Kodi Ndani Kwenikweni Amene Ali ndi Chiitano Chakumwamba?
YEHOVA amalikonda fuko la anthu. Eya, chikondi chimenechi nchachikulu kwakuti anapereka Mwana wake, Yesu Kristu, monga dipo kuwombola chimene kholo lathu Adamu anataya! Kodi chimenecho chinali chiyani? Moyo waumunthu wamuyaya, wangwiro limodzi ndi zoyenerera zake ndi ziyembekezo. (Yohane 3:16) Dipolo lidalinso chisonyezero cha chikondi cha Yesu kwa anthu.—Mateyu 20:28.
Chikondi chaumulungu chinasonyezedwa mwakutsegula ziyembekezo ziŵiri zoperekedwa ndi Mulungu pamaziko a nsembe yadipo ya Yesu. (1 Yohane 2:1, 2) Yesu asanamwalire monga munthu, chiyembekezo chokha chomwe chinalipo kwa awo omwe anali ndi chivomerezo chaumulungu chinali cha moyo padziko lapansi laparadaiso. (Luka 23:43) Komabe, pambuyo pa Pentekoste wa 33 C.E., Yehova anapereka chiyembekezo chakumwamba kwa “kagulu ka nkhosa.” (Luka 12:32) Koma kodi chachitika nchiyani m’nthaŵi zaposachedwapa? Chiyambire 1931 uthenga Waufumu wakhala ukusumika chisamaliro pa “nkhosa zina,” ndipo kuchokera 1935 kunka mtsogolo Mulungu wakhala akudzisonkhanitsira ‘khamu lalikulu’ la onga nkhosa amenewo kupyolera mwa Kristu. (Yohane 10:16; Chibvumbulutso 7:9) Mulungu waika mumtima mwawo chiyembekezo cha moyo wamuyaya padziko lapansi laparadaiso. Iwo amafuna kudya chakudya changwiro, kukhala ndi ulamuliro wachikondi pa zinyama, ndi kusangalala ndi mayanjano ndi anthu olungama anzawo kosatha.
Ansembe ndi Mafumu Achifundo
Popeza kuti chikondi ndicho chinasonkhezera Yesu kupereka moyo wake monga dipo, ndithudi adzakhala Mfumu yakumwamba yachifundo. Komabe, Yesu sadzakhala yekha m’kupangitsa anthu kukhala angwiro mu Ulamuliro wake wa Zaka Chikwi. Yehova wapereka makonzedwe a mafumu ena achifundo kumwamba. Inde, ‘adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi iye zaka chikwizo.’—Chibvumbulutso 20:1-6.
Kodi Kristu adzakhala ndi olamulira anzake angati, ndipo kodi amasankhidwa motani kaamba ka mwaŵi wozizwitsa umenewo? Eya, mtumwi Yohane anawona okwanira 144,000 ali pa Phiri la Ziyoni lakumwamba limodzi ndi Mwanawankhosa, Yesu Kristu. Pokhala ‘anagulidwa kuchokera kudziko,’ iwo adzadziŵa chimene kukumana ndi ziyeso, kupirira mavuto a kupanda ungwiro, kuvutika, ndi kufa monga anthu kumatanthauza. (Chibvumbulutso 14:1-5; Yobu 14:1) Chotero, iwo adzakhala mafumu ndi ansembe achifundo chotani nanga!
Umboni wa Mzimu
Anthu 144,000 amenewo ‘ali nako kudzoza kochokera kwa woyerayo,’ Yehova. (1 Yohane 2:20) Kuli kudzozedwa kwa chiyembekezo chakumwamba. Mulungu ‘wasindikiza chizindikiro chake, nawapatsa chikole cha mzimu mu mitima yawo.’—2 Akorinto 1:21, 22.
Inde, awo okhala ndi chiitano chakumwamba ali ndi umboni wa mzimu wa Mulungu umene umatsimikiza zimenezo. Ponena za chimenechi, Paulo analemba motere pa Aroma 8:15-17: ‘Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nawo, kuti, Abba, Atate. Mzimu wokha uchita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu; ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi iye.’ Odzozedwa amafuula kuti “Abba, Atate.” kupyolera mwa mzimu wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito.
