Kodi Yohane M’batizi Anali Ndani?
Yankho la m’Baibulo
Yohane M’batizi anali mneneri wa Mulungu. (Luka 1:76) Iye anabadwa Yesu anangotsala pang’ono kubadwa ndipo anakhala moyo mpaka m’zaka zoyambirira za m’ma C.E. Mulungu anamupatsa ntchito yokonza njira pokonzekera kubwera kwa Mesiya kapena kuti Khristu. Yohane anagwira ntchitoyi polalikira uthenga wa Mulungu kwa Ayuda anzake n’cholinga choti awathandize kubwerera kwa Mulungu.—Maliko 1:1-4; Luka 1:13, 16, 17.
Uthenga wa Yohane unathandiza anthu a mitima yabwino kuzindikira kuti Yesu wa ku Nazarete anali Mesiya wolonjezedwa. (Mateyu 11:10) Yohane analimbikitsa anthu kuti alape machimo awo kenako ndi kubatizidwa posonyeza kuti alapa. (Luka 3:3-6) Popeza Yohane anabatiza anthu ambiri, iye ankadziwika kuti M’batizi. Munthu wofunika kwambiri amene Yohane anabatiza anali Yesu.a—Maliko 1:9.
Zimene zili munkhaniyi
N’chifukwa chiyani Yohane M’batizi anali munthu wapadera?
Ntchito yake inanenedweratu: Pogwira ntchito yolalikira, Yohane anakwaniritsa ulosi wonena za mthenga wa Yehova. (Malaki 3:1; Mateyu 3:1-3) Iye anakwaniritsa udindo ‘wosonkhanitsira Yehova anthu okonzedwa,’ chifukwa anakonzekeretsa Ayuda anzake kuti alandire Yesu Khristu, yemwe ndi munthu amene anaimira Yehova Mulungu kuposa wina aliyense..—Luka 1:17.
Mbiri yake: Yesu ananena kuti “sanabadwepo wamkulu woposa Yohane M’batizi. Koma munthu amene ali wocheperapo mu ufumu wakumwamba ndi wamkulu kuposa iyeyu.” (Mateyu 11:11) Popeza Yohane anali mneneri komanso “mthenga” amene ananenedweratu, palibenso mtumiki wina amene anakhalapo Yohane asanabadwe, yemwe anali wamkulu kuposa iye. Mawu a Yesuwa amasonyezanso kuti Yohane sadzalamulira nawo mu Ufumu wakumwamba.b Mneneri wokhulupirikayu anamwalira Khristu asanatsegulire anthu mwayi wopita kumwamba. (Aheberi 10:19, 20) Koma Yohane adzakhala padziko lapansili monga nzika ya Ufumu wa Mulungu ndipo akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wamuyaya dzikoli likadzakhala Paradaiso.—Salimo 37:29; Luka 23:43.
Kodi makolo a Yohane M’batizi anali ndani?
Makolo a Yohane anali Zekariya ndi mkazi wake Elizabeti. Zekariya anali wansembe wa Chiyuda. Kubadwa kwa Yohane kunali kozizwitsa chifukwa mayi ake anali osabereka. Komanso Elizabeti ndi mwamuna wake Zekariya “anali okalamba.”—Luka 1:5-7, 13.
Kodi ndani anachititsa kuti Yohane M’batizi aphedwe?
Mfumu Herode Antipa analamula anthu kuti adule mutu wa Yohane. Iye anachita zimenezi chifukwa ndi zimene mkazi wake Herodiya, anamuuza. Herodiya ankadana ndi Yohane chifukwa choti Yohane anauza Herode, kuti ukwati wake ndi Herodiya sunali wogwirizana ndi malamulo a Ayuda.—Mateyu 14:1-12; Maliko 6:16-19.
Kodi Yohane M’batizi ndi Yesu Ankapikisana?
M’Baibulo mulibe umboni uliwonse wotsimikizira kuti ankapikisana ngati mmene anthu ena amaganizira. (Yohane 3:25-30) Yohane ananena mosabisa kuti udindo wake unali wokonzera njira Mesiya, osati kupikisana naye. Yohane anati: “Chimene ndikubatizira anthu m’madzi n’chakuti iyeyu aonekere kwa Isiraeli.” Kenako ananena za Yesu kuti: “Iyeyu ndi Mwana wa Mulungu.” (Yohane 1:26-34) Choncho Yohane ankasangalala kwambiri kumva kuti zinthu zikuyenda bwino pa utumiki wa Yesu.
a Yesu “sanachite tchimo.” (1 Petulo 2:21, 22) Choncho sanabatizidwe chifukwa choti ankafunika kulapa machimo koma chifukwa chosonyeza kuti wadzipereka kwa Mulungu kuti achite zofuna zake. Izi zinaphatikizapo kupereka moyo wake chifukwa cha ife.—Aheberi 10:7-10.
b Onani nkhani yakuti “Kodi Ndi Ndani Amene Amapita Kumwamba?”