Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’kalata ya Aroma
CHA mu 56 C.E., mtumwi Paulo anafika mu mzinda wa Korinto, paulendo wake wachitatu waumishonale. Ali kumeneku, anamva kuti panali kusiyana maganizo ku Roma pakati pa Akhristu achiyuda ndi omwe sanali Ayuda. Pofuna kuwagwirizanitsa mwa Khristu, Paulo anawalembera kalata.
M’kalata yopita kwa Aroma imeneyi, Paulo anafotokoza mmene munthu amayesedwera wolungama, ndi mmene munthuyo ayenera kukhalira pa moyo wake. Kalatayi imatithandiza kudziwa bwino Mulungu ndi Mawu ake, imafotokoza kwambiri za kukoma mtima kwa m’chisomo kwa Mulungu ndiponso za udindo umene Khristu ali nawo wotithandiza kupeza chipulumutso.—Aheb. 4:12.
KODI ANTHU AMAYESEDWA OLUNGAMA MOTANI?
Paulo analemba kuti: “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu . . . Kuyesedwa kwawo olungama chifukwa cha kukoma mtima kwa m’chisomo [kwa Mulungu] kumene wakusonyeza, powamasula ndi dipo lolipiridwa ndi Khristu Yesu, kuli ngati mphatso yaulere.” Paulo ananenanso kuti: “Munthu amayesedwa wolungama mwa chikhulupiriro, osati mwa ntchito za chilamulo.” (Aroma 3:23, 24, 28) Mwa kukhulupirira “chinthu chimodzi cholungamitsa,” Akhristu odzozedwa ndiponso “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” ‘amayesedwa olungama.’ Akhristu odzozedwa amayesedwa olungama kuti akalandire moyo kumwamba ndi kukhala olowa nyumba anzake a Khristu. A khamu lalikulu amayesedwa olungama kuti akhale mabwenzi a Mulungu ndipo amayembekeza kupulumuka “chisautso chachikulu.”—Aroma 5:18; Chiv. 7:9, 14; Yoh. 10:16; Yak. 2:21-24; Mat. 25:46.
Paulo anafunsa kuti: “Kodi tichite tchimo chifukwa chakuti sitili m’chilamulo koma m’kukoma mtima kwa m’chisomo?” Poyankha anati: “Tisayese n’komwe!” Ndipo anafotokoza kuti: ‘Mukhala akapolo a uchimo umene umatsogolera ku imfa, kapena akapolo a kumvera kumene kumatsogolera ku chilungamo.’ (Aroma 6:15, 16) Kenako anati: “Ngati mupha zochita za thupi mwa mzimu, mudzakhala ndi moyo.”—Aroma 8:13.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
1:24-32—Kodi makhalidwe oipa amene akufotokozedwa pano, akunena za Ayuda kapena anthu omwe sanali Ayuda? Ngakhale kuti zimene akufotokoza zingakhudze magulu onse awiri, Paulo anali kunena makamaka za Aisiraeli akale ampatuko. Iwo ankadziwa lamulo lolungama la Mulungu, koma ‘sanafune kum’dziwa Mulungu molondola.’ Motero anali ndi mlandu.
3:24, 25—Kodi “dipo lolipiridwa ndi Khristu” linaphimba bwanji “machimo amene anachitika kale,” dipolo lisanalipiridwe? Ulosi woyamba wonena za Mesiya wopezeka pa Genesis 3:15, unakwaniritsidwa mu 33 C.E., pamene Yesu anaphedwa pa mtengo wozunzikirapo. (Agal. 3:13, 16) Yehova atangonena ulosiwu, kwa iye dipolo linakhala ngati laperekedwa kale, chifukwa palibe chilichonse chimene chingalepheretse Mulungu kukwaniritsa cholinga chake. Choncho, pamaziko a nsembe imene Yesu Khristu anali kudzapereka, Yehova anakhululukira machimo a mbadwa za Adamu zimene zinakhulupirira lonjezo limenelo. Ndiponso anthu omwe anafa Chikhristu chisanayambe, adzaukitsidwa chifukwa cha dipo limeneli.—Mac. 24:15.
