Tidzayenda M’dzina la Yehova Mulungu Wathu
“Ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthawi yomka muyaya.”—MIKA 4:5.
1. Kodi anthu anali ndi makhalidwe otani m’masiku a Nowa, nanga Nowa anasiyana nawo motani?
MUNTHU woyamba amene Baibulo limanena kuti anayenda ndi Mulungu ndi Enoke. Wachiwiri ndi Nowa. Nkhani yake imati: “Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m’mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu.” (Genesis 6:9) Pofika m’masiku a Nowa, anthu anali atapatuka pa kupembedza koyera. Zinthu zinafika poipa kwambiri chifukwa cha angelo osakhulupirika amene anachita zachilendo pokwatira akazi ndi kubereka ana omwe ankatchedwa Anefili. Anefili anali “anthu amphamvu,” “anthu omveka” a masiku amenewo. Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti dziko lapansi linadzaza ndi chiwawa. (Genesis 6:2, 4, 11) Ngakhale ndi choncho, Nowa anali wangwiro m’mayendedwe ake ndipo anali “mlaliki wa chilungamo.” (2 Petro 2:5) Mulungu atamulamula kuti amange chingalawa choti anthu apulumukiremo, mosawiringula Nowa anachita “monga mwa zonse anamulamulira iye Mulungu, momwemo anachita.” (Genesis 6:22) Ndithudi, Nowa anayenda ndi Mulungu.
2, 3. Kodi n’chitsanzo chabwino chotani chimene Nowa akutipatsa masiku ano?
2 Paulo anaphatikiza Nowa pa mndandanda wa mboni zokhulupirika pamene anati: “Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.” (Ahebri 11:7) Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri. Chifukwa chakuti anali kutsimikiza ndi mtima wonse kuti mawu a Yehova adzachitika, Nowa anagwiritsa ntchito nthawi yake, mphamvu zake, ndi chuma chake kuti akwaniritse zimene Mulungu anamulamula. Mofananamo, anthu ambiri masiku ano amakana ntchito kaya maudindo enaake m’dzikoli n’cholinga choti agwiritse ntchito nthawi yawo, mphamvu zawo, ndi chuma chawo pomvera malamulo a Yehova. Iwo amasonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro kwambiri, ndipo chikhulupiriro chawocho chidzawapulumutsa komanso chidzapulumutsa ena.—Luka 16:9; 1 Timoteo 4:16.
3 Kukhala ndi chikhulupiriro kuyenera kuti kunali kovuta kwa Nowa ndi banja lake monganso mmene kunalili kovuta kwa Enoke, yemwe anali agogo awo a bambo ake a Nowa. Mungakumbukire kuti m’nkhani yapitayo tinakambirana za Enoke ameneyu. Mofanana ndi masiku a Enoke, opembedza oona analipo ochepa chabe m’masiku a Nowa, anthu eyiti okha ndi amene anali okhulupirika moti anapulumuka Chigumula. Nowa analalikira za chilungamo kwa anthu okonda chiwawa ndi chiwerewere. Ndiponso, iye ndi banja lake anali kumanga chingalawa chachikulu cha matabwa pokonzekera madzi amene anali kudzasefukira padziko lonse, ngakhale kuti panalibe amene anayamba waonapo madzi atasefukira moteromo. Anthu owaona anali kuona kuti iwo akuchita zachilendo kwambiri.
4. Kodi ndi cholakwa chiti cha anthu a m’masiku a Nowa chimene Yesu anatchula?
4 N’zochititsa chidwi kuti pamene Yesu anatchula za masiku a Nowa, sananene za chiwawa, chipembedzo chonyenga, kapena chiwerewere zomwe zinkachitika m’masikuwo, ngakhale kuti amenewa anali machimo akuluakulu. Cholakwa chimene Yesu anatchula chinali chakuti anthuwo anakana kumvera chenjezo limene anapatsidwa. Iye anati anthuwo anali “kudya ndi kumwa, anali kukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa.” Kodi chinalakwika n’chiyani ndi kudya, kumwa, kukwatira, ndi kukwatiwa? Iwo anali kukhala ndi moyo umene eni akewo ankati ndimo mmene anthu ayenera kukhalira nthawi zonse. Komatu kunali kubwera chigumula, ndipo Nowa anali kulalikira za chilungamo. Mawu akewo ndiponso khalidwe lake zinayenera kuwachenjeza anthuwo. Komabe iwo “sanadziwa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza,” ndipo “chinapululutsa iwo onse.”—Mateyu 24:38, 39.
