Akristu Amalambira Mumzimu ndi M’choonadi
“Mulungu ndiye mzimu; ndipo om’lambira Iye ayenera kum’lambira mumzimu ndi m’choonadi.”—YOHANE 4:24.
1. Kodi Mulungu amasangalala ndi kulambira kotani?
YESU KRISTU, mwana wobadwa yekha wa Yehova, anafotokoza bwino kulambira kumene kumasangalatsa Atate wake wakumwamba. Pamene anali kupereka umboni wogwira mtima kwa mkazi wachisamariya pachitsime china pafupi ndi mudzi wa Sukari, Yesu anati: “Inu mulambira chimene simuchidziŵa; ife tilambira chimene tichidziŵa; pakuti chipulumutso chichokera kwa Ayuda. Koma ikudza nthaŵi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake. Mulungu ndiye mzimu; ndipo om’lambira Iye ayenera kum’lambira mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:22-24) Kodi mawu ameneŵa akutanthauza chiyani?
2. Kodi kulambira kwa Asamariya kunali ndi maziko otani?
2 Zimene Asamariya anali kukhulupirira m’chipembedzo chawo zinali zonyenga. Iwo anali kukhulupirira kuti mabuku asanu okha oyambirira ndiwo ouziridwa pa Malemba Opatulika onse ndiponso anali kunena kuti mabuku asanu ouziridwawo amangopezeka m’Baibulo limene iwo analitembenuza lotchedwa Pentatuke ya Asamariya basi. Pamene Asamariya sanali kudziŵa Mulungu bwinobwino, Ayuda ndiwo anapatsidwa Malemba ndipo anali kuwadziŵa. (Aroma 3:1, 2) Zinali zotheka kuti Yehova ayanje Ayuda okhulupirika ndi anthu ena. Koma kodi anafunika kuchita chiyani?
3. Kodi chofunika n’chiyani kuti tilambire Mulungu “mumzimu ndi m’choonadi”?
3 Kodi Ayuda, Asamariya ndi anthu ena akale anafunika kuchita chiyani kuti asangalatse Yehova? Anafunika kum’lambira “mumzimu ndi m’choonadi.” Ifenso tiyenera kutero. Ngakhale kuti tifunika kukangalika potumikira Mulungu, ndiponso kuchita zimenezi chifukwa cha mtima wodzala ndi chikondi ndi chikhulupiriro, kulambira Mulungu mumzimu makamaka kumafuna kuti ife tikhale ndi mzimu wake ndi kuulola kuti utitsogolere. Mwa kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kuwatsatira, mzimu wathu, kapena kuti maganizo athu, ayenera kugwirizana ndi a Mulungu. (1 Akorinto 2:8-12) Ndiponso, kuti Yehova avomereze kulambira kwathu, kufunika kuchitike m’choonadi. Kuyenera kugwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu, Baibulo, amavumbula za iye ndi zolinga zake.
Choonadi Chingapezeke
4. Kodi ena amaganiza bwanji za choonadi?
4 Ena ophunzira nzeru za anthu ali ndi maganizo akuti anthu sangapeze choonadi chenicheni. N’zimene mlembi wina wa ku Sweden, Alf Ahlberg, analemba. Anati: “Mafunso ambiri amene amafunsa m’maphunziro a nzeru za anthu ndi oti sikutheka kupeza mayankho ake enieni.” Ngakhale kuti ena amati palibe choonadi chenicheni, kodi zimenezi n’zoona? Yesu Kristu sanaganize choncho.
5. N’chifukwa chiyani Yesu anadza ku dziko lapansi?
5 Tiyeni tiyerekeze kuti tikuona zochitika zotsatirazi: N’kuchiyambi kwa chaka cha 33 C.E., ndipo Yesu waima pamaso pa Kazembe wachiroma Pontiyo Pilato. Yesu akuuza Pilato kuti: “Ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi.” Pilato akufunsa kuti: “Choonadi n’chiyani?” Koma sakudikira kuti Yesu alankhulenso.—Yohane 18:36-38.
6. (a) Kodi “choonadi” achimasulira motani? (b) Kodi Yesu analamula otsatira ake kuchita chiyani?