Umboni waukulu wakuti munthu wadzozedwa ku chiitano chakumwamba ndiwo mzimu, kapena lingaliro lokhalirira la umwana. (Agalatiya 4:6, 7) Munthu woteroyo amakhala wotsimikiza kotheratu kuti wadzozedwa ndi Mulungu kukhala mwana wauzimu monga mmodzi wa a 144,000 oloŵa nyumba a Ufumu wakumwamba. Iye angatsimikize kuti chiyembekezo chake chakumwamba sichiri chikhumbo chodzikulitsira yekha kapena kuyerekeza kwake; mmalomwake, nchochokera kwa Yehova monga chotulukapo cha kachitidwe ka mzimu wa Mulungu kulinga kwa iye.—1 Petro 1:3, 4.
Pansi pa chisonkhezero cha mzimu woyera wa Mulungu, mzimu, kapena maganizo okhalirira, wa odzozedwa umachita monga mphamvu yosonkhezera. Iwo umawafulumiza kuvomereza ku zimene Mawu a Mulungu akunena ponena za chiyembekezo chakumwamba. Iwo amavomerezanso ku zochita za Yehova ndi iwo kupyolera mwa mzimu woyera. Chotero, iwo amakhala otsimikiza kuti ali ana auzimu a Mulungu ndi oloŵa nyumba.
Pamene odzozedwa aŵerenga zimene Mawu a Mulungu amanena ponena za ana ake auzimu ndi chiyembekezo chakumwamba, chikhoterero chawo chapachokha chimachititsa kudziuza kuti, ‘Ichi chikunena za ine!’ Inde, iwo amavomereza mwachimwemwe pamene Mawu a Atate wawo alonjeza mphotho yakumwamba. Iwo amati, ‘Ichi chikunena za ine!’ pamene aŵerenga kuti: “Okondedwa, tsopano tiri ana a Mulungu.” (1 Yohane 3:2) Ndipo pamene odzozedwa aŵerenga kuti Mulungu anagula anthu kuti ‘akhale ngati zipatso zoundukula za zolengedwa zake,’ chikhoterero chawo cha m’maganizo chimakhala kuvomereza kuti, ‘Inde, iye anandigula kaamba ka chifuno chimenecho.’ (Yakobo 1:18) Iwo amadziŵa kuti ‘anabatizidwa mwa Kristu Yesu’ ndi mu imfa yake. (Aroma 6:3) Chotero iwo ali ndi chikhutiro cholimba chakukhala mbali ya thupi lauzimu la Kristu ndikusangalala ndi chiyembekezo chakupyola imfa yofanana ndi yake ndi kuukitsidwira ku moyo wakumwamba.
Kuti aloŵe Ufumu wakumwamba, odzozedwa ayenera ‘kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe awo.’ (2 Petro 1:5-11) Iwo amayenda ndi chikhulupiriro ndikupitirizabe kukula mwauzimu, monga momwe amachitira awo amene ali ndi chiyembekezo chapadziko lapansi. Chotero, kodi nchiyaninso chimene chimachitira umboni mzimuwo?
Chifukwa Chake Amadya
Akristu odzozedwa samafuna kupita kumwamba chifukwa chosakhutira ndi moyo wapadziko lapansi walerolino. (Yerekezerani ndi Yuda 3, 4, 16.) Mmalomwake, mzimu woyera umachita umboni ndi mzimu wawo kuti ali ana a Mulungu. Iwo ngotsimikizanso kuti atengedwera m’pangano latsopano. Anthu amene ali m’pangano limeneli ndi Yehova Mulungu ndi Israyeli wauzimu. (Yeremiya 31:31-34; Agalatiya 6:15, 16; Ahebri 12:22-24) Pangano limeneli, logwira ntchito mwa mwazi wokhetsedwa wa Yesu, limatenga anthu a dzina la Yehova ndikupanga Akristu odzozedwa ameneŵa kukhala mbali ya ‘mbewu’ ya Abrahamu. (Agalatiya 3:26-29; Machitidwe 15:14) Pangano latsopano limagwira ntchito kufikira Aisrayeli auzimu onse aukitsidwira ku moyo wosakhoza kufa kumwamba.
