Zimene Zimafunika Kuti Munthu Akhaledi Wachimwemwe
YEHOVA, “Mulungu wachimwemwe,” ndi Yesu Kristu, “Mwini Mphamvu wachimwemwe ndi wayekha” amadziŵa kuposa wina aliyense zimene zimafunika kuti munthu akhale wachimwemwe. (1 Timoteo 1:11; 6:15, NW) Choncho n’zosadabwitsa kuti chinsinsi chopezera chimwemwe chimapezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo.—Chivumbulutso 1:3; 22:7.
Mu Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri, Yesu anafotokoza zimene zimafunika kuti munthu akhale wachimwemwe. Iye anati: “Odala [“achimwemwe,” NW] ali” (1) osauka mumzimu [ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu, NW], (2) achisoni, (3) akufatsa, (4) akumva njala ndi ludzu la chilungamo, (5) akuchitira chifundo, (6) oyera mtima, (7) akuchita mtendere, (8) akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo, ndi (9) amene anthu adzawanyoza ndi kuwazunza chifukwa cha iye.—Mateyu 5:3-11.a
Kodi Zimene Ananena Yesuzo N’zolondola?
Mawu ena amene Yesu ananena n’ngosachita kufuna kufotokozera kuti munthu aone kuti ndi oonadi. Ndani angatsutse zoti munthu wofatsa, wachifundo, ndi wamtendere chifukwa chokhala woyera mtima amakhala wachimwemwe kusiyana ndi munthu wokwiya, wandewu, ndiponso wopanda chifundo?
Koma mwina tingadabwe kuti kodi anthu amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo kapena anthu achisoni angatchedwe bwanji achimwemwe? Anthu oterowo amaona moyenera zochitika zapadziko lapansili. Iwo “akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse” zimene zikuchitika masiku ano. (Ezekieli 9:4) Zimenezi siziwasangalatsa. Koma akaphunzira za cholinga cha Mulungu chobweretsa chilungamo padziko lapansi kwa anthu oponderezedwa, amakhala ndi chimwemwe chachikulu kwambiri.—Yesaya 11:4.
Kukonda chilungamo kumachititsanso anthu kumva chisoni chifukwa cholephera nthaŵi zambiri kuchita zinthu zoyenera. Akamatero ndiye kuti akuzindikira kusoŵa kwawo kwauzimu. Anthu oterowo amakhala ofunitsitsa kuti Mulungu awatsogolere chifukwa akudziŵa kuti ndi iye yekha amene angathandize anthu kuthana ndi zofooka zawo.—Miyambo 16:3, 9; 20:24.
Anthu amene amamva chisoni, amene amamva njala ndi ludzu la chilungamo, ndi amene amazindikira kusoŵa kwawo kwauzimu amadziŵa kufunika kokhala paubwenzi wabwino ndi Mlengi wawo. Kukhala paubwenzi wabwino ndi anthu kumabweretsa chimwemwe, koma kukhala paubwenzi wabwino ndi Mulungu kumabweretsa chimwemwe chambiri kuposa chimenecho. Indedi, anthu okondadi chilungamo, amene amafunitsitsa kutsogozedwa ndi Mulungu, angatchedwedi achimwemwe.
Komabe, zingakuvuteni kukhulupirira kuti munthu amene akuzunzidwa ndi kunyozedwa angakhale wachimwemwe. Koma ziyenera kukhala zoona, chifukwa Yesu mwiniwakeyo anatero. Choncho, kodi mawu akewo tiyenera kuwamva motani?
Kodi Zingatheke Bwanji Munthu Kukhala Wachimwemwe Akuzunzidwa?
Taonani kuti Yesu sananene kuti kunyozedwa ndi kuzunzidwa pakokha kumabweretsa chimwemwe. Iye anati: “Odala [“achimwemwe,” NW] ali akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo: . . . mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, . . . chifukwa cha Ine.” (Mateyu 5:10, 11) Choncho chimwemwe chimabwera kokha ngati munthu akunyozedwa chifukwa chotsatira Kristu ndi chifukwa choyendera mfundo zachilungamo zimene Yesu anaphunzitsa.
