Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Liwu la Mulungu Limvedwa Nthaŵi Yachitatu
PAMENE adakali pa kachisi, Yesu wakhala akuvutitsidwa maganizo ndi imfa imene ayenera kuyang’anizana nayo posachedwapa. Nkhaŵa yake yaikulu iri mmene dzina la Atate wake lidzayambukiridwira, chotero akupemphera kuti: “Atate, lemekezani dzina lanu.”
Pamenepo, liwu lalikulu limveka kuchokera kumwamba, likulengeza kuti: “Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.”
Khamu la anthu loimirira momuzinga lizizwitsidwa. “Mngelo walankhula ndi iye,” ena a iwo akutero. Ena akutinso linali bingu. Komatu, alidi Yehova Mulungu amene walankhula! Komabe, iyi, sindiyo nthaŵi yoyamba pamene liwu la Mulungu limveka m’chigwirizano ndi Yesu.
Pa ubatizo wa Yesu, zaka zitatu ndi theka kuchiyambiyambi, Yohane Mbatizi anamva Mulungu akunena za Yesu kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.” Kenaka, nthaŵi ina pambuyo pa Paskha wapita, pamene Yesu anasandulizika pamaso pawo, Yakobo, Yohane, ndi Petro anamva Mulungu akulengeza kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani iye.” Ndipo tsopano, kwa nthaŵi yachitatu, pa Nisani 10, masiku anayi imfa ya Yesu isadakhale, liwu la Mulungu lamvedwanso ndi anthu. Koma nthaŵi ino Yehova akulankhula m’njira yakuti makamuwo akhoza kumva!
Yesu akulongosola kuti: “Mawu awa sanafika chifukwa cha ine, koma cha inu.” Zikupereka umboni wakuti Yesu alidi Mwana wa Mulungu, Mesiya wolonjezedwayo. “Tsopano pali kuweruza kwa dziko ili lapansi;” Yesu akupitiriza kuti, “[wolamulira, NW] wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja tsopano.” Kwenikwenidi, njira yokhulupirika ya moyo wa Yesu, ikutsimikizira kuti Satana Mdyerekezi, wolamulira wa dziko, ayenerera ‘kutayidwa kunja,’ kuphedwa.
Akumasonya ku zotulukapo za imfa yake yomayandikira, Yesu akunena kuti: “Ndipo ine, mmene ndikakwezedwa kudziko, ndidzakoka anthu onse kwa ine ndekha.” Imfa yake siiri kulakidwa m’njira iriyonse, popeza kupyolera mwa iyo, iye adzakokera ena kwa iyemwini kotero kuti asangalale ndi moyo wosatha.
Koma khamulo likutsutsa kuti: “Tidamva ife m’chilamulo kuti Kristu akhala ku nthaŵi yonse; ndipo inu munena bwanji, kuti Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wamunthu amene ndani?”
Mosasamala kanthu za umboni wonsewo, kuphatikizapo kumva liwu la Mulungu lenileni, ambiri sakukhulupirira kuti Yesu ali Mwana wa munthu wowona, Mesiya wolonjezedwayo. Komabe, monga mmene anachitira miyezi isanu ndi umodzi yapita pa Phwando la Misasa, Yesu akulankhulanso za iyemwini kukhala “kuunika” nalimbikitsa amvetseri ake kuti: “Pokhala muli nako kuunika, khulupirirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako.” Pambuyo ponena zinthu izi, Yesu achokapo nakabisala, mwachiwonekere chifukwa chakuti moyo wake unali pangozi.
Kusoŵa chikhulupiriro mwa Yesu kwa Ayuda kumakwaniritsa mawu a Yesaya onena za ‘maso a anthu akuchititsidwa khungu ndi mitima yawo ikulimbitsidwa kotero kuti sakutembenuka kuti achiritsidwe.’ Yesaya anawona m’masomphenya mabwalo akumwamba a Yehova, kuphatikizapo Yesu mu ulemerero wake asanakhale munthu ali ndi Yehova. Komabe, m’kukwaniritsa chimene Yesaya analemba, mowuma khosi Ayuda akukana umboniwo kuti Iyeyu ndiye Mpulumutsi wawo wolonjezedwa.
Ku mbali ina, ambiri ngakhale olamulira omwe (mwachiwonekere ziŵalo za khoti lalikulu Lachiyuda, Bwalo Lalikulu Lamilandu la Ayuda) akukhulupiriradi Yesu. Nikodemo ndi Yosefe wa ku Arimateya ali aŵiri a olamulira ameneŵa. Koma olamulirawo, kwa nthaŵi ino, akulephera kulengeza chikhulupiriro chawo, kuwopa kuchotsedwa pa malo awo m’sunagoge. Ndi kuphonya mwaŵi kotani nanga kumene otereŵa akuchita!
Yesu apitirizabe kudziŵitsa kuti: “Iye wokhulupirira ine, sakhulupirira ine, koma iye wondituma ine. Ndipo wondiwona ine awona amene anandituma ine. . . . Ndipo ngati wina akumva mawu anga, ndi kusawasunga, ine sindimweruza; pakuti sindinadza kudzaweruza dziko lapansi, koma kuti ndipulumutse dziko lapansi. . . . Mawu amene ndalankhula, iwowa adzamweruza tsiku lomaliza.”
Chikondi cha Yehova kaamba ka dziko la mtundu wa anthu chinamsonkhezera iye kutumiza Yesu kotero kuti awo okhulupirira iye angapulumutsidwe. Kaya anthu adzapulumutsidwa zidzadziŵika kaya iwo alabadira zinthu zimene Mulungu analangiza Yesu kulankhula. Chiweruzocho chidzachitika mu “tsiku lomaliza,” mkati mwa Kulamulira kwa Kristu kwa Zaka Chikwi.
Yesu akumaliza mwakumati: “Pakuti sindinalankhula mwa ine ndekha; koma Atate wondituma ine, yemweyo anandipatsa ine lamulo, limene ndikanene, ndi limene ndikalankhule. Ndipo ndidziŵa kuti lamulo lake liri moyo wosatha; chifukwa chake zimene ndilankhula, monga momwe Atate wanena ndi ine, momwemo ndilankhula.” Yohane 12:28-50; 19:38, 39; Mateyu 3:17; 17:5; Yesaya 6:1, 8-10.
◆ Kodi ndi pa zochitika zitatu ziti pamene liwu la Mulungu linamvedwa ponena za Yesu?
◆ Kodi ndimotani mmene mneneri Yesaya anawonera ulemerero wa Yesu?
◆ Kodi ndi olamulira ati omwe anaika chikhulupiriro mwa Yesu, koma kodi nchifukwa ninji sanamvomereze iye?
◆ Kodi nchiyani chiri “tsiku lomaliza,” ndipo anthu nthaŵi imeneyo adzaweruzidwa pa maziko otani?