Anthu Afunikira Chidziŵitso Chonena za Mulungu
“Udzazindikira kuwopa Yehova ndi kumdziŵadi Mulungu.”—MIYAMBO 2:5.
1. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti mtima wa munthu uli wopangidwa ndi luso laumulungu?
PANTHAŴI inoyi, mitima ya anthu pafupifupi 5,600,000,000 ikugunda padziko lapansi. Tsiku lililonse, mtima wanu umagunda nthaŵi 100,000 ndipo umapopa malita a mwazi okwanira 7,600 pamtunda wamakilomita 100,000 m’njira zake za mitsempha yogwirizana ndi mtima. Palibe chiŵalo china chilichonse chimene chimagwira ntchito kwambiri monga chiŵalo chimenechi chopangidwa ndi luso laumulungu.
2. Kodi mungaufotokoze motani mtima wophiphiritsira?
2 Palinso mitima yophiphiritsira yokwanira 5,600,000,000 imene ikugwira ntchito padziko lapansi. Mumtima wophiphiritsira umenewo ndimo mumakhala mikhalidwe yathu, zikhumbo, ndi zolinga zathu. Ndiwo magwero a ndingaliro zathu, kuzindikira kwathu, chifuno chathu. Mtima wophiphiritsira ungakhale wonyada kapena wodzichepetsa, wachisoni kapena wokondwa, wamdima kapena woŵala.—Nehemiya 2:2; Miyambo 16:5; Mateyu 11:29; Machitidwe 14:17; 2 Akorinto 4:6; Aefeso 1:16-18.
3, 4. Kodi mitima ikufikidwa motani ndi uthenga wabwino?
3 Yehova Mulungu amadziŵa za mumtima wa munthu. Miyambo 17:3 imati: “Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golidi ali ndi ng’anjo; koma Yehova ayesa mitima.” Komabe, m’malo mongodziŵa za mumtima uliwonse ndi kuweruza, Yehova akugwiritsira ntchito Mboni zake kufika mitima ya anthu ndi uthenga wabwino. Zimenezi zikugwirizana ndi mawu a mtumwi Paulo akuti: “Aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka. Ndipo iwo adzaitana bwanji pa iye amene sanamkhulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira? Ndipo adzalalikira bwanji ngati satumidwa? Monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira uthenga wabwino wa zinthu zabwino.”—Aroma 10:13-15.
4 Chakomera Yehova kutuma Mboni zake kumalekezero a dziko lapansi ‘kukalalikira uthenga wabwino wa zinthu zabwino’ ndi kupeza aja amene ali ndi mtima womvera. Tsopano tikuposa pa 5,000,000—chiŵerengero cha Mboni imodzi kwa anthu pafupifupi 1,200 padziko lapansi. Kufikira mabiliyoni a anthu padziko lapansi ndi uthenga wabwino si nkhani yapafupi. Koma Mulungu akutsogolera ntchito imeneyi kupyolera mwa Yesu Kristu ndipo akukoka anthu oona mtima. Motero, ulosi wolembedwa pa Yesaya 60:22 ukukwaniritsidwa: “Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.”
5. Kodi chidziŵitso nchiyani, ndipo nchiyani chimene chinganenedwe ponena za nzeru ya dziko?
5 Ino ndiyo nthaŵiyo, ndipo chinthu chimodzi nchotsimikizirika—mabiliyoni a anthu padziko lapansi afunikira chidziŵitso. Kwenikweni, chidziŵitso ndicho kudziŵa zinthu zoona mwa kuzichita, kuziona, kapena kuziphunzira. Dziko lakundika chidziŵitso chochuluka kwambiri. Zinthu zapita patsogolo m’zamayendedwe, kusamalira umoyo, ndi njira zolankhulirana. Koma kodi ndi nzeru ya dziko imene munthu afunikira kwenikweni? Kutalitali! Nkhondo, kupondereza ena, matenda, ndi imfa zikupitirizabe kuvutitsa anthu. Nzeru ya dziko kaŵirikaŵiri yakhala monga mchenga womasunthasuntha ndi chimphepo m’chipululu.