Chitsanzo cha zimenezi n’zimene zinachitikira Akristu oyambirira. Akuluakulu a bwalo lalikulu la Ayuda la Sanihedirini “adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.” Kodi atumwiwo anachita chiyani? ‘Pamenepo ndipo anapita kuchokera ku bwalo la akulu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo. Ndipo masiku onse, m’Kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.’—Machitidwe 5:40-42; 13:50-52.
Mtumwi Petro anapereka mfundo zina zosonyeza kugwirizana kumene kulipo pakati pa kunyozedwa ndi chimwemwe. Iye analemba kuti: “Mukatonzedwa pa dzina la Kristu, odala [“achimwemwe,” NW] inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.” (1 Petro 4:14) Zoonadi, kuzunzidwa monga Mkristu chifukwa chochita zinthu zabwino, ngakhale kukhale kosasangalatsa, kumabweretsa chimwemwe chimene munthu amakhala nacho chifukwa chodziŵa kuti walandira mzimu woyera wa Mulungu. Kodi mzimu wa Mulungu umagwirizana bwanji ndi chimwemwe?
Ntchito za Thupi Kapena Chipatso cha Mzimu?
Mzimu woyera wa Mulungu umakhala pa anthu okhawo amene amamumvera monga wolamulira. (Machitidwe 5:32) Yehova sapatsa mzimu wake kwa anthu amene amachita “ntchito za thupi.” Ntchito zimenezo ndi “dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, nyanga, madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magaŵano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere.” (Agalatiya 5:19-21) N’zoona kuti masiku ano “ntchito za thupi” zili paliponse. Komabe, anthu amene amachita zimenezo sakhala ndi chimwemwe chenicheni ndiponso chokhalitsa. M’malo mwake, kuchita zinthu zimenezo kumawononga ubwenzi wa munthu ndi abale ake, anzake, ndi anansi ake. Kuwonjezera apo, Mawu a Mulungu amati anthu ochita zinthu zimenezi “sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.”
Mosiyana ndi zimenezo, Mulungu amapereka mzimu wake kwa anthu amene amakulitsa “chipatso cha Mzimu.” Chipatso chimenechi chili ndi makhalidwe monga “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.” (Agalatiya 5:22, 23) Tikamasonyeza makhalidwe ameneŵa, zimatithandiza kuti tikhale pamtendere ndi anthu ena ndiponso ndi Mulungu, zimene zimabweretsa chimwemwe chenicheni. (Onani bokosi.) Kuposa pamenepo, tikamasonyeza chikondi, chifundo, kukoma mtima, ndi makhalidwe ena a Mulungu, timasangalatsa Yehova ndipo timakhala ndi chiyembekezo chosangalatsa chodzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu lachilungamo.
Munthu Amachita Kusankha Kuti Akhale Wachimwemwe
Pamene Wolfgang ndi Brigitte, anthu okwatirana a ku Germany, anayamba kuphunzira Baibulo mwakhama, anali ndi zinthu zambiri zimene anthu amati n’zimene zimabweretsa chimwemwe. Anali achinyamata ndiponso anali ndi thanzi labwino. Ankavala zovala zapamwamba, amakhala m’nyumba yokongoletsedwa bwino, ndipo anali ndi bizinesi yabwino. Nthaŵi yawo yambiri imathera pofuna kupeza zinthu zina zowonjezereka, komabe zimenezo sizinawapatse chimwemwe chenicheni. Koma patapita nthaŵi, Wolfgang ndi Brigitte anasankha kuchita zinthu zimene zinasinthiratu moyo wawo. Anayamba kumathera nthaŵi yambiri ndi kuchita khama pa zinthu zauzimu ndipo anafunafuna njira zoti ayandikire kwambiri kwa Yehova kuposa kale. Pasanapite nthaŵi yaitali, kuchita zimenezi kunasintha kaonedwe kawo ka zinthu, ndipo anakhala ndi moyo wosafuna zambiri ndiponso anayamba kutumikira monga apainiya, kapena kuti olengeza Ufumu nthaŵi zonse. Masiku ano, amatumikira mongodzipereka pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Germany. Kuwonjezera apo, akuphunzira chilankhulo cha ku Asia kuti athe kuthandiza alendo okhala m’dziko lawolo kuphunzira choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo.