6 “Choonadi” chimatanthauza “gulu la zinthu, zochitika, ndiponso mfundo zenizeni.” (Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary) Koma kodi Yesu anachitira umboni choonadi wamba? Ayi. Anali kuganiza za choonadi chinachake. Analamula otsatira ake kulalikira choonadi chimenecho, pakuti anawauza kuti: “Phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Mapeto a nthaŵi ya pansi pano asanafike, otsatira enieni a Yesu akalalikira “choonadi cha Uthenga Wabwino” padziko lonse. (Mateyu 24:3; Agalatiya 2:14) Akachita zimenezo pokwaniritsa mawu a Yesu akuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) N’chifukwa chake m’pofunika kwambiri kuti tiwadziŵe amene akuphunzitsa mitundu yonse choonadi mwa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu.
Mmene Tingadziŵire Choonadi
7. Kodi mungatsimikize bwanji kuti Yehova ndiye Gwero la choonadi?
7 Yehova ndiye Gwero la choonadi chauzimu. Ndipotu, wamasalmo Davide anati Yehova ndi “Mulungu wa choonadi.” (Salmo 31:5; 43:3) Yesu anazindikira kuti mawu a Atate wake ndiwo choonadi, ndiponso ananena kuti: “Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine.” (Yohane 6:45; 17:17; Yesaya 54:13) Ndiyetu, n’zachionekere kuti amene akufuna choonadi ayenera kuphunzitsidwa ndi Yehova, Mlangizi Wamkulu. (Yesaya 30:20, 21) Ofunafuna choonadi afunika “kum’dziŵadi Mulungu.” (Miyambo 2:5) Ndipo Yehova waphunzitsa kapena kupereka choonadi mwachikondi m’njira zosiyanasiyana.
8. Kodi Mulungu waphunzitsa ndi kupereka choonadi m’njira zotani?
8 Mwachitsanzo, Mulungu anapereka Chilamulo kwa Aisrayeli kudzera mwa angelo. (Agalatiya 3:19) Analonjeza madalitso kwa Abrahamu ndi Yakobo, makolo akale, kudzera m’maloto. (Genesis 15:12-16; 28:10-19) Mulungu analankhulanso kuchokera kumwamba, monga panthaŵi imene Yesu anali kubatizidwa, ndipo padziko lapansi mawu osangalatsa anamveka akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3:17) Tingayamikirenso kuti Mulungu anapereka choonadi mwa kuuzira olemba Baibulo. (2 Timoteo 3:16, 17) Motero, ngati tiphunzira Mawu a Mulungu, tingakhale ndi “chikhulupiriro cha choonadi.”—2 Atesalonika 2:13.
Kugwirizana kwa Choonadi ndi Mwana wa Mulungu
9. Kodi Mulungu wagwiritsa ntchito bwanji Mwana wake kuvumbula choonadi?
9 Mulungu wagwiritsa ntchito makamaka Mwana wake, Yesu Kristu, kuvumbula choonadi kwa anthu. (Ahebri 1:1-3) Inde, Yesu analankhula choonadi chimene munthu wina aliyense sanalankhulepo chiyambire. (Yohane 7:46) Iye anavumbula choonadi cha Atate wake ngakhale atakwera kumwamba. Mwachitsanzo, mtumwi Yohane analandira “chivumbulutso cha Yesu Kristu, chimene Mulungu anam’vumbulutsira achionetsere akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa.”—Chivumbulutso 1:1-3.
10, 11. (a) Kodi choonadi chimene Yesu anachitira umboni chikukhudzana ndi chiyani? (b) Kodi Yesu anachititsa bwanji choonadi kukhala chenicheni?
10 Yesu anauza Pontiyo Pilato kuti Iye anabwera padziko lapansi kudzachitira umboni choonadi. Yesu muutumiki wake, anavumbula kuti choonadi chimenecho chinakhudza za kutsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndi kuti adzachita zimenezo kudzera mu Ufumu wa Mulungu womwe Mfumu yake ndi Kristu. Komabe Yesu anafunika kuchita zambiri kuti achitire umboni choonadi osati kulalikira ndi kuphunzitsa kokha ayi. Yesu anakwaniritsa choonadi ndipo chinakhala chenicheni. N’chifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Munthu aliyense asakuweruzeni inu m’chakudya, kapena chakumwa, kapena m’kunena tsiku la phwando, kapena tsiku lokhala mwezi, kapena la Sabata; ndizo mthunzi wa zilinkudzazo; koma thupi ndi la [“zenizeni zake ndi,” NW] Kristu.”—Akolose 2:16, 17.
