Opatulidwa Kukhala Atamandi Achimwemwe pa Dziko Lonse
“Haleluya; lemekezani, inu atumiki a Yehova; lemekezani dzina la Yehova.”—SALMO 113:1.
1, 2. (a) Mogwirizana ndi Salmo 113:1-3, kodi ndani woyenerera chitamando chathu chochokera mumtima? (b) Kodi tiyenera kufunsa funso lotani?
YEHOVA MULUNGU ndiye Mlengi Wamkulu wa kumwamba ndi dziko lapansi, Mfumu yathu Yachilengedwe Chonse kunthaŵi zosatha. Iye ngwoyenerera zedi chitamando chathu chochokera mumtima. Ndiye chifukwa chake Salmo 113:1-3 limatilamula kuti: “Haleluya; lemekezani, inu atumiki a Yehova; lemekezani dzina la Yehova. Lodala dzina la Yehova kuyambira tsopano kufikira kosatha. Chitulukire dzuŵa kufikira kuloŵa kwake lilemekezedwe dzina la Yehova.”
2 Monga Mboni za Mulungu, tili okondwa kuchita zimenezi. Nzosangalatsa chotani nanga kuti posachedwapa Yehova Mulungu adzachititsa nyimbo imeneyi yachimwemwe imene tikuimba tsopano kudzaza dziko lonse lapansi! (Salmo 22:27) Kodi liwu lanu likumveka m’gulu lalikulu limeneli loimba la padziko lonse? Ngati zili choncho, muyenera kuti ndinu okondwa chotani nanga kuti mwapatulidwa padziko losagwirizanali ndi lopanda chimwemwe!
3. (a) Kodi nchiyani chimachititsa anthu a Yehova kukhala osiyana ndi ena? (b) Kodi tapatulidwa m’njira yotani?
3 Kutamanda kwathu Yehova mogwirizana kumatisiyanitsadi ndi ena. Timalankhula ndi kuphunzitsa zinthu zimodzimodzi ndi kugwiritsira ntchito njira zimodzimodzi zobukitsira ‘ubwino wa Yehova waukulu.’ (Salmo 145:7) Inde, monga anthu odzipatulira a Yehova, tapatulidwira utumiki wa Mulungu wathu, Yehova. Mulungu anauza anthu ake akale odzipatulira, Israyeli, kudzipatula ku mitundu yowazinga ndi kusadetsedwa ndi zochita za mitundu imeneyo. (Eksodo 34:12-16) Anapatsa anthu ake malamulo owathandiza kuchita zimenezi. Leronso, Yehova watipatsa Mawu ake Opatulika, Baibulo. Malangizo ake amatisonyeza mmene tingapatukire ku dzikoli. (2 Akorinto 6:17; 2 Timoteo 3:16, 17) Sitinapatulidwe mwa kukhala kwatokha ku nyumba za amonke ndi za avirigo, monga amachitira amonke ndi avirigo a Babulo Wamkulu. Kutsatira chitsanzo cha Yesu Kristu, ndife atamandi apoyera a Yehova.
Timatsanzira Mtamandi Wamkulu wa Yehova
4. Kodi Yesu anaika motani chitsanzo cha kutamanda Yehova?
4 Yesu sanapatuke pachifuno chake chotamanda Yehova. Ndipo zimenezi zinampatula ku dziko. M’masunagoge ndi pakachisi m’Yerusalemu, anatamanda dzina loyera la Mulungu. Kaya anali pamwamba pa phiri kapena pagombe, kulikonse kumene makamu anasonkhana, Yesu analalikira choonadi cha Yehova poyera. Analengeza kuti: “Ndikutamandani poyera, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi.” (Mateyu 11:25, NW) Ngakhale poyesedwa pamaso pa Pontiyo Pilato, Yesu anavomereza kuti: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi.” (Yohane 18:37) Yesu anazindikira kufunika kwa ntchito yake. Kulikonse kumene anali, Yesu anakhalira umboni Yehova ndi kumtamanda poyera.
