MUTU 133
Anakonza Thupi la Yesu ndi Kukaliika M’manda
MATEYU 27:57–28:2 MALIKO 15:42–16:4 LUKA 23:50–24:3 YOHANE 19:31–20:1
ANATSITSA THUPI LA YESU PAMTENGO
ANAKONZA THUPI LA YESU POKONZEKERA KUKALIIKA M’MANDA
AZIMAYI ANAPEZA KUTI M’MANDA MULIBE KANTHU
Lachisanu masana pa Nisani 14 panachitika zinthu zambiri zodabwitsa. Pamene dzuwa linkalowa, tsiku la Nisani 15 linayamba ndipo tsikuli linali la Sabata. Pa nthawiyi Yesu anali atamwalira kale koma anthu awiri amene anakhomeredwa naye limodzi aja anali asanamwalire. Chilamulo chinkanena kuti munthu akapachikidwa pamtengo, mtembo wake ‘usamakhale pamtengopo usiku wonse’ koma azimuika m’manda “tsiku lomwelo.”—Deuteronomo 21:22, 23.
Komanso Lachisanu masana anthu ankakonzeratu chakudya ndiponso kugwiriratu ntchito zina zofunika, tsiku la Sabata lisanafike. Chifukwa cha zimenezi tsikuli ankalitchula kuti Tsiku Lokonzekera. Dzuwa litalowa, Sabata “lalikulu” linayamba. (Yohane 19:31) Linali Sabata lalikulu chifukwa Nisani 15 linali tsiku loyamba la Chikondwerero cha Mkate Wopanda Chofufumitsa ndipo nthawi zonse tsikuli linkakhala Sabata. Chikondwererochi chinkachitika kwa masiku 7. Levitiko 23:5, 6) Koma pa nthawiyi, tsikuli linali pa Loweruka, lomwe mlungu uliwonse linkakhala la Sabata.
Chifukwa cha zimenezi, Ayuda anapempha Pilato kuti afulumizitse imfa ya Yesu komanso ya zigawenga zija. Kodi akanachita bwanji zimenezi? Polamula kuti awathyole miyendo. Kuti munthu amene wapachikidwa athe kupuma, ankakhala ngati akudzikankhira m’mwamba pogwiritsa ntchito miyendo yake. Koma akakhala kuti amuthyola miyendo, ankalephera kuchita zimenezi choncho sankachedwa kufa.Ndiyeno asilikali anapita n’kukathyola miyendo ya zigawenga ziwiri zija. Koma poti anapeza Yesu atafa kale sanamuthyole miyendo. Zimenezi zinakwaniritsa ulosi wa pa Salimo 34:20 womwe umati: “Amateteza mafupa onse a wolungamayo. Ndipo palibe fupa ngakhale limodzi limene lathyoledwa.”
Pofuna kutsimikizira kuti Yesu wafadi, msilikali wina anamubaya ndi mkondo chapambali ndipo mkondowo unalasa pafupi ndi mtima. “Nthawi yomweyo panatuluka magazi ndi madzi.” (Yohane 19:34) Zimenezi zinakwaniritsanso ulosi wina womwe unanena kuti: “Iwo adzayang’ana kwa munthu amene anamulasa.”—Zekariya 12:10.
Ndiyeno panali “munthu wina wachuma” dzina lake Yosefe wa ku Arimateya. Munthuyu anali mmodzi wa anthu olemekezeka m’khoti la Sanihedirini ndipo analipo pa nthawi imene Yesu ankaphedwa. (Mateyu 27:57) Ankadziwika kuti anali “munthu wabwino ndi wolungama” yemwenso “anali kuyembekezera ufumu wa Mulungu.” Yosefe sanagwirizane ndi zimene khoti la Sanihedirini linaweruza pa mlandu wa Yesu chifukwa iye anali “wophunzira wa Yesu koma wamseri chifukwa anali kuopa Ayuda.” (Luka 23:50; Maliko 15:43; Yohane 19:38) Iye analimba mtima n’kukapempha Pilato kuti amupatse thupi la Yesu. Pilato anafunsa kapitawo wa asilikali ngati Yesu analidi atafa ndipo msilikaliyo anamutsimikizira kuti wafadi. Kenako Pilato analoleza Yosefe kuti akhoza kukatenga thupilo.
Yosefe anagula nsalu yoyera komanso yapamwamba kenako anakatsitsa thupi la Yesu pamtengo paja. Anakulunga thupi la Yesu ndi nsaluyo pokonzekera kuti amuike m’manda. Nikodemo, yemwe “anabwera kwa [Yesu] usiku poyamba paja” anamuthandiza kukonza mtembowo. (Yohane 19:39) Nikodemo anatenga mule wosakaniza ndi aloye wopitirira makilogalamu 33. Anakulunga thupi la Yesu ndi nsalu zomwe anazipaka zonunkhiritsa potsatira zimene Ayuda ankachita poika maliro.
Yosefe anali ndi manda, omwe anali asanaikemo munthu, chapafupi ndi pamene anapachika Yesu. Mandawo anali ogobedwa pa chimwala chachikulu ndipo thupi la Yesu analiika mmenemo. Kenako anagubuduza chimwala chachikulu n’kutseka pakhomo la mandawo. Iwo anachita zimenezi mofulumira tsiku la Sabata lisanayambe. N’kutheka kuti Mariya Mmagadala komanso Mariya, yemwe anali mayi ake a Yakobo Wamng’ono ankathandiza nawo pokonza thupi la Yesu. Koma anabwerera kunyumba mofulumira kuti ‘akakonze zonunkhiritsa ndi mafuta onunkhira’ oti adzapake thupi la Yesu pambuyo pa Sabata.—Luka 23:56.
Tsiku lotsatira, lomwe linali Sabata, ansembe aakulu ndi Afarisi anapita kwa Pilato n’kumuuza kuti: “Ife takumbukira kuti wonyenga uja adakali moyo ananena kuti, ‘Patapita masiku atatu ndidzauka.’ Choncho lamulani kuti akhwimitse chitetezo pamandapo kufikira tsiku lachitatu, kuti ophunzira ake asabwere kudzamuba ndi kuuza anthu kuti, ‘Anauka kwa akufa!’ pakuti chinyengo chotsirizachi chidzakhala choipa kwambiri kuposa choyamba chija.” Pilato anawayankha kuti: “Inu muli nawo asilikali olondera. Pitani kakhwimitseni chitetezo monga mmene mukudziwira.”—Mateyu 27:63-65.
Lamlungu m’mawa kwambiri, Mariya Mmagadala, Mariya mayi ake a Yakobo pamodzi ndi azimayi ena anatenga zonunkhiritsa n’kupita kumanda kuja kuti akakonze thupi la Yesu. Ali m’njira ankafunsana kuti: “Nanga ndani amene akatigubuduzire chimwala chija pakhomo la manda achikumbutso?” (Maliko 16:3) Koma pa nthawiyi kunali kutachitika chivomezi ndipo anapezanso kuti mngelo wa Mulungu wakankha chimwala chija, asilikali olondera palibe komanso m’manda muja mulibe kanthu.