11 Imodzi mwa njira zimene choonadi chinakhalira chenicheni ndiyo kubadwa kwa Yesu ku Betelehemu kumene ananeneratu. (Mika 5:2; Luka 2:4-11) Choonadi chinakhalanso chenicheni pamene ulosi wa Danieli wakuti Mesiya adzafika kumapeto kwa ‘masabata a zaka’ 69 unakwaniritsidwa. Zimenezo zinachitika pamene Yesu anadzipereka kwa Mulungu pa ubatizo wake ndi kudzozedwa ndi mzimu woyera mu 29 C.E., ndendende ndi nthaŵi imene analosera. (Danieli 9:25; Luka 3:1, 21, 22) Utumiki wa Yesu umene unatsegula anthu m’maso monga wolengeza Ufumu unachititsanso choonadi kukhala chenicheni. (Yesaya 9:1, 2, 6, 7; 61:1, 2; Mateyu 4:13-17; Luka 4:18-21) Chinakhalanso chenicheni mwa imfa ndi kuuka kwake.—Salmo 16:8-11; Yesaya 53:5, 8, 11, 12; Mateyu 20:28; Yohane 1:29; Machitidwe 2:25-31.
12. N’chifukwa chiyani m’pake kuti Yesu anati, ‘Ine ndine choonadi’?
12 Popeza choonadi chimanena kwambiri za Yesu, m’pake kuti anati: “Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.” (Yohane 14:6) Anthu amamasuka mwauzimu ‘akakhala mwa choonadi’ mwa kuvomereza udindo wa Yesu pa cholinga cha Mulungu. (Yohane 8:32-36; 18:37) Popeza anthu onga nkhosa amavomera choonadi ndi kutsatira Kristu mwa chikhulupiriro, adzalandira moyo wosatha.—Yohane 10:24-28.
13. Kodi tipenda choonadi cha m’Malemba m’mbali zitatu ziti?
13 Mfundo za choonadi zimene Yesu ndi ophunzira ake ouziridwa anapereka n’zimene zonse pamodzi zimapanga chikhulupiriro chenicheni chachikristu. Motero, amene ‘amamvera chikhulupirirocho,’ ‘amayenda m’choonadi.’ (Machitidwe 6:7; 3 Yohane 3, 4) Nangano ndani amene akuyenda m’choonadi lerolino? Ndani amene akuphunzitsadi mitundu yonse choonadi? Kuti tiyankhe, tiika maganizo athu pa Akristu oyambirira ndi kupenda choonadi cha m’Malemba chokhudza (1) zikhulupiriro, (2) kalambiridwe, ndiponso (3) khalidwe la munthu payekha.
Choonadi pa Nkhani ya Zikhulupiriro
14, 15. Kodi mungati Akristu oyambirira anawaona bwanji Malemba ndipo Mboni za Yehova zimawaona bwanji?
14 Akristu oyambirira anali kulemekeza kwambiri Mawu olembedwa a Yehova. (Yohane 17:17) Anali muyeso wa zikhulupiriro zawo ndi zochita zawo. Clement wa ku Alexandria wa m’zaka za m’ma 100 ndi 200 anati: “Amene ali ndi khama lofuna kuchita bwino sadzaleka kufunafuna choonadi, mpaka atapeza umboni wa m’Malemba wa zimene amakhulupirira.”
15 Mboni za Yehova, mofanana ndi Akristu oyambirira, zimalemekeza Baibulo kwambiri. Zimakhulupirira kuti “lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso.” (2 Timoteo 3:16) Motero, tiyeni tione zikhulupiriro zingapo za Akristu oyambirira ndi kuziyerekeza ndi zomwe atumiki a Yehova masiku ano aphunzira chifukwa chogwiritsa ntchito Baibulo monga buku lalikulu lophunzirira.
