Pamene Sikudzakhalanso Uchimo
“KODI timabadwira mu uchimo?” Funso limenelo linamvutitsa wophunzira wina wa digirii ku United States atangoyamba kuphunzira Baibulo. Pokhala Mhindu, lingaliro la uchimo wobadwa nawo linali lachilendo kwa iye. Koma anaganiza kuti, ngati uchimo ulidi wobadwa nawo, ndiye kuti kunyalanyaza kapena kukana kuti ulipo kungakhale kosathandiza. Kodi munthu angadziŵe bwanji yankho la funso limeneli?
Ngati uli wobadwa nawo, ndiye kuti uchimo uli ndi chiyambi chake. Kodi munthu woyambayo analengedwa ali woipa, kotero kuti anagaŵira ana ake mikhalidwe yoipa? Kapena kodi anakhala ndi chilemacho pambuyo pake? Kwenikwenidi kodi uchimo unayamba liti? Chabwino, ngati uchimo uli choipa china chapambali, kapena khalidwe, kodi tingayembekezere kuti tidzawonjokamo?
Malinga ndi zimene Ahindu amakhulupirira, kuvutika ndi kuipa zangokhala mbali ya chilengedwe. “Kuvutika [kapena kuipa],” akutero katswiri wina wa maphunziro Mhindu, “monga nyamakazi yachikhalire, kumangochoka pamalo ena kumka pamalo ena koma sikungatheretu.” Ndithudi kuipa kwakhala ndi anthu m’mbiri yonse. Ngati kunachitika mbiri ya munthu isanayambe kulembedwa, ndiye kuti mayankho odalirika ponena za mmene kunayambira ayenera kuchokera kwa munthu wapamwamba kuposa munthu wathupi. Mayankho ayenera kuchokera kwa Mulungu.—Salmo 36:9.
Munthu—Analengedwa Wopanda Uchimo
Wafilosofi wachihindu, Nikhilananda, akuvomereza kuti mafotokozedwe a kulengedwa kwa munthu amene ali mu Vedas ngophiphiritsira. Mofananamonso, zipembedzo zambiri za Kummaŵa zimangolongosola chilengedwe mwa nthanthi basi. Komabe, tili ndi zifukwa zomveka ndipo zogwirizana ndi sayansi zokhulupirira nkhani ya Baibulo ya kulengedwa kwa munthu woyamba.a Chaputala chake choyambirira chimati: “Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.”—Genesis 1:27.
Kodi kumatanthauzanji kulengedwa “m’chifanizo cha Mulungu”? Kumangotanthauza izi: Munthu anapangidwa m’chifanefane cha Mulungu, ali ndi mikhalidwe yaumulungu—yonga chilungamo, nzeru, ndi chikondi—imene imamsiyanitsa ndi nyama. (Yerekezerani ndi Akolose 3:9, 10.) Mikhalidwe imeneyi inamtheketsa kusankha kuchita chabwino kapena choipa, inampanga kukhala munthu wokhoza kudzisankhira. Munthu woyambayo analibe uchimo, sanali kuvutika ndi choipa pamoyo wake, pamene analengedwa.
Munthuyo Adamu, Yehova Mulungu anamlamula kuti: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Mwa kusankha kumvera, Adamu ndi mkazi wake, Hava, akanatamanda ndi kulemekeza Mlengi wawo ndi kukhalabe opanda uchimo. Komano, kusamvera kukanasonyeza kulephera kwawo kukwaniritsa mikhalidwe yapamwamba ya Mulungu ndipo kukanawapangitsa kukhala opanda ungwiro—ochimwa.
Adamu ndi Hava sanalengedwe ngati milungu. Komabe, anali nayo mikhalidwe yaumulungu ndi nzeru yosankhira chabwino ndi choipa. Poti anali chilengedwe cha Mulungu, anali opanda uchimo, kapena kuti anali angwiro. (Genesis 1:31; Deuteronomo 32:4) Kulengedwa kwawo sikunadodometse chigwirizano chimene chinalipo pakati pa Mulungu ndi chilengedwe chonse kwa zaka zosaŵerengeka mpaka pamene analengedwa. Ndiye nanga uchimo unayambika bwanji?
