Mpingo Uyenera Kulimbikitsidwa
“Mpingo . . . unalowa m’nyengo ya mtendere, ndipo unakhala wolimbikitsidwa.”—MACHITIDWE 9:31.
1. Kodi ndi mafunso otani omwe tingafunse okhudza “mpingo wa Mulungu”?
PATSIKU la Pentekoste mu 33 C.E.,Yehova anavomereza ophunzira a Khristu kukhala mtundu watsopano womwe ndi “Isiraeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16) Baibulo limati Akhristu odzozedwa ndi mzimu amenewa anakhalanso “mpingo wa Mulungu.” (1 Akorinto 11:22) Koma kodi chinafunika n’chiyani kuti iwo akhale mu mpingo umenewu? Kodi “mpingo wa Mulungu” unadzalinganizidwa motani? Kodi unagwira ntchito motani kulikonse kumene kunali anthu ake? Ndipo zimenezi zikukhudza motani moyo wathu?
2, 3. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti mpingo uyenera kudzakhala wa dongosolo?
2 Monga momwe nkhani yapitayi yasonyezera, Yesu ananeneratu za kupangidwa kwa mpingo wa odzozedwa amenewa. Iye anauza mtumwi Petulo kuti: “Pathanthwe ili [lomwe ndi Yesu Khristu], ndidzamangapo mpingo wanga, ndipo zipata za Manda sizidzaugonjetsa.” (Mateyo 16:18) Ndiponso, pamene Yesu anali pamodzi ndi atumwi, anawauza kuti pasanapite nthawi yaitali padzapangidwa mpingo wachikhristu. Anawauzanso mmene mpingowo udzakhalire ndiponso mmene udzidzayendera.
3 Yesu anaphunzitsa mwa mawu ndi zochita zake, kuti anthu ena mumpingo adzakhala otsogolera. Iwo adzachita zimenezi mwa kutumikira ena mumpingo. Iye anati: “Inu mukudziwa kuti amene amaoneka ngati akulamulira amitundu amapondereza anthuwo ndipo akuluakulu awo amasonyeza mphamvu zawo pa iwo. Sizili choncho pakati panu; koma aliyense wofuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala mtumiki wanu, ndipo aliyense wofuna kukhala woyamba pakati panu ayenera kukhala kapolo wa onse.” (Maliko 10:42-44) Zinali zoonekeratu kuti “mpingo wa Mulungu” sudzakhala womwazikana, wa anthu osagwirizana moti n’kukhala wopanda dongosolo. M’malo mwake, mpingowo unayenera kudzakhala wa dongosolo ndiponso wa anthu ogwirizana.
4, 5. Kodi tikudziwa bwanji kuti mpingo unafunikira kuphunzitsidwa mwauzimu?
4 Yesu, yemwe anadzakhala Mutu wa “mpingo wa Mulungu,” ananena kuti atumwi ake ndi anthu ena omwe iye anawaphunzitsa, adzakhala ndi maudindo mumpingo. Kodi maudindo awo adzakhala otani? Udindo wofunika kwambiri ndiwo kuphunzitsa anthu mumpingo. Takumbukirani kuti Yesu ataukitsidwa anauza Petulo, ali pamodzi ndi atumwi ena kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda?” Ndipo Petulo anayankha kuti: “Inde Ambuye, inunso mukudziwa kuti ndimakukondani kwambiri.” Kenako Yesu anati kwa iye: “Dyetsa ana ankhosa anga. . . . Weta tiana tankhosa tanga. . . . Dyetsa tiana tankhosa tanga.” (Yohane 21:15-17) Uwutu unali udindo wofunika kwambiri!
5 Mawu a Yesu akutisonyeza kuti anthu omwe akusonkhanitsidwa mu mpingo ali ngati nkhosa zomwe zili m’khola. Nkhosazi ndi amuna, akazi, ndi ana ndipo afunikira kudyetsedwa mwauzimu komanso kuwetedwa bwinobwino. Ndiponso, Yesu analamula otsatira ake onse kuti aphunzitse anthu ena ndi kupanga ophunzira. Motero anthu atsopano onse omwe anakhala nkhosa zake anafunikira kuphunzitsidwa mmene angagwirire ntchito imene Mulungu anawapatsayi.—Mateyo 28:19, 20.