5. Kodi Salmo 22:22 limanena za yani, ndipo tiyenera kukhala ndi maganizo otani?
5 Pa Salmo 22:22, tikupezapo mawuwa aulosi onena za Mtamandi Wamkulu wa Yehova: “Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga: pakati pa msonkhano ndidzakulemekezani.” Ndipo pa Ahebri 2:11, 12, mtumwi Paulo akugwiritsira ntchito mavesi ameneŵa kunena za Ambuye Yesu ndi awo amene Yehova Mulungu wawapatula kaamba ka ulemerero wakumwamba. Monga iye, iwo sachita manyazi kutamanda Yehova pakati pa msonkhano. Kodi timaganiza mofananamo pamene tili pamisonkhano yathu ya mpingo? Kutengamo mbali kwathu mwachangu m’misonkhano, mwa kumvetsera, kuyankhapo ndi kuimba, kumatamanda Yehova. Koma kodi chitamando chathu chachimwemwe chimathera pamenepo?
6. Kodi Yesu anatuma ophunzira ake kuchitanji, ndipo kodi okonda kuunika amamlemekeza motani Mulungu?
6 Malinga ndi kunena kwa Mateyu 5:14-16, Ambuye Yesu analamulanso otsatira ake kulola kuunika kwawo kuŵala kuti enanso atamande Yehova. Iye anati: “Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. . . . Muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.” Okonda kuunika amadzetsa ulemerero kwa Mulungu. Kodi amachita zimenezi mwa kungonena ndi kuchita zinthu zabwino, zothandiza ena? Ayi, m’malo mwake amazichita mwa kulemekeza Yehova mogwirizana. Inde, okonda kuunika amadzipatulira kwa Mulungu ndi kukhala atamandi ake achimwemwe. Kodi mwatenga sitepe lachimwemwe limeneli?
Chimwemwe Chifukwa Chotamanda Yehova
7. Kodi nchifukwa ninji atamandi a Yehova ali achimwemwe chonchi, ndipo anasangalala ndi chiyani patsiku la Pentekoste wa 33 C.E.?
7 Kodi atamandi a Yehova akhaliranji achimwemwe chonchi? Chifukwa chakuti chimwemwe ndi chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu. Pa Agalatiya 5:22, ndicho chimatsatira chikondi. Ophunzira a Yesu m’zaka za zana loyamba anasonyeza chipatso chimenechi cha mzimu wa Yehova. Eetu, patsiku la Pentekoste wa 33 C.E., pamene Mulungu anatsanulira mzimu wake pa ophunzira a Yesu ngati 120, onsewo anayamba kutamanda Yehova m’malilime osiyanasiyana. Ayuda opembedza amene anadza ku Yerusalemu kuchokera m’mitundu yosiyanasiyana ‘anasokonezeka ndi kudabwa.’ Iwo anadabwa nati: “Tiwamva iwo alikulankhula m’malilime athu zazikulu za Mulungu”! (Machitidwe 2:1-11) Kodi kutamanda Yehova kodabwitsaku m’zinenero zosiyanasiyana kunachititsanji? Ayuda ndi otembenukira ku Chiyuda ngati 3,000 analandira uthenga wabwino wa Ufumu wonena za Mesiya. Iwo anabatizidwa, kulandira mzimu woyera, ndipo mofunitsitsa iwonso anakhala atamandi achimwemwe a Yehova. (Machitidwe 2:37-42) Linalitu dalitso lalikulu chotani nanga!
8. Pambuyo pa Pentekoste, kodi Akristu anatani kuti awonjezere chimwemwe chawo?
8 Lipotilo likupitiriza kuti: “Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi m’kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwawo, analandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona; nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawawonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.” (Machitidwe 2:46, 47) Kodi kunali chabe kukumana kwawo pamodzi ndi kudyera chakudya limodzi kumene kunawapatsa chimwemwe chachikulu? Ayi, anapeza chimwemwe chachikulu chifukwa chotamanda Yehova Mulungu tsiku ndi tsiku. Ndipo chimwemwe chawo chinakula pamene anaona zikwizikwi akulabadira uthenga wawo wachipulumutso. Ndi mmene zililinso ndi ife lero.
Atamandi Achimwemwe m’Mitundu Yonse
9. (a) Ndi liti pamene Mulungu anayamba kupatsa anthu a mitundu yonse mwaŵi wa kumva uthenga wake wabwino, ndipo motani? (b) Kodi nchifukwa ninji mzimu woyera unatsanuliridwa pa Korneliyo ndi anzake asanabatizidwe?