Kuwonjezerapo, awo amene mowonadi ali ndi chiitano chakumwamba alibe chikaikiro chakuti alinso m’pangano la Ufumu wakumwamba. Yesu anasonya ku pangano limeneli pakati pa iyemwini ndi atsatiri ake pamene anati: ‘Inu ndinu amene munakhala ndi ine chikhalire m’mayesero anga; ndipo ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira ine, kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu ufumu wanga; ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli.’ (Luka 22:28-30) Pangano limeneli linakhazikitsidwa kwa ophunzira a Yesu mwa kukhala kwawo odzozedwa ndi mzimu woyera patsiku la Pentekoste wa 33 C.E. Ilo limakhalabe logwira ntchito pakati pa Kristu ndi mafumu anzake kosatha.—Chibvumbulutso 22:5.
Awo okhala ndi chiitano chakumwamba ngotsimikiza kuti ali m’pangano latsopano ndi pangano la Ufumu. Chotero, moyenerera amadyako mkate ndi vinyo zophiphiritsira pa zikumbukiro zachaka ndi chaka za Mgonero wa Ambuye, kapena Chikumbutso cha imfa ya Yesu Kristu. Mkate wopanda chotupitsawo umaphiphiritsira thupi laumunthu losachimwa la Yesu, ndipo vinyo amaphiphiritsira mwazi wangwiro wokhetsedwa pa imfa ndi kutsimikizira pangano latsopano.—1 Akorinto 11:23-26.
Ngati Yehova wakulitsa mwa inu chiyembekezo chosakanika cha moyo wakumwamba, mukudalira pa icho. Mumapereka mapemphero osonyeza chiyembekezo chimenecho. Chimakukutani, ndipo simungathe kuchichotsa m’dongosolo lanu. Mumakhala ndi changu choyaka moto cha zinthu zauzimu. Koma ngati ndinu wogaŵanikana ndi wosatsimikiza, pamenepo ndithudi simuyenera kudyako ziphiphiritso za Mgonero wa Ambuye.
Nchifukwa Ninji Pamakhala Malingaliro Olakwa?
Ena angadye molakwika ziphiphiritso za Chikumbutso chifukwa chakuti samazindikira kwenikweni kuti kudzozedwa ‘sikufuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu.’ (Aroma 9:16) Sichiri kwa munthuyo kusankha kuti angakonde kutengedwera m’pangano latsopano ndikukhala woloŵa nyumba mnzake wa Kristu mu Ufumu wakumwamba. Chosankha cha Yehova ndicho chiri nkanthu. Mu Israyeli wakale, Mulungu anasankha awo omwe akatumikira monga ansembe ake, ndipo anapha Kora chifukwa chofuna mwansontho utumiki waunsembe woikidwa mwaumulungu pa banja la Aroni. (Eksodo 28:1; Numeri 16:4-11, 31-35; 2 Mbiri 26:18; Ahebri 5:4, 5) Mofananamo, kukakhala kosakondweretsa Yehova ngati munthu anadziika yekha kukhala woitanidwa pakati pa mafumu ndi ansembe akumwamba pamene Mulungu sanampatse chiitano choterocho.—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 5:24, 25.
Munthu angalingalire molakwa kuti ali ndi chiitano chakumwamba chifukwa cha malingaliro amphamvu ochititsidwa ndi mavuto oipitsitsa. Imfa ya wamuukwati kapena tsoka lina lingapangitse munthu kutaya chikondwerero m’moyo wapadziko lapansi. Kapena bwenzi lapamtima linganene kukhala lodzozedwa, ndipo munthu angakhumbe kukhala ndi chonulirapo chofananacho. Mfundo zimenezo zingampangitse kulingalira kuti moyo wakumwamba ngoyenerera kwa iye. Koma umu simmene Mulungu amapatsira munthu aliyense mzimu wa umwana. Kukasonyeza kusoŵeka kwa chiyamikiro cha chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi ngati munthu akakhumba kupita kumwamba chifukwa cha mikhalidwe yosakhumbirika kapena kupsinjika kwa moyo wapadziko lapansi.