6. Pankhani ya mwazi, kodi chidziŵitso chonena za Mulungu chimasiyana motani ndi nzeru ya dziko?
6 Mwachitsanzo: Zaka mazana aŵiri kalelo, kuchotsa mwazi m’thupi kunali njira yofala yochiritsira matenda. George Washington, pulezidenti woyamba wa United States, anachotsedwa mwazi mobwerezabwereza m’maola otsirizira a moyo wake. Panthaŵi ina iye anati: “Ndilekeni ndife mwamtendere; sindingakhalenso ndi moyo nthaŵi yaitali.” Ananena zoona, pakuti anafa tsiku lomwelo—December 14, 1799. M’malo mwa kuchotsa mwazi m’thupi, lerolino akugogomezera za kuika mwazi mu thupi la munthu. Njira ziŵirizo zakhala ndi mavuto akupha. Komabe, kwa nthaŵi yonseyi, Mawu a Mulungu anena kuti: “Musale . . . mwazi.” (Machitidwe 15:29) Chidziŵitso chonena za Mulungu chimakhala cholondola, chodalirika, ndi chapanthaŵi yake masiku onse.
7. Kodi chidziŵitso cholongosoka cha Malemba chimasiyana motani ndi nzeru ya dziko pa kaleredwe ka ana?
7 Talingaliraninso za chitsanzo china cha kusadalirika kwa nzeru ya dziko. Kwa zaka zambiri akatswiri azamaganizo anachirikiza kulera ana molekerera, koma wina wa ochirikiza zimenezo anavomereza pambuyo pake kuti zimenezo zinali zolakwika. Panthaŵi ina German Philological Association inanena kuti kulekerera “kwachititsa mavuto amene tili nawo ndi achichepere pamlingo wina wake.” Nzeru ya dziko imatengekatengeka ngati kuti ikuombedwa ndi mphepo, koma chidziŵitso cholongosoka cha Malemba chakhala chosagwedezeka. Baibulo limapereka uphungu woyenera pa kulera ana. Miyambo 29:17 imati: “Langiza mwana wako, ndipo adzakupumitsa; nadzasangalatsa moyo wako.” Chilango chimenecho chiyenera kuperekedwa mwachikondi, pakuti Paulo analemba kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”—Aefeso 6:4.
“Kumdziŵadi Mulungu”
8, 9. Kodi mungafotokoze motani zimene Miyambo 2:1-6 imanena pa chidziŵitso chimene anthu afunikiradi?
8 Ngakhale kuti Paulo anali munthu wophunzira, iye anati: “Ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu m’nthaŵi ino ya pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru. Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu.” (1 Akorinto 3:18, 19) Mulungu yekha ndiye angapereke chidziŵitso chimene anthu afunikira kwenikweni. Ponena za chidziŵitso chimenecho, Miyambo 2:1-6 imati: “Mwananga, ukalandira mawu anga, ndi kusunga malamulo anga; kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira; ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuwopa Yehova ndi kumdziŵadi Mulungu. Pakuti Yehova apatsa nzeru; kudziŵa ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake.”
9 Aja amene amasonkhezeredwa ndi mtima wabwino amatchera khutu kunzeru mwa kugwiritsira ntchito bwino chidziŵitso chopatsidwa ndi Mulungu. Amalozetsa mitima yawo kukuzindikira, akumapenda mosamala zinthu zimene akuphunzira. Kwenikweni, amafuulira kuzindikira, kapena luntha la kuona mmene mfundo za nkhani zikugwirizanirana. Amitima yoongoka amagwira ntchito ngati kuti akukumba siliva ndi kufunafuna chuma chobisika. Koma kodi ndi chuma chotani chimene aja amtima womvera amapeza? Ndicho “kumdziŵadi Mulungu.” Kodi nchiyani chimenecho? Mwachidule, ndicho chidziŵitso chopezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo.
