Yesu Kristu
Tanthauzo: Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, Mwana yekha wolengedwa ndi Yehova yekha. Mwanayo ndiye wachisamba wa chilengedwe chonse. Kudzera mwa iye zinthu zina zonse kumwamba ndi padziko lapansi zinalengedwa. Ndiye munthu wachiŵiri kwa munthu wamkulu koposa onse m’chilengedwe chonse. Ali Mwana ameneyu amene Yehova anatuma kudziko lapansi kudzapereka moyo wake kukhala dipo la anthu, mwa kutero anatsegula njira yomka kumoyo wamuyaya kaamba ka ana a Adamu amene akasonyeza chikhulupiriro. Mwana mmodzimodzi ameneyu, wobwezeretsedwa ku ulemerero wakumwamba, tsopano akulamulira monga Mfumu, limodzi ndi ulamuliro wa kuwononga oipa onse ndi kukwaniritsa chifuno choyambirira kaamba ka dziko lapansi cha Atate wake. Mpangidwe Wachihebri wa dzina lakuti Yesu umatanthauza “Yehova Ndiye Chipulumutso”; Kristu ndiro liwu lofanana ndi Lachihebri Ma·shiʹach (Mesiya), kutanthauza “Wodzozedwa.”
Kodi Yesu Kristu anali munthu weniweni, wa m’mbiri?
Baibulo lenilenilo ndiro umboni waukulu wakuti Yesu Kristu ndimunthu wa m’mbiri. Cholembedwa cha Uthenga Wabwino sichiri mafotokozedwe osamvekera bwino a zochitika panthaŵi ina yosadziŵika bwino ndipo pamalo osatchulidwa dzina. Chimafotokoza bwino momvekera nthaŵi ndi malo mwatsatanetsatane kwambiri. Mwachitsanzo, wonani Luka 3:1, 2, 21-23.
Wolemba mbiri Wachiyuda wa m’zaka za zana loyamba Josephus anasonya ku kuponyedwa miyala kwa “Yakobo, mbale wa Yesu amene anali kutchedwa Kristu.” (The Jewish Antiquities, Josephus, Bukhu XX, gawo 200) Umboni wachindunji ndi wabwino kwambiri ponena za Yesu, wopezedwa m’Bukhu XVIII, chigawo 63, 64, wakaikiridwa ndi ena amene amanena kuti uyenera kukhala kaya utawonjezeredwa pambuyo pake kapena kupititsidwa patsogolo ndi Akristu; koma kukuvomerezedwa kuti mpambo wa mawu ndi kalembedwe ziri kwakukulukulu za Josephus, ndipo mawuŵa akupezeka m’malemba onse apamanja amene ali opezeka.
Tacitus, wolemba mbiri Wachiroma amene anakhalako m’mbali yotsirizira ya zaka za zana loyamba C.E., analemba kuti: “Christus [ndiko kuti “Kristu” m’Chilatini] kumene kwachokera dzina lakuti [Mkristu], anavutika ndi chilango chopweteka kopambana m’nthaŵi ya kulamulira kwa Tiberiyo choperekedwa ndi mmodzi wa akazembe athu, Pontiyo Pilato.”—The Complete Works of Tacitus (New York, 1942), “The Annals,” Bukhu 15, ndime 44.
Posonya ku maumboni oyambirira osakhala Achikristu a m’mbiri onena za Yesu, The New Encyclopædia Britannica imafotokoza kuti: “Zolembedwa za pazokha zimenezi zimatsimikizira kuti m’nthaŵi zakale ngakhale otsutsa Chikristu sanakaikire konse kuti Yesu anali munthu weniweni wa m’mbiri, chimene chinali chotsutsidwa kwa nthaŵi yoyamba ndipo popanda maziko okwanira ndi olemba angapo cha kumapeto kwa zaka za zana la 18, mkati mwa zana la 19, ndi kuchiyambi kwa zaka za zana la 20.”—(1976), Macropædia, Vol. 10, p. 145.
Kodi Yesu Kristu anali kokha munthu wabwino chabe?
