Ndife “Osakhalitsa” M’dziko Loipali
“Onsewa . . . analengeza poyera kuti iwo anali alendo ndi osakhalitsa m’dzikolo.”—AHEB. 11:13.
1. Kodi Yesu ananena kuti ophunzira ake adzakhala otani m’dzikoli?
YESU ananena kuti ophunzira ake ‘adakali m’dzikoli koma sali mbali ya dziko, monganso iye sanali mbali ya dziko.’ (Yoh. 17:11, 14) Ndi mawu amenewa, Yesu anasonyeza kuti otsatira ake sali mbali ya dzikoli lomwe mulungu wake ndi Satana. (2 Akor. 4:4) Akhristu amakhala m’dzikoli koma sali mbali yake. Iwo amangokhala monga “alendo ndiponso anthu osakhalitsa.”—1 Pet. 2:11.
Ankakhala Monga Anthu “Osakhalitsa M’dzikolo”
2, 3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Inoki, Nowa ndiponso Abulahamu ndi Sara anakhala ndi moyo monga alendo ndiponso anthu osakhalitsa m’dziko?
2 Kuyambira kalekale, atumiki a Yehova okhulupirika akhala akuchita zinthu mosiyana kwambiri ndi anthu ena m’dzikoli. Ena mwa anthu amenewa anali Inoki ndi Nowa omwe “anayendabe ndi Mulungu woona” Chigumula chisanachitike. (Gen. 5:22-24; 6:9) Onsewa ankalalikira molimba mtima kuti Yehova aweruza dziko loipa la Satana. (Werengani 2 Petulo 2:5; Yuda 14, 15.) Chifukwa chakuti Inoki anayenda ndi Mulungu m’dziko loipa, ‘Mulungu anakondwera naye.’ Nayenso Nowa anali “wopanda cholakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake.”—Aheb. 11:5; Gen. 6:9.
3 Abulahamu ndi Sara anasiya moyo wabwino mumzinda wa Uri wa Akasidi ndipo anayamba kukhala moyo wosamukasamuka m’dziko lachilendo. (Gen. 11:27, 28; 12:1) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mwa chikhulupiriro, Abulahamu ataitanidwa, anamvera ndi kupita kumalo amene anali kuyembekezera kuwalandira monga cholowa. Iye anapitadi, ngakhale sanadziwe kumene anali kupita. Mwa chikhulupiriro, anakhala monga mlendo m’dziko la lonjezo ngati kuti akukhala m’dziko lachilendo. Ndipo anali kukhala m’mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, anzake olandira nawo limodzi lonjezolo.” (Aheb. 11:8, 9) Ponena za atumiki a Yehova okhulupirikawa, Paulo ananena kuti: “Onsewa anafa ali ndi chikhulupiriro, ngakhale kuti sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezowo. Koma anawaona ali patali ndi kuwalandira, ndipo analengeza poyera kuti iwo anali alendo ndi osakhalitsa m’dzikolo.”—Aheb. 11:13.
Aisiraeli Anachenjezedwa
4. Kodi Aisiraeli anachenjezedwa za chiyani asanalowe m’dziko lomwe anapatsidwa?
4 Aisiraeli omwe ndi mbadwa za Abulahamu anadzakhala mtundu waukulu ndipo Mulungu anawapatsa Chilamulo komanso dziko. (Gen. 48:4; Deut. 6:1) Aisiraeli anafunika kukumbukira nthawi zonse kuti Mwini wa dziko lawo anali Yehova. (Lev. 25:23) Iwo anali ngati anthu a lendi ndipo anafunika kumvera Mwini malowo. Anafunikanso kukumbukira kuti “munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha.” Iwo sanayenere kulola kuti zinthu zakuthupi ziwaiwalitse Yehova. (Deut. 8:1-3) Asanalowe m’dziko lawo, Aisiraeli anachenjezedwa kuti: ‘Ndiyeno Yehova Mulungu wanu akadzakulowetsani m’dziko limene analumbirira makolo anu Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti adzakupatsani, dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu yooneka bwino imene simunamange ndinu, yokhalanso ndi nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino zimene simunaikemo ndinu, ndi zitsime zimene simunakumbe ndinu, minda ya mpesa ndi mitengo ya maolivi imene simunabzale ndinu, n’kudya ndi kukhuta, samalani kuti musaiwale Yehova.’—Deut. 6:10-12.