Malingaliro akale achipembedzo angapangitsenso munthu kutsimikiza molakwa kuti ali ndi chiitano chakumwamba. Mwinamwake iye poyamba ankayanjana ndi chipembedzo chonyenga chimene chinapereka lingaliro la moyo wakumwamba kukhala chiyembekezo chokha cha okhulupirika. Chotero, Mkristu afunikira kuchenjera ndi kupeyutsidwa ndi malingaliro ndi maganizo olakwika akale.
Kusanthula Kosamalitsa Nkofunika
Mfundo yofunika koposa inapangidwa ndi mtumwi Paulo pamene analemba kuti: ‘Chifukwa chake yense amene akadya mkate, kapena akamwera chikho cha Ambuye kosayenera, adzakhala wochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye. Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate, ndi kumwera chikho. Pakuti iye wakudya ndi wakumwa, adya namwa chiweruziro kwa iye yekha, ngati sazindikira thupilo.’ (1 Akorinto 11:27-29) Chotero, Mkristu wobatizidwa amene posachedwapa anayamba kulingalira kuti analandira chiitano chakumwamba ayenera kulingalira nkhaniyo mosamalitsa ndi mwapemphero.
Munthu woteroyo angadzifunse kuti: ‘Kodi ena andisonkhezera kusangalala ndi lingaliro la moyo wakumwamba?’ Ichi chikakhala chosayenerera, popeza kuti Mulungu sanapatse wina aliyense ntchito yomemeza ena kaamba ka mwaŵi woterowo. Chikhoterero chirichonse cha maloto sichingakhale chisonyezo chakudzozedwa ndi Mulungu, ndipo iye samadzoza oloŵa Ufumu mwakuwapangitsa kumva mawu okhala ndi uthenga wa chiitanocho.
Ena angadzifunse kuti: ‘Ndisanakhale Mkristu, kodi ndinagwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa? Kodi ndimagwiritsira ntchito mankhwala amene amayambukira malingaliro? Kodi ndalandira thandizo lamankhwala a misala kapena mavuto amaganizo?’ Ena anena kuti poyamba ankalimbana ndi chimene anachilingalira kukhala chiyembekezo chakumwamba. Ena ananena kuti kwanthaŵi yakutiyakuti Mulungu anawachotsera chiyembekezo chapadziko lapansi ndipo pomalizira pake nkuwapatsa chakumwamba. Koma dongosolo loterolo nlosemphana ndi zochita zaumulungu. Kuwonjezerapo, chikhulupiriro sichimakhala chosatsimikizirika; nchotsimikiza.—Ahebri 11:6.
Munthu angadzifunsenso kuti: ‘Kodi ndimafuna kutchuka? Kodi ndimakhumbira udindo waulamuliro tsopano kapena kukhala mmodzi wa mafumu ndi ansembe oyanjana ndi Kristu?’ M’zaka za zana loyamba C.E., pamene chiitano chachisawawa chinaperekedwa kufuna oloŵa Ufumu wakumwamba, Akristu onse odzozedwa sanali ndi maudindo athayo monga ziŵalo za bungwe lolamulira kapena monga akulu kapena atumiki otumikira. Ambiri anali akazi, ndipo analibe udindo wapadera; ndiponso kudzozedwa ndi mzimu sikumabweretsa kumvetsetsa kwachilendo Mawu a Mulungu, popeza kuti Paulo anachipeza kukhala choyenera kulangiza ndi kupatsa uphungu odzozedwa ena. (1 Akorinto 3:1-3; Ahebri 5:11-14) Awo okhala ndi chiitano chakumwamba samadzilingalira kukhala anthu otchuka, ndipo samabukitsa kudzozedwa kwawo. Mmalomwake, iwo amasonyeza kudzichepetsa komwe kumayembekezeredwa moyenerera kwa anthu okhala ndi “maganizo a Kristu.” (1 Akorinto 2:16, NW) Iwo amazindikiranso kuti ziyeneretso zolungama za Mulungu ziyenera kufikiridwa ndi Akristu onse, kaya chiyembekezo chawo chikhale chakumwamba kapena chapadziko lapansi.
