Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Ntchito ya Chifundo mu Yudeya
MILUNGU ingapo kumayambiriro, mkati mwa Phwando la Kukonzetsanso mu Yerusalemu, Ayuda anayesera kupha Yesu. Chotero iye anapita kumpoto, mwachiwonekere kumalo osati kutali kuchokera ku Nyanja ya Galileya.
Posachedwapa, iye anali kupita kum’mwera kachiŵirinso kulinga ku Yerusalemu, akumalalikira m’njira m’midzi ya Pereya, boma la kum’mawa kwa Mtsinje wa Yordano. Iye wangotsiriza kunena fanizo lonena za mwini chuma ndi Lazaro. Tsopano iye akupitiriza kuphunzitsa ophunzira ake zinthu zimene anali ataphunzitsa poyambirira pamene anali mu Galileya.
Iye akunena, mwachitsanzo, kuti chidzakhala chabwinopo kaamba ka munthu “kukolowekedwa mwala wamphero m’khosi mwake ndi kuponyedwa iye m’nyanja” kuposa ndi iye kuchititsa mmodzi wa “ang’ono” a Mulungu kukhumudwa. Iye akugogomezeranso kufunika kwa kukhululukira, akumalongosola kuti: “Ndipo akakuchimwira [mbale] kasanu ndi kaŵiri pa tsiku lake, nakakutembenukira kasanu ndi kaŵiri ndi kunena, Ndalapa ine; uzimkhululukira.”
Pamene phunzira anafunsa kuti, “Mutiwonjezere chikhulupiriro,” Yesu akuyankha kuti: “Mukakhala nacho chikhulupiriro ngati kambewu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuwokedwe m’nyanja; ndipo ukadamvera inu.” Chotero ngakhale chikhulupiriro chaching’ono chingakwaniritse zinthu zazikulu.
Chotsatira, Yesu akulongosola mkhalidwe wowona ku moyo womwe umachitira fanizo maganizo oyenera a mtumiki wa Mulungu wamphamvuyonse. “Koma ndani mwa inu ali naye kapolo wolima, kapena woweta nkhosa,” Yesu akulingalira, “amene pobwera iye kuchokera kumunda adzanena kwa iye, Lowa tsopano, khala pansi kudya; wosanena naye makamaka, Undikonzere chakudya ine, nudzimangire, nunditumikire kufikira ndadya ndi kumwa; ndipo nditatha ine udzadya nudzamwa iwe? Kodi ayamika kapoloyo chifukwa anachita zolamulidwa? Chotero inunso mmene mutachita zonse anakulamulirani, nenani, Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita.” Chotero, atumiki a Mulungu sayenera konse kudzimva kuti akumuchitira Mulungu momukomera mwa kumtumikira iye. M’malomwake, iwo nthaŵi zonse ayenera kukumbukira mwaŵi umene ali nawo wa kumulambira iye monga ziŵalo zokhulupirika za mnyumba yake.
Mwachiwonekere chiri mwamsanga pambuyo popereka fanizo limeneli kuti mthenga akufika. Iye watumizidwa ndi Mariya ndi Malita, alongo a Lazaro, omwe amakhala mu Betaniya ku Yudeya. “Ambuye, onani, amene mumkonda adwala,” mthengayo akulongosola.
Yesu akuyankha kuti: “Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.” Pambuyo pa kukhala masiku aŵiri kumene iye ali, Yesu akunena kwa ophunzira ake kuti: “Tiyeni tipitenso ku Yudeya.” Ngakhale kuli tero, iwo akumukumbutsa iye kuti: “[Rabi, NW] Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo mumukanso komweko kodi?”
“Kodi sikuli maora khumi ndi aŵiri usana?” Yesu akufunsa mwa kuyankha. “Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, chifukwa apenya kuwunika kwa dziko lino lapansi. Koma ngati munthu ayenda usiku, akhumudwa, chifukwa mulibe kuwunikwa mwa iye.”
Chimene Yesu kwenikweni akutanthauza chiri chakuti “maora a usana,” kapena nthaŵi imene Mulungu waika kaamba ka utumiki wake wa pa dziko lapansi, sinathe kale, ndipo kufikira itatero, palibe angamuvulaze. Iye afunikira kugwiritsira ntchito mokwanira nthaŵi yaifupi ya “usana” yosiyidwa kaamba ka iye, chifukwa pambuyo pake padzabwera “usiku” pamene adani ake adzamupha iye.
Yesu akuwonjezera kuti: “Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.”
Mwachiwonekere akumaganiza kuti Lazaro akupumula m’tulo ndipo kuti chimenechi chiri chizindikiro chotsimikizirika kuti iye adzachira, ophunzirawo akuyankha kuti: “Ambuye, ngati ali m’tulo adzachira.”
Kenaka Yesu akuwawuza iwo momvekera: “Lazaro wamwalira, ndipo ndikondwera chifukwa cha inu kuti kunalibe Ine komweko, chakuti mukakhulupirire; koma tiyeni; tipite kwa iye.”
Akumazindikira kuti Yesu angaphedwe mu Yudeya, komabe akukhumba kumuchirikiza iye, Tomasi akulimbikitsa ophunzira anzake: “Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi.” Chotero akumaika pachiswe miyoyo yawo, ophunzirawo akutsagana ndi Yesu pa ntchito ya chifundo imeneyi mu Yudeya. Luka 13:22; 17:1-10; Yohane 10:22, 31, 40-42; 11:1-16.
◆ Kodi nkuti kumene Yesu anali kulalikira posachedwapa?
◆ Kodi ndi ziphunzitso zotani zimene Yesu akubwereza, ndipo ndi mkhalidwe weniweni wotani umene iye akulongosola kuchitira fanizo nsonga yotani?
◆ Kodi ndi mbiri yotani imene Yesu akulandira, ndipo nchiyani chimene iye akutanthauza ndi “usana”ndi “usiku”?
◆ Kodi nchiyani chomwe Tomasi akutanthauza pamene akunena kuti, ‘Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi’?