ake ayenera kulolera kufa chifukwa cha okhulupirira anzawo ngati zochitika zingafune zimenezo? Ndimo mmene Yohane, amene analipo pomwe Yesu ankanena mawuwo, anamverera chifukwa anadzalemba kuti: “Umo tizindikira chikondi, popeza Iyeyu [Yesu Kristu] anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.”—1 Yohane 3:16.
11. (a) Kodi timakwaniritsa motani chilamulo cha Kristu? (b) Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani?
11 Chotero, sitikwaniritsa chilamulo cha Kristu mwa kungophunzitsa ena za iye. Tiyeneranso kukhala ndi kuchita zinthu monga momwe Yesu anachitira. Zoonadi, Yesu anagwiritsa ntchito mawu ogwira mtima ndi osankhidwa bwino m’nkhani zake. Komanso, anaphunzitsa mwa kusonyeza chitsanzo. Ngakhale kuti Yesu anali cholengedwa chauzimu champhamvu kumwamba, iye sanalekerere mwayi wotumikira zofuna za Atate wake padziko lapansi ndi kusonyeza mmene tiyenera kukhalira. Anali wodzichepetsa, wokoma mtima, ndi woganizira ena, wothandiza othodwa ndi oponderezedwa. (Mateyu 11:28-30; 20:28; Afilipi 2:5-8; 1 Yohane 3:8) Ndipo Yesu analimbikitsa otsatira ake kuti azikondana, monga momwe iye anawakondera.
12. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chilamulo cha Kristu sichitanthauza kuti kukonda Yehova n’kosafunika kwenikweni?
12 Kodi kukonda Yehova—lamulo lalikulu koposa m’Chilamulo—n’kofunika motani m’chilamulo cha Kristu? (Mateyu 22:37, 38; Agalatiya 6:2) Kodi n’kosafunika kwenikweni? Kutalitali! Kukonda Yehova ndi kukonda Akristu anzathu zimayendera pamodzi nthaŵi zonse. Munthu sangakonde Yehova moona mtima popanda kukondanso mbale wake, popeza mtumwi Yohane anati: “Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: Pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.”—1 Yohane 4:20; yerekezani ndi 1 Yohane 3:17, 18.
13. Kodi panatsatira zotani pamene ophunzira analabadira lamulo la Yesu latsopano?
13 Pamene Yesu anapatsa ophunzira ake lamulo latsopano lakuti azikondana monga momwe iye anawakondera, ananenanso zotsatira za chikondicho. Iye anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Malinga n’kunena kwa Tertullian, amene anakhalako patapita zaka zoposa zana limodzi kuchokera panthaŵi ya imfa ya Yesu, chikondi chaubale cha Akristu oyambirira chinalidi ndi zotsatira zomwezo. Tertullian anagwira mawu a anthu osakhala Akristu akunena za otsatira a Kristu kuti: ‘Onani mmene amakonderana komanso mmene alili okonzekera kufa m’malo mwa anzawo.’ Tingadzifunse kuti, ‘Kodi Akristu anzanga ndimawasonyeza chikondi choterocho moti ndimaonekeratu kuti ndine mmodzi wa ophunzira a Yesu?’
Mmene Timasonyezera Chikondi Chathu
14, 15. Kodi n’chiyani chingapangitse chilamulo cha Kristu kukhala chovuta kuchilabadira, koma kodi n’chiyani chimene chingatithandize kuchilabadira?
14 N’kofunika kwambiri kuti atumiki a Yehova azisonyeza chikondi chonga cha Kristu. Koma kodi zimakuvutani kusonyeza chikondi kwa Akristu anzanu amene amachita zinthu zina modzikonda? Komatu monga taonera kale, ngakhale atumwi anakangana nafuna zinthu zokonda iwo okha. (Mateyu 20:20-24) Agalatiya nawonso anakangana okhaokha. Atafotokoza kuti chikondi cha pa mnansi chinakwaniritsa Chilamulo, Paulo anawachenjeza kuti: “Koma ngati mulumana ndi kudyana, chenjerani mungawonongane.” Atafotokoza ntchito za thupi ndi chipatso cha mzimu wa Mulungu, Paulo anawonjezaponso uphungu wakuti: “Tisakhale odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.” Kenako mtumwiyo analimbikitsa kuti: “Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Kristu.”—Agalatiya 5:14–6:2.