10. Kodi tiyenera kuchitanji kuti tikhale ndi thanzi labwino lauzimu?
10 Chidziŵitso chonena za Mulungu ndi choona, chodalirika, chopatsa moyo. Chimapatsa thanzi lauzimu. Paulo analimbikitsa Timoteo kuti: “Gwira chitsanzo cha mawu amoyo, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Kristu Yesu.” (2 Timoteo 1:13) Chinenero chimakhala ndi chitsanzo cha mawu ake. Momwemonso, “chinenero choyera” cha choonadi cha Malemba chili ndi “chitsanzo cha mawu amoyo,” ozikidwa makamaka pa mutu wankhani wa Baibulo wa kutsimikiziritsa kuyenera kwa ulamuliro wa Yehova mwa Ufumu wake. (Zefaniya 3:9, NW) Tifunikira kusunga chitsanzo cha mawu amoyo chimenechi m’maganizo ndi m’mitima. Kuti tipeŵe matenda a mtima wophiphiritsira ndi kukhalabe amoyo mwauzimu, tiyenera kugwiritsira ntchito Baibulo m’moyo wathu ndi kugwiritsira ntchito zogaŵira zonse zauzimu zimene Mulungu akupereka kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47; Tito 2:2) Tiyeni nthaŵi zonse tikumbukire kuti tifunikira chidziŵitso chonena za Mulungu kuti tikhale amoyo mwauzimu.
11. Kodi zifukwa zina zimene anthu afunikira chidziŵitso chonena za Mulungu nzotani?
11 Talingalirani zifukwa zina zimene mabiliyoni a anthu padziko lapansi amafunikira chidziŵitso chonena za Mulungu. Kodi onse amadziŵa mmene dziko lapansi ndi anthu anakhalirapo? Iyayi, iwo samadziŵa. Kodi anthu onse amadziŵa Mulungu woona ndi Mwana wake? Kodi onse akudziŵa nkhani zimene Satana anabutsa ponena za ulamuliro waumulungu ndi umphumphu wa anthu? Sakudziŵa. Kodi anthu ambiri akudziŵa chimene timakalambira ndi kufa? Apanso tiyenera kunena kuti ayi. Kodi onse okhala padziko lapansi amadziŵa kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira tsopano ndi kuti tikukhala m’masiku otsiriza? Kodi akudziŵa za mizimu yoipa? Kodi anthu onse ali ndi chidziŵitso chodalirika cha mmene angakhalire ndi moyo wa banja lachimwemwe? Ndipo kodi makamu a anthu akudziŵa kuti chifuno cha Mlengi wathu nchakuti anthu omvera adzakhale ndi moyo wosangalatsa m’Paradaiso? Pamafunso awanso yankho ndi lakuti iyayi. Chotero, nkwachionekere kuti anthu afunikira chidziŵitso chonena za Mulungu.
12. Kodi ndi motani mmene tingalambirire Mulungu “mumzimu ndi m’choonadi”?
12 Anthu afunikiranso chidziŵitso chonena za Mulungu chifukwa cha zimene Yesu ananena m’pemphero pausiku womaliza wa moyo wake wapadziko lapansi. Atumwi ake ayenera kukhala atakhudzidwa mtima kwambiri kumumva iye akunena kuti: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Kugwiritsira ntchito chidziŵitso chimenecho ndiko njira yokha yolambirira Mulungu movomerezeka. “Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m’choonadi,” Yesu anatero. (Yohane 4:24) Timalambira Mulungu “mumzimu” pamene mitima yodzaza chikhulupiriro ndi chikondi imatisonkhezera kutero. Nanga timamlambira motani “m’choonadi”? Mwa kuphunzira Mawu ake ndi kumlambira iye mogwirizana ndi choonadi chake chovumbulidwa—“kumdziŵadi Mulungu.”
13. Kodi pa Machitidwe 16:25-34 palembedwa za chochitika chotani, ndipo chingatiphunzitsenji?
13 Anthu zikwi zambiri amayamba kulambira Yehova chaka ndi chaka. Komabe, kodi tiyenera kuchititsa maphunziro a Baibulo kwa anthu okondwerera kwa nthaŵi yaitali, kapena kodi nkotheka kwa anthu oona mtima kufika paubatizo mofulumira? Chabwino, talingalirani zimene zinachitika kwa wosunga ndende ndi banja lake wosimbidwa pa Machitidwe 16:25-34. Paulo ndi Sila anali m’ndende ku Filipi, koma pakati pa usiku, chivomezi chachikulu chinatsegula zitseko za ndendeyo. Poganiza kuti andende onse athaŵa ndi kuti iye adzalangidwa mowopsa, wosunga ndendeyo anali pafupi kudzipha pamene Paulo anamuuza kuti onse analimo. Paulo ndi Sila “anamuuza iye mawu a Ambuye, pamodzi ndi onse a pabanja pake.” Wosunga ndendeyo ndi banja lake anali Akunja amene sanadziŵe za Malemba Oyera. Komabe, pausiku umenewo, anakhala okhulupirira. Ndipotu, ‘anabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pake.’ Mikhalidwe imeneyo inali yapadera, koma atsopano anaphunzitsidwa zoyambirira za choonadi ndipo anaphunzira zinthu zina pamisonkhano ya mpingo. Kuyenera kukhala kotheka kuchita zofanana ndi zimenezo lerolino.
