Kodi Kuthetsa Nkhaniyo Kwatengeranji Nthaŵi Yaitali Chotero?
ZAKA 6,000 zapitazo, ufumu wa Mulungu sunali pamlandu. Pamene anamaliza ntchito zake zolenga zozizwitsa, “anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.” (Genesis 1:31) Kenaka iye analoŵa m’nyengo yaitali ya “kupumula”; ndithudi, osati kuti iye anatopa mwakuthupi. Mmalomwake, iye anapumula m’chakuti analeka ntchito zake zolenga padziko lapansi, ali ndichidaliro kuti chifuno chake chabwino kulinga ku izo chikakwaniritsidwa mwachipambano.—Genesis 2:1-3; Yesaya 55:11.
Kodi chifuno chimenecho chinali chiyani? Yehova anaika anthu aŵiri oyambirira m’munda wotchedwa Edene. Thayo lawo loyambirira linali kusamalira mudzi wawo wa paradaiso, kuphatikizapo nyama zamoyo zosiyanasiyana. Ndiponso, iwo anafunikira kubala ndi kulera ana. M’kupita kwa nthaŵi, pamene banja lawo likakula, iwo anafunikira kufutukulira Paradaiso ameneyo kumalekezero adziko lapansi pomvera lamulo la Mulungu la ‘kuligonjetsa dziko lapansi.’ Chotero, dziko lapansi pomalizira pake likakhala mudzi waukulu, wodzazidwa ndi banja lachimwemwe, logwirizana lotumikira Atate wawo wakumwamba. Chimenecho ndicho chinali chifuno choyambirira cha Mulungu.—Genesis 1:27, 28; 2:8, 15, 20-22.
Kodi Adamu ndi Hava akakhalamo ndi phande m’kukwaniritsa chifuno chachikulu chimenechi kufikira kumapeto? Zimenezo zikadalira pa kupitiriza kwawo kugwirizana ndi kumvera Mlengi wawo. Chimvero chawo sichinali chochitidwa mwakhungu, popanda kulingalira. Makolo athu oyamba anapatsidwa ufulu wodzisankhira, popeza kuti Mulungu anafuna kuti iwo amtumikire ndi mtima woyamikira. Monga chokumbutsa chowonekera cha kuyenera kwake kwa kulamulira, iye anawapatsa chiyeso chokhweka. Iwo akanatha kudyako zakudya zirizonse za m’mundamo kuchotsapo chimodzi chokha. Mudali mtengo wa zipatso womwe Mulungu ananena motere za uwo: “Tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.”—Genesis 2:16, 17.
Mawu ameneŵa akutiuza kuti Adamu ndi Hava sanalengedwe kuti akalambe ndi kumwalira. Imfa ikadza kokha ngati sanamvere lamulo lokhweka limeneli. Ngati Adamu ndi Hava akanakhalabe omvera kwa Mulungu, iwo akanakhala adakali ndi moyo padziko lapansi lerolino monga makolo a banja la ana angwiro lapadziko lonse.—Onani lamulo lamakhalidwe abwino lofotokozedwa pa Salmo 37:29.
Komabe, chimodzi cha zolengedwa zaungelo za Mulungu, chomwe tsopano chikutchedwa Satana, chinakhala chosuliza njira ya kulamulira kwa Mulungu. Iye anakakamiza Hava kudya chipatso choletsedwacho, mwachinyengo akumapereka lingaliro lakuti mwakukhala wosadalira pa ulamuliro wa Mulungu, iye akakhala bwinopo. Komabe, cholinga chenicheni cha Satana chinali chikhumbo chakukhala mulungu wa banja la anthu lomayembekezeredwalo.—Genesis 3:1-5; Mateyu 4:8, 9; Yohane 8:44.
Popeza kuti Yehova anaŵapatsa anthu aŵiri oyambirirawo chirichonse chomwe anachifunikira, Hava akanachilikiza ufumu wake ndikukana lingaliro lonama la Satana. Komabe, mwatsoka, iye analivomereza naswa lamulo la Mulungu. Pambuyo pake, Adamu anasankha kugwirizana ndi mkazi wake m’njira yake yopanda nzeru. Chotero okwatirana odzifunirawo, limodzi ndi Satana, anapandukira Mulungu, ndipo nkhani ya ulamuliro waumulungu inadzutsidwa.—Genesis 3:6.
Nthaŵi Inafunikira Kuthetsa Nkhani Zofunikazo
Yehova akanawononga opanduka atatuwo panthaŵi yomweyo. Komatu zimenezo sizikanathetseratu mafunso omwe kupanduka kwawo kunadzutsa. Kodi munthu akanatha kudzilamulira yekha mwachipambano popanda Mulungu? Kodi kunali kolungama kwa Mulungu kufuna chigonjero ku ulamuliro wake? Kuwonjezerapo, polingalira mkhalidwe wa okwatirana oyambawo, kodi anthu ena aliwonse akakhoza kusankha mopanda dyera kutumikira Mulungu modzifunira—ngakhale pamene ayesedwa ndi Satana? (Yobu 1:7-11; 2:4) Zikatenga nthaŵi kuyankha mafunso ameneŵa. Kukatenganso nthaŵi kulaka ziyambukiro za kupanduka koyambako ndi kukwaniritsa chifuno cha Mulungu chakupanga dziko lapansi kukhala paradaiso wokhalidwa ndi fuko la anthu losachimwa. Tidakadikirirabe chigamulo chomalizira cha nkhanizi.
