Lingaliro la Baibulo
Kudzichinjiriza Kodi Mkristu Ayenera Kufika Pati?
“Kodi nkukhaliranji m’mantha? Phunzirani njira zodzichinjirizira ndi zothaŵira woukira. Maluso osavuta ndi othandiza amasonyezedwa mwatsatanetsatane. Video yamalangizo iyi ingakupangitseni kukhala wopulumuka m’malo mwa mnkhole.”—Chilengezo cha “ video” ya kudzichinjiriza.
PALIBE amene afunikira kulongosola kugulika kwa video yoteroyo lerolino. Mumzinda wa Philadelphia, Pennsylvania, U.S.A., magulu a achichepere achiwawa amadzuma kuti “Menya, menya, menya” pamene akuunguzaunguza m’makwalala kufunafuna minkhole yakuti aimenye. “Kuwopa upandu kumayambukira nzika zonse za mzinda” wa Rio de Janeiro, anasimba motero magazini a Time. Mu Hong Kong kuba kogwiritsira ntchito zida ndi kuwombera kumachitika m’malo kumene upandu wachiwawa unali pafupifupi wosadziŵika—kufikira tsopano.
Malipoti ofananawo akumvedwa padziko lonse. Ndi chotulukapo chotani? “Nzika zimapenda maupandu a kuwombera kobwezera,” imatero Newsweek. Akristu sanachinjirizidwe ku ‘nthaŵi zowawitsa’ zimenezi, koma kodi kuwombera kobwezera kudzakupangitsanidi “kukhala wopulumuka mmalo mwa mnkhole”?—2 Timoteo 3:1.
Kodi Mungalake Chiwawa ndi Chiwawa?
‘Ngati ndinyamula mfuti,’ ena amakhulupirira motero, ‘ndidzakhala wosungika. Ndidzamupha asanandiphe. Mwina ndidzangomuwopseza!’ Komabe, sikokhweka motero.
George Napper, wa ku Atlanta, Georgia, U.S.A., nduna ya chisungiko cha anthu, akunena kuti: “Kukhala ndi mfuti yakumanja kumatanthauza kukonzekera kukhala ndi chikumbumtima chapambuyo pake chakupha munthu mnzako.” Kodi Mkristu ali wokonzeka kukhala ndi chotulukapo choterocho, chimene chingaphatikizepo liŵongo lamwazi?—Yerekezerani ndi Numeri 35:11, 12.
Ndiponso, Mawu a Mulungu amalamula kuti, ‘Sulani malupanga anu akhale makasu’ ndi kuti, ‘Funafunani mtendere ndi kuulondola.’ (Mika 4:3; 1 Petro 3:11) Kodi ndimotani mmene Akristu angafunire chitetezero m’zida ndipo panthaŵi imodzimodziyo kukhala ogwirizana ndi ziyeneretso za Baibulo? Mulimonse momwe zingakhalire, woukirayo mwachiwonekere amakhala wofulumira kutulutsa mfuti kuposa mnkhole.
Yesu anatsutsa kulimbana kwa zida. Zowonadi, iye analangiza atumwi ake kunyamula malupanga aŵiri popita ku munda wa Getsemane, kumalo kumene anakagwidwa. Koma kodi iye anachitiranji zimenezi? Kukhala ndi zida, komano osazigwiritsira ntchito, kunasonyeza mwamphamvu kuti otsatira a Yesu sakayenera kutembenukira ku zida zakupha. Nkofunika kudziŵa kuti pokhala ndi chida, Petro mwaukali anachigwiritsira ntchito. Yesu anamdzudzula mwamphamvu kaamba ka kachitidwe kogwiritsira ntchito lupanga mwasontho kuti: ‘Onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.’—Mateyu 26:36, 47-56; Luka 22:36-38, 49-51.
‘Zimenezo zimanena za kukhala ndi zida,’ wina angatero. ‘Koma bwanji ponena za kuphunzira maluso omenyera kaamba ka kudzichinjiriza, monga ngati judo, karate, ndi kendo?’ Tadzifunsani nokha, kodi cholinga cha malangizo amenewo sindicho kumenya kapena kuvulaza ena? Ndipo kodi kuphunzira zoterozo sikulingana ndi kudzikonzekeretsa enife ndi zida zakupha? (1 Timoteo 3:3) Ngakhale magawo akuyeseza atulukapo kuvulala kowopsa ndi kwakupha.