9 Yehova sanafune kuti ntchito yonyamula kuunika ya atumiki ake ingokhala ya mtundu umodzi wa anthu. Choncho, kuyambira mu 36 C.E., anapatsa anthu a mitundu yonse mwaŵi wa kumva uthenga wake wabwino. Motsogozedwa ndi Mulungu, Petro anapita kunyumba ya Mkulu wa asilikali wa ku Kaisareya amene anali Wakunja. Kumeneko anapeza Korneliyo atasonkhana ndi anzake onse apafupi kwambiri ndi banja lake. Pamene anali kumvetsera mawu a Petro mwachidwi, iwo anakhulupirira mwa Yesu m’mitima yawo. Tikudziŵa motani? Chifukwa chakuti mzimu woyera wa Mulungu unadza pa okhulupirira Akunja amenewo. Nthaŵi zonse, mphatso ya mzimu wa Mulungu inali kuperekedwa kokha pambuyo pa ubatizo, koma pachochitikacho Yehova anasonyeza kuti wayanja osakhala Ayuda ameneŵa asanabatizidwe. Yehova akadapanda kutero, Petro sakanatsimikiza kuti tsopano Mulungu anali kulandira Akunja kukhala atumiki Ake ndi kuti anayenerera ubatizo wa m’madzi.—Machitidwe 10:34, 35, 47, 48.
10. Kodi zinanenedweratu motani kuyambira kalekale kuti anthu a mitundu yonse adzatamanda Yehova?
10 Kuyambira kalekale, Yehova ananeneratu kuti anthu a mitundu yonse adzamtamanda. Anali kudzakhala ndi atamandi achimwemwe m’dziko lililonse. Potsimikiza zimenezi, mtumwi Paulo anagwira mawu maulosi a m’Malemba Achihebri. Anauza mpingo wa ku Roma wa Akristu ochokera m’mitundu yonse kuti: ‘Mulandirane wina ndi mnzake, monganso Kristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero. Ndipo ndinena kuti Kristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, chifukwa cha choonadi cha Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa makolo, ndi kuti anthu a mitundu ina akalemekeze Mulungu, chifukwa cha chifundo; monga kwalembedwa [pa Salmo 18:49], Chifukwa cha ichi ndidzakuvomerezani inu pakati pa anthu amitundu, ndidzaimbira dzina lanu. Ndiponso anena [pa Deuteronomo 32:43], Kondwani, amitundu inu, pamodzi ndi anthu ake. Ndiponso [pa Salmo 117:1], Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse; ndipo anthu onse amtamande.’—Aroma 15:7-11.
11. Kodi Mulungu wawathandiza motani anthu a mitundu yonse kuphunzira choonadi chake, ndipo patsatiranji?
11 Anthu sangatamande Yehova mogwirizana ngati saika chiyembekezo chawo pa Yesu Kristu, uyo amene Mulungu wasankha kuti alamulire anthu a mitundu yonse. Kuti awathandize kuzindikira choonadi Chake chotsogolera ku moyo wosatha, Mulungu wakonza programu yophunzitsa ya padziko lonse. Iye akupereka malangizo kudzera mwa kagulu kake ka kapolo wokhulupirika. (Mateyu 24:45-47) Zotsatirapo zake? Mawu achimwemwe oposa mamiliyoni asanu akuimba zitamando za Yehova m’maiko oposa 230. Ndipo mamiliyoni enanso akusonyeza kuti nawonso akufuna kutero. Taonani amene anapezeka pa Chikumbutso mu 1996: 12,921,933. Zodabwitsa!
Khamu Lalikulu la Atamandi Achimwemwe Linenedweratu
12. Kodi ndi masomphenya odzutsa chikondwerero otani amene mtumwi Yohane anaona, ndipo zenizeni zake zikuchitika motani?
12 M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona “khamu lalikulu” la ochokera m’mitundu yonse. (Chivumbulutso 7:9) Kodi zitamando zimene khamu lalikululi likuimba pamodzi ndi otsalira odzozedwa a Mulungu zikunena chiyani? Yohane akutiuza kuti: “Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 7:10) Chitamandochi chikulengezedwa molimba mtima kumbali iliyonse ya dziko. Titanyamula makhwatha a kanjedza, titero kunena kwake, tipereka ulemu kwa Mulungu pokhala Mfumu Yachilengedwe Chonse ndipo mwachimwemwe tivomereza pamaso pa miyamba ndi dziko lapansi kuti chipulumutso chathu chili kwa iye ndi Mwana wake, Mwanawankhosa, Yesu Kristu. Ndithudi, mtumwi Yohane ayenera kuti anasangalala chotani nanga ataona masomphenya olimbitsa ameneŵa a khamu lalikulu! Ndipo tili osangalala chotanga nanga lerolino poona zochitika zenizeni, ngakhale kukhala mbali, ya zimene Yohane anaona!