15 Pofuna kuti tizilabadira chilamulo cha Kristu, kodi Yehova akufuna zinthu zimene sitingathe kuchita? Ngakhale kuti zingakhale zovuta ndithu kusonyeza kukoma mtima kwa anthu amene atilalatira ndi kutikhumudwitsa, tikulamulidwabe ‘kukhala akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; ndi kuyenda m’chikondi.’ (Aefeso 5:1, 2) Tisaleke kuyang’ana chitsanzo cha Mulungu, amene “atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife.” (Aroma 5:8) Mwa kuyesetsa patokha kuthandiza ena, kuphatikizapo awo amene anatikhumudwitsa, tingakhale okhutira mumtima podziŵa kuti tikutsanzira Mulungu ndipo tikulabadira chilamulo cha Kristu.
16. Kodi timasonyeza motani chikondi chathu kwa Mulungu ndi Kristu?
16 Tiyenera kukumbukira kuti timasonyeza chikondi chathu mwa zinthu zimene timachita, osati mwa zimene timanena zokha. Ngakhale Yesu panthaŵi inayake anaona kuti kuchita mbali inayake ya chifuno cha Mulungu kunali kovuta kwambiri chifukwa cha zoloŵetsedwamo zake. “Atate, mukafuna Inu, chotsani chikho ichi pa Ine,” anapemphera motero Yesu. Komano anawonjezeranso kuti: “Koma si kufuna kwanga ayi, komatu kwanu kuchitike.” (Luka 22:42) Ngakhale kuti Yesu anavutika kwambiri, iye anachita chifuno cha Mulungu. (Ahebri 5:7, 8) Kumvera ndiko umboni wa chikondi chathu ndiponso kumasonyeza kuti tikuvomereza kuti njira ya Mulungu ndiyo njira yabwino koposa. Baibulo limati: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake.” (1 Yohane 5:3) Yesu anauzanso atumwi ake kuti: “Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.”—Yohane 14:15.
17. Kodi ndi lamulo lapadera lotani limene Yesu anapatsa otsatira ake, ndipo tikudziŵa bwanji kuti ifenso lerolino tiyenera kulitsatira?
17 Kuwonjezera pa kulamula otsatira ake kuti azikondana, kodi Kristu anawapatsa lamulo lina lapadera lotani? Anawalamula kuchita ntchito yolalikira imene anawaphunzitsa. Petro anati: “Anatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni.” (Machitidwe 10:42) Yesu anawalamula mwachindunji kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 1:8) Yesu ananena kuti otsatira ake lerolino mu “nthaŵi ya chimaliziro,” adzayeneranso kutsatira malangizo ameneŵa, popeza anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Danieli 12:4; Mateyu 24:14) Ndithudi, n’chifuno cha Mulungu kuti tizilalikira. Komabe, ena angamaganize kuti Mulungu akufuna zosatheka kwa ife ngati akufuna kuti tizichita ntchito imeneyi. Koma kodi zimenezo n’zoona?
Chifukwa Chimene Zingaonekere Ngati Zovuta
18. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani ngati tikuvutika chifukwa chakuti tikuchita zimene Yehova akufuna kuti tichite?
18 Monga momwe taonera, m’zochitika zonse za m’mbiri Yehova wakhala akufuna kuti anthu azitsatira zofunika zosiyanasiyana. Ndipo monga momwe zimene auzidwa kuchita zakhalira zosiyanasiyana, ziyesonso zimene akumana nazo zakhala zosiyana. Mwana wokondedwa wa Mulungu anakumana ndi ziyeso zovuta koposa, ndipo kufikira anaphedwa mwankhanza zadzaoneni chifukwa chochita zimene Mulungu anafuna. Koma ngati tivutika chifukwa chakuti tikuchita zimene Yehova akufuna kwa ife, tiyenera kukumbukira kuti sindiye amene akuchititsa ziyeso zathuzo. (Yohane 15:18-20; Yakobo 1:13-15) Kupanduka kwa Satana kunayambitsa uchimo, kuvutika, ndi imfa, ndipo ndiye amene wayambitsa mikhalidwe imene nthaŵi zambiri yapangitsa kuti kuchita zimene Yehova amafuna kwa atumiki ake kukhale kovuta kwambiri.—Yobu 1:6-19; 2:1-8.