6:3-5—Kodi kubatizidwa mu mgwirizano ndi Khristu Yesu komanso kubatizidwa mu imfa yake, kukutanthauza chiyani? Yehova akadzoza otsatira a Khristu ndi mzimu woyera, iwo amagwirizana ndi Yesu ndi kukhala ziwalo za mpingo umene ndi thupi la Khristu, ndipo Yesu ndiye Mutu. (1 Akor. 12:12, 13, 27; Akol. 1:18) Kumeneku ndiko kubatizidwa mu mgwirizano ndi Khristu Yesu. Akhristu odzozedwa ‘amabatizidwanso mu imfa’ ya Khristu m’njira yakuti amakhala ndi moyo wodzimana ndipo amasiya chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Choncho imfa yawo imakhala nsembe ngati imfa ya Yesu, ngakhale kuti imfa yawoyo si dipo lowombola anthu. Ubatizo wa mu imfa ya Khristu umenewu umamalizidwa odzozedwawo akamwalira n’kuukitsidwa kukakhala ndi moyo kumwamba.
7:8-11—Kodi ‘uchimo unadzutsidwa ndi lamulo’ m’njira yotani? Chilamulo chinathandiza anthu kuzindikira mphamvu ya uchimo, ndipo iwo anamvetsa kuchimwa kwawo. Mapeto ake, anazindikira zinthu zambirimbiri zimene anali kulakwitsa, ndipo anthu ambiri anazindikira kuti ndi ochimwa. Choncho tinganene kuti uchimo unadzutsidwa ndi Chilamulo.
Zimene Tikuphunzirapo:
1:14, 15. Tili ndi zifukwa zambiri zolalikirira mwachangu uthenga wabwino. Chifukwa china ndi chakuti tili ndi ngongole kwa anthu amene anagulidwa ndi magazi a Yesu ndipo ndi udindo wathu kuwathandiza mwauzimu.
1:18-20. Anthu osam’dziwa Mulungu ndiponso osalungama alibe “chifukwa chomveka chodzilungamitsira,” popeza makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera m’zinthu zimene iye analenga.
2:28; 3:1, 2; 7:6, 7. Paulo atanena mawu omveka ngati onyoza kwa Ayuda, anawonjezera mawu olimbikitsa. Izi zikutipatsa chitsanzo kuti timafunika kusamala komanso luso tikamakambirana ndi anthu nkhani zovuta.
3:4. Zonena za anthu zikasemphana ndi zimene Mulungu amanena m’Mawu ake, ife timalola kuti “Mulungu akhale wonena zoona.” Timatero mwa kukhulupirira uthenga wa m’Baibulo ndi kuchita chifuniro cha Mulungu. Tikamagwira mwachangu ntchito yolengeza Ufumu ndi kupanga ophunzira, timathandiza ena kuzindikira kuti Mulungu amanena zoona.
4:9-12. Abulahamu anayesedwa wolungama chifukwa cha chikhulupiriro chake, zaka zambiri asanadulidwe. Iye anadulidwa ali ndi zaka 99. (Gen. 12:4; 15:6; 16:3; 17:1, 9, 10) Mwa njira imeneyi, Mulungu anasonyeza mwamphamvu kuti munthu amakhala wolungama chifukwa cha chikhulupiriro.
4:18. Chiyembekezo ndi mbali yofunika ya chikhulupiriro. Choncho sitingakhale ndi chikhulupiro popanda chiyembekezo.—Aheb. 11:1.
5:18, 19. Polongosola mfundo zosatsutsika za kufanana kwa Yesu ndi Adamu, Paulo anafotokoza mwachidule mmene munthu mmodzi ‘anaperekera moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.’ (Mat. 20:28) Kufotokoza mfundo zosatsutsika komanso zachidule, ndi njira zabwino zophunzitsira zimene tiyenera kutengera.—1 Akor. 4:17.
7:23. Ziwalo za thupi lathu, monga manja, miyendo ndi lilime zitha ‘kutipanga kapolo wa chilamulo cha uchimo.’ Choncho, tizisamala pozigwiritsa ntchito.
8:26, 27. Tikakumana ndi zinthu zothetsa nzeru ndipo sitikudziwa chonena m’pemphero, “mzimu umachonderera m’malo mwathu.” Kenako Yehova, “Wakumva pemphero,” amalandira mapemphero olembedwa m’Mawu ake ngati kuti akuchokera kwa ifeyo.—Sal. 65:2.
