Kodi Zipembedzo Zonse Zimalambira Mulungu Mmodzi?
“Inetu ndili ndi chipembedzo changa ndipo sindingasinthe zimene ndimakhulupirira. Ndipo zilibe kanthu kuti munthu ali m’chipembedzo chotani chifukwa Mulungu ndi mmodzi.”
KODI munamvapo munthu wina akunena mawu ngati amenewa? Anthu ambiri amati chipembedzo chilichonse chimathandiza anthu kudziwa Mulungu ndiponso cholinga cha moyo. Komanso anthu ambiri amakhulupirira kuti chipembedzo chilichonse chili ndi ubwino ndiponso kuipa kwake. Ndipo iwo amati palibe amene ayenera kunena kuti chipembedzo chake chokha n’chimene chimaphunzitsa choonadi ndiponso kuti n’chimene chimathandiza anthu kudziwadi Mulungu.
Anthu ambiri masiku ano alinso ndi maganizo amenewa chifukwa iwo amati zimene chipembedzo chilichonse chimaphunzitsa n’zofunika kwambiri. Iwo amanenanso kuti anthu amene sagwirizana ndi maganizo amenewa ndi atsankho. Nanga kodi inuyo maganizo anu ndi otani pankhani imeneyi? Kodi mumakhulupirira kuti zipembedzo zonse zimalambira Mulungu mmodzi?
Kodi Pali Kusiyana Kulikonse?
Buku lina linafotokoza kuti masiku ano pali zipembedzo zokwana 9,900. Zina mwa zipembedzozi zimapezeka m’madera ambiri padziko lonse ndiponso zili ndi anthu mamiliyoni ambiri. Kafukufuku amasonyeza kuti anthu 70 pa 100 alionse padziko lonse ali mu zipembedzo zikuluzikulu zomwe ndi Chibuda, Chihindu, Chikhristu, Chisilamu ndi Chiyuda. Zikanakhala kuti zipembedzo zonsezi zimalambira Mulungu mmodzi, ndiye kuti zikanamaphunzitsa zinthu zofanana pankhani yokhudza Mulungu komanso cholinga chake. Koma kodi umboni wa nkhaniyi umasonyeza chiyani?
Katswiri wina wamaphunziro achikatolika dzina lake Hans Küng anafotokoza kuti zipembedzo zikuluzikulu zisanuzi zimaphunzitsa zinthu zambiri zofanana zokhudza mmene tiyenera kukhalira bwino ndi ena. Mwachitsanzo, zipembedzozi zimaphunzitsa kuti kupha munthu, kunama ndiponso kugonana ndi wachibale n’zolakwika. Zimaphunzitsanso kuti ana ayenera kulemekeza makolo komanso kuti makolo ayenera kukonda ana awo. Komabe pankhani zina, makamaka zokhudza mmene Mulungu alili, zipembedzozi zimaphunzitsa zosiyana kwambiri.
Mwachitsanzo, Ahindu amalambira milungu yambiri koma zikuoneka kuti Abuda sakhulupirira kuti Mulungu ndi munthu weniweni. Asilamu amaphunzitsa kuti kuli Mulungu mmodzi. Ndipo matchalitchi omwe amati ndi achikhristu amakhulupiriranso zimenezi ngakhale kuti ambiri mwa matchalitchiwa amati pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu. Ndipotu ngakhale matchalitchi achikhristu okhaokha, amakhulupirira zinthu zosiyana kwambiri. Mwachitsanzo, Akatolika amalambira Mariya, mayi ake a Yesu, koma Apulotesitanti sachita zimenezi. Akatolika amaletsa kugwiritsa ntchito njira zakulera koma Apulotesitanti ambiri amavomereza njirazi. Komanso Apulotesitanti okhaokha sagwirizana chimodzi pankhani yokhudza kugonana kwa akazi kapena amuna okhaokha.
Ndiyeno kodi n’zomveka kukhulupirira kuti zipembedzo zimene zimaphunzitsa zinthu zotsutsana chonchi, zimalambira Mulungu mmodzi? Ndithudi n’zosamveka. Ndipotu zimenezi zingalepheretse anthu kudziwa zoona pankhani yokhudza Mulungu komanso zimene iye amafuna kuti anthu amene amamulambira azichita.
Kodi Zipembedzo Zimagwirizanitsa Anthu Kapena Zimawagawanitsa?