19. N’chifukwa chiyani ndi mwayi kuchita zimene Mulungu watiuza kuchita kudzera mwa Mwana wake?
19 Kudzera mwa Mwana wake, Yehova walamula kuti m’nthaŵi ino yamapeto, atumiki Ake alengeze padziko lonse kuti njira yokha yothetsera kuvutika konse kwa anthu ndiyo ulamuliro wa Ufumu. Boma la Mulungu limeneli lidzathetsa mavuto onse padziko lapansi—nkhondo, upandu, umphaŵi, ukalamba, matenda, imfa. Ufumuwo udzakhazikitsanso paradaiso waulemerero padziko lonse, ndipo ngakhale akufa onse adzaukitsidwa mmenemo. (Mateyu 6:9, 10; Luka 23:43; Machitidwe 24:15; Chivumbulutso 21:3, 4) Ndi mwayitu waukulu zedi kulengeza uthenga wabwino wa zinthu zimenezi! Chotero n’zoonekeratu kuti palibe vuto ndi zimene Yehova amafuna kuti tichite. Timakumana ndi chitsutso, koma Satana Mdyerekezi ndi dziko lake ndi amene amazichititsa.
20. Kodi tingapirire motani vuto lililonse lochititsidwa ndi Mdyerekezi?
20 Kodi tingapirire motani vuto lililonse lochititsidwa ndi Satana? Mwa kukumbukira mawu aŵa: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miyambo 27:11) Yesu anapatsa Yehova yankho loti ayankhe mtonzo wa Satana mwa kusiya moyo wotetezeka wakumwamba kudzachita chifuno cha Atate wake padziko lapansi. (Yesaya 53:12; Ahebri 10:7) Pamene anali munthu padziko lapansi, Yesu anapirira chiyeso chilichonse chimene anakumana nacho, ngakhale imfa pamtengo wozunzirapo. Ngati tim’tsatira monga Chitsanzo chathu, ifenso tingapirire mavuto ndi kuchitabe zimene Yehova akufuna kwa ife.—Ahebri 12:1-3.
21. Kodi m’mamva bwanji ponena za chikondi chimene Yehova ndi Mwana wake atisonyeza?
21 Eti chikondi chake kukula chimene Mulungu ndi Mwana wake atisonyeza! Chifukwa cha nsembe ya Yesu, anthu omvera ali ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso. Chotero tisalole kalikonse kusokoneza chiyembekezo chathu. M’malo mwake, tiyeni aliyense payekha tiziganizira zimene Yesu anatheketsa, monga momwe ankachitira Paulo, amene anati: ‘Mwana wa Mulungu . . . anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.’ (Agalatiya 2:20) Ndipo tiyeni tisonyeze kuyamikira kochokeradi pansi pa mtima kwa Mulungu wathu wachikondiyo, Yehova, amene safuna konse zimene sitingathe.
Kodi Mungayankhe Kuti Bwanji?
◻ Kodi Yehova amafunanji kwa ife lerolino?
◻ Patsiku lomaliza kukhala ndi atumwi ake madzulo, kodi Kristu anamveketsa motani kufunika kwa chikondi?
◻ Kodi tingasonyeze motani kuti Mulungu timam’konda?
◻ N’chifukwa chiyani uli mwayi kuchita zimene Yehova akufuna kwa ife?
[Chithunzi patsamba 23]
Kodi Yesu anapereka phunziro lotani pamene anasambitsa mapazi a atumwi ake?
[Chithunzi patsamba 25]
Mosasamala kanthu za chitsutso, kuuza ena uthenga wabwino ndi mwayi wosangalatsa