5. Kodi Nowa ndi banja lake anafunika kukhala ndi makhalidwe ati?
5 Tikaganizira zimene zinachitika masiku amenewo, timaona kuti n’chanzeru kukhala ndi moyo umene Nowa anali nawo. Komabe, masiku amenewo Chigumula chisanafike, munthu anafunika kulimba mtima kuti akhale wosiyana ndi anthu ena onse. Nowa ndi banja lake anafunika chikhulupiriro cholimba kuti amange chingalawa chachikulu ndi kuikamo nyama zosiyanasiyana. Kodi ena mwa anthu okhulupirika ochepawo nthawi zina anali kulakalaka kuti asachite kukhala osiyana kwambiri ndi ena onse, koma azingokhala moyo umene enawo ankati ndimo mmene anthu ayenera kukhalira nthawi zonse? Ngakhale ngati maganizo amenewa anali kuwabwerera panthawi zina, iwo sanafooke n’kukhala osakhulupirika. Patapita zaka zambirimbiri, zambiri kuposa zimene wina aliyense wa ife afunika kupirira m’dongosolo lino la zinthu, chikhulupiriro cha Nowa chinamuthandiza kupulumuka Chigumula. Komabe, Yehova anaweruza onse amene anali kukhala ndi moyo umene ankati ndimo mmene anthu ayenera kukhalira nthawi zonse ndipo sanazindikire kuopsa kwa nthawi imene anali kukhalamo.
Anthu Avutikanso ndi Chiwawa
6. Chigumula chitachitika, kodi n’chiyani chimene chinali chidakalipo?
6 Madzi a Chigumula ataphwera, anthu anayambiranso mwatsopano kukhala ndi moyo padziko lapansi. Komabe anthuwo anali adakali opanda ungwiro, ndipo “ndingaliro ya mtima wa munthu” inali idakali “yoipa kuyambira pa unyamata wake.” (Genesis 8:21) Ndiponso, ngakhale kuti ziwanda sizikanatha kuvalanso matupi a anthu, izo zinali kuvutitsabe kwambiri. Dziko la anthu osapembedza silinachedwe kusonyeza kuti linali ‘kugona mwa woipayo,’ ndipo monganso mmene zilili masiku ano, opembedza oona anafunika kulimbana ndi “machenjerero a Mdyerekezi.”—1 Yohane 5:19; Aefeso 6:11, 12.
7. Kodi chiwawa chinawonjezeka motani pambuyo pa Chigumula?
7 Mwina kuyambira m’masiku a Nimrode, dziko lapansi linadzazanso chiwawa pakati pa anthu omwe analipo pambuyo pa Chigumula. Chiwawa chakhala chikuwonjezeka m’kupita kwa nthawi chifukwa cha kuchuluka kwa anthu ndiponso kupita patsogolo kwa ntchito za sayansi. Poyamba anthu anali kugwiritsa ntchito malupanga, mikondo, uta ndi mivi, ndiponso magaleta. Chaposachedwapa kunabwera mfuti za gogodera, limodzi ndi mfuti zikuluzikulu zochita kunyamulira pa ngolo. Kenako kunabwera mfuti zing’onozing’ono zamakono ndi mizinga yodabwitsa yomwe inatuluka kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900. Nkhondo yoyamba ya padziko lonse inabweretsa zida zoopsa kwambiri, monga ndege, akasinja, sitima zankhondo zam’madzi, ndi mpweya wa poizoni. Pankhondo imeneyo, zida zimenezi zinapha anthu mamiliyoni ambiri. Kodi n’zodabwitsa kuti zinachitika choncho? Ayi sizodabwitsa.