Mokondweretsa, Yesu anadzudzula mwamuna wina amene anamuitana ndi dzina laulemu lakuti “Mphunzitsi Wabwino,” chifukwa chakuti Yesu sanadziwone iye mwini kukhala muyeso wa chabwino koma Atate wake. (Marko 10:17, 18) Komabe, kuyenerana ndi zimene anthu kaŵirikaŵiri amatanthauza pamene anena kuti chinthu ichi nchabwino, ndithudi Yesu ayenera kukhala anali ndi chowonadi. Ndithudi, ngakhale adani ake anavomereza kuti anali nacho. (Marko 12:14) Iye mwiniyo adanena kuti anakhalako asadakhale munthu, ndi kuti iye anali Mwana wapadera wa Mulungu, kuti iye anali Mesiya, iye amene kudza kwake kudanenedweratu m’Malemba onse Achihebri. Iye mwina anali chimene adanena kuti anali kapena kuti anali wonyenga weniweni, koma palibe iriyonse ya mbali ziŵirizo imene imapereka lingaliro lakuti iye anali kokha munthu wabwino.—Yoh. 3:13; 10:36; 4:25, 26; Luka 24:44-48.
Kodi Yesu anali kokha mneneri amene ulamuliro wake unali wofanana ndi wa Mose, Buddha, Muhammadi, ndi atsogoleri ena achipembedzo?
Yesu mwiniyo anaphunzitsa kuti anali Mwana wapadera wa Mulungu (Yoh. 10:36; Mat. 16:15-17), Mesiya wonenedweratu (Marko 14:61, 62), kuti anali ndi moyo kumwamba asanadzakhale munthu (Yoh. 6:38; 8:23, 58), kuti akaphedwa ndiyeno akaukitsidwira kumoyo patsiku lachitatu ndiyeno pambuyo pake kubwerera kumwamba. (Mat. 16:21; Yoh. 14:2, 3) Kodi mawu onenedwa ameneŵa anali owona, ndipo chotero kodi iye analidi wosiyana ndi aneneri ena owona a Mulungu ndi wosiyana kotheratu ndi atsogoleri achipembedzo odzikhazikitsa okha? Chowonadi cha nkhaniyi chikawonekera patsiku lachitatu pambuyo pa imfa yake. Kodi Mulungu pamenepo anamuukitsa kwa akufa, ndipo mwakutero kutsimikizira kuti Yesu Kristu adalankhula chowonadi ndi kuti analidi Mwana wapadera wa Mulungu? (Aroma 1:3, 4) Zoposa mboni 500 zinamuwonadi Yesu ali wamoyo pambuyo pa chiukiriro chake, ndipo atumwi ake okhulupirika anali mboni zowona ndi maso pamene anayamba kukwera kubwerera kumwamba ndiyeno kuzimiririka kumaso kwawo kuloŵa m’thambo. (1 Akor. 15:3-8; Mac. 1:2, 3, 9) Chotero iwo anali okhutira kotheratu kuti iye anaukitsidwa kwa akufa kwakuti unyinji wa iwo unaika miyoyo yawo pa chiswe kukusimbira ena za izo.—Mac. 4:18-33.
Kodi nchifukwa ninji Ayuda ambiri sanavomereze Yesu kukhala Mesiya?
Encyclopaedia Judaica imati: “Ayuda a nyengo ya Aroma adakhulupirira kuti [Mesiya] akaukitsidwa ndi Mulungu kuthyola goli la akunja ndi kulamulira pa Ufumu wa Israyeli wobwezeretseredwanso.” (Jerusalem, 1971, Vol. 11, danga 1407) Iwo anafuna kumasuka kugoli la Aroma. Mbiri ya Ayuda imachitira umboni kuti pamaziko a ulosi wonena za Mesiya wolembedwa pa Danieli 9:24-27 panali Ayuda oyembekezera Mesiya mkati mwa zaka za zana loyamba C.E. (Luka 3:15) Koma ulosi umenewo unagwirizanitsanso kudza kwake ndi ‘kuthetsa tchimo,’ ndipo Yesaya mutu 53 anasonyeza kuti Mesiya mwiniyo akafa kuti atheketse zimenezi. Komabe, Ayuda ambiri sanawone kufunika kwakuti munthu wina afere machimo awo. Iwo anakhulupirira kuti anali ndi mkhalidwe wolungama pamaso pa Mulungu pamaziko a kukhala kwawo mbadwa za Abrahamu. A Rabbinic Anthology imati, “[Kuyenera] kwa Abrahamu nkwakukulu kwambiri kotero kuti angakhoze kutetezera machimo onse ochitidwa ndi mabodza onenedwa ndi Aisrayeli m’dziko lino.” (London, 1938, C. Montefiore ndi H. Loewe, p. 676) Mwa kukana kwawo Yesu kukhala Mesiya, Ayuda anakwaniritsa ulosi umene unali utaneneratu za iye kuti: “Iye ananyozedwa, ndipo tinamuwona kukhala wosanunkha kanthu.”—Yesaya 53:3, JP.