6. Kodi “mpingo wa Mulungu” wopangidwa kumene unali ndi dongosolo lotani?
6 Pamene “mpingo wa Mulungu” unapangidwa, anthu a mumpingomo ankasonkhana nthawi zonse kuti aphunzitsidwe ndiponso kulimbikitsana. Ndipo “anapitiriza kulabadira zimene atumwiwo anali kuphunzitsa, anali kugawana zinthu wina ndi mnzake, anali kudya zakudya komanso anali kupemphera.” (Machitidwe 2:42, 46, 47) Nkhani ina yodziwika bwino imanena kuti amuna ena oyenerera anapatsidwa udindo woti athandize kusamalira nkhani zina. Iwo sanasankhidwe chifukwa cha kuphunzira kwambiri kapena luso linalake lapadera. Iwo anali amuna “odzala ndi mzimu ndi nzeru.” Mmodzi mwa amuna amenewa anali Sitefano, ndipo nkhaniyo imafotokoza kuti iye anali “mwamuna wodzala ndi chikhulupiriro ndi mzimu woyera.” Chifukwa choti mipingo inakhazikitsidwa, “mawu a Mulungu anapitirira kufalikira ponseponse. Chiwerengero cha ophunzira chinali kuwonjezeka mowirikiza kwambiri mu Yerusalemu.”—Machitidwe 6:1-7.
Amuna Omwe Mulungu Amagwiritsa Ntchito
7, 8. (a) Kodi atumwi ndi akulu ku Yerusalemu ankatumikira monga ndani m’nthawi ya Akhristu oyambirira? (b) Kodi panakhala zotsatirapo zotani atapereka malangizo m’mipingo?
7 Atumwi analidi oyenerera kutsogolera m’mipingo yoyambirira, ndipo panalinso amanu ena omwe ankathandiza pa ntchito imeneyi. Panthawi ina, Paulo ndi anzake anabwerera ku Antiokeya wa ku Siliya. Lemba la Machitidwe 14:27 limati: “Atafika kumeneko ndi kusonkhanitsa mpingo pamodzi, anafotokoza zinthu zambiri zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo.” Iwo adakali pa mpingo wa kumeneko, kunabuka nkhani yamdulidwe yokhudza anthu omwe sanali Ayuda. Funso linali lakuti, kodi anthuwa anafunikira kudulidwa kapena ayi? Kuti athetse nkhaniyi, Paulo ndi Baranaba anatumizidwa “kwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu,” omwe anali m’bungwe lolamulira.—Machitidwe 15:1-3.
8 Yakobe, yemwe sanali mtumwi, koma anali m’bale wa Yesu ndiponso mkulu mumpingo, anatsogolera pamene “atumwi ndi akulu anasonkhana pamodzi kuti akambirane nkhaniyi.” (Machitidwe 15:6) Ataiona bwinobwino nkhaniyo mothandizidwa ndi mzimu woyera, anamanga mfundo imodzi mogwirizana ndi Malemba. Ndipo analemba zomwe anagwirizanazo m’kalata yomwe anaitumiza ku mipingo yonse. (Machitidwe 15:22-32) Anthu atalandira kalatayi anagwirizana ndi chigamulocho ndipo anayamba kutsatira mfundo zake. Kodi zotsatirapo zinali zotani? Abale ndi alongo analimbikitsidwa. Ndipo Baibulo limati: “Choncho mipingo inapitiriza kulimba m’chikhulupiriro ndi kuwonjezeka m’chiwerengero tsiku ndi tsiku.”—Machitidwe 16:5.