13. Kodi nchiyani chimapatula anthu a Yehova ku dziko?
13 Monga atumiki a Yehova, tinyamula dzina lake monyadira. (Yesaya 43:10, 12) Kukhala kwathu Mboni za Yehova kumatisiyanitsa ndi dziko lino. Nkokondweretsa chotani nanga kunyamula dzina la Mulungu losiyana ndi maina onse ndipo kuchita ntchito yake yaumulungu kukhala chifuno chathu m’moyo! Chifuno chachikulu cha Yehova choyeretsa dzina lake lopatulika ndi kukweza uchifumu wake wachilengedwe chonse mwa Ufumu wake chachititsa moyo wathu kukhala watanthauzo. Ndipo watithandiza kukhala ndi malo pachifuno chake chaumulungu chokhudza dzina lake ndi Ufumu wake. Wachita zimenezi m’njira zitatu.
Watipatsa Choonadi
14, 15. (a) Kodi Mulungu watithandiza m’njira ina yotani kuti tikhale ndi malo pachifuno chake chaumulungu chokhudza dzina lake ndi Ufumu wake? (b) Kodi Ufumu wokhazikitsidwa mu 1914 C.E. ukusiyana motani ndi umene unagwetsedwa mu 607 B.C.E.?
14 Choyamba, Yehova wapatsa anthu ake choonadi. Vumbulutso losangalatsa kwambiri ndilo lakuti Ufumu wake unayamba kulamulira mu 1914. (Chivumbulutso 12:10) Boma lakumwamba limeneli nlosiyana ndi ufumu woyambawo wa ku Yerusalemu, kumene mafumu a mumzere wa Davide ankakhala. Ufumu umenewo unagwetsedwa, ndipo kuyambira mu 607 B.C.E., Yerusalemu yense anayamba kulamulidwa ndi mphamvu zadziko zachikunja. Ufumu watsopano umene Yehova anakhazikitsa mu 1914 uli ulamuliro wakumwamba umene sudzagonjera wina aliyense koma Yehova yekha, ndipo sudzawonongedwa konse. (Danieli 2:44) Ndiponso, ulamuliro wake ngwosiyana. Motani? Chivumbulutso 11:15 chikuyankha kuti: ‘Panakhala mawu aakulu m’mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthaŵi za nthaŵi.’
15 “Ufumu . . . wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wake” ukulamulira dziko lonse la mtundu wa munthu. Chisonyezero chatsopano chimenechi cha uchifumu wa Yehova, chimene chikuphatikizapo Mwana wake Waumesiya ndi abale a Yesu 144,000, ambiri amene tsopano aukitsidwira kuulemerero wakumwamba, sinkhani yophunzira chabe—imene ophunzira angakonde kukambitsirana. Ayi, Ufumu wakumwamba umenewu ndi boma lenileni. Ndipo chiyembekezo chathu chosangalatsa chokhala ndi moyo kosatha mu ungwiro chifukwa cha ulamuliro wake chimatipatsa chifukwa chabwino kwambiri chokhalirabe okondwa. Kupatsidwa choonadi chimenechi cha Mawu a Yehova kumatisonkhezera nthaŵi zonse kulankhula bwino za icho. (Salmo 56:10) Kodi mumachita zimenezi nthaŵi zonse mwa kuuza aliyense kuti Ufumu wa Mulungu Waumesiya tsopano ukulamulira kumwamba?
Timathandizidwa ndi Mzimu Woyera ndi Ubale wa Padziko Lonse
16, 17. Kodi njira yachiŵiri ndi yachitatu zimene Mulungu watithandizira kuti tikhale ndi mbali pachifuno chake chaumulungu ndi ziti?
