Lemekezani Mulungu Ndi ‘Pakamwa Pamodzi’
‘[Ndi] pakamwa pamodzi, mulemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu.’—AROMA 15:6.
1. Kodi ndi mfundo iti yokhudza kuthetsa kusiyana maganizo imene Paulo anaphunzitsa okhulupirira anzake?
AKRISTU akamasankha zinthu sikuti onse amasankha zinthu zofanana, ndiponso zimene amakonda si zofanana. Ngakhale ndi choncho, Akristu onse ayenera kuyenda mogwirizana panjira ya ku moyo. Kodi zimenezi n’zotheka? Inde, n’zotheka. Zimatheka ngati sitilola kuti kusiyana maganizo pang’ono kukhale nkhani yaikulu. Imeneyi ndiyo mfundo imene mtumwi Paulo anaphunzitsa okhulupirira anzake m’zaka 100 zoyambirira. Kodi mfundo yofunika kwambiri imeneyi anaifotokoza motani? Nanga kodi ife tingatsatire bwanji malangizo ake ouziridwa ameneŵa?
M’pofunika Kuti Akristu Azigwirizana
2. Kodi Paulo anati chiyani potsindika kufunika kogwirizana?
2 Paulo anadziŵa kuti m’pofunika kwambiri kuti Akristu azigwirizana, ndipo anapereka malangizo abwino othandiza Akristuwo kulolerana mwachikondi. (Aefeso 4:1-3; Akolose 3:12-14) Komabe, iye atakhazikitsa mipingo yambiri ndi kuyendera ina pazaka zoposa 20, anadziŵa kuti zingakhale zovuta kuti Akristu apitirize kugwirizana. (1 Akorinto 1:11-13; Agalatiya 2:11-14) N’chifukwa chake analimbikitsa okhulupirira anzake amene anali ku Roma kuti: “Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu . . . kuti nonse pamodzi, m’kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu.” (Aroma 15:5, 6) Masiku anonso ifeyo, monga anthu ake ogwirizana, tiyenera kulemekeza Yehova Mulungu ndi ‘pakamwa pamodzi.’ Kodi tikuchita bwanji pankhani imeneyi?
3, 4. (a) Kodi ku Roma kunali Akristu osiyana otani? (b) Kodi Akristu a ku Romawo akanatha bwanji kutumikira Yehova ndi ‘pakamwa pamodzi’?
3 Akristu ambiri ku Roma anali mabwenzi apamtima a Paulo. (Aroma 16:3-16) Ngakhale kuti abale ake onsewo anakulira kosiyanasiyana, Paulo anawaona onse monga “okondedwa a Mulungu.” Iye analemba kuti: “Ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Kristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idamveka padziko lonse lapansi.” N’zoonekeratu kuti Aromawo anapereka chitsanzo chabwino pa zinthu zambiri. (Aroma 1:7, 8; 15:14) Komabe, ena mumpingomo anali ndi maganizo osiyana ndi anzawo pankhani zina. Popeza kuti Akristu masiku ano amakulira kosiyanasiyana ndipo miyambo yawo imasiyananso, kuphunzira malangizo ouziridwa amene Paulo anapereka okhudza zimene iwo angachite akasiyana maganizo kungawathandize kulankhula ndi ‘pakamwa pamodzi.’
4 Ku Roma kunali anthu okhulupirira achiyuda ndiponso akunja. (Aroma 4:1; 11:13) Zikuoneka kuti panali Akristu ena amene anali Ayuda omwe sanasiye kutsatira miyambo ina imene anali kutsatira m’Chilamulo cha Mose, ngakhale kuti anayenera kudziŵa kuti munthu sanafunikire miyambo imeneyo kuti apeze chipulumutso. Komanso panali Akristu ena amene anali Ayuda omwe anazindikira kuti nsembe ya Yesu inawamasula ku malamulo amene anali kutsatira asanakhale Akristu. Iwoŵa anasiya zizoloŵezi zawo ndi miyambo yawo ina. (Agalatiya 4:8-11) Koma ngakhale zinali choncho, onse anali “okondedwa a Mulungu” monga momwe Paulo ananenera. Onse akanatha kulemekeza Mulungu ndi ‘pakamwa pamodzi’ ngati akanapitiriza kuonana moyenera. Ifenso masiku ano tingasiyane maganizo ndi anzathu pankhani zina. Choncho, tiyenera kupenda bwinobwino mmene Paulo anafotokozera mfundo yofunika imeneyi.—Aroma 15:4.
