TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO | MARIYA
Sanafooke Chifukwa cha Chisoni
MARIYA anali atagwada pansi akulira chifukwa cha chisoni chachikulu chomwe anali nacho. Ankangoganizirabe mawu omaliza amene mwana wake ananena atangotsala pang’ono kufa chifukwa cha ululu woopsa. Ngakhale kuti anali masana, kunja kunali kutachita kale mdima. Kenako dziko lapansi linagwedezeka kwambiri. (Mateyu 27:45, 51) N’kutheka kuti Mariya ataona zimenezi anaganiza kuti Yehova akufuna kuti anthu onse adziwe kuti Yehovayo wamva chisoni kwambiri ndi imfa ya Yesu Khristu kuposa munthu aliyense.
Kenako mdima uja unayamba kuchoka. Zonsezi zinkachitikira pamalo otchedwa Chibade kapena kuti Gologota, ndipo Mariya anali ndi chisoni chifukwa cha imfa ya mwana wake. (Yohane 19:17, 25) Pa nthawiyi Mariya ayenera kuti ankaganiza zinthu zambirimbiri. Koma mawu amene ankawaganizira kwambiri ayenera kuti ndi amene analankhulidwa zaka 33 izi zisanachitike. Pa nthawiyo, iye ndi mwamuna wake Yosefe, anapita ndi mwana wawo kukachisi ku Yerusalemu. Ali kukachisiko, mwamuna wina wachikulire dzina lake Simiyoni motsogoleredwa ndi Mulungu, ananena mawu aulosi. Ananeneratu zinthu zazikulu zomwe Yesu adzachite, koma ananenanso kuti tsiku lina Mariya adzamva chisoni kwambiri ngati lupanga lalitali lalasa moyo wake. (Luka 2:25-35) Pa nthawi ya imfa ya mwana wakeyu, m’pamene Mariya anamvetsa tanthauzo la mawuwa.
Anthu amati imfa ya mwana imakhala yowawa kwambiri kwa kholo kuposa imfa iliyonse. Imfa ndi mdani wamkulu, ndipo munthu akamwalira zimakhudza anthu ambiri. (Aroma 5:12; 1 Akorinto 15:26) Koma kodi n’zotheka kukhalabe wolimba zoterezi zikachitika? Tiyeni tikambirane nkhani ya Mariya, kuyambira pamene Yesu anayamba utumiki wake, pa nthawi ya imfa yake komanso pambuyo pake. Zimenezi zitithandiza kudziwa zambiri za chikhulupiriro cha Mariya chomwe chinamuthandiza kuti asafooke ngakhale kuti anali ndi chisoni chachikulu.
“CHILICHONSE CHIMENE ANGAKUUZENI, CHITANI CHIMENECHO”
Tiyeni tikambirane kaye zomwe zinachitika Yesu atangoyamba kumene utumiki wake. Mariya anazindikira kuti moyo wa Yesu usintha. M’mudzi wonse wa Nazareti nkhani yomwe inali m’kamwam’kamwa inali yonena za Yohane M’batizi komanso za uthenga umene iye ankalalikira, woti anthu alape. Mariya anazindikira kuti mwana wake waona kuti ichi ndi chizindikiro choti nthawi yoti ayambe utumiki wake yakwana. (Mateyu 3:1, 13) Kwa Mariya ndi banja lake, izi sizinali zophweka chifukwa zinatanthauza kuti Yesu achoka panyumba. N’chifukwa chiyani kuchoka panyumba kwa Yesu inali nkhani yovuta kwa Mariya ndi banja lake?
Zikuoneka kuti pa nthawiyi n’kuti Yosefe atamwalira kale. Ngati zinalidi choncho, ndiye kuti Mariya anali atadziwa kale kuwawa kwa imfa.a Pa nthawiyi Yesu sankangodziwika kuti ndi “mwana wa mmisiri wamatabwa,” koma ankadziwikanso kuti “mmisiri wamatabwa.” Choncho Yesu ayenera kuti ankayendetsa ntchito ya ukalipentala imene bambo ake anasiya, ndipo ankasamalira banja lonse, lomwe linali ndi ana enanso 6. (Mateyu 13:55, 56; Maliko 6:3) N’kutheka kuti Yesu anaphunzitsa mng’ono wake, Yakobo, ntchitoyi, komabe kuchoka kwake panyumba kunakhudza banja lawo popeza iye anali mwana wamkulu. N’zodziwikiratu kuti Mariya anali kale ndi udindo waukulu, choncho mwina anada nkhawa atazindikira kuti Yesu akuyenera kuchoka panyumba. Koma kodi iye anamva bwanji pamene Yesu wa ku Nazareti anakhala Khristu, Mesiya amene anthu ankamuyembekezera kwa nthawi yaitali? Nkhani ina ya m’Baibulo imatithandiza kudziwa mmene anamvera.—Yohane 2:1-12.