Zotuta Zichulukadi!
14. Kodi nchifukwa ninji pali kufunika kwa kuchititsa maphunziro a Baibulo ochuluka kwambiri opita patsogolo panthaŵi yofupikirapo?
14 Zingakhale bwino ngati Mboni za Yehova zingamachititse maphunziro a Baibulo ochuluka opita patsogolo kwambiri panthaŵi yaifupi chabe. Zimenezi zikufunika kwenikweni. Mwachitsanzo, m’maiko a ku Eastern Europe, anthu amaikidwa pampambo woyembekezera wa maphunziro a Baibulo. Ndi mmenenso zilili kumaiko ena. M’tauni ina ku Dominican Republic, Mboni zisanu zinali ndi mapempho ambiri kwakuti sizinakhoze kuchititsa maphunziro onse. Kodi zinachita chiyani? Zinalimbikitsa okondwerera kumafika pamisonkhano ku Nyumba ya Ufumu ndi kulembetsa maina awo pampambo woyembekezera wa maphunziro a Baibulo. Ndi mmenenso zinthu zilili kumadera ambiri padziko lonse lapansi.
15, 16. Kodi nchiyani chimene chaperekedwa kuti chidziŵitso chonena za Mulungu chifalitsidwe mofulumira kwambiri, ndipo ndi zinthu zina zotani zimene zikudziŵika pankhaniyi?
15 Magawo aakulu—minda yaikulu ya zotuta—akutsegukira anthu a Mulungu. Ngakhale kuti Yehova, “Mwini Zotuta,” akutumiza antchito ochuluka, pakali ntchito yochuluka yofuna kuchita. (Mateyu 9:37, 38) Chifukwa chake, kuti afalitse chidziŵitso chonena za Mulungu mofulumira kwambiri, “kapolo wokhulupirika” wapereka kanthu kena kamene mwachidule kamapereka chidziŵitso cholunjika kuti ophunzira Baibulo azipita patsogolo paphunziro lililonse. Ndiko chofalitsa chatsopano chimene chingamalizidwe mofulumira pamaphunziro a Baibulo apanyumba—mwinamwake pamiyezi yoŵerengeka chabe. Ndipo chinganyamulike mosavuta m’chola chathu, m’chikwama chathu, kapena ngakhale m’thumba! Anthu zikwi mazana ambiri amene anasonkhana pa Msonkhano Wachigawo wa “Atamandi Achimwemwe” wa Mboni za Yehova anakondwa kulandira buku latsopano limeneli la masamba 192 lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.
16 Alembi a m’maiko osiyanasiyana anakonza nkhani zimene zinaikidwa pamodzi kupanga buku la Chidziŵitso. Motero, liyenera kukhala lokomera mitundu yonse. Koma kodi buku latsopano limeneli lidzatenga nthaŵi yaitali kuti lituluke m’zinenero zina za anthu kuzungulira dziko? Iyayi, chifukwa chakuti buku la masamba 192 likhoza kutembenuzidwa mofulumira kuposa mabuku aakulu. Pofika October 1995, Komiti ya Kulemba ya Bungwe Lolamulira inali itavomereza kutembenuzidwa kwa buku limeneli m’zinenero zoposa 130 kuchoka m’Chingelezi.