“Mulandirane Wina ndi Mnzake”
5, 6. N’chifukwa chiyani anthu mu mpingo wa Roma ankasiyana maganizo?
5 M’kalata yake yopita kwa Aroma, Paulo anatchula nkhani ina imene anthu anasiyanapo maganizo. Analemba kuti: “Munthu mmodzi akhulupirira kuti adye zinthu zonse, koma wina wofooka angodya zitsamba.” Zinali choncho chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti, malinga ndi Chilamulo cha Mose, nkhumba inali yosaloleka kudya. (Aroma 14:2; Levitiko 11:7) Komabe Kristu atamwalira, Chilamulo chinasiya kugwira ntchito. (Aefeso 2:15) Ndiyeno patapita zaka zitatu ndi theka Yesu atamwalira, mngelo anauza mtumwi Petro maganizo a Mulungu akuti asaone chakudya china chilichonse ngati chodetsedwa. (Machitidwe 11:7-12) Chifukwa cha mfundo zimenezi, Akristu ena amene anali Ayuda ayenera kuti anaganiza zoti angadye nkhumba, kapena chakudya china chimene chinaletsedwa m’Chilamulo.
6 Komabe kwa Akristu ena amene analinso Ayuda, kungoganiza zoti angadye zakudya zimene kale zinali zodetsedwa kuyenera kuti kunawanyansa. Ndipo anthu ameneŵa pokhala ndi maganizo otero ayenera kuti anakhumudwa kuona Ayuda anzawo amene analinso abale awo mwa Kristu akudya zakudya zotero. Kuwonjezera apo, panali Akristu ena amene anali Akunja omwe pachipembedzo chawo chakale analibe malamulo oletsa zakudya zina. Ameneŵa ayenera kuti zinawadabwitsa kwambiri kuona kuti anthu anali kukangana pa nkhani ya zakudya. Zoona zake n’zakuti, sizinali zolakwika ngati munthu sanali kudya zakudya zina, malinga ngati iye sanaumirire kuti ngati munthu akufuna kupeza chipulumutso ayenera kupewa zakudyazo. Ngakhale ndi tero, kusiyana maganizo kumeneku kukanayambitsa mikangano mu mpingo mosavuta. Akristu ku Roma anafunika kusamala kuti kusiyana maganizo kwawoko kusawalepheretse kulemekeza Mulungu ndi ‘pakamwa pamodzi.’
7. Kodi panali kusiyana maganizo kotani pa nkhani yoona tsiku lina pamlungu kukhala lapadera?
7 Ndiyeno Paulo anapereka chitsanzo chachiŵiri. Iye anati: “Munthu wina aganizira kuti tsiku lina liposa linzake; wina aganizira kuti masiku onse alingana.” (Aroma 14:5a) Chilamulo cha Mose sichinali kulola kugwira ntchito pa Sabata. Ndipo ndi maulendo ochepa kwambiri amene anali kuchitika tsiku limenelo. (Eksodo 20:8-10; Mateyu 24:20; Machitidwe 1:12) Koma pamene Chilamulo chinatha, ziletso ngati zimenezo zinatha ntchito. Ngakhale ndi tero, Akristu ena amene anali Ayuda ayenera kuti zinawavuta kugwira ntchito ya mtundu uliwonse kapena kuyenda ulendo wautali kwambiri tsiku limenelo, limene kale linali lopatulika. Moti ngakhale atakhala Akristu, ayenera kuti anasankha tsiku lachisanu ndi chiŵiri kukhala lapadera lochitira zinthu zauzimu zokha, ngakhale kuti kwa Mulungu lamulo lokhudza tsiku la Sabata silinalinso kugwira ntchito. Kodi iwo analakwa pochita zimenezo? Iyayi sanalakwe, malinga ngati sanaumirire kuti Mulungu akufuna kuti anthu azisunga Sabata. Choncho poganizira za chikumbumtima cha abale ake achikristu, Paulo analemba kuti: ‘Aliyense akhale wotsimikiza m’maganizo ake.’—Aroma 14:5b, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.