9. Kodi Baibulo limafotokoza maudindo otani amene amuna achikhristu ayenera kuchita mu mpingo?
9 Kodi mipingo inayenera kuyenda bwanji nthawi zonse? Mwachitsanzo, taganizirani mipingo yomwe inali pa chilumba cha Kerete. Ngakhale kuti anthu ambiri omwe ankakhala pa chilumbachi anali ndi makhalidwe oipa, ena anasintha n’kukhala Akhristu. (Tito 1:10-12; 2:2, 3) Iwo ankakhala m’mizinda yosiyanasiyana, ndipo onse anali kutali ndi bungwe lolamulira lomwe linali ku Yerusalemu. Koma limeneli silinali vuto lalikulu, chifukwa mumpingo uliwonse pachilumbachi munali “akulu” auzimu, mofanana ndi m’madera ena onse. Amunawo anakwaniritsa ziyeneretso zomwe zili m’Baibulo. Iwo anaikidwa kukhala akulu kapena kuti oyang’anira, kuti “athe kulimbikitsa ndi chiphunzitso chopindulitsa ndi kudzudzula otsutsa.” (Tito 1:5-9; 1 Timoteyo 3:1-7) Amuna ena auzimu omwe anakwaniritsa ziyeneretso anaikidwa kukhala atumiki othandiza m’mipingo.—1 Timoteyo 3:8-10, 12, 13.
10. Malinga ndi Mateyo 18:15-17, kodi mavuto aakulu amafunikira kuthetsedwa motani?
10 Yesu anasonyeza kuti padzakhala dongosolo loterolo. Takumbukirani nkhani yomwe ili pa Mateyo 18:15-17. Palembali Yesu ananena kuti nthawi zina mavuto angabuke pakati pa atumiki awiri a Mulungu, pamene wina walakwira mnzake. Munthu wolakwiridwa anafunikira kupita kwa mnzakeyo ndi “kukam’fotokozera cholakwacho” ali awiri pawokha. Ngati nkhaniyo sinathe atachita zimenezi, angaitane munthu wina mmodzi kapena awiri omwe akudziwa nkhaniyo kuti awathandize. Bwanji ngati nkhaniyo yalepherekabe kutha? Yesu anati: “Akapanda kuwamvera amenewanso, uuze mpingo. Ndipo mpingowo akapandanso kuumvera, kwa iwe akhale ngati munthu wamitundu komanso ngati wokhometsa msonkho.” Pamene Yesu ananena kuti Ayuda ndi omwe anali “mpingo wa Mulungu,” zikutanthauza kuti choyamba, mawuwa ankagwira ntchito kwa iwowo.a Koma mpingo wachikhristu utapangidwa, malangizo a Yesu anayamba kugwira ntchito mumpingowu. Umenewu ndi umboni wina woti anthu a Mulungu anayenera kudzakhala ndi dongosolo la mpingo loti aliyense azilangizidwa ndi kulimbikitsidwa.
11. Kodi akulu amachita mbali yotani pothetsa mavuto?
11 N’chifukwa chake n’koyenera kuti akulu, kapena kuti oyang’anira amayenera kuimira mpingo posamalira kapena kuthetsa mavuto, ngakhalenso kuweruza milandu. Zimenezi n’zogwirizana ndi ziyeneretso za akulu zotchulidwa pa Tito 1:9. Kunena zoona, akulu ndi anthu opanda ungwiro, monga momwe analili Tito. Komatu Titoyu anatumidwa ndi Paulo kumipingo kuti “[akonze] zinthu zosalongosoka.” (Tito 1:4, 5) Masiku ano, anthu omwe amavomerezedwa kuti akhale akulu afunikira kukhala atasonyeza kwanthawi yaitali kuti ndi okhulupirika ndiponso odzipereka. Motero, anthu onse mumpingo angadalire akulu ndiponso malangizo omwe angapereke.
12. Kodi akulu ali ndi udindo wotani mumpingo?
12 Paulo analembera akulu a mumpingo wa ku Efeso kuti: “Mudziyang’anire nokha ndi gulu lonse la nkhosa, limene mzimu woyera wakuikani pakati pawo kukhala oyang’anira, kuti muwete mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi magazi a Mwana wake wa iye mwini.” (Machitidwe 20:28) N’zoonadi, masiku ano oyang’anira mumpingo amaikidwa “kuti [awete] mpingo wa Mulungu.” Iwo ayenera kuchita zimenezi mwachikondi, osati mochita ufumu pankhosa. (1 Petulo 5:2, 3) Oyang’anira ayenera kuyesetsa kulimbikitsa ndi kuthandiza “gulu lonse la nkhosa.”