Imfa yake isanachitike, Mose adaneneratu kuti mtunduwo ukapatuka pakulambira kowona ndi kuti monga, chotulukapo, tsoka likaŵagwera. (Ŵerengani Deuteronomo 31:27-29.) Bukhu la Oweruza limachitira umboni kuti zimenezi zinachitika mobwerezabwereza. M’masiku a mneneri Yeremiya, kusakhulupirika kwa mtunduwo kunauchititsa kutengeredwa ku ukapolo ku Babulo. Ndiponso kodi nchifukwa ninji Mulungu analolera Aroma kuwononga Yerusalemu ndi kachisi wake mu 70 C.E.? Kodi mtundu umenewu unali ndi liwongo la kusakhulupirika lotani limene linachititsa Mulungu kusawatetezera monga momwe anali atachitira pamene anali atamkhulupirira? Kunali mwamsanga zimenezi zisanachitike pamene iwo anali atakana Yesu monga Mesiya.
Kodi Yesu Kristu kwenikweni ali Mulungu?
Yohane 17:3: “[Yesu anapemphera kwa Atate wake:] Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu wowona yekha [“amene inu nokha ndinu Mulungu wowona,” NE], ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Tawonani kuti Yesu sanasonye kwa iyemwini koma kwa Atate wake kumwamba kukhala “Mulungu wowona yekha.”)
Yoh. 20:17: “Yesu ananena naye [Mariya wa Magadala], Usandikhudze, pakuti sindinathe kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kumka kwa Atate wanga, ndi Atate wanu, ndi Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.” (Motero kwa Yesu woukitsidwayo, Atate anali Mulungu monga momwedi Atateyo analiri Mulungu kwa Mariya wa Magadala. Mokondweretsa, sitimapeza ngakhale nthaŵi imodzi m’Malemba kumene Atate akutchula Mwanayo kukhala “Mulungu wanga.”)
Wonaninso tsamba 397, 398, 403, 404, pamutu wakuti “Utatu.”
Kodi Yohane 1:1 amatsimikizira kuti Yesu ali Mulungu?
Yoh. 1:1: “Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu ndiye Mulungu [ndiponso KJ, JB, Dy, Kx, NAB].” NE imati “amene anali Mulungu, anali Mawu.” Mo imati “Logos anali waumulungu.” AT ndi Sd amatiuza kuti “Mawuwo anali aumulungu.” Matembenuzidwe a interlinear a ED ndiwo akuti “mulungu anali Mawu.” NW imati “Mawu anali mulungu”; NTIV imagwiritsira ntchito mawu ofananawo.
Kodi nchiyani chimene otembenuza amenewa amawona m’malemba apamanja Achigiriki chimene chikusonkhezera ena a iwo kupeŵa kunena kuti “Mawu anali Mulungu”? Mfotokozi Wachigiriki (ho) amawonekera pakutchulidwa koyamba kwa the·osʹ (Mulungu) kusanachitike. Koma osati pambuyo pa wachiŵiri. Mpangidwe wa mawu (pamene mfotokozi aphatikizidwa) umasonyeza chinthu, umunthu, pamene kuli kwakuti mpangidwe wa chimodzi (wopanda mfotokozi) patsogolo pamneni (monga momwe mawuwo alembedwera m’Chigiriki) umasonyeza ku ukulu wa munthuyo. Motero lemba limeneli silikunena kuti Mawuyo (Yesu) anali Mulunguyo amene iye anali naye koma, mmalo mwake, Mawuyo anali wofanana ndi Mulungu, waumulungu, mulungu. (Wonani kope la Malifarensi la 1984 la NW, p. 1579.)
Kodi nchiyani chimene mtumwi Yohane anatanthauza pamene analemba Yohane 1:1? Kodi anatanthauza kuti Yesu mwiniyo ali Mulungu kapena mwinamwake kuti Yesu ali Mulungu mmodzi ndi Atate? M’chaputala chimodzimodzicho, vesi 18, Yohane analemba kuti: ‘Palibe aliyense [“palibe munthu,” KJ, Dy] anayamba wawonapo Mulungu; Mwana yekha [“mulungu wobadwa yekha,” NW], amene ali pa chifuwa cha Atate, wamdziŵikitsa.’ (RS) Kodi alipo munthu amene anawonapo Yesu Kristu, Mwanayo? Ndithudi! Chotero, pamenepo, kodi Yohane anali kunena kuti Yesu anali Mulungu? Mwachiwonekere sichoncho. Chakumapeto kwa Uthenga wake Wabwino, Yohane anafotokoza mwachidule nkhaniyo mwakumati: “Zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Kristu, [osati Mulungu, koma] Mwana wa Mulungu.”—Yoh. 20:31, RS.