Zoona Zake za Mzimu
16. Kodi zoona zake za mzimu n’ziti?
16 Popeza Akristu oyambirira anakhulupirira zimene Malemba amanena, anaphunzitsa zoona pankhani ya mzimu. Anali kudziŵa kuti mzimu si chinachake m’kati mwa munthu chomwe chimapulumuka munthuyo akamwalira. Uwo ndiwo mphamvu ya moyo imene imathandiza thupi kukhala lamoyo koma sutha kuchita kalikonse popanda thupi. (Yakobo 2:26) Anali kudziŵanso kuti “akufa sadziŵa kanthu bi.”—Mlaliki 9:5, 10.
17. Kodi mungati akufa akuyembekezera chiyani?
17 Komabe, ophunzira a Yesu oyambirira anali ndi chiyembekezo chodalirika chakuti akufa amene Mulungu akuwakumbukira adzawaukitsa, kapena kuti kuwapatsanso moyo. Paulo anafotokoza momveka bwino chikhulupiriro chimenechi pamene anati: “Ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Patapitanso nthaŵi, wina amene anati ndi Mkristu dzina lake Minucius Felix analemba kuti: “Ndani wopanda nzeru kapena wosazindikira amene angatsutse kuti munthu amene Mulungu anam’panga, sangam’pangenso?” Mofanana ndi Akristu oyambirira, Mboni za Yehova zimatsatira choonadi cha m’Malemba pankhani ya mzimu wa munthu, imfa, ndi kuuka kwa akufa. Tiyeni tsopano tione kuti kodi Mulungu ndi Yesu ndani.
Choonadi pa Nkhani ya Utatu
18, 19. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Malemba saphunzitsa Utatu?
18 Akristu oyambirira sanakhulupirire kuti Mulungu, Kristu, ndi mzimu woyera ali Utatu. Buku lakuti Encyclopaedia Britannica linati: “Mawu akuti Utatu kapena chiphunzitso chonsecho sizipezeka n’komwe m’Chipangano Chatsopano, ndipo Yesu ndi ophunzira ake sanafune kutsutsana ndi Shema [pemphero la Chihebri] la m’Chipangano Chakale lomwe limati: ‘Imvani, Israyeli: Ambuye Mulungu wathu, ndiye Ambuye mmodzi.’ (Deut. 6:4)” Akristu sanalambire milungu itatu kapena milungu ina ya Aroma. Anakhulupirira zimene Yesu ananena kuti Yehova yekha ndiye woyenera kumulambira. (Mateyu 4:10) Ndiponso, anakhulupirira mawu a Kristu akuti: “Atate ali wamkulu ndi Ine.” (Yohane 14:28) Mboni za Yehova zimakhulupiriranso zomwezi masiku ano.
19 Otsatira a Yesu oyambirira anadziŵa bwinobwino kusiyana kwa Mulungu, Kristu, ndi mzimu woyera. Ndipotu, anali kubatiza ophunzira (1) ‘m’dzina la Atate, (2) m’dzina la Mwana, ndi (3) m’dzina la mzimu woyera,’ osati m’dzina la Utatu. N’chimodzimodzinso ndi Mboni za Yehova. Zimaphunzitsa choonadi cha m’Malemba ndipo zimasiyanitsa Mulungu, Mwana wake, ndi mzimu woyera.—Mateyu 28:19.
Choonadi pa Nkhani ya Ubatizo
20. Kodi anthu ofuna kubatizidwa afunika kudziŵa chiyani?
20 Yesu analamula otsatira ake kuti apange ophunzira mwa kuphunzitsa anthu choonadi. Kuti abatizidwe, iwo afunika kudziŵa ziphunzitso zazikulu zoyamba za m’Malemba. Mwachitsanzo, ayenera kuzindikira udindo wa Atate ndi wa Mwana wake, Yesu Kristu, ndiponso ulamuliro wawo. (Yohane 3:16) Ofuna kubatizidwa afunikanso kudziŵa kuti mzimu woyera sindiwo munthu koma ndi mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito.—Genesis 1:2, NW, mawu a m’munsi.
21, 22. N’chifukwa chiyani munganene kuti anthu ofunika kubatizidwa ndi okhulupirira okha?
21 Akristu oyambirira, anali kubatiza anthu okhawo amene anaphunzira ndi kulapa ndipo anadzipatulira ndi mtima wonse kwa Mulungu kuti achite chifuniro chake. Ayuda ndi otembenukira ku Chiyuda amene anasonkhana ku Yerusalemu pa Pentekoste wa 33 C.E., anali akudziŵa kale Malemba Achihebri. Atamva zimene mtumwi Petro ananena za Yesu Mesiyayo, anthu pafupifupi 3,000 “analandira mawu ake” ndipo “anabatizidwa.”—Machitidwe 2:41; 3:19–4:4; 10:34-38.