16 Njira yachiŵiri imene Mulungu watithandizira kukhala ndi malo pachifuno chake chaumulungu ndiyo mwa kutipatsa mzimu wake woyera, umene umatikhozetsa kubala zipatso zake zokongola m’moyo wathu ndi kupeza chiyanjo chake. (Agalatiya 5:22, 23) Ndiponso, Paulo analembera Akristu odzozedwa kuti: “Tinalandira ife . . . Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziŵe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu.” (1 Akorinto 2:12) Mwa kulabadira mzimu wa Yehova, tonsefe tsopano titha kudziŵa ndi kumvetsa zinthu zabwino zimene watipatsa lerolino mwaufulu—malonjezo ake, malamulo ake, mapulinsipulo ake, ndi zina zotero.—Yerekezerani ndi Mateyu 13:11.
17 Ponena za njira yachitatu imene Mulungu akutithandizira nayo, tili ndi ubale wathu wa padziko lonse ndi makonzedwe a Yehova abwino kwambiri olambira monga gulu. Mtumwi Petro analankhula za makonzedwewo pamene anatilimbikitsa ‘kukhala ndi chikondi kwa gulu lonse la abale.’ (1 Petro 2:17, NW) Banja lathu lachikondi la padziko lonse la abale ndi alongo limatithandiza kutumikira Yehova ndi mtima wokondwa kwambiri, monga momwe Salmo 100:2 limalamulira kuti: “Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera.” Vesi 4 limapitiriza kuti: “Loŵani ku zipata zake ndi chiyamiko, ndi ku mabwalo ake ndi chilemekezo: myamikeni; lilemekezeni dzina lake.” Choncho kaya tikulalikira poyera kapena tili pamisonkhano, tidzakhala okondwa. Tapezatu mtendere weniweni ndi chisungiko chotani nanga m’mabwalo okongola a kachisi wauzimu wa Yehova!
Tamandani Yehova Mokondwa!
18. Nchifukwa ninji tingasangalale ndi kutamanda Yehova mosasamala kanthu za chizunzo kapena mavuto ena amene timakumana nawo?
18 Kaya tivutike ndi mikhalidwe yotani, chizunzo, kapena mavuto ena, tiyeni tikhale okondwa kuti tili m’nyumba ya Yehova yolambiriramo. (Yesaya 2:2, 3) Kumbukirani kuti chimwemwe ndi mkhalidwe wa mtima. Abale ndi alongo athu achikristu oyambirira anali atamandi achimwemwe a Yehova ngakhale anavutika kwambiri ndi kutaya zambiri. (Ahebri 10:34) Okhulupirira anzathu lerolino ali monga iwo.—Mateyu 5:10-12.
19. (a) Kodi ndi malamulo otani obwerezabwereza amene amatisonkhezera kutamanda Yehova? (b) Moyo wathu wamuyaya umadalira pa chiyani, ndipo tatsimikiza mtima kuchitanji?
19 Tonsefe amene tikutumikira Yehova timakondwa kulabadira malamulo a Baibulo akuti timtamande. Mobwerezabwereza buku la Chivumbulutso litatchula zitamando za Mulungu limatchulanso mawu akuti “Aleluya.” (Chivumbulutso 19:1-6) M’mavesi asanu ndi limodziwo a Salmo 150, tikuuzidwa nthaŵi 13 kuti titamande Yehova. Ili ndi pempho loitanira chilengedwe chonse kuti chigwirizane kuimbira Yehova zitamando mwachimwemwe. Moyo wathu wamuyaya ukudalira pa kugwirizana nawo kuimba mang’ombe aakulu ameneŵa akuti Aleluya! Inde, anthu amene adzakhala ndi moyo kosatha ndi okhawo amene akutamanda Yehova mosalekeza. Chotero, tatsimikiza mtima kumamatira mwamphamvu ku mpingo wake wokhulupirika wa padziko lonse pamene mapeto akuyandikira. Tikatero, tidzakhala ndi chiyembekezo cha kuona mawu omaliza a Salmo 150 atakwaniritsidwa onse: “Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Haleluya.”
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchiyani chimasiyanitsa anthu a Yehova ndi ena?
◻ Kodi nchifukwa ninji atumiki a Yehova ali achimwemwe chonchi?
◻ Kodi nchiyani chimatipatula ku dziko?
◻ Kodi Mulungu watithandiza m’njira zitatu ziti kuti tikhale ndi malo pachifuno chake chaumulungu?
[Chithunzi patsamba 17]
Kulikonse kumene Yesu anali, anachitira umboni Yehova ndi kumtamanda poyera