Yesu anapita kwa Yohane kukabatizidwa ndipo anakhala Wodzozedwa wa Mulungu kapena kuti Mesiya. (Luka 3:21, 22) Kenako anayamba kusankha ophunzira ake. Ngakhale kuti ankakhala wotanganidwa ndi ntchito yake, ankapeza nthawi yosangalala ndi a m’banja lake komanso anthu ena. Mwachitsanzo pa nthawi ina iye, mayi ake komanso azichimwene ake anapita ku ukwati ku Kana, tauni yomwe inali paphiri linalake, makilomita 13 kuchokera ku Nazareti. Phwando la ukwati lili mkati, Mariya anazindikira kuti pali vuto linalake. Mwina anaona achibale a anthu okwatiranawo akukokerana pambali n’kumauzana kuti vinyo watha. Pa chikhalidwe chawo, kuchereza alendo powapatsa vinyo chinali chinthu chofunika kwambiri. Choncho vinyo akatha pa ukwati chinkakhala chinthu chochititsa manyazi. Mariya anawamvera chisoni kwabasi ndipo anapita kwa Yesu n’kumuuza za vutoli.
Anamuuza kuti: “Vinyo waathera.” Kodi pamenepa Mariya ankafuna kuti Yesu atani? Sitikudziwa, komabe Mariya ayenera kuti ankadziwa zoti mwana wakeyo angathe kuchita zozizwitsa chifukwa sanali munthu wamba. Mwinanso ankaganiza kuti nthawi yoti ayambe kuchita zozizwitsa yafika. Choncho pomuuza mawu amenewa kunali kumupempha kuti achitepo kanthu powathandiza anthuwo. Koma ayenera kuti anadabwa ndi mmene Yesu anayankhira. Iye anati: “Kodi ndili nanu chiyani mayi?” Anthu ena amaona kuti mawu amene Yesu ananenawa ndi achipongwe, koma zimenezi si zoona. Yesu analankhula mawuwa mwaulemu ndipo cholinga chake chinali kuthandiza Mariya kuti asakhale ndi maganizo olakwika. Ankafuna kumukumbutsa kuti sunali udindo wake kuuza Yesu zoyenera kuchita pa utumiki wake chifukwa umenewu unali udindo wa Atate wake, Yehova.
Mariya anatsatira malangizo a mwana wakewo popeza anali wodzichepetsa komanso womvetsa zinthu. Choncho anangopita kwa anthu amene ankatumikira pa ukwatiwu n’kuwauza kuti: “Chilichonse chimene angakuuzeni, chitani chimenecho.” Mariya anadziwa kuti sankayeneranso kumauza mwana wakeyo zochita, m’malomwake iyeyo mofanana ndi anthu ena onse, ankafunika kumatsatira malangizo a Yesu. Komabe Yesu anasonyeza kuti, mofanana ndi mayi ake, nayenso anamvera chisoni banja latsopanolo. Choncho anachita chozizwitsa chake choyamba, moti anasandutsa madzi n’kukhala vinyo. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Baibulo limati: “Ophunzira ake anakhulupirira mwa iye.” Mariya nayenso anakhulupirira Yesu. Sankangomuona ngati mwana wake chabe, koma ankamuonanso monga Mbuye ndi Mpulumutsi wake.
Masiku ano makolo angaphunzire zambiri kuchokera kwa Mariya. N’zoona kuti palibe kholo limene linalerapo mwana wofanana ndi Yesu. Koma mwana aliyense akafika msinkhu wodziimira payekha, zimakhala zovuta kwa makolo chifukwa nthawi zambiri makolo amapitirizabe kumuona mwanayo ngati wamng’ono, koma zimenezi si zoyenera. (1 Akorinto 13:11) Ndiye kodi makolo angatani mwana wawo akafika msinkhu wodziimira payekha? Ayenera kusonyeza kuti akumukhulupirira mwanayo kuti apitiriza kutsatira mfundo za m’Baibulo ndipo Yehova amudalitsa chifukwa cha zimenezi. Mtima wodzichepetsa umenewu ungathandize kwambiri mwanayo. Yesu ayenera kuti ankayamikira kwambiri khalidwe la Mariya komanso zimene ankachita pomuthandiza.
‘ABALE AKE SANALI KUMUKHULUPIRIRA’
Mauthenga Abwino sanena zambiri zimene Mariya anachita pa zaka zitatu ndi hafu za utumiki wa Yesu. Komatu musaiwale kuti anali mayi wamasiye, ndipo anali ndi ana angapo amene ankafunikabe kuwasamalira. N’kutheka kuti zimenezi n’zimene zinam’chititsa kuti asamayende ndi Yesu, Yesuyo akamalalikira kudera lakwawo. (1 Timoteyo 5:8) Komabe, anapitiriza kuganizira zinthu zimene anaphunzira zokhudza Mesiya. Anapitirizanso kupita kusunagoge kukaphunzira Mawu a Mulungu monga mmene ankachitira ndi mwamuna wake.—Luka 2:19, 51; 4:16.