5. N’chifukwa chiyani Yehova anakana Aisiraeli, ndipo kodi anasankha mtundu watsopano uti?
5 Aisiraeli sanatsatire chenjezo la Yehova limeneli. Alevi ena m’masiku a Nehemiya anakumbukira zimene zinachitika Aisiraeli atalowa m’Dziko Lolonjezedwa. Aisiraeli atakhala ndi nyumba zabwino, chakudya ndiponso vinyo, ‘anayamba kudya, kukhuta komanso kunenepa.’ Iwo anapandukira Mulungu ndipo ankapha aneneri amene anatumizidwa kuti akawachenjeze. Izi zinachititsa kuti Yehova awapereke m’manja mwa adani awo. (Werengani Nehemiya 9:25-27; Hos. 13:6-9) Kenako mu ulamuliro wa Aroma, Ayuda opanda chikhulupiriro amenewo, mpaka anafika popha Mesiya amene Mulungu analonjeza. Izi zinachititsa kuti Yehova awakane n’kusankha mtundu watsopano, womwe ndi Isiraeli wauzimu.—Mat. 21:43; Mac. 7:51, 52; Agal. 6:16.
“Simuli Mbali ya Dzikoli”
6, 7. (a) Kodi Yesu anati otsatira ake ayenera kukhala bwanji m’dzikoli? (b) N’chifukwa chiyani Akhristu oona sankafunikira kukhala mbali ya dziko la Satana?
6 Monga taonera kumayambiriro kwa nkhani ino, Yesu Khristu yemwe ndi Mutu wa mpingo wachikhristu ananena kuti otsatira ake sadzakhala mbali ya dziko la Satana loipali. Atatsala pang’ono kuphedwa, iye anauza otsatira ake kuti: “Mukanakhala mbali ya dziko, dziko likanakukondani monga mbali yake. Koma popeza simuli mbali ya dzikoli, koma ine ndinakusankhani kuchokera m’dziko, pa chifukwa chimenechi dziko likudana nanu.”—Yoh. 15:19.
7 Pamene Chikhristu chinayamba kufala, kodi Akhristu anafunika kugwirizana ndi dziko n’kukhala mbali yake? Ayi. Iwo anafunika kusiyana ndi dziko la Satanali, kulikonse kumene angakhale. Zaka 30 pambuyo poti Khristu waukitsidwa, mtumwi Petulo analembera Akhristu amene anali m’madera olamuliridwa ndi Roma kuti: “Okondedwa, popeza ndinu alendo ndiponso anthu osakhalitsa m’dzikoli, ndikukudandaulirani kuti muzipewa zilakolako za thupi zimene zili pa nkhondo yolimbana ndi moyo. Khalani ndi khalidwe labwino pakati pa anthu a m’dzikoli.”—1 Pet. 1:1; 2:11, 12.
8. Kodi wolemba mbiri wina anafotokoza chiyani zokhudza Akhristu oyambirira zosonyeza kuti iwo sanali mbali ya dzikoli?
8 Akhristu oyambirira ankakhala monga “alendo ndi osakhalitsa” m’madera onse olamuliridwa ndi Roma. Katswiri wolemba mbiri yakale, dzina lake Kenneth Scott Latourette analemba kuti Akhristu ankazunzidwa nthawi ndi nthawi. Ananena kuti ankanamiziridwa kuti sankakhulupirira Mulungu chifukwa choti sankapanga nawo zikondwerero zachipembedzo. Iwo ankatchedwa “anthu odana ndi anzawo.” Zinali choncho chifukwa sankachita zinthu zomwe anthu owazungulira ankachita monga zikondwerero zokhudza kulambira konyenga komanso chiwerewere.
Tisagwiritse Ntchito Dzikoli Mokwanira
9. Kodi Akhristufe timasonyeza bwanji kuti si ife “anthu odana ndi anzawo”?
9 Nanga kodi masiku ano zinthu zili bwanji? Akhristu amaona dziko loipali mmene Akhristu oyambirira ankalionera. (Agal. 1:4) Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri satha kutimvetsa ndipo ena amafika mpaka podana nafe. Koma ifeyo si “anthu odana ndi anzawo.” Chifukwa chokonda anthu timapita ku nyumba ndi nyumba kukawauza “uthenga wabwino wa Ufumu” wa Mulungu. (Mat. 22:39; 24:14) Timatero chifukwa timakhulupirira kuti Ufumu wa Yehova, womwe ndi boma lolamulidwa ndi Khristu, udzathetsa maufumu onse n’kubweretsa chilungamo padziko lonse.—Dan. 2:44; 2 Pet. 3:13.
10, 11. (a) Kodi tingatani kuti tisamagwiritse ntchito dzikoli mokwanira? (b) Kodi ndi njira zina ziti zomwe Akhristu amene ali maso angasonyezere kuti sakugwiritsa ntchito dzikoli mokwanira?