Kumamatira Mpingo
13. N’chiyani chingachitike mu mpingo nthawi zina, ndipo n’chifukwa chiyani?
13 Akulu ndiponso anthu ena onse mumpingo ndi opanda ungwiro. Nthawi zina kusamvana kumabuka, monga momwe zinachitikira m’nthawi ya atumwi. (Afilipi 4:2, 3) Woyang’anira kapena munthu wina anganene zinazake zooneka kuti n’zachipongwe, zamwano, kapena zabodza. Kapena tingaganize kuti chinachake chosemphana ndi Malemba chikuchitika, koma zikuoneka kuti akulu sakusamalira nkhaniyo ngakhale kuti akuidziwa. Koma n’kutheka kuti nkhaniyo inasamaliridwa kale kapena ikusamaliridwa mogwirizana ndi Malemba ndiponso mfundo zina zomwe ifeyo sitikuzidziwa. Ngakhale zinthu zitakhaladi monga mmene tikuonera, taganizirani izi: Mumpingo wa ku Korinto womwe Yehova ankausamalira, munachitika tchimo lalikulu kwakanthawi ndithu. M’kupita kwanthawi, Yehova anaonetsetsa kuti nkhaniyo yasamaliridwa bwino ndiponso mosayang’ana nkhope. (1 Akorinto 5:1, 5, 9-11) Tiyeni tidzifunse kuti, ‘Ndikanakhala kuti ndinali mu mpingo wa ku Korinto, kodi ndikanatani?’
14, 15. Kodi n’chifukwa chiyani anthu ena anasiya kutsatira Yesu, ndipo zimenezi zikutiphunzitsa chiyani?
14 Taganiziraninso izi: Tinene kuti munthu wina mumpingo akuvutika kumvetsa ndi kuvomereza mfundo inayake ya m’Malemba. Iye angakhale kuti anafufuza m’Baibulo ndi m’zofalitsa zomwe timalandira mu mpingo, ndiponso anafunsa Akhristu anzake okhwima mwauzimu, ngakhalenso akulu amene. Koma akuvutikabe kumvetsa ndi kuvomereza mfundoyo. Kodi angachite chiyani? Zofanana ndi zimenezi zinachitika kutatsala chaka chimodzi kuti Yesu aphedwe. Yesu ananena kuti iye anali “chakudya chopatsa moyo” ndipo munthu angakhale kosatha ngati atadya “mnofu wa Mwana wa munthu ndi kumwa magazi ake.” Zimenezi zinaimitsa mitu ena mwa ophunzira ake. M’malo moti afunse kapena kungodikira moleza mtima kuti Yehova adzakonze zinthu panthawi yake, ophunzira ambiri “sanayendenso [ndi Yesu].” (Yohane 6:35, 41-66) Tikanakhala kuti tinaliko panthawi imeneyo, kodi tikanatani?
15 Masiku ano, anthu ena asiya kusonkhana ndi mpingo, moti amaganiza kuti angatumikire Mulungu paokha. Iwo anganene kuti anasiya kusonkhana chifukwa choti munthu wina anawalakwira, kapena nkhani yokhudza tchimo linalake siikusamaliridwa, mwinanso sakufuna kuvomereza mfundo zinazake za m’Malemba. Kodi kuchita zinthu mwanjira imeneyi n’kwanzeru? N’zoona kuti Mkhristu aliyense ayenera kukhala paubwenzi ndi Mulungu, koma mfundo n’njakuti Yehova akugwiritsa ntchito mpingo monga momwe anachitira m’nthawi ya atumwi. Ndiponso, m’nthawi ya atumwi, Yehova anagwiritsa ntchito mipingo ndi kuidalitsa. Ndipo anakonza zoti akulu ndi atumiki othandiza oyenerera azisankhidwa kuti athandize mipingoyo. N’chimodzimodzinso masiku ano.
16. Munthu akhala ndi maganizo ofuna kusiya kugwirizana ndi mpingo, kodi ayenera kuganizira kaye za chiyani?
16 Ngati Mkhristu akuona kuti angathe kungodalira ubwenzi wake ndi Mulungu, ndiye kuti akukana dongosolo la Mulungu la mpingo womwe amasonkhanako komanso dongosolo la mpingo wa atumiki a Mulungu padziko lonse. Mkhristuyo angamalambire Mulungu ali yekhayekha kapena angamagwirizane ndi anthu ochepa chabe, koma kodi si zoona kuti dongosolo lokhala ndi akulu ndi atumiki othandiza lili mu mpingo mokha basi? Pamene Paulo analembera kalata Akhristu a mumpingo wa ku Kolose, anawauza kuti kalatayo iwerengedwenso ku Laodikaya. M’kalatayo analankhulamo za kukhala “ozika mizu ndi omangirika mwa [Khristu].” Anthu okhawo amene anali m’mipingo ndi omwe akanapindula ndi malangizo otero, osati omwe anasiya mpingo.—Akolose 2:6, 7; 4:16.