Kodi kunena modabwa kwa Tomasi pa Yohane 20:28 kumatsimikizira kuti Yesu alidi Mulungu?
Yoh. 20:28 imati: “Tomasi anayankha nati kwa iye, Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga.”
Palibe cholakwa kutcha Yesu kukhala “Mulungu,” ngati zimenezo ndizo zimene Tomasi anali kulingalira. Zimenezi zingakhale zogwirizana ndi kugwira mawu kwa Yesu mwiniyo m’Masalmo mmene amuna amphamvu, oweruza, anali kunenedwa kukhala “mulungu.” (Yoh. 10:34, 35; Sal. 82:1-6) Ndithudi, Kristu ali ndi malo a ntchito apamwamba kwambiri koposa amuna amenewo. Chifukwa cha kukhala ndi malo ake a ntchito apadera kwa Yehova, Yesu akutchulidwa pa Yohane 1:18 (NW) kukhala “mulungu wobadwa yekha.” (Wonaninso Ro, By.) Yesaya 9:6 amafotokozanso Yesu molosera kukhala “Mulungu Wamphamvu,” koma osati monga Mulungu Wamphamvuyonse. Zonsezi ziri zogwirizana ndi kufotokozedwa kwa Yesu kuti ali “mulungu,” kapena “waumulungu,” pa Yohane 1:1 (NW, AT).
Mawu apatsogolo ndi pambuyo amatithandiza kufika palingaliro loyenera pa mfundoyi. Mwamsanga imfa ya Yesu isanachitike, Tomasi anali atamva pemphero la Yesu m’limene anasonya kwa Atate wake kukhala “Mulungu wowona yekha.” (Yoh. 17:3) Pambuyo pa chiukiriro cha Yesu, Yesu anali atatumiza uthenga kwa atumwi ake kuphatikizapo Tomasi, mu umene anali atanena kuti: ‘Ndikwera . . . kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanu.’ (Yoh. 20:17) Pambuyo pa kulemba zimene Tomasi adanena pamene anawonadi ndi kukhudza Kristu woukitsidwayo, mtumwi Yohane anati: “Zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Kristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pa kukhulupirira mukhale nawo moyo m’dzina lake.” (Yoh. 20:31) Chotero, ngati aliyense watsimikiza kuchokera ku mawu odabwa a Tomasi kuti Yesu mwiniyo ali “Mulungu wowona yekha” kapena kuti Yesu anali “Mulungu Mwana” wa Utatu afunikira kuyang’ananso pa zimene Yesu mwiniyo adanena (vesi 17) ndi kuchitsimikizo chimene chafotokoza momvekera bwino ndi mtumwi Yohane (vesi 31).
Kodi Mateyu 1:23 amasonyeza kuti pamene Yesu anali padziko lapansi anali Mulungu?
Mat. 1:23: “Wonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake Emanueli; ndilo losandulika, Mulungu nafe (“Mulungu ali ndi ife,” NE].”
Polengeza kubadwa kumene kunalinkudza kwa Yesu, kodi mngelo wa Yehova adanena kuti mwanayo akakhala Mulungu mwiniyo? Ai, chilengezocho chinali chakuti: “Iye adzakhala wamkulu, ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba.” (Luka 1:32, 35; kanyenye wawonjezeredwa.) Ndipo Yesu mwini sananene konse kuti anali Mulungu koma, mmalo mwake, anali “Mwana wa Mulungu.” (Yoh. 10:36; kanyenye wawonjezeredwa.) Yesu anatumidwa m’dziko ndi Mulungu; chotero kupyolera mwa Mwana wobadwa yekha ameneyu, Mulungu anali ndi anthu.—Yoh. 3:17; 17:8.
Sikunali kwachilendo ponena za maina Achihebri kuphatikizamo liwu lonena za Mulungu kapena ngakhale mpangidwe wa chidule wa dzina lenileni la Mulungu. Mwachitsanzo, Eliyata limatanthauza “Mulungu Wadza”; Yehu limatanthauza “Yehova Ali Iye” Eliya amatanthauza “Mulungu Wanga Ndiye Yehova.” Koma palibe lirilonse la maina ameneŵa limene limapereka tanthauzo lakuti wokhala naloyo anali Mulungu mwiniyo.
Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la Yohane 5:18?
Yoh. 5:18: “Chifukwa cha ichi Ayuda anawonjeza kufuna kumupha sichifukwa cha kuswa dzuŵa la Sabata kokha, komatu amatchanso Mulungu Atate wake wa iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.”
Anali Ayuda osakhulupirira amene analingalira kuti Yesu anali kuyesayesa kudzipanga kukhala wolingana ndi Mulungu mwa kunena kuti Mulungu anali Atate wake. Pamene moyenerera anatcha Mulungu kukhala Atate wake, Yesu sananene konse kukhala wolingana ndi Mulungu. Iye molunjika anayankha Ayuda kuti: “Indetu, indetu, ndinena kwa inu, sakhoza Mwana kuchita kanthu payekha, koma chimene awona Atate achichita, ndicho.” (Yoh. 5:19; wonaninso Yohane 14:28; Yohane 10:36.) Anali Ayuda osakhulupirira omwewonso, amene adanena kuti Yesu anaswa Sabata, koma iwo analinso olakwa pa mfundoyo. Yesu anasunga Chilamaulo mosalakwitsa konse, ndipo analengeza kuti: “Kuloleka kuchita zabwino tsiku la Sabata.”—Mat. 12:10-12.
Kodi chenicheni chakuti kulambira kukuperekedwa kwa Yesu chimatsimikizira kuti Iye ali Mulungu?
Pa Ahebri 1:6, angelo akulangizidwa “kulambira” Yesu, mogwirizana ndi matembenuzidwe a RS, TEV, KJ, JB, ndi NAB. NW imati “kuŵeramira.” Pa Mateyu 14:33, ophunzira a Yesu akunenedwa kukhala ‘atamlambira,’ mogwirizana ndi RS, TEV, KJ; matembenuzidwe ena amanena kuti “anamsonyeza ulemu” (NAB), “anamgwadira” (JB), “kugwa pamapazi ake” (NE), “anamchitira ulemu” (NW).
Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “kulambira” ndilo pro·sky·neʹo limene A Greek-English Lexicon of the New Testament and Other Early Christian Literature limanenanso kuti “linagwiritsiridwa ntchito kutanthauza mwambo wakuŵerama pamaso pa munthu ndi kupsopsona mapazi ake, mpendero wa chovala chake, ndi pansi.” (Chicago, 1979, Bauer, Arndt, Gingrich, Danker; kope lachiŵiri Lachingelezi; p. 716) Limeneli ndiro liwu logwiritsiridwa ntchito pa Mateyu 14:33 kusonyeza zimene ophunzira anachita kwa Yesu; pa Ahebri 1:6 kusonyeza zimene angelo ayenera kuchitira Yesu; pa Genesis 22:5 m’Septuagint Yachigiriki kulongosola zimene Abrahamu anachitira Yehova ndi pa Genesis 23:7 kulongosola zimene Abrahamu anachita, mogwirizana ndi mwambo wa panthaŵiyo, kulinga kwa anthu amene anali kuchita nawo bizinesi; pa 1 Mafumu 1:23 m’Septuagint kulongosola kachitidwe ka mneneri Natani pofika kwa Mfumu Davide.
Pa Mateyu 4:10, Yesu anati: “Ambuye Mulungu wako udzamgwadira [kuchokera ku pro·sky·neʹo], ndipo iye yekhayekha udzamlambira.” (Pa Deuteronomo 6:13, pamene mwachiwonekere Yesu panopa akugwira mawu, pali dzina la Mulungu, Tetragrammaton.) Mogwirizana ndi zimenezo tiyenera kuzindikira kuti pro·sky·neʹo wokhala ndi mkhalidwe wa mtima ndi maganizo zimene ziyenera kulunjikitsidwa kwa Mulungu yekha.
Kodi zozizwitsa zochitidwa ndi Yesu zimatsimikizira kuti iye ali Mulungu?
Mac. 10:34, 38, RS: “Petro anatsegula pakamwa pake nati, . . . Mulungu anamdzoza Yesu wa ku Nazarete, ndi mzimu woyera ndi mphamvu; . . . anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdyerekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi iye.” (Motero Petro mwa zozizwitsa zimene anawona sananene kuti Yesu anali Mulungu, koma mmalo mwake, kuti Mulungu anali ndi Yesu. Yerekezerani ndi Mateyu 16:16, 17.)