Chiyambi cha Uchimo
Uchimo unayambika kumalo a mizimu. Mulungu asanalenge dziko lapansi ndi munthu, analenga zolengedwa zauzimu zaluntha—angelo. (Yobu 1:6; 2:1; 38:4-7; Akolose 1:15-17) Mmodzi wa angelo ameneŵa anaganiza kwambiri za kukongola kwake ndi nzeru yake. (Yerekezerani ndi Ezekieli 28:13-15.) Atamva Mulungu akulangiza Adamu ndi Hava kuti abale ana, mngelo ameneyo anadziŵa kuti posakhalitsa dziko lapansi lidzadzaza anthu olungama, onse olambira Mulungu. (Genesis 1:27, 28) Cholengedwa chauzimu chimenechi chinafuna kuti iwo azichilambira. (Mateyu 4:9, 10) Kuganizabe za chikhumbo chimenechi kunampangitsa kutenga njira yolakwika.—Yakobo 1:14, 15.
Polankhula ndi Hava kupyolera mwa njoka, mngelo wopandukayo anati pomletsa kudya chipatso cha mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa, Mulungu anali kummana chidziŵitso china chimene Hava anayenera kukhala nacho. (Genesis 3:1-5) Limenelo linali bodza laudani—uchimo. Mwa kunena bodza limenelo, mngeloyo anakhala wochimwa. Nchifukwa chake anatchedwa Mdyerekezi, woneneza, ndi Satana, wotsutsa Mulungu.—Chivumbulutso 12:9.
Kunyengerera kwa Satana kunamsokeretsa Hava. Atakhulupirira mawu a Woyesayo, iye ananyengeka ndipo anadya zipatso zina za mtengo woletsedwawo. Mwamuna wake, Adamu, nayenso anadya chipatsocho, ndipo onsewo anakhala ochimwa. (Genesis 3:6; 1 Timoteo 2:14) Inde, mwa kusankha kusamvera Mulungu, makolo athu oyambawo anaphonya ungwiro ndipo anakhala ochimwa.
Bwanji nanga za ana a Adamu ndi Hava? Baibulo likufotokoza kuti: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Lamulo lacholoŵa linali litayamba kale kugwira ntchito. Adamu sakanapatsa ana ake zimene iye analibe. (Yobu 14:4) Atataya ungwiro wawo, mwamuna ndi mkazi oyambawo anali ochimwa pamene anabala ana awo. Ndiye tonsefe—popanda wotsala—tinabadwa tili ochimwa. (Salmo 51:5; Aroma 3:23) Ndiyeno, uchimo wangobala kuipa ndi kuvutika. Ndiponso, chifukwa cha uwo, tonsefe timakalamba ndi kufa, “pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa.”—Aroma 6:23.
Chikumbumtima ‘Chimaneneza’ kapena ‘Kukanira’
Talingaliraninso zimene anthu aŵiri oyambawo anachita chifukwa cha mphamvu yauchimo. Anaphimba mbali zina za matupi awo ndipo anayesa kubisala kuti Mulungu asawaone. (Genesis 3:7, 8) Chotero uchimo unawapangitsa kudziimba mlandu, kuda nkhaŵa, ndi kuchita manyazi. Leronso anthu akuzidziŵa bwino kwambiri zimenezi.
Ndani amene sanavutikepo maganizo chifukwa cholephera kuchitira chifundo munthu wina wosoŵa kapena yemwe sanamvepo chisoni chifukwa chonena mawu amene sanayenere kunena? (Yakobo 4:17) Nchifukwa ninji timavutika maganizo ndi zimenezo? Mtumwi Paulo akufotokoza kuti ‘lamulo linalembedwa m’mitima yathu.’ Kungolakwira lamulo limenelo munthu amavutika mtima kwambiri, pokhapokha ngati chikumbumtima chake chili chokakala. Ndiye zilidi choncho kuti liwu la chikumbumtima ‘limatineneza’ kapena ‘kutikanira.’ (Aroma 2:15; 1 Timoteo 4:2; Tito 1:15) Kaya timadziŵa kapena sitidziŵa, koma mkati mwathu timazindikira cholakwa, uchimo!
Paulo anawadziŵa bwino maganizo ake auchimo. “Pamene ndifuna chabwino, choipa chiliko,” anavomereza choncho. “Ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiona lamulo lina m’ziŵalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziŵalo zanga.” Choncho Paulo anafunsa kuti: “Adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi?”—Aroma 7:21-24.
Kumasuka ku Uchimo—Motani?
“Kumasuka, pamwambo wachihindu,” akutero katswiri wina wa maphunziro, “ndiko kumasuka pakubadwa ndi kufa mobwerezabwereza.” Monga yankho, Chibudanso chimanena za Nirvana—mkhalidwe woiŵala zakunja. Pokhala atalephera kuzindikira kuti pali uchimo wobadwa nawo, Ahindu amangolonjeza kuti anthu adzawonjoka pamoyo ulipowu.