Zikanakhala kuti zipembedzo zonse zimalambira Mulungu mmodzi, ndiye kuti zipembedzozi zikanayesetsa kulimbikitsa anthu kuti azikhala mogwirizana ndiponso mwamtendere. Kodi zochita za zipembedzozi zimasonyeza kuti zimalimbikitsadi anthu kuti azikhala mwamtendere? Mbiri imasonyeza kuti zipembedzo si zimagwirizanitsa anthu, m’malomwake zimawagawanitsa ndiponso kuwachititsa kuti azimenyana. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.
Kuyambira m’zaka za m’ma 1000 C.E. mpaka m’ma 1200 C.E., mayiko omwe amati ndi a Chikhristu anamenyana kangapo konse ndi mayiko a Chisilamu. Ndipo m’zaka za m’ma 1600, akatolika ndi apulotesitanti anamenyana pankhondo imene inatenga zaka 30. Mu 1947, anthu a ku India atangolandira ufulu wodzilamulira kuchokera ku dziko la Britain, Ahindu ndi Asilamu anayamba kumenyana. Ndipo chaposachedwapa, Akatolika ndi Apolotesitanti akhala akumenyana ku Northern Ireland. Komanso ku Middle East, Ayuda ndi Asilamu samwerana madzi. Ndiponso anthu a m’zipembedzo zikuluzikulu zija anamenya nawo yachiwiri ya padziko lonse, ngakhalenso kupha anthu a m’chipembedzo chawo chomwe, amene anali ku mbali ya adani awo.
Pamenepa n’zoonekeratu kuti zipembedzo sizinathandize anthu kukhala mwamtendere ndiponso mogwirizana. Ndipo m’malo mothandiza kulambira Mulungu mmodzi yekha, zawagawanitsa ndiponso zawasokoneza kwambiri pankhani yokhudza mmene Mulungu alili komanso zimene angachite pomulambira. Choncho, aliyense amene akufuna kulambira Mulungu woona ayenera kutsatira mosamala zimene Iye amafuna. Mfundo imeneyi ndi yogwirizana ndi zimene Baibulo, lomwe ndi buku lodziwika bwino kwambiri pankhani za chipembedzo, limanena.
Sankhani Amene Mukufuna Kumutumikira
Baibulo limasonyeza kuti munthu ayenera kuganiza mosamala ndiponso kusankha yekha ngati akufuna kutumikira Mulungu woona. Yoswa, yemwe anali mtumiki wa Yehova Mulungu, anauza mtundu wa Isiraeli kuti: “Mudzisankhire lero amene mudzam’tumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m’dziko lawo; koma ine, ndi a m’nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.” Patapita zaka zambiri, mneneri Eliya analimbikitsanso anthu kuchita zomwezi. Iye anati: “Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, m’tsateni iye; ngati Baala [mulungu wa Akanani], mum’tsate iyeyo.”—Yoswa 24:15, 16; 1 Mafumu 18:21.
Mavesi amenewa komanso ena amasonyeza mosapita m’mbali kuti anthu onse omwe ankafuna kulambira Mulungu anayenera kusankha zinthu mwanzeru. N’chimodzimodzinso masiku ano. Ngati tikufuna kulambira ndiponso kutumikira Mulungu woona, tiyenera kusankha mwanzeru. Koma kodi n’chiyani chimene chingatithandize kuti tisankhe zinthu mwanzeru pankhani yolambira? Kodi tingadziwe bwanji anthu amene akulambira Mulungu moona?
Olambira Oona Amadziwika ndi Zipatsa Zawo
Ponena za olambira oona ndiponso onyenga, Yesu Khristu anauza otsatira ake kuti: “Anthu sathyola mphesa pa minga kapena nkhuyu pa mitula, amatero kodi? Momwemonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo uliwonse wovunda umabala zipatso zopanda pake; mtengo wabwino sungabale zipatso zopanda pake, ndiponso mtengo wovunda sungabale zipatso zabwino. . . . Chotero anthu amenewo mudzawazindikira ndi zipatso zawo.” Choncho, tingathe kuzindikira olambira oona, mwa kuona zipatso kapena kuti zochita zawo. Kodi zipatso zimenezi ndi ziti?—Mateyo 7:16-20.
Chipembedzo choona chimalimbikitsa anthu ake kuti azikondana. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana wina ndi mnzake. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana wina ndi mnzake. Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.” Otsatira oona a Khristu ayenera kusonyezana chikondi chenicheni ndipo n’zimene zimachititsa kuti anthu adziwe kuti iwo ndi olambira oona.—Yohane 13:34, 35.