Aroma 12:17-19 amapereka chilangizo chanzeru pa chimenechi kuti: ‘Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. . . . Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, ine ndidzabwezera, ati [Yehova, NW].’ Liwu Lachigiriki limene Paulo wagwiritsira ntchito lotembenuzidwa ‘choipa’ (ka·kosʹ) lingatanthauzenso “chowononga, chovulaza.” Chotero, Akristu ayenera kupatuka ku lingaliro lirilonse lakuwononga kapena kuvulaza munthu wina kobwezera.
M’malo mwakusonyeza mkwiyo wake mwaukali, Mkristu amadalira kotheratu pa Mulungu, amene amati ponena za anthu ake: ‘Iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m’diso langa.’ Mogwirizana ndi chimenechi, Mulungu akulonjeza ‘kuwononga oipa’ panthaŵi yake.—Zekariya 2:8; Salmo 145:20.
Kodi Pali Nthaŵi Yakumenyana?
‘Sindidzalola ndalama zanga kupita popanda kumenyana!’ ena amadzuma motero molimba mtima. Dick Mellard, manijala wa maphunziro pa National Crime Prevention Institute, akuchenjeza kuti: “Nchibadwa chaumunthu kulimbana, koma chibadwa chaumunthu chingakuphetseni mumkhalidwe wosayenera.” Achifwamba ambiri amakhala odzikonzekeretsa mowopsa ndi zida ndipo ngaamantha. Ndalama zotaidwa zingapezedwenso, koma bwanji ponena za moyo wotaidwa? Kodi ngwoyenerera kuikidwa pachiswe?
George Napper akupereka uphungu uwu: “Mwinamwake njira yabwino koposa yodzitetezerera inumwini ndiyo kuika pachiswe katundu wanu mmalo mwa moyo wanu. Mbala zambiri ndi othyola amafuna kuba, osati kupha.” M’mikhalidwe pamene munthu wangowopsezedwa kapena pamene ndalama zake zikufunidwa, lamulo labwino nlakuti: ‘Kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndewu.’—2 Timoteo 2:24.a
Kumeneku sindiko kulephera kuchitapo kanthu, lingaliro losafuna kulimbana pansi pa mkhalidwe uliwonse. Pa Eksodo 22:2, 3, pakufotokozedwa mkhalidwe m’mene mbala inamenyedwa mpaka kufa poloŵa m’nyumba ya winawake nthaŵi ya masana. Kachitidwe kodzichinjiriza koteroko kanalingaliridwa kukhala mbanda, popeza kuti mbalayo ikanadziŵidwa ndi kubweretsedwa pamaso pa oweruza. Koma m’nthaŵi yausiku, kukakhala kovuta kwa mwininyumba kumuwona woloŵererayo ndi kudziŵa cholinga chake. Chotero, munthu wakupha woloŵerera mumdima analingaliridwa kukhala wopanda liŵongo.
Chotero, Baibulo silimaletsa zoyesayesa zodzichinjiriza. Komabe, posachirikiza kusachitapo kanthu, Baibulo limasonyeza kuti pali nthaŵi yakudzichinjiriza. Akristu angalepheretse kuukira kowopsa kochitidwa pa iwo eniwo, mabanja awo, kapena ena ofunikira chitetezero choyenerera.b Koma iwo sakayambitsa kuukira, kapena sadzabwezera mwakuthupi kuti apulumutse katundu wawo. Iwo sakanyamula zida moyembekezera kuukiridwa koteroko; m’malomwake, amayesayesa ‘kukhala mwamtendere.’—2 Akorinto 13:11.
[Mawu a M’munsi]
a Pamene kuli kwakuti mawu apatsogolo ndi pambuyo amasonyeza kuti Paulo panopa anali kusonya ku ndewu zapakamwa, liwu la chinenero choyambirira lomasuliridwa ‘ndewu’ (maʹkhe·sthai) mwachisawawa nlogwirizanitsidwa ndi kumenyana ndi zida kapena ndi manja.
b Mkazi wowopsezedwa kugwiriridwa chigololo ayenera kukuwa ndi kugwiritsira ntchito njira iriyonse imene angathe kuti akane kugonedwa.—Deuteronomo 22:23-27.
[Mawu a Chithunzi patsamba 12]
Betrayal of Christ, lolembedwa ndi Albrecht Dürer, 1508