8. Ngakhale kuti Akristu ku Roma anayenera kuganizira chikumbumtima cha ena, kodi sanayenere kuchita chiyani?
8 N’zoona kuti Paulo mokoma mtima analimbikitsa abale ake kuti azileza mtima ndi anthu amene anali kuvutika ndi nkhani zokhudza chikumbumtima. Komabe iye anadzudzula mwamphamvu onse amene ankayesa kuumiriza okhulupirira anzawo kutsatira Chilamulo cha Mose ngati akufuna kuti adzapeze chipulumutso. Mwachitsanzo, m’chaka cha m’ma 61 Kristu Atabwera, Paulo analemba buku la Ahebri. Buku limeneli ndi kalata yamphamvu imene analembera Akristu amene anali Ayuda kuwafotokozera bwinobwino kuti kutsatira Chilamulo cha Mose kunalibe phindu kwa Akristu ndi kuti iwo anali ndi chiyembekezo chapamwamba chifukwa cha nsembe ya dipo la Yesu.—Agalatiya 5:1-12; Tito 1:10, 11; Ahebri 10:1-17.
9, 10. Kodi Akristu ayenera kupewa kuchita chiyani? Fotokozani.
9 Malinga ndi mmene taonera, Paulo anafotokoza kuti kusankha zinthu zosiyana sikuyenera kusokoneza mgwirizano malinga ngati mfundo zachikristu sizikuphwanyidwa. N’chifukwa chake iye anafunsa Akristu amene chikumbumtima chawo chinali chofooka kuti: “Iwe uweruziranji mbale wako?” Ndipo anafunsa olimba (mwinamwake amene chikumbumtima chawo chinawalola kudya zakudya zina zimene Chilamulo chinaletsa kapena kugwira ntchito tsiku la Sabata) kuti: “Iwenso upeputsiranji mbale wako?” (Aroma 14:10) Apa Paulo anali kunena kuti Akristu amene ali ndi chikumbumtima chofooka ayenera kupewa kuweruza abale awo ololera zambiri. Komanso Akristu olimba sayenera kupeputsa anthu amene chikumbumtima chawo n’chofooka pambali zina. Onse ayenera kulemekeza zolinga zabwino zimene anzawo ali nazo ndipo “asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa.”—Aroma 12:3, 18.
10 Pofotokoza maganizo oyenera ameneŵa, Paulo anati: “Wakudyayo asapeputse wosadyayo; ndipo wosadyayo asaweruze wakudyayo; pakuti Mulungu wam’landira.” Ndipo anapitiriza kuti: “Kristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero.” Popeza kuti olimba ndi ofooka omwe ali olandirika kwa Mulungu ndi Kristu, ifenso tiyenera kukhala ndi maganizo omwewo ndi ‘kulandirana wina ndi mnzake.’ (Aroma 14:3; 15:7) Ndi ndaninso akanatsutsa zimenezi?
Kukonda Abale Kumabweretsa Mgwirizano Masiku Ano
11. Kodi ndi vuto liti lapadera limene linaliko masiku a Paulo?
11 M’kalata yake yopita kwa Aroma, Paulo anali kulankhula za vuto lapadera. Si kale kwambiri pamene Yehova anali atathetsa pangano lakale n’kukhazikitsa lina latsopano. Ena zinali kuwavuta kusintha. Vuto ngati limenelo kulibe masiku ano, koma nthaŵi zina nkhani zofanana ndi zimene zinaliko nthaŵi imeneyo zingabuke.
12, 13. Kodi ndi pankhani ziti masiku ano pamene Akristu angalemekezere chikumbumtima cha abale awo?
12 Mwachitsanzo, zingachitike kuti m’mbuyomo mkazi wina wachikristu anali m’chipembedzo chimene chimalimbikitsa mavalidwe ndi maonekedwe opanda zokongoletsa. Ataphunzira choonadi, zingam’vute kusintha ndi kuvomereza kuti sikoletsedwa kuvala zovala zokongola ndi zaulemu panthaŵi yoyenera kapena kugwiritsa ntchito zodzoladzola mosapitirira malire. Popeza kuti palibe mfundo ya m’Baibulo imene ikuphwanyidwa, sichingakhale chanzeru kuti wina ayese kuumiriza Mkristu ameneyo kulakwira chikumbumtima chake. Mkaziyonso amazindikira kuti sayenera kuweruza akazi anzake achikristu amene chikumbumtima chawo chimawalola kugwiritsa ntchito zinthu zimenezo.