10 Popeza tikudziwa kuti dzikoli latsala pang’ono kuwonongedwa, ife monga atumiki a Yehova timadziwa kuti inoyi si nthawi yomanga maziko m’dziko lomwe likupitali. Timatsatira mawu a Paulo akuti: “Abale dziwani izi: Nthawi yotsalayi yafupika. Choncho amene . . . amagula zinthu azikhala ngati opanda kanthu. Amene amagwiritsira ntchito dzikoli azikhala ngati amene sakuligwiritsira ntchito mokwanira, pakuti zochitika za padzikoli zikusintha.” (1 Akor. 7:29-31) Kodi Akhristu masiku ano amagwiritsa ntchito bwanji dziko? Iwo amagwiritsa ntchito luso lamakono pothandiza anthu a zinenero zosiyanasiyana kudziwa Baibulo. Amagwiritsa ntchito dzikoli pang’ono kuti apeze zofunika pa moyo wa tsiku ndi tsiku. Komanso amagula ndiponso kugwiritsa ntchito zinthu zimene dzikoli limapanga. Komabe iwo amapewa kugwiritsa ntchito dzikoli mokwanira. Amapewa kuika zinthu zakuthupi pamalo oyamba.—Werengani 1 Timoteyo 6:9, 10.
11 Pa nkhani ya maphunziro apamwamba, Akhristu amene ali maso sagwiritsa ntchito dzikoli mokwanira. Anthu ambiri m’dzikoli amaganiza kuti akachita maphunziro apamwamba azidzalemekezedwa ndipo zinthu zizidzawayendera bwino pa moyo wawo. Koma Akhristufe timakhala ndi zolinga zosiyana ndi zimene anthu ena amakhala nazo ndipo tili ngati anthu osakhalitsa m’dzikoli. Timapewa ‘kufunafuna zinthu zazikulu.’ (Aroma 12:16; Yer. 45:5) Popeza ndife otsatira a Yesu, timatsatira chenjezo lake lakuti: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse, chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Choncho Akhristu achinyamata akulimbikitsidwa kukhala ndi zolinga zauzimu. Iwo ayenera kukhala ndi maphunziro okhawo amene angawathandize kupeza zinthu zofunika pa moyo wa tsiku ndi tsiku, koma maganizo awo onse ali potumikira Yehova ndi ‘mtima wawo wonse, moyo wawo wonse, mphamvu zawo zonse, ndi maganizo awo onse.’ (Luka 10:27) Kuchita zimenezi kungawathandize kukhala ‘olemera kwa Mulungu.’—Luka 12:21, werengani Mateyu 6:19-21.
Musalemedwe ndi Nkhawa za Moyo
12, 13. Kodi kutsatira mawu a Yesu a pa Mateyu 6:31-33 kumatisiyanitsa bwanji ndi anthu a m’dzikoli?
12 Atumiki a Yehova amasiyana ndi anthu a m’dzikoli pa nkhani ya kukonda zinthu zakuthupi. Yesu anauza otsatira ake kuti: “Musamade nkhawa n’kumanena kuti, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapena, ‘Tivala chiyani?’ Pakuti anthu a mitundu ina akufunafuna mwakhama zinthu zonsezi. Koma Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi. Chotero pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mat. 6:31-33) Akhristu anzathu ambiri aona umboni woti Atate wathu wakumwamba amapereka zofuna zawo.
13 ‘Kukhala wodzipereka kwa Mulungu komanso kukhala wokhutira ndi zimene tili nazo, ndi njiradi yopezera phindu lalikulu.’ (1 Tim. 6:6) Maganizo amenewa ndi osiyana kwambiri ndi amene anthu a m’dzikoli amayendera. Mwachitsanzo, achinyamata ambiri akangokwatira amafuna atangokhala ndi chilichonse nthawi yomweyo. Amafuna kukhala ndi zinthu ngati nyumba yodzaza bwino ndi katundu wamakono komanso galimoto yabwino. Koma Akhristu amene akukhala monga anthu osakhalitsa m’dzikoli salimbana ndi kugula zinthu zimene sangakwanitse. N’zosangalatsa kuti Akhristu ambiri amadzimana zinthu zambiri n’cholinga choti agwiritsire ntchito nthawi ndi mphamvu zawo kutumikira Yehova polalikira uthenga wa Ufumu mwachangu. Ena amatumikira monga apainiya, ena pa Beteli, mu utumiki woyendayenda komanso monga amishonale. Tonsefe timayamikira kwambiri kudzipereka kumene olambira anzathu amachita potumikira Yehova.
14. Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizo la Yesu la wofesa mbewu?
14 M’fanizo la munthu wofesa mbewu, Yesu ananena kuti, “nkhawa za moyo wa m’nthawi ino ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma” zimalepheretsa mawu a Mulungu kukula m’mitima yathu ndipo timakhala osabala zipatso. (Mat. 13:22) Kukhala okhutira monga anthu osakhalitsa m’dziko loipali kungatithandize kupewa msampha umenewu. Choncho timakhala ndi diso “lolunjika pa chinthu chimodzi” chomwe ndi Ufumu wa Mulungu ndipo zinthu zokhudza ufumuwo timaziika patsogolo pa moyo wathu.—Mat. 6:22.
‘Dzikoli Likupita’
15. Kodi mtumwi Yohane ananena chiyani za dzikoli?
15 Chifukwa chachikulu chimene Akhristufe timakhalira monga “alendo ndiponso osakhalitsa” m’dzikoli n’chakuti kwatsala nthawi yochepa. (1 Pet. 2:11; 2 Pet. 3:7) Kudziwa zimenezi kumatithandiza posankha zochita pa moyo wathu, ndipo kumakhudza zinthu zimene timafuna. Mtumwi Yohane analangiza Akhristu anzake kuti asamakonde dziko kapena zinthu za m’dziko chifukwa chakuti “dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake, koma wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.”—1 Yoh. 2:15-17.
16. Kodi tingasonyeze bwanji kuti Yehova watipatula kukhala anthu ake?
16 Aisiraeli anauzidwa kuti ngati amvera Yehova, adzakhala ‘chuma chake chapadera pakati pa anthu ena onse.’ (Eks. 19:5) Aisiraeli akakhala okhulupirika, ankasiyana kwambiri ndi mitundu ina pa nkhani ya kulambira ndiponso zochita pa moyo wawo. N’chimodzimodzinso masiku ano. Yehova wasankha anthu ena kuti akhale akeake ndipo ndi osiyana ndi anthu a m’dziko la Satanali. Baibulo limanena kuti: ‘Tiyenera kukana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko, koma tiyenera kukhala amaganizo abwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu m’nthawi ino. Tizichita zimenezi pamene tikuyembekeza kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chosangalatsa ndi kuonetsedwa kwaulemerero kwa Mulungu wamkuluyo ndiponso kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu. Iyeyo anadzipereka m’malo mwa ife kuti atilanditse ku moyo wochita zinthu zosamvera malamulo za mtundu uliwonse ndiponso kuti atiyeretse, kuti tikhale anthu akeake, odzipereka pa ntchito zabwino.’ (Tito 2:11-14) “Anthu akeake” amenewa ndi Akhristu odzozedwa ndiponso anthu mamiliyoni ambiri a “nkhosa zina” amene amathandiza odzozedwawo.—Yoh. 10:16.
17. N’chifukwa chiyani odzozedwa limodzi ndi a nkhosa zina sadzanong’oneza bondo chifukwa chokhala ndi moyo monga osakhalitsa m’dziko loipali?
17 “Chiyembekezo chosangalatsa” chomwe odzozedwa ali nacho n’chokalamulira limodzi ndi Khristu kumwamba. (Chiv. 5:10) Chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi chikadzakwaniritsidwa kwa a nkhosa zina, iwo sadzafunikiranso kukhala monga anthu osakhalitsa m’dziko loipali. M’malomwake iwo adzakhala ndi nyumba zabwino ndi zakudya ndi zakumwa zambiri. (Sal. 37:10, 11; Yes. 25:6; 65:21, 22) Mofanana ndi Aisiraeli, iwo sadzaiwala kuti zinthu zonsezo zimachokera kwa Yehova, yemwe ndi “Mulungu wa dziko lonse lapansi.” (Yes. 54:5) Magulu onse awiri, odzozedwa ndi a nkhosa zina, sadzanong’oneza bondo kuti anakhala ndi moyo monga osakhalitsa m’dziko loipali.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi anthu okhulupirika akale anasonyeza bwanji kuti ankakhala monga anthu osakhalitsa m’dziko?
• Kodi Akhristu oyambirira ankasiyana bwanji ndi anthu a m’dzikoli?
• Kodi Akhristu amapewa bwanji kugwiritsa ntchito dzikoli mokwanira?
• N’chifukwa chiyani tinganene kuti sitidzanong’oneza bondo chifukwa chokhala ndi moyo monga osakhalitsa m’dzikoli?
[Chithunzi patsamba 18]
Akhristu oyambirira ankapewa zosangalatsa zachiwawa ndi zoipa