22 Ubatizo wachikristu ndi wa anthu okhulupirira. Anthu a ku Samariya analandira choonadi, ndipo “pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Kristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.” (Machitidwe 8:12) Mdindo wa ku Etiopia yemwe anali wotembenukira ku Chiyuda wodzipereka amene anali kudziŵa za Yehova, anayamba kaye wakhulupirira zimene Filipo ananena za kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Mesiya ndiyeno anabatizidwa. (Machitidwe 8:34-36) Patapita nthaŵi, Petro anauza Korneliyo ndi Akunja ena kuti “wakumuwopa [Mulungu] ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye” ndi kutinso aliyense amene akhulupirira Yesu Kristu machimo ake adzakhululukidwa. (Machitidwe 10:35, 43; 11:18) Zonsezi zikugwirizana ndi lamulo la Yesu la ‘kuphunzitsa anthu ndi kuwaphunzitsa asunge zinthu zonse zimene analamulira.’ (Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 1:8) Nazonso Mboni za Yehova zimatsatira muyezo womwewu. Zimabatiza anthu okhawo amene adziŵa ziphunzitso zazikulu zoyamba za m’Malemba ndiponso amene adzipatulira kwa Mulungu.
23, 24. Kodi ubatizo woyenera wa Akristu ndi uti?
23 Ubatizo woyenerera ndi womiza thupi lonse la munthu wokhulupirirayo m’madzi. Yesu atabatizidwa mu mtsinje wa Yordano, anakwera ‘kutuluka m’madzi.’ (Marko 1:10) Mdindo wa ku Etiopia anabatizidwa ku “madzi.” Iye ndi Filipo “anatsikira . . . kumadzi” ndiyeno “anakwera kutuluka m’madzi.” (Machitidwe 8:36-40) Malemba amagwirizanitsa ubatizo ndi kuikidwa m’manda kophiphiritsa. Zimenezinso zikusonyeza kuti ubatizowo uyenera kukhala womiza thupi lonse m’madzi.—Aroma 6:4-6; Akolose 2:12.
24 Buku lakuti The Oxford Companion to the Bible limati: “Mmene amafotokozera maubatizo a m’Chipangano Chatsopano zikusonyeza kuti munthu wobatizidwayo anali kum’miza m’madzi.” Malinga ndi buku lachifalansa lakuti Larousse du XXe Siècle (Paris, 1928), “Akristu oyambirira anali kuwabatiza mwa kuwamiza m’madzi kulikonse kumene anapeza madzi.” Ndiponso buku lakuti After Jesus—The Triumph of Christianity limati: “[Ubatizo] kwenikweni unafuna kuti munthu woti abatizidweyo alengeze chikhulupiriro chake, ndiyeno anali kum’miza thupi lonse m’madzi m’dzina la Yesu.”
25. Kodi tikambirana zotani m’nkhani yotsatirayi?
25 Mfundo zimene takambiranazi zokhudza zikhulupiriro ndi zinthu zina zimene Akristu oyambirira anali kuchita potsatira zimene Baibulo limanena n’zitsanzo zochepa chabe. N’zotheka kufotokoza kufanana kwinanso kwa zikhulupiriro zawo ndi za Mboni za Yehova. M’nkhani yotsatirayi, tikambirana njira zinanso zimene tingadziŵire amene akuphunzitsa athu choonadi.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi Mulungu amafuna kulambira kotani?
• Kodi choonadi chinakhala bwanji chenicheni kudzera mwa Yesu Kristu?
• Kodi zoona zake za mzimu ndi imfa n’zotani?
• Kodi ubatizo wachikristu umachitika bwanji, ndipo ofuna kubatizidwa amafunika chiyani?
[Chithunzi patsamba 16]
Yesu anauza Pilato Kuti: ‘Ndinadza kudzachitira umboni choonadi’
[Chithunzi patsamba 17]
Kodi mungafotokoze chifukwa chake Yesu anati: ‘Ine ndine choonadi’?
[Chithunzi patsamba 18]
Kodi zoona zake za ubatizo wachikristu n’zotani?