13 Taganizirani chitsanzo china. Mwamuna wina wachikristu angakhale woti anakulira kumene sanali kulola kumwa moŵa. Atadziŵa choonadi, angaphunzire zimene Baibulo limanena kuti vinyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu ndi kuti munthu atha kumwa moŵa mosapitirira malire. (Salmo 104:15) Iye angayambe kukhulupirira zimenezo. Komabe chifukwa cha mmene anakulira, angasankhe kupeweratu moŵa, koma saweruza ena amene amamwa moŵa mosapitirira malire. Mwa kutero, amatsatira mawu a Paulo akuti: “Tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.”—Aroma 14:19.
14. Kodi ndi pankhani ziti pamene Akristu angagwiritse ntchito mfundo ya malangizo amene Paulo anapereka kwa Aroma?
14 Pamakhalanso nkhani zina zimene zimafuna kuti munthu agwiritse ntchito mfundo ya malangizo amene Paulo anapereka kwa Aroma. Mu mpingo wachikristu muli anthu osiyanasiyana, ndipo amakonda zinthu zosiyanasiyana. Chifukwa cha zimenezi, iwo angasankhe zinthu mosiyana monga pankhani ya kavalidwe ndi kudzikongoletsa. Baibulo lili ndi mfundo zomveka zimene Akristu enieni onse amatsatira. Ife tonse sitiyenera kuvala zovala zachilendo kapena zodzichotsera ulemu kapena zimene zingaonetse ngati timagwirizana ndi anthu oipa a dzikoli. N’chimodzimodzinso ndi masitayelo a tsitsi lathu. (1 Yohane 2:15-17) Akristu amakumbukira nthaŵi zonse, ngakhale pamene akucheza, kuti iwo ali atumiki oimira Wolamulira wa Chilengedwe Chonse. (Yesaya 43:10; Yohane 17:16; 1 Timoteo 2:9, 10) Komabe, m’madera ambiri pali mitundu yambiri ya zinthu zovomerezeka zimene Akristu angasankhepo.a
Pewani Kukhumudwitsa Ena
15. Kodi ndi pankhani iti pamene Mkristu angapewe kugwiritsa ntchito ufulu wake chifukwa choganizira abale ake?
15 Palinso mfundo ina yofunika imene Paulo akutiuza popereka malangizo kwa Akristu ku Roma. Nthaŵi zina, Mkristu amene chikumbumtima chake n’chophunzitsidwa bwino angasankhe kusachita chinthu chimene pachokha si cholakwika. Angachite zimenezo chifukwa chiyani? Chifukwa chozindikira kuti ngati achita chinthucho angakhumudwitse ena. Choncho, kodi tiyenera kutani posankha chochita pankhani ngati imeneyi? Paulo ananena kuti: “Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusachita chinthu chilichonse chakukhumudwitsa mbale wako.” (Aroma 14:14, 20, 21) Chotero, “ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha. Yense wa ife akondweretse mnzake, kum’chitira zabwino, zakum’limbikitsa.” (Aroma 15:1, 2) Ngati chikumbumtima cha Mkristu mnzathu chingavutike ndi zimene tikufuna kuchita, kukonda abale athu kudzatithandiza kuwaganizira ndi kupewa kuchita chinthucho. Mwachitsanzo, pali nkhani ya kumwa moŵa. N’zololeka Mkristu kumwa vinyo mosapitirira malire. Koma ngati mnzake angakhumudwe nazo, Mkristuyo saumirira kumwabe mowawo ngakhale kuti ali ndi ufulu wochita zimenezo.
16. Kodi tingachite chiyani pofuna kuwaganizira anthu a m’gawo lathu?
16 Mfundo imeneyi ingagwirenso ntchito pamene tili ndi anthu ena amene sali mu mpingo wachikristu. Mwachitsanzo, tingamakhale kudera limene chipembedzo cha anthu ambiri kumeneko chimaphunzitsa anthu kuona tsiku limodzi pamlungu kukhala lopuma. Pachifukwa chimenechi, tidzayesetsa mmene tingathere kupewa kuchita chilichonse tsikulo chimene anansi athu angakwiye nacho. Tidzatero posafuna kuwakhumudwitsa ndi posafuna kuchita zinthu zimene zingalepheretse ntchito yathu yolalikira. Zingachitikenso kuti Mkristu wina wolemera angasamukire kudera limene kukufunika thandizo lolalikira kumene anthu ake ali osauka. Ndiye angasankhe kuwaganizira anansi ake atsopanowo mwa kuvala zovala zosakhala zapamwamba kapena kukhala ndi moyo wotsikirapo ngakhale kuti ali ndi ndalama zambiri.