Mogwirizana ndi lamulo lake, Mulungu anachotsera Adamu ndi Hava mwaŵi wakukhala ndi moyo kosatha. Iwo sanalinso oyenerera kukhala ndi phande m’kukwaniritsa chifuno chake chachikulu. Komabe, iwo asanamwalire, analoledwa kubala ndi kulera ana. Zowonadi, Adamu ndi Hava sakanakhozanso kupatsira ana awo moyo wathanzi, wosachimwa. (Aroma 5:12) Koma ngakhale kuti mibadwo yomwe inatsatirapo inabadwa yopanda ungwiro ndipo yoweruzidwa ku imfa, anthu ambiri anali ndi mwaŵi wakusonyeza mbali yomwe akachilikiza ponena za nkhani yaikulu ya ufumu.
Kuthetsa Nkhaniyo
Kodi Mulungu adzathetsa motani nkhani zokhudza ufumu wakezi? M’lingaliro limodzi mafunso omwe anadzutsidwa kalelo mu Edene ayankhidwa tsopano. Zaka zikwi zambiri za mbiri ya anthu zachipanga kukhala chowonekeratu kuti zinenezo za Satana zakuti Hava akakhala bwinoko popanda kudalira pa Mulungu zinali bodza. Ulamuliro wa anthu umene umanyalanyaza Mulungu wakhala wolephera kosalekeza. Monga momwe Baibulo likunenera kuti: ‘Wina apweteka mnzake pomlamulira.’—Mlaliki 8:9.
Kumbali ina, zinthu zina zambiri zabwino zalembedwa mkati mwa zaka zambiri chiyambire kuchimwa kwa Adamu ndi Hava. Anthu ambiri asonyeza kumamatira kosasweka ku ulamuliro wa Yehova, chitsanzo chabwino koposa chikumakhala cha “Mwana wa munthu,” Yesu Kristu iyemwini. (Mateyu 20:18; Ahebri 11:1–12:3) Anthu omwe atsatira malamulo a Mulungu ndikuvomereza ulamuliro wake apeza kuti iyi ndiyodi njira yabwino koposa. Iwo akumana ndi chowonadi cha mwambi uwu: ‘Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.’ (Miyambo 10:22) Kuwonjezerapo, chiyamikiro chinke ku makonzedwe a chiukiriro, popeza kuti iwo pomalizira pake adzakhala ndi phande m’kukwaniritsa chifuno chachikulu cha Mulungu.—Yohane 5:28, 29.
Yehova sanaiŵale chifuno chake choyambirira. Anthu amene amakana ufumu wake sadzaloledwa kulamulira dziko lapansi kwanthaŵi yonse, ndipo Baibulo likuchenjeza kuti posachedwapa Mulungu adzachitapo kanthu motsutsana nawo. Timaŵerenga kuti: ‘Mkwiyo wa Mulungu wochokera kumwamba, uwonekera pa chisapembedzo chonse.’ (Aroma 1:18) Kudza kwa mkwiyo wa Mulungu kumeneku, kumene Baibulo limakutcha Armagedo, mosakaikira kudzasonyeza kuti iye alikodi. Kokha awo amene amavomereza ufumu wake ndiwo adzapulumuka chochitika chimenecho. ‘Pakuti owongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko.’—Miyambo 2:21, 22.
Nkhani Yaikuluyo ndi Inu
Polingalira nsonga zonsezi, aliyense wa ife—mofanana ndi Adamu ndi Hava—ayenera kupanga chosankha. Kodi tidzayesera kukhala ndi moyo osadalira pa Mulungu? Kapena kodi tidzagonjera ku ufumu wake? Kumbukirani kuti, imeneyi ndiyo nkhani yaikulu koposa yomwe mukuyang’anizana nayo lerolino. Nkhani zina, ngakhale kuti zingawoneke kukhala zofunika, zimayambukira moyo wanu panthaŵi ino. Nkhaniyi njokhudza moyo wosatha. Chosankha chimene mudzachipanga chidzayambukira mtsogolo mwanu mwamuyaya.
Kodi mungasonyeze motani kuti mukuvomereza ufumu wa Mulungu? Mwakuphunzira mwakhama Mawu ake, Baibulo, ndikufuna kumvera chifuniro chake mogwirizana ndi Akristu ena owona. (Zefaniya 2:2, 3) Mutachita zimenezo, mudzakhala ndi chiyembekezo chachimwemwe chakuwona kukwaniritsidwa kwa chifuno chachikulu cha Mulungu. Mudzawonanso kukwaniritsidwa kwa lonjezo lodabwitsa ili: ‘Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.’ (Salmo 37:10, 11) Ha, nchotulukapo chodabwitsa chotani nanga kwa onse ogonjera ku ufumu wa Mulungu! Nchifukwa champhamvu chotani nanga chosankhira mwanzeru m’nkhani yofunika koposa imeneyi!