Yoh. 20:30, 31: “Ndipo zizindikiro [“zozizwitsa,” TEV, Kx] zina zambiri Yesu anazichita pamaso pa akuphunzira ake, zimene sizinalembedwa m’bukhu iri; koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Kristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nawo moyo m’dzina lake.” (Chotero chitsimikizo chimene moyenerera tiyenera kupeza kuchokera ku zozizwitsa nchakuti Yesu ndiye “Kristuyo,” Mesiya, “Mwana wa Mulungu.” Mawu akutiwo “Mwana wa Mulungu” ngosiyana kwambiri ndi akuti “Mulungu Mwana.”)
Aneneri a nyengo ya Chikristu chisanakhale monga Eliya ndi Elisa anachita zozizwitsa zofanana ndi zimene Yesu anachita. Chikhalirechobe zimenezo siziridi umboni wakuti iwo anali Mulungu.
Kodi Yesu ali Wofanana ndi Yehova mu “Chipangano Chakale”?
Wonani 421, 422, pamutu waukulu wakuti “Yehova.”
Kodi kukhulupirira Yesu Kristu ndiko chofunika chokha kaamba ka chipulumutso?
Mac. 16:30-32, RS: “Amuna inu, ndichitenji kuti ndipulumuke? Ndipo iwo [Paulo ndi Sila] anati, Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi a pabanja ako.’ Ndipo anamuuza iye mawu a Ambuye [“Mulungu,” mawu amtsinde a NAB, ndiponso JB ndi NE; “Uthenga wa Mulungu,” AT], pamodzi ndi onse apabanja pake.” (Kodi ‘kukhulupirira mwa Ambuye Yesu’ kwa mwamunayo kunali kokha nkhani ya kunena kwake mowona mtima kuti anakhulupirira? Paulo anasonyeza kuti zowonjezereka zinali kufunika—ndiko kuti, chidziŵitso ndi kuvomerezedwa kwa mawu a Mulungu, monga momwe Paulo ndi Sila kenako anapitirizira kuwalalikira kwa wosunga ndende. Kodi chikhulupiriro cha munthuyo mwa Yesu chingakhale chowona mtima ngati iye sanalambire Mulungu amene Yesu anamlambira, ngati sanagwiritsire ntchito zimene Yesu anaphunzitsa ponena za mtundu wa anthu umene ophunzira ake ayenera kukhala, kapena ngati sanachite ntchito imene Yesu analamulira omtsatira kuchita? Sitingalipidwe chipulumutso; chiri chotheka kokha pamaziko a kukhulupirira mtengo wa nsembe ya moyo waumunthu wa Yesu. Koma miyoyo yathu iyenera kukhala yogwirizana ndi chikhulupiriro chimene tikunena kuti tiri nacho, ngakhale kuli kwakuti kungaphatikizepo mavuto. Pa Mateyu 10:22 Yesu anati: “Iye wakupirira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa.”
Kodi Yesu anali ndi moyo kumwamba asanakhale munthu?
Akol. 1:15-17: “[Yesu] ali fanizo la Mulungu wosawonekeyo, wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse . . . Zinthu zonse zinalengedwa kupyolera mwa Iye ndi kwa Iye. Ndipo Iye ali woyamba wa zonse.”
Yoh. 17:5: “[M’pemphero Yesu anati:] Atate inu, lemekezani ine ndi inu nokha ndi ulemelero umene ndinali nawo ndi inu lisanakhale dziko lapansi.” (Ndiponso Yohane 8:23)
Kodi Yesu ali ndi thupi lake lanyama kumwamba?
1 Akor. 15:42-50: “Chomwechonso kudzakhala kuuka kwa akufa. Lifesedwa m’chivundi, liukitsidwa m’chisavundi. . . . Lifesedwa thupi lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu . . . Koteronso kwalembedwa, ‘Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo.’ Adamu wotsirizayo [Yesu Kristu, amene anali munthu wangwiro monga momwe analiri Adamu pachiyambi] anakhala mzimu wa kulenga moyo. . . . Ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kuloŵa Ufumu wa Mulungu; kapena chivundi sichiloŵa chisavundi.” (Kanyenye wawonjezeredwa.)
1 Pet. 3:18: “Kristunso adamva zoŵaŵa kamodzi, chifukwa cha machimo athu, . . . wophedwatu m’thupi, koma wopatsidwa moyo m’mzimu [“mu mzimu,” NE, AT, JB, Dy].” (Wonani tsamba 107, 108.)