Choncho, Mariya ayenera kuti analipo tsiku limene Yesu anauza anthu zokhudza ulosi winawake m’sunagoge wa ku Nazareti. Iye ayenera kuti anasangalala kumva mwana wake akunena kuti ulosi umene unalembedwa zaka zambiri m’mbuyomo wokhudza Mesiya, wakwaniritsidwa pa iye. Komabe n’kutheka kuti anakhumudwa kuona kuti anthu a ku Nazareti sanakhulupirire mwana wakeyu, moti mpaka ankafuna kumupha.—Luka 4:17-30.
Chinthu chinanso chimene chinamukhumudwitsa Mariya n’choti ana ake ena 4 sankakhulupirira Yesu, ngati mmene iyeyo ankachitira. Lemba la Yohane 7:5 limati: “Abale akewo [a Yesu] sanali kumukhulupirira.” Koma Baibulo silinena ngati azichemwali ake a Yesu, omwe mwina analipo awiri, ankakhulupirira Yesu kapena ayi.b Choncho Mariya ankadziwa mavuto amene amakhalapo, m’banja mukakhala anthu azipembedzo zosiyana. Ankafunika kuthandiza ana ake omwe sankakhulupirira Yesuwo popanda kuwakakamiza, kwinaku akuyesetsanso kuti asamaphwanye mfundo za m’Malemba.
Pa nthawi ina, gulu la abale a Yesu, amene mwina anaphatikizapo azichimwene ake, anaganiza zopita “kukamugwira” Yesu. Iwo ankanena kuti “wachita misala.” (Maliko 3:21, 31) Ngakhale kuti Mariya sanali ndi maganizo amenewa, anapita limodzi ndi ana akewa. Mwina anachita zimenezi poganiza kuti zimene zikachitike kumeneko zithandiza ana akewo kusintha n’kuyamba kukhulupirira Yesu. Koma kodi anasinthadi? Ngakhale kuti Yesu ankachita zozizwitsa zambiri komanso kuphunzitsa choonadi, abale akewa sanamukhulupirirebe. Mwina Mariya ankalakalaka atapeza njira yoti ana akewa asinthe.
Kodi m’banja lanu muli anthu a zipembedzo zosiyana? Ngati ndi choncho, ndiye kuti mungaphunzire zambiri kwa Mariya. Iye sanafooke ngakhale kuti ana ake sankakhulupirira Yesu. Koma iye ankafuna kuti ana akewo aone kuti chikhulupiriro chake chinkamuthandiza kuti azisangalala. Komanso ankayesetsa kuthandiza Yesu pa utumiki wake. Kodi n’kutheka kuti nthawi zina ankalakalaka Yesu akukhalabe pakhomo? Ngati ndi choncho, sanalole kuti maganizo amenewa amusokoneze. Ankaona kuti ndi mwayi waukulu kuthandiza komanso kulimbikitsa Yesu. Kodi inunso mungayesetse kuthandiza ana anu kuti azikonda Mulungu?
“LUPANGA LALITALI LIDZALASA MOYO WAKO”
Kodi Yehova anadalitsa Mariya chifukwa cha chikhulupiriro chake? Inde, chifukwa Yehova nthawi zonse amadalitsa anthu okhulupirika. (Aheberi 11:6) Tangoganizirani mmene Mariya ankasangalalira akamva mwana wake akulankhula kapena akamva zimene anthu omwe amva ulaliki wa Yesu ankanena.
N’kutheka kuti Mariya ankaona kuti mafanizo amene mwana wake ankapereka anali ogwirizana ndi zimene zinkachitika Yesu ali mwana ku Nazareti. Mafanizo monga la mayi amene anasesa m’nyumba pofufuza ndalama, kupera ufa komanso kuyatsa nyali n’kuiika pamwamba, ayenera kuti ankakumbutsa Mariya zimene ankachita atabereka Yesu kumsana kwinaku akugwira ntchito zapakhomo. (Luka 11:33; 15:8, 9; 17:35) Pamene Yesu ananena kuti goli lake ndi lofewa, n’kutheka kuti Mariya anakumbukira nthawi ina, pamene Yosefe ankaphunzitsa Yesu kapangidwe ka goli labwino limene silikanavulaza nyama. (Mateyu 11:30) Mariya ankasangalala kwambiri akaganizira mwayi umene Yehova anam’patsa wolera komanso kuphunzitsa mwana amene anakhala Mesiya. Iye ankasangalalanso kumva Yesu, yemwe ndi mphunzitsi waluso, akugwiritsa ntchito zinthu za masiku onse pophunzitsa anthu mfundo zofunika kwambiri. Ngakhale zinali choncho, Mariya anapitirizabe kukhala wodzichepetsa.
