“Zidziŵa Mawu Ake”
“YEHOVA ndiye mbusa wanga.” Ameneŵa ndi mawu oyamba a Salmo 23. Malemba amayerekezeranso Yehova Mulungu ndi mbusa wa mu ulosi wa Yesaya, umene umati: “Iye adzadyetsa zoŵeta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa ana a nkhosa pachapa pake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwino bwino zimene ziyamwitsa.”—Yesaya 40:11.
Mofananamo, Yesu Kristu akufaniziridwa ndi mbusa. Iye anati: “Ine ndine Mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.” (Yohane 10:11) Yesu ananena kuti “nkhosa zimva mawu [a mbusa]; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina awo, nazitsogolera kunja.” Iye anawonjezera kuti “nkhosa zimtsata [mbusa] chifukwa zidziŵa mawu ake. Koma mlendo sizidzamtsata, koma zidzamthaŵa; chifukwa sizidziŵa mawu a alendo.”—Yohane 10:2-5.
Onse aŵiri Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, achita mogwirizana ndi chithunzi chosonyezedwa m’malemba otchulidwawo. Iwo amachitira nkhosa zawo zophiphiritsira mwachifundo ndi mwachikondi. Monga chotulukapo, onga nkhosawo amadziona kukhala okondedwa, otetezereka, ndi ochinjirizidwa.
Unansi umenewu moyenerera wafaniziridwa ndi uja wa nkhosa zenizeni ndi mbusa wawo. Kalelo mu 1831, John Hartley analemba ponena za zimene anaona pa nkhani imeneyi. Iye anaona kuti mu Girisi kunali kwachizoloŵezi kwa abusa kupatsa maina nkhosa zawo. Ikaitanidwa ndi dzina, nkhosayo ikayankha liwu la mbusayo. Zaka pafupifupi 51 pambuyo pake, mu 1882, J. L. Porter anapereka ndemanga zofananazo. Iye anadzionera yekha abusa “akutchula . . . mawu ofuula apadera” amene nkhosazo zimawayankha mwa kutsatira momvera abusawo. Chaka chimodzimodzicho William M. Thomson analemba ponena za zoyesa zobwerezabwereza zimene zinatsimikizira kuti nkhosa zingaphunzitsidwe kutsatira mbusa wawo ndi kuzindikira mawu ake.
Kodi unansi wapadera umenewu pakati pa abusa ndi nkhosa zawo waonedwa ngakhale m’nthaŵi zaposachedwapa? Inde. M’kope la September 1993 la National Geographic, woyendayenda wa ku Australia Robyn Davidson analemba zotsatirazi ponena za mtundu wa wa abusa wa Rabari wa kumpoto koma chakumadzulo kwa India: “Mbusa aliyense ali ndi kaitanidwe kosiyana pang’ono, pa zochitika zosiyanasiyana. Pali maitanidwe a m’mawa a kutuluka, maitanidwe a kubweretsa nkhosa kudzamwa madzi, ndi ena otero. Munthu aliyense amadziŵa nkhosa zake momwemonso nkhosazo, ndipo gulu lake lankhosa lidzapatuka ku gulu lonse ndi kumtsata pambuyo mmaŵa.”
Mosakayikira, Yesu anaona zimene zafotokozedwa ndi apaulendo anayi ongotchulidwawo. Zimene iye mwiniyo anaona zinawonjezera kutsimikizirika kwa fanizo la kudziŵa liwu la mbusa kwa nkhosa. Kodi ndinu mmodzi wa nkhosa za Yesu? Kodi mumadziŵa mawu ake ndi kuwamva? Ngati muzindikira ndi kuvomereza ziphunzitso zake kukhala choonadi ndipo ngati mumvera malamulo ake ndi kutsatira chitsogozo chake m’kulambira Yehova, pamenepo mungaone kuŵeta kwachikondi ndi kokoma mtima kwa Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu.—Yohane 15:10.