Fanizo: Ngati munthu alipirira ngongole bwenzi lake ndiyeno mwamsanga atenganso malipirowo, mwachiwonekere ngongoleyo imapitirizabe. Mofananamo, ngati, pamene anaukitsidwa, anatenganso thupi lake laumunthu lanyama ndi mwazi limene linali litaperekedwa nsembe kulipirira mtengo wa dipo, kodi chimenecho chikanakhala ndi chiyambukiro chotani pakakonzedwe kamene anali kupanga ka kulanditsa anthu okhulupirika pamangaŵa a uchimo?
Nzowona kuti Yesu anawonekera kwa ophunzira ake mumpangidwe wathupi pambuyo pa chiukiriro chake. Koma panthaŵi zina, kodi nchifukwa ninji iwo sanamzindikire pakumuwona koyamba? (Luka 24:15-32; Yoh. 20:14-16) Panthaŵi ina, kuti athandize Tomasi, Yesu anawonekera ndi umboni wakuthupi wa zipsera za misomali mmanja ake ndi bala lamkondo m’nthiti mwake. Koma kodi kunali kotheka motani kwa iye panthaŵi imeneyo kuwonekera mwadzidzidzi pakati pawo ngakhale kuli kwakuti makomo anali otsekedwa? (Yoh. 20:26, 27) Mwachiwonekere Yesu anavala matupi panthaŵi zimenezi, monga momwe angelo anali atachitira kalelo pamene anawonekera kwa anthu. Kuwononga thupi lanyama la Yesu panthaŵi ya chiukiriro chake sikunali vuto kwa Mulungu. Mokondweretsa, ngakhale kuli kwakuti thupilo silinasiyidwe ndi Mulungu m’manda (mwachiwonekere kulimbikitsa chikhutiro cha ophunzirawo chakuti Yesu anali ataukadi), zovala za bafuta zimene anakulungidwamo zinasiyidwa mmenemo; chikhalirechobe, Yesu woukitsidwayo nthaŵi zonse anawonekera ali wovala mokwanira.—Yoh. 20:6, 7.
Kodi Yesu Kristu ali munthu mmodzimodzi ndi Mikaeli mngelo wamkulu?
Dzina la Mikaeli ameneyu limawonekera nthaŵi zisanu zokha m’Baibulo. Munthu wauzimu waulemerero wokhala ndi dzinali amatchulidwa kukhala “mmodzi wa akalonga aakulu,” “kalonga wamkulu wokhala ndi ulamuliro pa anthu ako [Danieli],” ndipo monga “mngelo wamkulu.” (Dan. 10:13; 12:1; Yuda 9) Mikaeli limatanthauza “Ndani Ali Wofanana ndi Mulungu?” Dzinalo mwachiwonekere likusonyeza Mikaeli kukhala wotsogoza m’kuchirikiza ufumu wa Yehova ndi kuwononga adani a Mulungu.
Pa 1 Atesalonika 4:16, lamulo la Yesu Kristu lakuti chiukiriro chiyambe lafotokozedwa kukhala “mfuu ya mngelo wamkulu,” ndipo Yuda 9 amanena kuti mngelo wamkuluyo ndiye Mikaeli. Kodi kungakhale koyenerera kuyerekezera mfuu yolamula ya Yesu ndi ya munthu aliyense wokhala ndi ulamuliro wocheperapo? Pamenepa, mwachiwonekere, Mikaeli mngelo wamkulu ndiye Yesu Kristu. (Mokondweretsa, mawu akuti “mngelo wamkulu” sakupezedwa mu mpangidwe wa zochuluka m’Malemba, motero kupereka tanthauzo lakuti kuli mmodzi yekha.)
Chiv. 12:7-12 chimanena kuti Mikaeli ndi angelo ake akachita nkhondo ndi Satana ndi kumponyera iye ndi angelo ake oipa kuchokera kumwamba panthaŵi ya kupatsidwa ulamuliro waufumu kwa Kristu. Pambuyo pake Yesu akulongosoledwa kukhala akutsogolera magulu ankhondo kumwamba kumenyana ndi mitundu ya dziko. (Chiv. 19:11-16) Kodi sikuli koyenera kuti Yesu akakhalanso iye amene angachitepo kanthu motsutsana ndi munthu wolongosoledwa kukhala ‘wolamulira wa dziko lino,’ Satana Mdyerekezi? (Yoh. 12:31) Danieli 12:1 amagwirizanitsa ‘kuimirira kwa Mikaeli’ kuchitapo kanthu mwaukumu ndi ‘nthaŵi ya masautso, imene siinakhalepo yotero kuyambira kukhalako kwa mtundu wa anthu kufikira nthaŵi yomwe ija.’ Ndithudi zimenezo zikayenereradi chokumana nacho cha amitundu pamene Kristu monga wolipsira wakumwamba achitapo kanthu motsutsana nawo. Motero umboni ukusonyeza kuti Mwana wa Mulungu anali kudziŵika monga Mikaeli asanadze kudziko lapansi ndipo amadziŵikanso ndi dzinalo chiyambire pamene anabwerera kumwamba kumene amakhala monga Mwana wauzimu wolemekezedwa wa Mulungu.
