Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Pemphero Lomalizira m’Chipinda Chosanja
POSONKHEZEREDWA ndi chikondi chapamtima kaamba ka atumwi ake, Yesu wakhala akuwakonzekeretsa kaamba ka kuchoka kwake koyandikirako. Tsopano, pambuyo powalangiza ndi kuwatonthoza kwa nthaŵi yaitali, iye akweza maso ake kumwamba napembedzera Atate wake motere: “Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni Inu; monga mwampatsa Iye ulamuliro pa thupi liri lonse, kuti onse amene mwampatsa Iye, awapatse iwo moyo wosatha.”
Ndinkhani yosangalatsa chotani nanga imene Yesu akuiyamba—moyo wosatha! Pokhala kuti wapatsidwa “ulamuliro pa thupi liri lonse,” Yesu angapereke mapindu a nsembe yake yadipo kwa anthu onse omafa. Komabe, iye akupereka “moyo wosatha” kokha kwa awo amene Atate avomereza. Pomangirira nkhani ya moyo wosatha imeneyi, Yesu akupitiriza pemphero lake motere:
“Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” Inde, chipulumutso chimadalira pakudziŵa kwathu onse aŵiri Mulungu ndi Mwana wake. Koma zowonjezereka zikufunikira kuposa chidziŵitso wamba chokha.
Munthu ayenera kuwadziŵa iwo mwathithithi, kuyambitsa unansi womvana ndi iwo. Munthu ayenera kumva ndi kulingalira za zinthu monga momwe iwo anazionera. Ndipo kuposa zonse, munthuyo ayenera kukalamira kutsanzira mikhalidwe yawo yosayerekezeka m’kuchita ndi ena.
Kenaka Yesu akupemphera motere: ‘Ine ndalemekeza inu pa dziko lapansi, mmene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite.’ Pokhala atakwaniritsa gawo lake kufikira pa mfundoyi ndikukhala wachidaliro za chipambano chake chamtsogolo, iye akupembedzera kuti: ‘Atate inu, lemekezani ine ndi inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nawo ndi inu lisanakhale dziko lapansi.’ Inde, iye tsopano akupempha kuti abwezeretsedwe ku ulemerero wake wakumwamba wakalewo kupyolera m’chiukiriro.
Polongosola mwachidule ntchito yake yaikulu padziko lapansi, Yesu akuti: ‘Ndalionetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa ine m’dziko lapansi; anali anu, ndipo mwandipatsa ine iwo; ndipo adasunga mawu anu.’ Yesu anagwiritsira ntchito dzina la Mulungu, Yehova, muuminisitala wake ndikusonyeza katchulidwe kolondola ka ilo, koma anachita zowonjezereka kuposa apa kudziŵikitsa dzina la Mulungu kwa atumwi ake. Iye anafutukulanso chidziŵitso ndi chiyamikiro chawo cha Yehova, umunthu wake, ndi zifuno zake.
Pozindikiritsa Yehova monga Wamkulu kwa iye, Uyo amene iye akugwira ntchito pansi pa chitsogozo chake, Yesu modzichepetsa akuvomereza motere: ‘Mawu amene munandipatsa ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinatuluka kwa inu, ndipo anakhulupira kuti inu munandituma ine.’
Akumasiyanitsa pakati pa atsatiri ake ndi anthu ena onse, Yesu potsatira akupemphera kuti: ‘Ine ndiwapempherera iwo; sindipempherera dziko lapansi, koma iwo amene mwandipatsa ine . . . Pamene ndinakhala nawo, ine ndinalikuwasunga iwo . . . ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayika mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko,’ wotchedwa, Yudase Isikariote. Pamphindi imeneyi, Yudase ali pantchito yake yoipa yopereka Yesu. Chotero, Yudase akukwaniritsa Malemba popanda kuchidziŵa.
“Dziko lapansi linadana nao,” Yesu akupitiriza kupemphera. ‘Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo. Siali a dziko lapansi monga ine sindiri wa dziko lapansi.’ Atsatiri a Yesu ali m’dziko, chitaganya cholinganizidwa chino cholamulidwa ndi Satana, koma iwo ali ndipo nthaŵi zonse ayenera kukhala osiyana nalo limodzi ndi kuipa kwake.
‘Patulani iwo m’chowonadi,’ Yesu akupitiriza tero, ‘mawu anu ndi chowonadi.’ Panopa Yesu akutcha Malemba ouziridwa Achihebri, amene anaŵagwira mawu mobwerezabwereza kukhala ‘chowonadi.’ Komabe zimene anawaphunzitsa ophunzira ake ndi zimene iwo analemba pambuyo pake mouziridwa monga Malemba Achikristu Achigiriki zikudziŵikanso kukhala ‘chowonadi.’ Chowonadi chimenechi chingapatule munthu, kusintha moyo wake kotheratu, ndikumpanga kukhala munthu wosiyana ndi dziko.
Yesu tsopano akupempherera osati ‘iwo okha, komanso iwo akukhulupirira [iye] chifukwa cha mawu awo.’ Chotero Yesu akupempherera anthu amene adzakhala atsatiri ake odzozedwa ndi ophunzira ena amtsogolo amene adzasonkhanitsidwa mu “gulu limodzi.” Kodi iye akupemphanji kaamba ka onsewa? ‘Kuti onse akakhale amodzi, monga inu Atate mwa ine, ndi ine mwa inu, . . . kuti akhale amodzi, monga ife tiri mmodzi.’
Yesu ndi Atate wake sali munthu mmodzi weniweni, koma iwo amagwirizana pa zinthu zonse. Yesu akupemphera kuti atsatiri ake akasangalale ndi umodzi umenewu kotero kuti “dziko lapansi lizindikire kuti Inu munandituma Ine, nimunawakonda iwo, monga momwe munakonda Ine.”
M’chigwirizano ndi omwe akakhala atsatiri ake odzozedwa, Yesu tsopano akupempha kwa Atate wake akumwamba. Kupemphanji? “Kuti, kumene ndiri Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang’anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi,” ndiko kuti, Pamene Adamu ndi Hava anakhala ndi pathupi pa mwana wawo woyamba. Mulungu anakonda Mwana wake wobadwa yekha, kalekale zimenezo zisanachitike, amene anadzakhala Yesu Kristu.
Pomaliza pemphero lake, Yesu akugogomezeranso kuti: ‘Ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo.’ Kudziŵa dzina la Mulungu kwa atumwiwo kwaphatikizapo kudziŵa kwaumwini chikondi cha Mulungu. Yohane 17:1-26; 10:16; Miyambo 8:22, 30.
▪ Kodi ndi m’lingaliro lotani mmene Yesu wapatsidwira “ulamuliro pa thupi liri lonse”?
▪ Kodi kudziŵa Mulungu ndi Mwana wake kumatanthauzanji?
▪ Kodi Yesu anadziŵikitsa mwanjira zanji dzina la Mulungu?
▪ Kodi ‘chowonadi’ nchiyani, ndipo kodi ndimotani mmene icho ‘chimapatulitsira’ Mkristu?
▪ Kodi ndimotani mmene Mulungu, Mwana wake, ndi alambiri onse owona aliri mmodzi?
▪ Kodi ‘kukhazikika kwa dziko lapansi’ kunachitika liti?