Koma tsopano, njira yachimasuko imene Baibulo limanena idzakhala yongochotseratu mkhalidwe wauchimo. Atafunsa kuti nanga adzalanditsidwa bwanji ku uchimo, mtumwi Paulo akupitiriza kuyankha kuti: “Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu”! (Aroma 7:25) Inde, wolanditsa ndiye Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu.
Malinga ndi Uthenga Wabwino wa Mateyu, “Mwana wa Munthu,” Yesu Kristu, anadza ‘kudzapereka moyo wake dipo la anthu ambiri.’ (Mateyu 20:28) Paulo analemba pa 1 Timoteo 2:6, kuti Yesu “anadzipereka yekha chiwombolo [“dipo lolinganiza,” NW], m’malo mwa onse.” Liwu lakuti “dipo” limatanthauza kulipira mtengo wowombolera andende. Kunena koti dipo lolinganiza kumasonyeza kuti mtengowo uli ndi mphamvu yolinganiza muyezo wachilungamo. Komano kodi imfa ya munthu mmodzi ingaonedwe bwanji ngati “dipo lolinganiza m’malo mwa onse”?
Anthu onse, kuphatikizapo ifeyo, Adamu anatigulitsa ku uchimo ndi imfa. Mtengo, kapena faindi, imene analipira inali moyo wake wangwiro. Ndiye kuti umenewo uwomboledwe, moyo wina wangwiro—dipo lolinganiza—unayenera kuperekedwa. (Eksodo 21:23; Deuteronomo 19:21; Aroma 5:18, 19) Popeza munthu wopanda ungwiro sangathe kupereka dipo limenelo, Mulungu, mwa nzeru zake zakuya, anatsegula njira yochokera m’vuto limeneli. (Salmo 49:6, 7) Anasamutsa moyo wangwiro wa Mwana wake wobadwa yekha kuuchotsa kumwamba nkuuika m’mimba ya namwali wina padziko lapansi, kuti abadwe ali munthu wangwiro.—Luka 1:30-38; Yohane 3:16-18.
Kuti akwaniritse ntchito yowombola anthu, Yesu anafunikira kukhalabe wokhulupirika kwa nthaŵi yonse imene anali padziko lapansi. Ndipo anakhulupirikadi. Ndiyeno anafa imfa yansembe. Mwa njira imeneyo Yesu anatsimikiza kuti mtengo wa moyo wangwiro—wakewake—udzakhala dipo lowombolera anthu.—2 Akorinto 5:14; 1 Petro 1:18, 19.
Zimene Dipo la Kristu Lingatichitire
Nsembe ya dipo ya Yesu ingatipindulitse ngakhale tsopano. Mwa kuikhulupirira, tingakhale ndi kaimidwe koyera pamaso pa Mulungu ndipo Yehova angatisamale mwachikondi. (Machitidwe 10:43; Aroma 3:21-24) M’malo mosweka mtima ndi machimo amene tingakhale titachita, tingapemphe mwaufulu chikhululukiro kwa Mulungu chifukwa cha dipo limenelo.—Yesaya 1:18; Aefeso 1:7; 1 Yohane 2:1, 2.
Masiku akudzawo, dipo limenelo lidzatheketsa kuti anthu achiritsidwe pamatenda awo onse amene anayamba chifukwa cha uchimo. Buku lotsiriza la Baibulo limasimba za “mtsinje wa madzi a moyo” wochokera ku mpando wachifumu wa Mulungu. M’mphepete mwa mtsinjewo muli mitengo yambiri yazipatso yokhala ndi masamba “akuchiritsa nawo amitundu.” (Chivumbulutso 22:1, 2) Mophiphiritsira, Baibulo pano likunena za makonzedwe odabwitsa a Mlengi omasula anthu ku uchimo ndi imfa kwamuyaya mwa nsembe ya dipo ya Yesu.
Masomphenya olosera a m’buku la Chivumbulutso adzakwaniritsidwa posachedwapa. (Chivumbulutso 22:6, 7) Ndiyeno owongoka mtima onse adzakhala angwiro, ‘atamasulidwa ku ukapolo wa chivundi.’ (Aroma 8:20, 21) Kodi zimenezi siziyenera kutisonkhezera kuphunzira zambiri ponena za Yehova Mulungu ndi Mwana wake wokhulupirikayo, Yesu Kristu, yemwe anadzakhala dipo?—Yohane 17:3.
[Mawu a M’munsi]
a Onani buku lakuti Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation?, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 6]
Adamu analoŵetsa anthu mu uchimo ndi imfa
[Chithunzi patsamba 7]
Nsembe ya dipo ya Yesu imatimasula ku uchimo ndi imfa