8. Kodi lemba la Chivumbulutso 6:1-4 lakwaniritsidwa motani?
8 M’chaka cha 1914, Yesu anaikidwa pa mpando wachifumu monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu, ndipo “tsiku la Ambuye” linayamba. (Chivumbulutso 1:10) M’masomphenya amene analembedwa m’buku la Chivumbulutso, Yesu monga Mfumu anaoneka atakwera pa kavalo woyera akuyenda mosonyeza kupambana. Enanso okwera pa akavalo anali kum’tsatira, ndipo aliyense anaimira tsoka la mtundu winawake lodzagwera anthu. Mmodzi wa iwo anakwera kavalo wofiira, ndipo iye anapatsidwa mphamvu “yakuchotsa mtendere pa dziko ndi kuti aphane; ndipo anam’patsa iye lupanga lalikulu.” (Chivumbulutso 6:1-4) Kavalo ameneyo ndi wom’kwera wake amaimira nkhondo, ndipo lupanga lalikulu limaimira kusakaza kosaneneka, komwe sikunachitikepo moteromo n’kalelonse, kwa nkhondo zamakono ndi zida zake zamphamvu. Masiku ano zida zimenezo zikuphatikizapo mabomba a nyukiliya, omwe bomba limodzi lokha likhoza kuwononga anthu zikwizikwi; maroketi otha kunyamula mabombawo n’kukawaponyera kutali, mtunda wa makilomita ambirimbiri; ndiponso kugwiritsa ntchito mankhwala oopsa ndi kufalitsa tizirombo topereka matenda zomwe zimapha anthu ambiri.
Timalabadira Machenjezo a Yehova
9. Kodi dziko la masiku ano likufanana motani ndi limene linalipo Chigumula chisanachitike?
9 M’masiku a Nowa, Yehova anawononga anthu chifukwa cha chiwawa choopsa chimene anthu oipa mothandizidwa ndi Anefili anali kuchita. Nanga bwanji masiku ano? Kodi chiwawa ndi chochepa m’dzikoli kusiyana ndi mmene chinalili masiku a Nowa? Palibe kusiyana kulikonse. Ndiponso, mofanana ndi masiku a Nowa, masiku ano anthu akuchita zochita zawo za tsiku ndi tsiku, akuyesa kukhala ndi moyo umene amati ndimo mmene anthu ayenera kukhalira nthawi zonse, ndipo akukana kulabadira machenjezo amene akuperekedwa. (Luka 17:26, 27) Ndiye kodi pali chifukwa chilichonse chokayikirira kuti Yehova adzawononganso anthu? Palibe.
10. (a) Kodi ndi chenjezo liti limene ulosi wa m’Baibulo umalibwerezabwereza? (b) Kodi chinthu chanzeru chimene tingachite masiku ano n’chiyani?
10 Zaka mazana angapo Chigumula chisanachitike, Enoke analosera kuwonongedwa kwa anthu kumene kudzachitika m’masiku athu. (Yuda 14, 15) Nayenso Yesu analankhula za “masauko aakulu” amene akubwera. (Mateyu 24:21) Aneneri enanso anachenjeza za nthawi imeneyo. (Ezekieli 38:18-23; Danieli 12:1; Yoweli 2:31, 32) Ndipo buku la Chivumbulutso limafotokoza mopereka chithunzi chooneka bwino cha chiwonongeko chomaliza chimenecho. (Chivumbulutso 19:11-21) Tonse, payekhapayekha timatsanzira Nowa, ndipo ndife achangu polalikira za chilungamo. Timamvera machenjezo a Yehova ndipo mwachikondi timathandiza anansi athu kuti nawonso achite zomwezo. Motero timayenda ndi Mulungu mofanana ndi Nowa. Ndithudi, m’pofunika kwambiri kuti aliyense amene akufuna moyo apitirize kuyenda ndi Mulungu. Kodi zimenezi tingazichite bwanji popeza kuti tsiku lililonse timakumana ndi zovuta? Tifunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba pa kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Mulungu.—Ahebri 11:6.
Pitirizani Kuyenda ndi Mulungu M’nthawi Zovuta
11. Kodi Akristu a m’nthawi ya atumwi timawatsanzira motani?
11 Kalelo m’nthawi ya atumwi, Akristu odzozedwa anali kunenedwa kuti ndi otsatira “Njirayo.” (Machitidwe 9:2) Moyo wawo wonse unali kusonyeza chikhulupiriro mwa Yehova ndi Yesu Kristu. Iwo anayenda m’njira imene Mbuye wawo anayendamo. Akristu okhulupirika lerolino amachita chimodzimodzi.