17. Kodi n’chifukwa chiyani chili chilungamo kuganizira ena posankha zochita?
17 Kodi n’chilungamo kuyembekezera anthu “olimba” kusintha moteremu? Taganizirani fanizo ili: Tiyerekezere kuti tili pamsewu tikuyendetsa galimoto, ndipo kutsogoloko tikuona ana akuyenda mosasamala pafupi kwambiri ndi msewu. Kodi tidzapitiriza kuthamangitsabe galimotolo paliŵiro lololedwa pamsewu umenewo chifukwa chakuti lamulo lake limatipatsa ufulu umenewo? Iyayi sitidzatero. M’malo mwake, tidzachepetsa liŵirolo posafuna kugunda anawo. Ndi mmenenso ziyenera kukhalira ndi ife. Nthaŵi zina timafunika kukhala ndi mtima ngati umenewu wofuna kuchepetsako liŵiro, kapena kuti wololera, pochita zinthu ndi okhulupirira anzathu kapena anthu ena. Popanda kuphwanya mfundo za m’Baibulo, tingamachite chinthu chimene tili ndi ufulu wochichita. Koma ngati ena angakwiye nazo kapena ngati tingakhumudwitse amene ali ndi chikumbumtima chofooka, kukonda abale athu kudzatithandiza kuchita zinthu mosamala. (Aroma 14:13, 15) Chofunika kwambiri ndi kuteteza mgwirizano wathu ndi kulimbikitsa zinthu za Ufumu osati kuumirira ufulu wathu.
18, 19. (a) Tikamachita zinthu moganizira ena, timatengera motani chitsanzo cha Yesu? (b) Kodi ndi pankhani iti pamene tonsefe timachita zinthu mogwirizana kotheratu, ndipo tikambirana zotani m’nkhani yotsatira?
18 Tikamachita zinthu motero, ndiye kuti tikutengera chitsanzo chabwino kwambiri cha Yesu. Paulo anati: “Kristunso sanadzikondweretsa yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene anakunyoza iwe inagwa pa Ine.” Yesu anali wokonzeka kupereka moyo wake nsembe m’malo mwa ife. Kunena zoona ifenso ndife okonzeka kudzimana maufulu athu ena ngati kuchita zimenezo kudzathandiza “opanda mphamvu” kulemekeza Mulungu mogwirizana nafe. Inde, mtima wololera ndi woganizira kwambiri Akristu amene ali ndi chikumbumtima chofooka, kapena kusankha mwa kufuna kwathu kusachita zinthu zina ndi kusaumirira ufulu wathu, kumaonetsa kuti tili ndi ‘mtima umodzi monga wa Kristu Yesu.’—Aroma 15:1-5.
19 Ngakhale kuti penapake tingasiyane maganizo pa nkhani zimene siziphwanya mfundo za m’Malemba, pa nkhani zokhudza kulambira, timachita zinthu mogwirizana kotheratu. (1 Akorinto 1:10) Mwachitsanzo, kugwirizana kumeneku kumaoneka m’njira imene timachitira zinthu ndi adani a kulambira koona. Mawu a Mulungu amati adani amenewo ndi alendo ndipo amatiuza kuti tichenjere ndi “mawu a alendo.” (Yohane 10:5) Kodi tingawadziŵe bwanji alendo amenewo? Kodi tiyenera kuchita nawo zinthu m’njira yotani? Mafunso ameneŵa ayankhidwa m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Ana aang’ono ayenera kuvala mogwirizana ndi zimene makolo awo amafuna.
Kodi Mungayankhe Motani?
• N’chifukwa chiyani kusiyana maganizo pa zinthu zokhudza munthu payekha sikuyenera kusokoneza mgwirizano wathu?
• N’chifukwa chiyani Akristufe tiyenera kuganizirana mwachikondi?
• Kodi masiku ano tingagwiritsire ntchito m’njira ziti malangizo a Paulo onena za kugwirizana, ndipo n’chiyani chimene chingatilimbikitse kuchita zimenezo?
[Chithunzi patsamba 9]
Malangizo a Paulo onena za kugwirizana anali ofunika kwambiri mu mpingo
[Chithunzi patsamba 10]
Akristu amagwirizana ngakhale kuti anakulira kosiyanasiyana
[Chithunzi patsamba 12]
Kodi dalaivala ameneyu ayenera kuchita chiyani?