Kodi Ubatizo Umatanthauza Chiyani?
Yankho la m’Baibulo
Ubatizo ndi kuviika munthu m’madzi kenako n’kumuvuula.a Baibulo limafotokoza za anthu ambiri amene anabatizidwa. (Machitidwe 2:41) Yesu ndi mmodzi mwa iwo ndipo iye anabatizidwa mumtsinje wa Yorodano. (Mateyu 3:13, 16) Patadutsa zaka zingapo, munthu wina wa ku Itiyopiya anabatizidwa pamene panali “madzi ambiri” pafupi ndi msewu womwe ankadutsa.—Machitidwe 8:36-40.
Yesu ananena kuti anthu amene amamutsatira ayenera kubatizidwa. (Mateyu 28:19, 20) Mtumwi Petulo nayenso anafotokoza bwino mfundo imeneyi.—1 Petulo 3:21.
Zimene zili munkhaniyi
Zimene ubatizo umatanthauza
Ubatizo ndi chizindikiro chakuti munthu yemwe akubatizidwayo analapa machimo ake ndiponso analonjeza Mulungu kuti kwa moyo wake wonse, azichita zomwe Mulunguyo akufuna. Zimenezi zikuphatikizapo kumvera Mulungu ndi Yesu nthawi zonse. Anthu akabatizidwa amayamba kuchita zimene Mulungu amafuna n’cholinga choti adzakhale ndi moyo kwamuyaya.
Munthu akamizidwa m’madzi chimakhala chizindikiro chakuti wasintha moyo wake. Kodi zimatheka bwanji zimenezi? Baibulo limayerekezera ubatizo ndi kuika munthu wakufa m’manda. (Aroma 6:4; Akolose 2:12) Choncho munthu akabatizidwa m’madzi amakhala ngati wafa ku moyo wake wakale. Akavuuka m’madzi amakhala ngati wayamba moyo watsopano monga Mkhristu wodzipereka.
Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti makanda azibatizidwa?
Mawu akuti “ubatizo wa makanda”b sapezeka pena paliponse m’Baibulo ndipo siliphunzitsa kuti makanda azibatizidwa.
Ubatizo wa makanda sugwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Baibulo limaphunzitsa kuti pali zinthu zambiri zimene munthu yemwe akufuna kubatizidwa ayenera kuchita. Mwachitsanzo, ayenera kumvetsa bwino mfundo zosavuta za m’Mawu a Mulungu n’kumachita zinthu zogwirizana ndi zimene akuphunzirazo. Ayeneranso kulapa machimo ake, kenako afunika kupemphera kwa Mulungu kuti akudzipereka n’cholinga choti azichita zofuna za Mulunguyo. (Machitidwe 2:38, 41; 8:12) Sizingatheke kuti makanda achite zinthu zimenezi.
Kodi kubatizidwa m’dzina la Atate, la Mwana ndi la mzimu woyera kumatanthauza chiyani?
Yesu anauza otsatira ake kuti: “Mukaphunzitse anthu . . . , muziwabatiza mʼdzina la Atate, la Mwana ndi la mzimu woyera, ndipo muziwaphunzitsa kuti azisunga zinthu zonse zimene ndinakulamulani.” (Mateyu 28:19, 20) Mawu akuti “mʼdzina la,” akutanthauza kuti munthu amene akubatizidwayo akuzindikira komanso kuvomereza mphamvu komanso udindo wa Atate ndi Mwana komanso ntchito imene mzimu woyera wa Mulungu umagwira. Mwachitsanzo, Mtumwi Petulo anauza munthu yemwe anabadwa wolumala kuti: “Mʼdzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, yenda!” (Machitidwe 3:6) Apatu tanthauzo la mawuwa n’lomveka bwino. Petulo ankazindikira kuti Khristu ndi amene ali ndi mphamvu zochiritsa anthu modabwitsa.
“Atate” akutanthauza Yehovac Mulungu. Yehova yemwe ndi Mlengi, Wotipatsa Moyo komanso Mulungu Wamphamvuyonse ali ndi mphamvu zopanda malire.—Genesis 17:1; Chivumbulutso 4:11.
“Mwana” akutanthauza Yesu Khristu amene anatifera. (Aroma 6:23) Anthufe tingadzapulumuke pokhapokha ngati timazindikira udindo wofunika kwambiri womwe Yesu ali nawo pa cholinga cha Mulungu chokhudza anthu.—Yohane 14:6; 20:31; Machitidwe 4:8-12.