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Simumakhulupirira Yesu’
Mungayankhe kuti: ‘Mwachiwonekere inu mumakhulupirira Yesu. Inenso ndimatero; ngati sizinali zotero sindikanakhala pakhomo lanu lerolino.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Kwenikweni, kufunika kwa kukhulupirira Yesu kwasonyezedwa kwambiri m’mabukhu athu. (Tembenukirani chaputala choyenerera m’bukhu lirilonse limene mukugaŵira ndipo ligwiritsireni ntchito kukhala maziko a kukambitsirana, mukumagogomezera ntchito yake monga Mfumu. Kapena ŵerengani zofotokozedwa patsamba 2 la Nsanja ya Olonda, ponena za chifuno cha magazine.)’
Kapena munganene kuti: ‘Kodi mungalole kuti ndikufunseni kuti nchifukwa ninji mumalingalira motero?’
Kuthekera kwina: ‘Mwachiwonekere munthu wina anakuuzani zimenezo, koma ndingakuuzeni kuti zimenezo siziridi choncho, chifukwa chakuti tiri ndi chikhulupiriro champhamvu kwambiri mwa Yesu Kristu.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Koma sitimakhulupirira zonse zimene anthu amanena ponena za Yesu. Mwachitsanzo, ena amanena kuti anali munthu wabwino chabe, sanali Mwana wa Mulungu. Sitimakhulupirira zimenezo, kodi inu mumatero? . . . Baibulo silimaphunzitsa zimenezo.’ (2) ‘Ndipo sitimakhulupirira ziphunzitso za magulu amene amatsutsa zimene Yesu mwini adanena ponena za unansi wake ndi Atate wake. (Yoh. 14:28) Atate wake wampatsa mphamvu ya kulamulira imene imayambukira miyoyo ya ife tonse lerolino. (Dan. 7:13, 14)’
‘Kodi mumavomereza Yesu kukhala Mpulumutsi wanu?’
Mungayankhe kuti: ‘Baibulo limanena momvekera . . . (Gwirani mawu Machitidwe 4:12). Ndimakhulupirira zimenezo. Koma ndaphunziranso kuti pali mathayo aakulu oyenderana nako. Kodi ziri choncho motani? Eya, ngati ndikhulupiriradi Yesu, pamenepo sindingakhulupirire kokha malinga ngati kukuwonekera kukhala koyenera.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Moyo wake wangwiro woperekedwa nsembe umatitheketsa kupeza chikhululukiro cha machimo. Koma ndidziŵa kuti kulinso kufunika kulabadira malangizo ake onena za mathayo athu monga Akristu. (Mac. 1:8; Mat. 28:19, 20)’
Kapena munganene kuti: ‘(Pambuyo pa kutsimikizira chenicheni chakuti mumakhulupirira Yesu kukhala Mpulumutsi, osati kokha wa inu nokha, koma wa onse okhulupirira . . . ) Nkofunika kuti tilabadire moyamikira osati kokha zimene anachita kalero komanso zimene akuchita tsopano. (Mat. 25:31-33)’
‘Ndinavomereza Yesu kukhala Mpulumutsi wanga’
Mungayankhe kuti: ‘Ndakondwera kumva kuti mumakhulupirira Yesu, chifukwa chakuti pali anthu ochuluka kwambiri lerolino amene samalingalira zimene Yesu anatichitira. Inu mosakaikira mumadziŵa bwino lomwe lemba la Yohane 3:16, kodi sichoncho? . . . Koma kodi nkuti kumene anthu ameneŵa adzakhala ndi moyo kosatha? Ena adzakhala ndi Kristu kumwamba. Koma kodi Baibulo limasonyeza kuti anthu onse abwino amapita kumeneko? (Mat. 6:10; 5:5)’