Kodi banja limeneli linapeza chimwemwe chenicheni? Wolfgang akuti: “Chiyambireni kuchita zinthu zambiri zauzimu, takhala ndi chimwemwe chambiri kuposa kale. Kutumikira Yehova ndi mtima wonse kwalimbitsanso ukwati wathu. Tinali ndi ukwati wachimwemwe kale, koma tinali ndi maudindo ndi zinthu zina zimene timakonda zomwe zimadodometsa ukwati wathu. Tsopano tikuchita zinthu mogwirizana n’cholinga chimodzi.”
Kodi N’chiyani Chimafunika Kuti Munthu Akhale Wachimwemwe?
Mwachidule: Pewani “ntchito za thupi” ndipo kulitsani “chipatso cha Mzimu” wa Mulungu. Kuti munthu akhale wachimwemwe ayenera kulakalaka kukhala ndi ubwenzi wabwino kwambiri ndi Mulungu. Munthu amene amayesetsa kuchita zimenezi amafanana ndi munthu amene Yesu anamufotokoza kuti ndi wachimwemwe.
Choncho musaganize molakwika kuti simungathe kukhala munthu wachimwemwe. N’zoona kuti mwina panopa mukudwala kapena muli ndi mavuto a m’banja. Mwina simungathenso kukhala ndi ana kapena mukuyesetsa kupeza ntchito yabwino. Mwina panopa simukhalanso ndi ndalama zambiri ngati kale. Komabe, musataye mtima! Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto ameneŵa ndi mavuto enanso ambirimbiri. Zoonadi, posachedwapa Yehova Mulungu adzakwaniritsa mawu a wamasalmo otsatiraŵa kwa anthu amene amamutumikira: “Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya . . . Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.” (Salmo 145:13, 16) Monga mmene atumiki a Yehova ambirimbiri padziko lonse angavomerezere, kukumbukira lonjezo lolimbikitsa limeneli la Yehova kungakuthandizeni kwambiri kuti mukhale ndi chimwemwe panopa.—Chivumbulutso 21:3.
[Mawu a M’munsi]
a Iliyonse ya mfundo zimene Yesu ananenazi imayamba ndi mawu achigiriki oti ma·kaʹri·oi. M’malo momasulira mawu ameneŵa kuti “odala,” ngati mmene mabaibulo ena amachitira, Baibulo la New World Translation ndi mabaibulo ena, monga The Jerusalem Bible ndi Today’s English Version, amawamasulira molondola kuposa pamenepo kuti “achimwemwe.”
[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]
Zimene Zimathandiza Kuti Munthu Akhale Wachimwemwe
Chikondi chimachititsanso ena kuti azikukondani.
Mtendere umakuthandizani kuti mukhale ndi ubwenzi wabwino ndi anthu ena.
Kuleza Mtima kumakuthandizani kukhalabe achimwemwe ngakhale mukhale pachiyeso.
Chifundo chimakopa ena kuti akhale mabwenzi anu.
Kukoma Mtima kwanu kumachititsa ena kukuthandizani mukafunika thandizo.
Chikhulupiriro chimachititsa kuti Mulungu azikutsogolerani mwachikondi.
Chifatso chimakuthandizani kukhala ndi mtendere wa mu mtima ndi m’maganizo, ndi thanzi labwino.
Chiletso chimathandiza kuti zolakwitsa zanu zikhale zochepa.
[Zithunzi patsamba 7]
Kuti mukhale ndi chimwemwe, muyenera kukhutiritsa zosoŵa zanu zauzimu