Wolembedwa ndi Mateyu
27 Mʼmawa kutacha, ansembe aakulu onse limodzi ndi akulu a anthu anakambirana nʼkugwirizana kuti aphe Yesu.+ 2 Ndipo atamumanga, anapita kukamupereka kwa Bwanamkubwa Pilato.+
3 Kenako Yudasi amene anamupereka uja, ataona kuti Yesu waweruzidwa kuti aphedwe, anavutika koopsa mumtima moti anapita kukabweza ndalama 30 zasiliva zija kwa ansembe aakulu ndiponso akulu.+ 4 Iye anati: “Ndachimwa popereka munthu wosalakwa.”* Iwo anamuyankha kuti: “Ife sizikutikhudza zimenezo. Udziwa wekha chochita!”* 5 Choncho iye anaponya ndalama zasiliva zija mʼkachisi nʼkuchoka. Kenako anapita kukadzimangirira.+ 6 Koma ansembe aakulu anatenga ndalama zasilivazo nʼkunena kuti: “Nʼzosaloleka kuti ndalamazi ziikidwe mʼmalo opatulika osungiramo chuma, chifukwa ndi malipiro a magazi.” 7 Atakambirana, anagwiritsa ntchito ndalamazo pogulira munda wa woumba mbiya kuti ukhale manda a alendo. 8 Choncho munda umenewu umatchedwa Munda wa Magazi+ mpaka lero. 9 Zimenezi zinakwaniritsa mawu amene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri Yeremiya* kuti: “Ndipo anatenga ndalama 30 zasiliva, mtengo wogulira munthu, mtengo umene ena mwa ana a Isiraeli anamuikira, 10 ndipo anagulira munda wa woumba mbiya, mogwirizana ndi zimene Yehova* anandilamula.”+
11 Tsopano Yesu anaimirira pamaso pa bwanamkubwa ndipo bwanamkubwayo anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti: “Zili choncho, monga mmene mwanenera.”+ 12 Koma pamene ansembe aakulu komanso akulu ankamuneneza, iye sanayankhe chilichonse.+ 13 Ndiyeno Pilato anamufunsa kuti: “Kodi sukumva zinthu zambirimbiri zimene akukunenezazi?” 14 Koma iye anangokhala chete, osamuyankha chilichonse, moti bwanamkubwayo anadabwa kwambiri.
15 Pa chikondwerero chilichonse, bwanamkubwayu ankamasulira anthu mkaidi mmodzi amene anthuwo akufuna.+ 16 Ndiye pa nthawiyi panali mkaidi wina woopsa kwambiri, dzina lake Baraba. 17 Choncho anthu atasonkhana pamodzi, Pilato ananena kuti: “Kodi mukufuna kuti ndikumasulireni ndani, Baraba kapena Yesu amene mumati ndi Khristu?” 18 Chifukwa Pilato ankadziwa kuti anamupereka chifukwa cha kaduka. 19 Komanso atakhala pampando woweruzira milandu, mkazi wake anamutumizira uthenga wakuti: “Nkhani ya munthu wolungamayu isakukhudzeni chifukwa ine ndavutika kwambiri lero ndi maloto okhudza iyeyu.” 20 Komabe ansembe aakulu limodzi ndi akulu analimbikitsa anthu kupempha kuti awamasulire Baraba,+ koma kuti Yesu aphedwe.+ 21 Ndiyeno bwanamkubwayo anawafunsa kuti: “Kodi pa anthu awiriwa mukufuna kuti ndikumasulireni uti?” Iwo anati: “Baraba.” 22 Pilato anafunsanso kuti: “Nanga Yesu, amene mumati ndi Khristu uja, ndichite naye chiyani?” Onse anayankha kuti: “Apachikidwe ameneyo!”*+ 23 Iye anati: “Chifukwa chiyani? Kodi iyeyu walakwa chiyani?” Koma anthuwo anapitiriza kufuula mwamphamvu kuti: “Ameneyo apachikidwe basi!”+
24 Ataona kuti sizikuthandiza komanso kuti pakuyambika chipolowe, Pilato anangotenga madzi nʼkusamba mʼmanja pamaso pa gulu la anthulo ndipo ananena kuti: “Ine ndilibe mlandu wa magazi a munthu uyu. Zonse zili kwa inu.” 25 Atanena zimenezi anthu onse anayankha kuti: “Magazi ake akhale pa ife ndi pa ana athu.”+ 26 Choncho anawamasulira Baraba, koma analamula kuti Yesu akwapulidwe+ kenako anamupereka kuti akamuphe pomupachika pamtengo.+
27 Ndiyeno asilikali a bwanamkubwa anatenga Yesu nʼkulowa naye mʼnyumba ya bwanamkubwayo ndipo anasonkhanitsa gulu lonse la asilikali kwa iye.+ 28 Kumeneko anamuvula zovala zake nʼkumuveka chinsalu chofiira kwambiri.+ 29 Komanso analuka chisoti chachifumu chaminga nʼkumuveka kumutu ndipo anamupatsa bango mʼdzanja lake lamanja. Kenako anamugwadira nʼkumamunyoza kuti: “Moni, inu Mfumu ya Ayuda!” 30 Atatero anamulavulira+ ndipo anatenga bango lija nʼkuyamba kumumenya nalo mʼmutu. 31 Atamaliza kumunyozako, anamuvula chinsalu chija nʼkumuveka malaya ake akunja ndipo anapita naye kuti akamukhomerere pamtengo.+