Mzati ndi Mchirikizo wa Choonadi
17. Kodi lemba la 1 Timoteyo 3:15 likutiphunzitsa chiyani ponena za mpingo?
17 M’kalata yake yoyamba yomwe analembera Timoteyo, yemwe anali mkulu mumpingo, mtumwi Paulo anafotokozamo ziyeneretso za akulu ndi atumiki othandiza. Atangotchula zimenezi, Paulo ananena za “mpingo wa Mulungu wamoyo” kuti ndi “mzati ndi mchirikizo wa choonadi.” (1 Timoteyo 3:15) M’nthawi ya atumwi, mpingo wonse wa Akhristu odzozedwa unalidi mzati. Ndipo n’zodziwikiratu kuti Mkhristu aliyense anafunikira kulandira choonadi m’dongosolo la mpingo basi. M’mipingo imeneyi, choonadi chinkaphunzitsidwa ndi kuchirikizidwa ndiponso anthu ankalimbikitsidwa.
18. N’chifukwa chiyani misonkhano ya mipingo ndi yofunika kwambiri?
18 Izi zili chimodzimodzinso ndi mpingo wachikhristu padziko lonse. Mpingowu ndi nyumba ya Mulungu, kapena kuti “mzati ndi mchirikizo wa choonadi.” Njira yofunika kwambiri imene tingalimbikitsire ubwenzi wathu ndi Mulungu ndiponso kukhala okonzeka kuchita chifuniro chake, ndiyo kupezeka pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse ndi kutenga nawo mbali. Polembera mpingo wa ku Korinto, Paulo anatchula za nkhani zomwe zinkakambidwa pa misonkhano imeneyi. Iye ankafuna kuti zomwe zinkalankhulidwa pa misonkhanoyi zikhale zosavuta kumva kotero kuti anthu omwe anapezekapo ‘alimbikitsidwe.’ (1 Akorinto 14:12, 17-19) Nafenso masiku ano tingalimbikitsidwe ngati titazindikira kuti dongosolo la mipingo lakonzedwa ndi Yehova Mulungu ndipo akulichirikiza.
19. N’chifukwa chiyani mufunikira kuyamikira kwambiri mpingo wanu?
19 N’zoona, ngati ifeyo tikufuna kulimbikitsidwa, sitingayese dala kusiya mpingo. Kuyambira kalekale mpingo wakhaladi woteteza ku ziphunzitso zabodza. Ndipo Mulungu wakhala akuugwiritsa ntchito polalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mesiya padziko lonse. Mosakayikira, Mulungu wachita zinthu zambiri kudzera mu mpingo wachikhristu.—Aefeso 3:9, 10.
[Mawu a M’munsi]
a Katswiri wamaphunziro a Baibulo, Albert Barnes anazindikira kuti mawu a Yesu akuti “uuze mpingo” angatanthauze “anthu omwe ali ndi udindo wofufuza nkhani zotero, anthu omwe amaimira mpingo. Mu masunagoge a Ayuda munali akulu omwe ankaweruza nkhani zotero.”
Kodi Mungakumbukire?
• N’chifukwa chiyani tiyenera kuyembekezera kuti Mulungu amagwiritsa ntchito mipingo ya padziko lapansi?
• Kodi n’chiyani chomwe akulu amachita mu mpingo ngakhale kuti ndi opanda ungwiro?
• Kodi inuyo mukulimbikitsidwa motani ndi mpingo wanu?
[Chithunzi patsamba 26]
Atumwi ndi akulu ku Yerusalemu anatumikira m’bungwe lolamulira
[Chithunzi patsamba 28]
Akulu ndi atumiki othandiza amalandira malangizo kuti athe kukwaniritsa maudindo awo mumpingo