Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Yesu—“Mkate Wowona Wochokera Kumwamba”
TSIKU lakhaladi la zochitika zambiri. Yesu mozizwitsa wadyetsa zikwi ndipo kenaka wathawa kuyesera kwa anthuwo kwa kumpanga iye mfumu. Usiku umenewo iye akuwoloka pansi pa nyanja ya mafunde ya Galileya; kupulumutsa Petro, yemwe anayamba kumira pamene anayenda pa madzi okankhidwa ndi mphepo; ndipo akhalitsa bata mafunde kupulumutsa ophunzira ake kuchokera ku kumira m’ngalawa.
Tsiku lotsatira anthu amene Yesu anawadyetsa mozizwitsa kumpoto chakum’mawa kwa nyanja ya Galileya ampeza iye kufupi ndi Kapernao. Kuwadzudzula iwo, Yesu anena kuti iwo abwera kufunafuna iye chifukwa akuyembekezera chakudya china chaulere. Iye akukakamiza iwo kugwira ntchito, osati chifukwa cha chakudya chimene chitaika, koma chifukwa cha chakudya chimene chitsalira ku moyo wosatha. Chotero anthuwo akufunsa: “Tichite chiyani, kuti tichite ntchito za Mulungu?”
Yesu akutchula, kokha ntchito imodzi ya mtengo wapamwamba. “Ntchito ya Mulungu ndi iyi,” iye akulongosola, “mukhulupirire iye amene iyeyo anamtuma.”
Anthuwo, ngakhale kuli tero, sakhulupirira Yesu, mosasamala kanthu za zozizwitsa zonse zimene iye wachita. Tsiku limodzi lapitalo, iye mozizwitsa anadyetsa amuna 5,000, limodzinso ndi akazi ndi ana, ndipo ngakhale tsopano, mosakhulupirira, iwo akufunsa: “Ndipo muchita chizindikiro chanji, kuti tiwone ndi kukhulupirira inu? Muchita chiyani? Atate wathu anadya mana m’chipululu; monga kwalembedwa, ‘mkate wochokera m’mwamba anawapatsa iwo kudya.’”
M’kuyankha funso lawo kaamba ka chizindikiro, Yesu akumveketsa Magwero a zopereka zozizwitsa, akunena kuti: “Si Mose amene anakupatsani inu mkate wakumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate wowona wa kumwamba. Pakuti mkate wa Mulungu ndiwo wakutsika kuchokera kumwamba ndi kupatsa moyo padziko lapansi.”
“Ambuye,” anthuwo akutero, “tipatseni ife mkate umenewu nthaŵi zonse.”
“Ine ndine mkate wa moyo,” Yesu akulongosola. “Iye amene adza kwa ine sadzamva njala, ndi amene akhulupirira ine sadzamva ludzu nthaŵi zonse. Koma ndinati kwa inu, Kuti mungakhale mwandiwona, simukhulupirira. Chinthu chonse chimene anandipatsa ine Atate chidzadza kwa inu; ndipo wakudza kwa ine sindidzamutaya iye kunja. Pakuti ndinatsika kumwamba, koma sikuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha iye amene anandituma ine. Koma chifuniro cha iye amene anandituma ine ndi ichi, kuti za ichi chonse iye anandipatsa ine ndisatayeko kanthu, koma ndichiukitse tsiku lomaliza. Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wa kuyang’ana Mwana ndi kukhulupirira iye, akhale nawo moyo wosatha.”
Pa ichi Ayuda anayamba kung’ung’udza za Yesu chifukwa iye anati, “Ine ndine mkate wotsika kumwamba.” Iwo sakuwona mwa iye chirichonse choposa kokha mwana wa makolo aumunthu ndipo chotero akutsutsa m’mkhalidwe umodzimodzi monga mmene anachitira anthu a ku Nazarete: “Si Yesu uyu mwana wa Yosefe, atate wake ndi amake tiwadziŵa? Anena bwanji tsopano kuti, ‘Ndinatsika kumwamba’”?
“Musang’ung’udze wina ndi mnzake,” Yesu anayankha. “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa ine koma ngati Atate wondituma ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza. Chalembedwa mwa aneneri, ‘Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi [Yehova, NW].’ Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine. Sikuti munthu wina wawona Atate, koma Iye amene ali wochokera kwa Mulungu, ameneyo wawona Atate. Indetu indetu ndinena ndi inu, iye wokhulupirira ali nawo mo-yo wosatha.”
Kupitiriza, Yesu akubwereza: “Ine ndine mkate wamoyo. Makolo anu anadya m’chipululu, ndipo adamwalira. Mkate wotsika kumwamba ndi uwu, kuti munthu akadyeko ndi kusamwalira. Mkate wamoyo wotsika kumwamba ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umenewu, adzakhala ndi moyo kosatha.” Inde, mwakukhulupirira Yesu, mmodzi amene Mulungu anamutumiza, anthu angakhale ndi moyo wosatha. Osati mana, kapena mtundu wina uliwonse wa mkate woterowo, ungapereke chimenecho!
Kukambitsirana konena za mkate wochokera kumwamba mwachiwonekere kunayambika mwamsanga pamene anthu anamupeza Yesu pafupi ndi Kapernao. Koma kunapitiriza, kufika pachimake penipeni pambuyo pake pamene Yesu anali kuphunzitsa m’sunagoge mu Kapernao. Yohane 6:26-51, 59; Masalmo 78:24; Yesaya 54:13; Mateyu 13:55-57.
◆ Ndi zochitika zotani zimene zinachitika kuchiyambi kwa kukambitsirana kwa Yesu ponena za mkate wochokera kumwamba?
◆ M’chiyang’aniro cha zimene Yesu wangochita, nchifukwa ninji chifunsiro kaamba ka chizindikiro chiri chosayenerera?
◆ Ndi chifukwa ninji Ayuda akung’ung’udza za kudzinenera kwa Yesu kuti iye ali mkate wowona wochokera kumwamba?
◆ Ndi kuti kumene kukambitsirana ponena za mkate wochokera kumwamba kunachitikira?