17. Kodi ndi zinthu ziti zimene ziyenera kupeputsa zinthu pophunzira buku la Chidziŵitso?
17 Mfundo zachindunji m’mutu uliwonse wa buku la Chidziŵitso ziyenera kuchititsa ophunzira kupita patsogolo mwauzimu mofulumira. Bukulo limapereka choonadi cha Malemba m’njira yolimbikitsa. Silimalongosola kwambiri za ziphunzitso zonyenga. Kumveka bwino kwa chinenero ndiponso kalongosoledwe kake ka nkhani kotsatirika bwino ziyenera kulichititsa kukhala losavuta kugwiritsira ntchito pochititsa maphunziro a Baibulo ndi kuthandiza anthu kupeza chidziŵitso chonena za Mulungu. Kuwonjezera pa malemba ogwidwa mawu, pali malemba ena a Baibulo osonyezedwa amene wophunzira angaŵerenge pokonzekera makambitsirano. Ameneŵa angaŵerengedwe mkati mwa phunziro pamene nthaŵi ilola, komabe sikoyenera kuloŵetsamo nkhani zina zosiyana zimene zingaphimbe mfundo zazikulu. M’malo mwake, aja ochititsa maphunziro a Baibulo ayenera kuyesa kuzindikira ndi kufotokoza kwa wophunzirayo zimene buku likusonyeza m’mutu uliwonse. Zimenezi zikutanthauza kuti mphunzitsi ayenera choyamba kuphunzira bukuli mosamalitsa kuti mfundo zazikulu zikhale m’maganizo mwake.
18. Kodi ndi malingaliro otani amene aperekedwa ponena za kuphunzira buku la Chidziŵitso?
18 Kodi ndi motani mmene buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha lingafulumizire ntchito yopanga ophunzira? Buku limeneli la masamba 192 lingaphunziridwe m’nthaŵi yofupikirapo, ndipo mwa kuliphunzira, aja “ofuna moyo wosatha” ayenera kukhala okhoza kudziŵa zambiri zowatheketsa kudzipatulira kwa Yehova ndi kubatizidwa. (Machitidwe 13:48, NW) Chotero tiyeni tigwiritsire ntchito bwino buku la Chidziŵitso mu utumiki. Ngati wophunzira Baibulo wafika patali kuphunzira buku lina, kungakhale bwino kulimaliza. Koma ngati akali kuchiyambi, ndi bwino kuti ophunzira Baibulo asinthe nayambe buku la Chidziŵitso. Buku limeneli latsopano litamalizidwa, phunzirolo siliyenera kupitiriza m’buku lachiŵiri ndi wophunzira mmodzimodziyo. Aja olandira choonadi adzapeza chidziŵitso chokwana mwa kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova limodzi ndi kuŵerenga Baibulo ndi zofalitsa zina zachikristu paokha.—2 Yohane 1.
19. Musanayambe kuchititsa maphunziro a Baibulo m’buku la Chidziŵitso, kodi nchifukwa ninji kungakhale kothandiza kupenda masamba 175-218 a Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu?
19 Buku la Chidziŵitso linalembedwa ndi cholinga cha kuthandiza munthu kuyankha mafunso onse amene akulu amakambitsirana ndi ofalitsa osabatizidwa ofuna kubatizidwa kukhala Mboni za Yehova. Chotero, musanasinthe kuti muyambe kuphunzira buku latsopanoli ndi maphunziro anu a Baibulo, ndi bwino kupatula maola angapo ndi kupenda mafunso a pamasamba 175 mpaka 218 a buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu.a Zimenezi zidzakuthandizani kugogomezera mayankho a mafunso ameneŵo pamaphunziro a Baibulo m’buku la Chidziŵitso.
20. Kodi mwakonzekera kuchita chiyani ndi buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha?
20 Anthu kulikonse ayenera kumva uthenga wabwino umenewo. Inde, anthu afunikira chidziŵitso chonena za Mulungu, ndipo Yehova ali ndi Mboni zake zochidziŵikitsa. Tsopano tili ndi buku latsopano limene Atate wathu wakumwamba wachikondi watipatsa kupyolera mwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Kodi mudzaligwiritsira ntchito kuphunzitsa choonadi ndi kulemekezera dzina loyera la Yehova? Yehova adzakudalitsani zedi pamene mukuyesayesa mwanjira iliyonse kugaŵira ambiri chidziŵitso chotsogolera ku moyo wosatha.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi mungaufotokoze motani mtima wophiphiritsira?
◻ Kodi chidziŵitso chonena za Mulungu nchiyani?
◻ Kodi nchifukwa ninji anthu afunikira chidziŵitso chonena za Mulungu?
◻ Kodi ndi buku liti latsopano lomwe lilipo, ndipo mwakonzekera kuligwiritsira ntchito motani?
[Chithunzi patsamba 10]
Pali zifukwa zambiri zimene mabiliyoni apadziko lapansi afunikira chidziŵitso chonena za Mulungu