Choncho m’posayenera kuti Akhristu oona azimenya nawo nkhondo. Kodi anthu amene amapita kutchalitchi amatsatira malangizo amenewa? Pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, gulu lalikulu la chipembedzo limodzi lokha limene linakanitsitsa kumenya nawo kapena kulimbikitsa nkhondoyo, linali la Mboni za Yehova. Ponena za Mboni za Yehova, Dr. Hanns Lilje, yemwe anali bishopu wa tchalitchi cha Pulotesitanti ku Hannover, m’dziko la Germany analemba kuti: “Iwo ayeneradi kunena kuti chipembedzo chawo chokha n’chimene chinakanitsitsa kumenya nawo nkhondo mu ulamuliro wa Hitler. Iwo amachita zimenezi chifukwa cha zimene amakhulupirira.” Panthawiyo, Mboni za Yehova m’madera ambiri zinalolera kuzunzidwa chifukwa chokana kulimbikitsa kapena kumenya nawo nkhondoyo.
Kodi Yesu ananena za zipatso zinanso ziti zothandiza kudziwa olambira oona? M’pemphero la Ambuye, iye anayamba ndi kunena kuti: “Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.” M’pempheroli, Yesu anayamba kutchula za kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu lakuti Yehova. Iye anapempha kuti chifuniro cha Yehova chokhudza dziko lapansi chikwaniritsidwe kudzera mu Ufumu wa Mulungu. Kodi ndi chipembedzo chiti chimene chimalengeza za dzina la Yehova ndiponso kulengeza kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzabweretse mtendere kwa anthu padziko lapansili? Mboni za Yehova n’zimene zikulengeza uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu m’mayiko ndi m’madera okwana 236. Ndipo zikufalitsa mabuku ndi magazini m’zinenero zoposa 470.—Mateyo 6:9, 10.
Kuwonjezera pamenepa, Mboni za Yehova zimatsatira chitsanzo cha Yesu posalowerera ndale ndi mikangano ya anthu. Ponena za otsatira ake, Yesu anati: “Sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.” Ndiponso Mboni za Yehova zimaona kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu ndipo zimakhulupirira mfundo yakuti: “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu, kulangiza m’chilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera mokwanira, wokonzeka bwino lomwe kuchita ntchito iliyonse yabwino.”—Yohane 17:14, 17; 2 Timoteyo 3:16, 17.
Chipembedzo Choona N’chosiyana Kwambiri ndi Zipembedzo Zina
Tingadziwe olambira oona chifukwa iwo ali ndi chikondi chololera kuvutikira ena, amafunitsitsa kuyeretsa dzina la Yehova, amalengeza Ufumu wa Mulungu, sakhala mbali ya dziko ndiponso amakhulupirira kwambiri Baibulo. Zinthu zimenezi zimachititsanso kuti olambira oona akhale osiyana kwambiri ndi anthu a m’zipembedzo zina. Mwachitsanzo, mayi wina amene ankakonda kucheza ndi Mboni za Yehova ananena kuti: “Zipembedzo zambiri ndimazidziwa bwino ndipo ndimaona kuti zonse n’zofanana. Koma inuyo ndinu osiyana kwambiri ndi zipembedzo zina zonse.”
Apatu n’zoonekeratu kuti si zipembedzo zonse zomwe zimalambira Mulungu woona. Koma pali gulu limodzi limene ndi losiyana kwambiri ndi zipembedzo zina zonse. Gululi ndi la Mboni za Yehova zomwe tsopano zilipo zoposa 7 miliyoni padziko lonse. Mboni za Yehova zimalemekeza ndiponso kutsatira zimene Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, limanena. Ndipo palibe gulu kapena bungwe lina limene latha kugwirizanitsa anthu amitundu yonse, zinenero zonse, zikhalidwe zonse pa kulambira Yehova, yemwe ndi Mulungu yekha woona. Iwo angasangalale kukuthandizani kuti muphunzire za Mulungu woona n’cholinga choti mudziwe zimene iye amafuna kuti muzichita. Iwo angakuthandizeninso kupeza chimwemwe chimene anthu omwe akulambira Mulungu m’njira imene iye amavomereza amakhala nacho. Kodi inuyo simungakonde kuphunzira zimenezi?
[Chithunzi patsamba 14]
Wansembe wa tchalitchi cha Orthodox akudalitsa gulu latsopano la asilikali ku Ukraine mu 2004
[Mawu a Chithunzi]
GENIA SAVILOV/AFP/Getty Images
[Chithunzi patsamba 15]
Mboni za Yehova zikuthandiza anthu padziko lonse kuti adziwe za Mulungu ndiponso Ufumu wake
[Mawu a Chithunzi patsamba 12]
Page 12: Buddhist woman: © Yan Liao/Alamy; Hindu holy man: © imagebroker/Alamy; page 13: Man reading Koran: Mohamed Amin/Camerapix; Jewish man: Todd Bolen/Bible Places.com