12. Kodi chinachitika n’chiyani Yesu atadyetsa mozizwitsa khamu la anthu?
12 Tikuona bwino kufunika kokhala ndi chikhulupiriro kuchokera m’zimene zinachitika pamene Yesu anali kuchita utumiki wake. Nthawi ina, Yesu anadyetsa mozizwitsa khamu la amuna pafupifupi 5,000. Anthu anadabwa nazo ndiponso anasangalala. Koma taonani zimene zinachitika kenako. Nkhaniyo imati: “Anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m’dziko lapansi. Pamenepo Yesu, pozindikira kuti ali kufuna kudza kudzamugwira Iye, kuti amulonge ufumu, anachokanso kumka kuphiri payekha.” (Yohane 6:10-15) Usiku umenewo Yesu anapita ku dera lina. Mwachionekere ambiri anakhumudwa poona kuti Yesu wakana ufumu. Zinali zosadabwitsa kuti iwo akhumudwe chifukwa iye anasonyeza kuti anali wanzeru woyenera kukhala mfumu ndiponso anasonyeza kuti anali ndi mphamvu zopatsa anthu zinthu zofunika pamoyo wawo. Komabe, nthawi ya Yehova yoti Yesuyo alamulire monga Mfumu inali isanakwane. Ndiponso, Ufumu wa Yesu unali kudzakhala wakumwamba, osati wapadziko lapansi.
13, 14. Kodi anthu ambiri anasonyeza kuti anali ndi maganizo otani, nanga chikhulupiriro chawo chinayesedwa motani?
13 Ngakhale kuti zinali choncho, makamuwo analondola Yesu osamusiya ndipo anamupeza “tsidya lina la nyanja,” malinga n’kunena kwa Yohane. N’chifukwa chiyani anamulondola oti anawazemba pamene anafuna kumulonga ufumu? Ambiri anaonetsa kuti anali okonda zakuthupi, chifukwa analankhula motsindika kwambiri za zakudya zimene Yehova anapatsa makolo awo m’chipululu m’masiku a Mose. Zimene iwo anali kutanthauza zinali zakuti Yesu anayenera kupitiriza kuwapatsa chakudya. Yesu pozindikira maganizo awo olakwikawo, anayamba kuwaphunzitsa choonadi chauzimu chimene chikanawathandiza kusintha kaganizidwe kawo. (Yohane 6:17, 24, 25, 30, 31, 35-40) Ena mwa anthuwo anang’ung’udza iye atawauza zimenezi, makamaka pamene ananena fanizo ili: “Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha. Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nawo moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.”—Yohane 6:53, 54.
14 Nthawi zambiri mafanizo a Yesu anali kuchititsa anthu kusonyeza kuti akufunadi kuyenda ndi Mulungu kapena ayi. Fanizo ilinso linachita chimodzimodzi. Anthu anaipidwa nalo kwambiri. Nkhaniyi imati: “Ambiri a akuphunzira ake, pakumva izi, anati, Mawu awa ndi osautsa; akhoza kumva awa ndani?” Yesu anafotokoza kuti anthuwo aziganizira zinthu zauzimu zimene mawu akewo anali kutanthauza. Iye anati: “Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mawu amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.” Komabe ambiri sanamvere zimenezo, ndipo nkhaniyo imati: “Pa ichi ambiri a akuphunzira ake anabwerera m’mbuyo, ndipo sanayendayendanso ndi Iye.”—Yohane 6:60, 63, 66.
15. Kodi ena mwa otsatira a Yesu anali ndi maganizo abwino ati?
15 Komabe sikuti ndi ophunzira onse a Yesu amene anachita zimenezo. N’zoona kuti ophunzira okhulupirikawo sanamvetse tanthauzo la zonse zimene Yesu ananena. Komatu iwo anamudalirabe kwambiri. Petro, mmodzi wa ophunzira okhulupirikawo, anafotokoza maganizo a ophunzira ena onse amene anakhalabe ndi Yesu mwa kunena kuti: “Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha.” (Yohane 6:68) Amenewa analitu maganizo abwino kwambiri kukhala nawo, ndipo ndi chitsanzo chabwino zedi kwa ife.