“Mzimu woyera” ukutanthauza mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito.d Mulungu wakhala akugwiritsa ntchito mzimu wake woyera polenga zinthu, popereka moyo, potumiza mauthenga kwa aneneri ake ndi anthu ena komanso pothandiza anthu kuti akwaniritse zolinga zake. (Genesis 1:2; Yobu 33:4; Aroma 15:18, 19) Mulungu anagwiritsanso ntchito mzimu woyera pothandiza anthu omwe analemba Baibulo kuti alembe maganizo ake.—2 Petulo 1:21.
Kodi kubatizidwanso ndi tchimo?
N’zosadabwitsa kuona anthu akusintha chipembedzo. Ngati anabatizidwa kale m’chipembedzo chawo, kodi kubatizidwanso kungakhale kulakwa? Anthu ena amanena kuti kungakhale kulakwa potengera zomwe lemba la Aefeso 4:5 limanena kuti: “Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi.” Komatu vesi limeneli silikutanthauza kuti munthu sayenera kubatizidwanso. N’chifukwa chiyani tikutero?
Nkhani yonse. Nkhani yonse ya pa Aefeso 4:5 ikusonyeza kuti mtumwi Paulo ankatsindika mfundo yakuti Akhristu ayenera kukhala ogwirizana pa nkhani ya zimene amakhulupirira. (Aefeso 4:1-3, 16) Kuti zimenezi zitheke, Akhristuwa anafunika kumalambira Mulungu mmodzi; kukhala ndi chikhulupiriro chimodzi, kapena kuti onse anafunika kuti azimvetsa mofanana zimene Baibulo limaphunzitsa; komanso kuti onse azitsatira zimene Malemba amanena pa nkhani ya ubatizo.
Mtumwi Paulo analimbikitsa anthu omwe anali atabatizidwa kale kuti abatizidwenso. Anachita zimenezi chifukwa pa nthawi imene ankabatizidwa anali asanamvetse mokwanira ziphunzitso za Chikhristu.—Machitidwe 19:1-5.
Kodi munthu ayenera kubatizidwa pachifukwa chiti? Kuti ubatizo ukhale wovomerezeka kwa Mulungu, munthu ayenera kudziwa choonadi cha m’Baibulo molondola. (1 Timoteyo 2:3, 4) Mulungu sangavomereze ubatizo wa munthu yemwe wabatizidwa ataphunzira mfundo za chipembedzo zomwe n’zotsutsana ndi Baibulo. (Yohane 4:23, 24) N’kutheka kuti munthu wotereyu anali ndi zolinga zabwino koma limakhala vuto chifukwa ‘sanadziwe Mulungu molondola.’ (Aroma 10:2) Choncho, kuti ubatizo wake ukhale wovomerezeka kwa Mulungu, ayenera kuphunzira Baibulo, kugwiritsa ntchito zimene akuphunzira pa moyo wake, kudzipereka kwa Mulungu n’kubatizidwanso. Munthu amene wabatizidwanso pa zifukwa zimenezi sangakhale kuti wachita tchimo, m’malo mwake amakhala kuti wachita zoyenera kwambiri.
Maubatizo ena otchulidwa m’Baibulo
Baibulo limanena za mitundu ina ya ubatizo yomwe ili ndi tanthauzo losiyana ndi ubatizo wam’madzi womwe otsatira a Khristu amachita. Taonani zitsanzo zotsatirazi.
Ubatizo womwe unkachitika ndi Yohane M’batizi.e Ayuda ndi anthu otembenukira ku Chiyuda ankabatizidwa ndi Yohane monga chizindikiro choti alapa machimo omwe anachimwira Chilamulo cha Mose. Chilamulochi n’chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli kudzera mwa Mose. Ubatizo womwe unkachitika ndi Yohane unkathandiza anthu kuti athe kuzindikira komanso kuvomereza kuti Yesu wa ku Nazareti ndi Mesiya.—Luka 1:13-17; 3:2, 3; Machitidwe 19:4.
Ubatizo wa Yesu. Ubatizo womwe Yesu anabatizidwa ndi Yohane unali wosiyana ndi maubatizo ena onse. Yesu anali munthu wangwiro ndipo sanachite tchimo lina lililonse. (1 Petulo 2:21, 22) Choncho iye sanafunikire kulapa machimo ake kapena ‘kupempha Mulungu kuti amupatse chikumbumtima chabwino.’ (1 Petulo 3:21) M’malomwake, unali chizindikiro choti akudzipereka kwa Mulungu kuti achite zofuna za Mulunguyo monga Mesiya kapena kuti Khristu amene anthu ankayembekezera. Zimenezi zinkaphatikizapo kupereka moyo wake kuti awombole anthufe.—Aheberi 10:7-10.