32 Ali mʼnjira, anakumana ndi munthu wina wa ku Kurene, dzina lake Simoni. Iwo anakakamiza munthu ameneyu kuti asenze mtengo wozunzikirapo* wa Yesu.+ 33 Atafika pamalo otchedwa Gologota, kutanthauza kuti, Malo a Chibade,+ 34 anapatsa Yesu vinyo wosakaniza ndi zinthu zowawa zamadzimadzi kuti amwe,+ koma iye atalawa, anakana kumwa. 35 Atamukhomerera pamtengo, anagawana malaya ake akunja pochita maere+ 36 ndipo anakhala pansi nʼkumamuyangʼanira. 37 Komanso pamwamba pa mutu wake anakhomapo chikwangwani chosonyeza mlandu umene anamuphera kuti: “Uyu ndi Yesu, Mfumu ya Ayuda.”+
38 Ndiyeno achifwamba awiri anapachikidwa naye limodzi. Mmodzi anamupachika kudzanja lake lamanja ndipo wina anali kumanzere kwake.+ 39 Anthu amene ankadutsa pafupi ankanena mawu onyoza Yesu+ ndipo ankapukusa+ mitu yawo 40 nʼkumanena kuti: “Iwe amene unkanena kuti ungathe kugwetsa kachisi nʼkumumanga mʼmasiku atatu,+ dzipulumutse! Ngati ulidi mwana wa Mulungu, tsikatu pamtengo wozunzikirapowo!”*+ 41 Chimodzimodzinso ansembe aakulu limodzi ndi alembi komanso akulu. Nawonso anayamba kumunyoza nʼkumanena kuti:+ 42 “Ena anatha kuwapulumutsa, koma kuti adzipulumutse yekha zikumukanika! Ngati ali Mfumu ya Isiraeli,+ tiyeni tione ngati angatsike pamtengo wozunzikirapowo* ndipo ife timukhulupirira. 43 Paja iye amakhulupirira Mulungu, ndiye panopa Mulunguyo amupulumutse ngati akumufunadi+ chifukwa iye ankanena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu.’”+ 44 Nawonso achifwamba amene anapachikidwa naye limodzi ankamunyoza.+
45 Kuyambira cha mʼma 12 koloko masana* kunagwa mdima mʼdziko lonselo, mpaka 3 koloko masana.*+ 46 Cha mʼma 3 kolokomo, Yesu anafuula mwamphamvu kuti: “Eʹli, Eʹli, laʹma sa·bach·thaʹni?” kutanthauza kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?”+ 47 Ena mwa anthu amene anaimirira chapomwepo atamva zimenezi anayamba kunena kuti: “Munthuyu akuitana Eliya.”+ 48 Nthawi yomweyo mmodzi wa iwo anathamanga kukatenga siponji nʼkuiviika muvinyo wowawasa ndipo anaiika kubango nʼkumupatsa kuti amwe.+ 49 Koma enawo anati: “Mulekeni! Tione ngati Eliya angabwere kudzamupulumutsa.” 50 Ndiyeno Yesu anafuulanso mokweza mawu, kenako anatsirizika.+
51 Nthawi yomweyo nsalu yotchinga yamʼnyumba yopatulika+ inangʼambika pakati+ kuchokera pamwamba mpaka pansi.+ Dziko lapansi linagwedezeka ndipo matanthwe anangʼambika. 52 Manda* anatseguka ndipo mitembo yambiri ya anthu oyera amene anaikidwa mmenemo inaponyedwa kunja, 53 ndipo anthu ambiri anatha kuiona. (Pambuyo pa kuukitsidwa kwa Yesu, anthu amene ankachokera kumandako, analowa mumzinda woyera.) 54 Koma mtsogoleri wa asilikali ndi ena amene anali naye polondera Yesu ataona chivomerezicho ndi zimene zinkachitikazo, anachita mantha kwambiri ndipo anati: “Ndithu, uyu analidi Mwana wa Mulungu.”+
55 Komanso azimayi ambiri ochokera ku Galileya amene ankatsatira Yesu kuti azimutumikira, anali komweko nʼkumaonerera chapatali.+ 56 Ena mwa iwo anali Mariya wa ku Magadala, Mariya mayi a Yakobo ndi Yose, ndiponso panali mayi a Yakobo ndi Yohane.*+
57 Tsopano madzulo kwambiri, kunabwera munthu wina wachuma wa ku Arimateya, dzina lake Yosefe, amenenso anakhala wophunzira wa Yesu.+ 58 Iye anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu+ ndipo Pilato analamula kuti amupatse mtembowo.+ 59 Yosefe anatenga mtembowo nʼkuukulunga munsalu yoyera yabwino kwambiri,+ 60 ndipo anakauika mʼmanda*+ ake atsopano amene anawasema muthanthwe. Kenako atagubuduza chimwala chachikulu nʼkutseka pakhomo la mandawo,* anachoka. 61 Koma Mariya wa ku Magadala ndi Mariya wina anatsalira komweko, atakhala pansi pafupi ndi mandawo.+
62 Tsiku lotsatira, pambuyo pa Tsiku Lokonzekera,*+ ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhana pamaso pa Pilato, 63 nʼkunena kuti: “Bwana, ife takumbukira kuti munthu wachinyengo uja adakali moyo ananena kuti, ‘Pakadzadutsa masiku atatu ndidzaukitsidwa.’+ 64 Choncho lamulani kuti akhwimitse chitetezo pamandapo mpaka tsiku lachitatu, kuti ophunzira ake asabwere kudzamuba+ nʼkumauza anthu kuti, ‘Anaukitsidwa kwa akufa!’ Chifukwa chinyengo chotsirizachi chidzakhala choipa kwambiri kuposa choyamba chija.” 65 Pilato anawayankha kuti: “Tengani asilikali olondera awa. Pitani mukakhwimitse chitetezo monga mmene mukudziwira.” 66 Choncho anapita kukakhwimitsa chitetezo pamandawo potseka kwambiri mandawo ndi chimwala nʼkuikapo asilikali olondera.