16. Kodi tingayesedwe motani, nanga tiyenera kukhala ndi maganizo abwino ati?
16 Ifenso masiku ano tikhoza kuyesedwa monga mmene anachitira ophunzira oyambirira amenewo. Ifeyo tikhoza kukhumudwa poona kuti malonjezo a Yehova sakukwaniritsidwa mofulumira monga mmene ifeyo tikufunira patokha. Tingaone kuti mmene mabuku athu amafotokozera Malemba n’zovuta kumva. Zochita za Mkristu mnzathu zikhozanso kutikhumudwitsa. Kodi m’poyenera kusiya kuyenda ndi Mulungu pa zifukwa zimenezi, kapena pa zifukwa zina zangati zomwezi? Ndithu si poyenera. Ophunzira amene anasiya kuyenda ndi Yesu anaonetsa kuti maganizo awo anali pa zinthu zakuthupi. Tipewe kuchita zofanana ndi zimenezo.
“Si Ndife a Iwo Akubwerera”
17. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kupitiriza kuyenda ndi Mulungu?
17 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu.” (2 Timoteo 3:16) Kudzera m’Baibulo, Yehova amatiuza momveka bwino kuti: “Njira ndi iyi, yendani inu mmenemo.” (Yesaya 30:21) Kumvera Mawu a Mulungu kumatithandiza ‘kupenya bwino umo tiyendera.’ (Aefeso 5:15) Kuphunzira Baibulo ndi kusinkhasinkha zimene timaphunzirazo kumatithandiza kupitiriza ‘kuyenda m’choonadi.’ (3 Yohane 3) Ndithudi, monga mmene ananenera Yesu, “wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse.” Malangizo auzimu ndiwo malangizo okhawo odalirika amene angatithandize poyenda, ndipo malangizowa amaperekedwa kudzera m’Mawu a Yehova, mzimu wake, ndi gulu lake.
18. (a) Kodi mopanda nzeru ena amachita chiyani? (b) Kodi timakulitsa chikhulupiriro chotani?
18 Masiku ano, anthu amene amakhumudwa chifukwa cha kaganizidwe kawo kaumunthu kapena chifukwa choti zimene ankayembekezera sizinachitike, kawirikawiri amayamba kuchita zonse zimene angathe kuchita m’dzikoli. Chifukwa chakuti sakuona kufunika kokhala achangu, iwo saonanso chifukwa ‘chodikirira,’ ndipo amasankha kukwaniritsa zolinga zawozawo m’malo moika zinthu za Ufumu patsogolo. (Mateyu 24:42) Kuyenda mwa njira imeneyi ndi chinthu chopanda nzeru koposa zonse. Taonani mawu awa a mtumwi Paulo: “Ife si ndife a iwo akubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.” (Ahebri 10:39) Mofanana ndi Enoke ndi Nowa, tikukhala m’nthawi ya chipwirikiti, komabe mofanana ndi iwowo, tili ndi mwayi woyenda ndi Mulungu. Mwa kuchita zimenezi, tili ndi chiyembekezo chotsimikizika chakuti tidzaona malonjezo a Yehova akukwaniritsidwa, kuipa konse kukuthetsedwa, ndipo dziko latsopano la chilungamo likukhazikitsidwa. Ichitu n’chiyembekezo chabwino kwambiri!
19. Kodi Mika anafotokoza motani mmene opembedza oona amakhalira moyo wawo?
19 Mneneri wouziridwa Mika ananena za mitundu ya m’dzikoli kuti “idzayenda, wonse m’dzina la mulungu wake.” Ndiyeno ananena za iye mwini ndi opembedza ena okhulupirika kuti: “Ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthawi yomka muyaya.” (Mika 4:5) Ngati muli otsimikiza mtima monga mmene analili Mika, musasiyane naye Yehova ngakhale pakhale chipwirikiti chotani m’nthawi inoyi. (Yakobo 4:8) Tiyeni tonse tizilakalaka ndi mtima wonse kuyenda ndi Yehova Mulungu wathu panopa ndiponso ku nthawi zonse, inde mpaka muyaya.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi masiku a Nowa akufanana bwanji ndi masiku ano?
• Kodi Nowa ndi banja lake anali kukhala ndi moyo wotani, nanga tingatsanzire motani chikhulupiriro chawo?
• Kodi ena mwa otsatira a Yesu anasonyeza maganizo olakwika otani?
• Kodi Akristu oona ndi otsimikiza mtima kuchita chiyani?
[Zithunzi patsamba 20]
Mofanana ndi masiku a Nowa, anthu masiku ano alowerera mu zochita zawo za tsiku ndi tsiku
[Chithunzi patsamba 21]
Ife amene timalalikira za Ufumu, “si ndife a iwo akubwerera”