Kudzinenera kukhala ndi chiitano chakumwamba sikumabweretsera munthu zivumbulutso zapadera. Mulungu ali ndi dongosolo lolankhulira limene amaperekera chakudya chauzimu ku gulu lake lapadziko lapansi. (Mateyu 24:45-47) Chotero palibe aliyense amene ayenera kulingalira kuti kukhala Mkristu wodzozedwa kumampatsa nzeru zapamwamba kuposa ‘khamu lalikulu’ lokhala ndi chiyembekezo chapadziko lapansi. (Chibvumbulutso 7:9) Kudzozedwa ndi mzimu sikumasonyezedwa ndi kukhala waluso m’kuchitira umboni, kuyankha mafunso Amalemba, kapena kupereka nkhani za Baibulo, popeza kuti Akristu okhala ndi chiyembekezo chapadziko lapansi amachitanso bwino m’mbali zimenezi. Mofanana ndi odzozedwa, nawonso akukhala ndi moyo Wachikristu wopereka chitsanzo chabwino. Pa chifukwa chimenecho, Samsoni ndi ena a nthaŵi za Chikristu chisanakhale anali ndi mzimu wa Mulungu ndipo anadzazidwa ndi changu ndi kuzindikira. Komabe, palibe aliyense wa amenewo a ‘mtambo waukulu chotere wa mboni’ anali ndi chiyembekezo chakumwamba.—Ahebri 11:32-38; 12:1; Eksodo 35:30, 31; Oweruza 14:6, 19; 15:14; 1 Samueli 16:13; Ezekieli 2:2.
Kumbukirani Wosankhayo
Ngati wokhulupirira mnzathu afunsa ponena za chiitano chakumwamba, mkulu woikidwa kapena Mkristu wachikulire angakambitsirane naye nkhaniyi. Koma munthu sangapangire mnzake chosankhachi, ndipo ali Yehova amene amapereka chiyembekezo chakumwamba. Munthu amene alidi ndi chiitano chakumwamba samafunikira kufunsa Akristu anzake ngati ali ndi chiyembekezo chotero. Odzozedwa ‘anabadwanso, osati ndi mbewu yofeka, komatu yosaola, mwa mawu a Mulungu amoyo ndi okhalitsa.’ (1 Petro 1:23) Mwa mzimu wake ndi Mawu, Mulungu amadzala ‘mbewu’ imene imapangitsa munthuyo ‘kubadwanso,’ ndi chiyembekezo chakumwamba. (2 Akorinto 5:17) Inde, Yehova amapanga chosankha.
Chotero, pamene mukuphunzira Baibulo ndi atsopano, sibwino kupereka lingaliro lakuti aganize kaya ngati ali ndi chiitano chakumwamba. Koma bwanji ngati Mkristu wodzozedwa akakhala wosakhulupirika ndipo akafunikira kuloŵedwa mmalo? Pamenepo chikakhala chanzeru kulingalira kuti Mulungu akapatsa chiitano chakumwambacho kwa winawake amene wakhala wopereka chitsanzo chabwino m’kupereka utumiki wokhulupirika kwa Atate wathu wakumwamba kwa zaka zambiri.
Lerolino, mfundo yeniyeni ya uthenga wa Mulungu sindiyo yakuti anthu akhale ziŵalo za mkwatibwi wakumwamba wa Kristu. Mmalomwake, ‘mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani.’ Chiitano chimenechi ncha moyo wapadziko lapansi laparadaiso. (Chibvumbulutso 22:1, 2, 17) Pamene odzozedwa akutsogolera m’ntchito imeneyi, iwo amasonyeza ‘kudzichepetsa konse’ ndi kugwira ntchito ‘kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe awo.’—Aefeso 4:1-3; 2 Petro 1:5-11.