Kubatizidwa ndi mzimu woyera. Yohane M’batizi komanso Yesu ananenapo zokhudza kubatizidwa ndi mzimu woyera. (Mateyu 3:11; Luka 3:16; Machitidwe 1:1-5) Ubatizo umenewu ndi wosiyana ndi kubatizidwa m’dzina la mzimu woyera. (Mateyu 28:19) Kodi kusiyana kwake kuli pati?
Ndi otsatira a Khristu ochepa chabe amene amabatizidwa ndi mzimu woyera. Akhristuwa amadzozedwa ndi mzimu woyera chifukwa amasankhidwa kuti akatumikire limodzi ndi Khristu kumwamba monga mafumu ndi ansembe olamulira dzikoli.f (1 Petulo 1:3, 4; Chivumbulutso 5:9, 10) Iwo adzalamulira otsatira a Yesu mamiliyoni ambirimbiri amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo kwamuyaya m’Paradaiso padziko lapansili.—Mateyu 5:5; Luka 23:43.
Kubatizidwa mwa Khristu Yesu komanso mu imfa yake. Anthu amene amabatizidwa ndi mzimu woyera amabatizidwanso ‘mwa Khristu Yesu.’ (Aroma 6:3, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Choncho, ubatizo umenewu umachitikira otsatira a Yesu odzozedwa amene akukalamulira naye kumwamba. Iwo akabatizidwa mwa Yesu amakhala mumpingo wa odzozedwa ake. Yesu ndiye Mutu wa mpingowu ndipo odzozedwawa amakhala thupi la mpingo umenewu.—1 Akorinto 12:12, 13, 27; Akolose 1:18.
Akhristu odzozedwa amabatizidwanso “mu imfa yake [ya Yesu].” (Aroma 6:3, 4) Mofanana ndi Yesu, odzozedwa amayesetsa kumvera Mulungu pa moyo wawo ndipo sakhala moyo wongodzisangalatsa komanso amadziwa kuti chiyembekezo chawo cha moyo wosatha si cha padzikoli. Iwo akamwalira, amakhala kuti amaliza kubatizidwa mu imfa ya Yesu kenako amalandira moyo kumwamba monga zolengedwa zauzimu.—Aroma 6:5; 1 Akorinto 15:42-44.
Kubatizidwa ndi moto. Yohane M’batizi anauza anthu omwe ankamumvetsera kuti: “Ameneyo [Yesu] adzakubatizani ndi mzimu woyera komanso moto. Fosholo yake youluzira mankhusu ili mʼmanja mwake, ndipo malo ake opunthirapo mbewu adzawayeretseratu kuti mbee! Tirigu adzamututira munkhokwe, koma mankhusu adzawawotcha ndi moto umene sungazimitsidwe.” (Mateyu 3:11, 12) Mungaone kuti pali kusiyana pakati pa kubatizidwa ndi moto komanso kubatizidwa ndi mzimu woyera. Kodi Yohane ankatanthauza chiyani ponena fanizo limeneli?
Tirigu akuimira anthu omwe amamva mawu a Yesu komanso kumumvera. Anthu oterewa amakhala ndi chiyembekezo chobatizidwa ndi mzimu woyera. Mankhusu akuimira anthu amene samvera Yesu. Anthu amenewa adzabatizidwa ndi moto, zomwe zikutanthauza kuti adzawonongedwa kotheratu.—Mateyu 3:7-12; Luka 3:16, 17.
a Mogwirizana ndi zimene buku lina lotanthauzira mawu limanena, mawu a Chigiriki amene anamasuliridwa kuti “ubatizo” akutanthauza “kumiza, kuviika ndiponso kunyika.”—Vine’s Complete Expository Dictionary of Old and New Testament Words.
b “Ubatizo wa makanda” ndi mwambo umene umachitika m’matchalitchi ena ndipo makanda amapatsidwa dzina kenako “amabatizidwa” powawaza kapena kuwathira madzi pamutu.
c Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?”
d Onani nkhani yakuti “Kodi Mzimu Woyera N’chiyani?”
e Onani nkhani yakuti “Kodi Yohane M’batizi Anali Ndani?”
f Onani nkhani yakuti “Kodi Ndi Ndani Amene Amapita Kumwamba?”
g Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “maubatizo” pofotokoza miyambo inayake yoyeretsa zinthu, monga kuthira madzi pa ziwiya. (Maliko 7:4; Aheberi 9:10) Zimenezi n’zosiyana ndi ubatizo wa Yesu ndi otsatira ake woviika thupi lonse m’madzi.