Yesu sanachite zinthu zosonyeza kuti anthu ankayenera kupereka ulemu wapadera kwa Mariya kapena kumulambira. Mwachitsanzo pa nthawi ina Yesu akuphunzitsa, mayi wina anaimirira n’kunena kuti mayi wa Yesu ndi wodala chifukwa chobereka Yesuyo. Koma Yesu anayankha kuti: “Ayi, m’malomwake, odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!” (Luka 11:27, 28) Komanso pa nthawi ina, anthu ena anauza Yesu kuti kwabwera mayi ndi abale ake. Koma Yesu ananena kuti amene amachita chifuniro cha Mulungu, ndi omwe ali amayi komanso abale ake. M’malo mokhumudwa ndi mawu a Yesuwa, Mariya anamvetsa zimene Yesu ankatanthauza. Yesu ankatanthauza kuti anthu amene amatumikira Yehova ndi amene ali ofunika kwambiri kwa ife kuposa achibale athu omwe satumikira Yehova.—Maliko 3:32-35.
Komatu Mariya ayenera kuti anamva chisoni kwambiri kuona mwana wake akufa imfa yowawa pamtengo wozunzikirapo. Mtumwi Yohane analipo pamene zimenezi zinkachitika ndipo analemba kuti Mariya anali ataimirira “chapafupi ndi mtengo wozunzikirapo wa Yesu.” Palibe chimene chikanaletsa Mariya, yemwe anali mayi wachikondi, kukhalapo pamene mwana wakeyu ankaphedwa. Yesu anawaona mayi akewo, ndipo ngakhale kuti akamapuma komanso kulankhula ankamva ululu woopsa, anayesetsabe kuti alankhule. Iye anauza Yohane, mtumwi wake amene ankamukonda kwambiri kuti atenge udindo wosamalira mayi akewo. Anachita zimenezi chifukwa choti abale ake onse aja anali asanayambebe kumukhulupirira. Pamenepatu Yesu anasonyeza kuti Mkhristu ayenera kusamalira anthu a m’banja lake, makamaka pa nkhani zokhudza kulambira.—Yohane 19:25-27.
Pamene Yesu anatsirizika, Mariya anamva ululu ngati lupanga lalitali lalasa moyo wake, mogwirizana ndi mawu a Simiyoni aja. N’zovuta kumvetsa kukula kwa chisoni chomwe Mariya anali nacho. Koma patatha masiku atatu ayenera kuti anasangalala kwambiri atamva zoti mwana wake wauka. Kuukitsidwa kwa Yesu chinali chinthu chapadera kwambiri kwa Mariya pa zozizwitsa zonse zimene zinachitikapo. Chisangalalo chake chinawonjezekanso atamva kuti Yesu waonekeranso kwa m’bale wake Yakobo. (1 Akorinto 15:7) Zimenezi zinathandizanso kwambiri Yakobo komanso abale ake ena kuti asinthe maganizo awo. N’kupita kwa nthawi abale akewa anayamba kukhulupirira kuti Yesu ndi Khristu. Posakhalitsa, iwowo limodzi ndi mayi awo anayamba kusonkhana ndi okhulupirira ena ndipo “analimbikira kupemphera.” (Machitidwe 1:14) Awiri a abale akewo, omwe ndi Yakobo komanso Yuda, anadzalemba mabuku amene amapezeka m’Baibulo.
Mariya amatchulidwa komaliza pamene anali ndi ana ake limodzi ndi okhulupirira anzake akupemphera. Zimenezi zikusonyeza kuti anakhala wokhulupirika moyo wake wonse, ndipotu iye ndi chitsanzo chabwino kwa tonsefe. Chifukwa choti anali ndi chikhulupiriro cholimba, sanafooke chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo, ndipo anadalitsidwa kwambiri. Ngati titatengera chitsanzo cha Mariya, nafenso tingakhalebe olimba ngakhale kuti timakumana ndi mavuto osiyanasiyana m’dziko loipali, ndipo Yehova angatidalitse kwambiri.
a Nkhani yomaliza ya m’Baibulo yomwe imatchula Yosefe, ndi yonena za zimene zinachitika Yesu ali ndi zaka 12. Kuchokera pa nthawiyi, Baibulo limangotchula za amayi a Yesu ndi azibale ake basi, koma osati Yosefe. Komanso pa nthawi ina Yesu ankatchedwa “mwana wa Mariya,” popanda kutchula Yosefe.—Maliko 6:3.
b Yosefe sanali bambo ake a Yesu om’bereka. Choncho azichimwene ndi azichemwali akewa, sanali a bambo mmodzi ndi Yesu.—Mateyu 1:20.