Bokosi la Mafunso
◼ Tsopano pamene tili ndi buku lakuti Knowledge That Leads to Everlasting Life, kodi phunziro la Baibulo lapanyumba liyenera kuchititsidwa kwautali wotani?
Utumiki Wathu Waufumu wa September 1993 unati kuli bwino kuti phunziro la Baibulo lapanyumba lipitirize ndi okondwerera achatsopano mpaka mabuku aŵiri ataphunziridwa. Tsopano pamene tili ndi buku la Knowledge, pakuoneka kuti pali bwino kusintha njira imeneyi, monga momwe Nsanja ya Olonda ya January 15, 1996 ikusonyezera pamasamba 13 ndi 14.
Buku la Knowledge lalinganizidwira kuthandiza awo “ofuna moyo wosatha” kuti aphunzire zimene afunika kudziŵa kuti adzipatulire kwa Yehova ndi kubatizidwa. (Mac. 13:48, NW) Chotero, pambuyo pa kumaliza chofalitsa chatsopano chimenechi, sikuli koyenera kuphunzira buku lachiŵiri ndi wophunzira mmodzimodziyo. Pamene ophunzira Baibulo anu ayamba kulandira choonadi, mungawathandizire pang’ono ndi pang’ono kuwonjezera chidziŵitso chawo mwa kufika pamisonkhano ya Mboni za Yehova limodzinso ndi mwa kuŵerenga Baibulo ndi zofalitsa zosiyanasiyana zachikristu.
Ngati mumadziŵa bwino mafunso a pamasamba 175 mpaka 218 a m’buku lakuti Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, zimenezi zingakhale zothandiza. Ngakhale kuti simuyenera kumasonya ku mafunso ameneŵa kapena kuwapenda ndi wophunzira Baibulo, kungakhale bwino kugogomezera nsonga za mu Knowledge zimene zidzakhozetsa wophunzira kusonyeza kuti akuzindikira bwino choonadi choyambirira cha Baibulo pamene akulu apenda mafunso ndi ofuna kubatizidwa.
Palibe kufunika kwa kuwonjezera chidziŵitso pa chimene chili m’buku la Knowledge, kuloŵetsamo nsonga zakunja kapena mfundo zowonjezerapo pochirikiza ziphunzitso za Baibulo kapena kutsutsa ziphunzitso zonyenga. Zimenezi zingangotalikitsa nthaŵi ya phunziro. M’malo mwake, tikukhulupirira kuti bukuli lidzamalizidwa msanga, mwinamwake pafupifupi m’miyezi isanu ndi umodzi. Zimenezi zikusonyeza kuti tifunikira kuiphunzira nkhaniyo mosamalitsa pasadakhale kotero kuti tiilongosole bwino ndiponso mwachidule. Mofananamo wophunzira ayenera kulimbikitsidwa kuphunzira pasadakhale, kuŵerenga malemba osonyezedwa, ndi kufunitsitsa kuzindikira bwino zimene bukuli likuphunzitsa m’mutu uliwonse.
Nsanja ya Olonda yagogomezera kufunika kwa Mboni za Yehova kuchititsa maphunziro a Baibulo opita patsogolo ochuluka panthaŵi yaifupi. (Onani Yesaya 60:22.) Kugwiritsira ntchito bwino buku la Knowledge kungathandize atsopano kukhala ndi chidziŵitso chimene chimatsogolera ku moyo wosatha ndi kuchita mogwirizana nacho.—Yoh. 17:3.