8:38, 39. Masoka, mizimu yoipa, ndi maboma a anthu sangaletse Yehova kutikonda, ndipo tisalole zinthu zimenezi kutisiyitsa kukonda Yehova.
9:22-28; 11:1, 5, 17-26. Maulosi ambiri onena za kubwezeretsedwa kwa Isiraeli akukwaniritsidwa pa mpingo wa Akhristu odzozedwa, umene anthu ake ‘amaitanidwa osati kuchokera mwa Ayuda okha komanso mwa mitundu ina.’
10:10, 13, 14. Kuwonjezera pa kukonda Mulungu ndi anthu anzathu, chikhulupiriro cholimba mwa Yehova ndi malonjezo ake chingatilimbikitse kuchita utumiki wachikhristu mwachangu.
11:16-24, 33. “Kukoma mtima komanso kusalekerera kwa Mulungu” kumagwirizana bwino kwambiri. Zoonadi, “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo,” kapena kuti n’zolungama.—Deut. 32:4.
MAKHALIDWE OYENERERA ANTHU OYESEDWA OLUNGAMA
Paulo anati: “Chotero ndikukudandaulirani mwa chifundo chachikulu cha Mulungu, abale, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yoyera, yovomerezeka kwa Mulungu.” (Aroma 12:1) Mawu akuti “chotero,” kapena kuti popeza Akhristu ndi oyesedwa olungama chifukwa cha chikhulupiriro chawo, akusonyeza kuti mfundo zimene zikutsatira ziyenera kukhudza zimene iwo amaganiza za iwo eni, mmene amaonera anthu ena komanso akuluakulu a boma.
Paulo analemba kuti: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire koposa mmene muyenera kudziganizira.” Kenako, analangiza kuti: “Chikondi chanu chisakhale cha chiphamaso.” (Aroma 12:3, 9) “Munthu aliyense azimvera olamulira aakulu.” (Aroma 13:1) Pankhani zokhudza chikumbumtima, Paulo analimbikitsa Akhristu ‘kusaweruzana wina ndi mnzake.’—Aroma 14:13.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
12:20—Kodi ‘timaunjika [motani] makala a moto pamutu’ pa mdani wathu? M’nthawi za m’Baibulo, chitsulo chinkaikidwa mu ng’anjo yamoto, ndipo ankaunjika makala a moto pamwamba ndi pansi pake. Makala apamwamba ankathandiza chitsulo chija kusungunuka n’kulekana ndi zitsotso. Mofananamo, timaunjika makala a moto pamutu pa mdani pomuchitira zabwino, zimene zimathandiza kuti kuuma mtima kwake kusungunuke ndipo makhalidwe abwino aonekere.
12:21—Kodi tingachite chiyani kuti ‘tipitirize kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino’? Njira imodzi yochitira zimenezi ndiyo kugwirabe mopanda mantha ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu imene Mulungu anatipatsa, mpaka pamene Yehova adzakhutiritsidwe.—Maliko 13:10.
13:1—Kodi “olamulira amene alipowa ali m’malo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu” m’njira yotani? Olamulira a maboma “ali m’malo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu,” m’njira yakuti Mulungu wawalola kuti alamulire, ndipo nthawi zina Mulungu anali atadziwiratu za ulamuliro wawo. Mwachitsanzo, Baibulo linalosera za anthu ena amene anadzakhala olamulira.
Zimene Tikuphunzirapo:
12:17, 19. Sitiyenera kubwezera choipa ku choipa chifukwa Yehova yekha ndi amene ali ndi udindo wobwezera. Choncho, ‘kubwezera choipa ku choipa’ n’kudzikuza.
14:14, 15. Sitiyenera kukhumudwitsa kapena kupunthwitsa abale athu powapatsa chakudya ndi chakumwa chimene chikumbumtima chawo sichiwalola.
14:17. Kukhala pa ubale wabwino ndi Mulungu, sikudalira kwenikweni zimene munthu amadya ndi kumwa kapenanso zimene sadya ndi kumwa, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe.
15:7. Tiyenera kulandira mumpingo anthu onse ofuna choonadi, mopanda tsankho ndiponso kulalikira uthenga wa Ufumu kwa aliyense amene tingakumane naye muutumiki.
[Zithunzi patsamba 31]
Kodi dipo lingaphimbe machimo amene anachitidwa kale, dipolo lisanalipiridwe?