‘Chitani Zonse ku Ulemerero wa Mulungu’
Mfundo Zazikulu Zochokera m’Akorinto Woyamba
ULEMERERO wa Yehova Mulungu ngofunikira kuderedwa nkhaŵa ndi onse amene amamulambira ‘mumzimu ndi m’chowonadi.’ (Yohane 4:23, 24) Chotero, mtumwi Paulo anauza Akristu anzake mu Korinto wakale kuti: ‘Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.’ (1 Akorinto 10:31) Kuti ichi chichitidwe tifunikira kuvomereza njira ya Yehova ya kuthetsera mavuto athu m’dziko lokonda chuma chakuthupi, lachisembwere lozamitsidwa m’chipembedzo chonyengali.
Akristu a ku Korinto anafunikira thandizo laumulungu lothetsera mavuto, popeza kuti ankakhala mumzinda wokhupuka, wachisembwere wodzala ndi chipembedzo chonyenga. Pokhala pakamtunda kokhala pakati pa dera la Grisi ndi Peloponnisos, Korinto anali likulu la dera la Roma la Akaya ndipo munali chiŵerengero cha anthu choyerekezedwa kukhala 400,000. Paulo anakhazikitsa mpingo kumeneko pafupifupi mu 50 C.E.—Machitidwe 18:1-11.
Akorinto analembera Paulo akumamufunsa ponena za ukwati ndi kudya nyama zoperekedwa mafano. (7:1) Iye anaipidwa chifukwa chakuti malekano ndi nkhani ya chisembwere chachikulu zinkachitika pakati pawo. Iwo anafunikira uphungu wonena za njira yolongosoka yokumbukirira Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Munali ngakhale chiwopsezo cha mpatuko, ndipo mpingo unafunikira uphungu wonena za chikondi. Kaamba ka zifukwazi, Paulo analemba kalata yake yoyamba youziridwa kwa Akorinto ali mu Efeso pafupifupi 55 C.E. Koma nafenso tingapindule nayo.
Umodzi ndi Chiyero cha Makhalidwe Nzofunika
Ngati ‘tichita zonse ku ulemerero wa Mulungu,’ sitidzatsatira munthu aliyense wofuna kupangitsa malekano mumpingo—ili linali limodzi la mavuto oyang’anizidwa ndi Akorinto. (1:1–4:21) Paulo anawachonderera kuti ‘anene chimodzimodzi ndi kukhala omangika mu mtima womwewo ndi m’chiweruzo chomwecho.’ Umodzi udzakhalapo ngati titsatira uphunguwu ndi kupititsa patsogolo mikhalidwe yauzimu. Mmalo modzitukumula m’maumunthu ochimwa aliwonse, tiyenera kukumbukira kuti chinkana kuti ‘timaoka ndi kuthirira, Mulungu ndiye amazikulitsa’ mwauzimu. Odzitukumula mu Korinto analibe chinthu chimene anakhala nacho popanda kuchilandira; chotero tisadzilingalire konse kukhala abwinopo kuposa akhulupiriri anzathu. Mzimu wodzichepetsa woterowo udzatithandiza kupititsa patsogolo umodzi.
Ngati umodzi uti ufalikire, akulu oikidwa ayenera kugwira ntchito yosunga mpingo kukhala woyera mwauzimu. (5:1–6:20) Popeza kuti ‘chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda wonse,’ adama osalapa, aumbombo, olambira mafano, andewu, oledzera, kapena olanda afunikira kuchotsedwa. Makhalidwe odetsedwa, amene amadetsa kachisi wa Mulungu, safunikira kulekereredwa pakati pa anthu a Yehova. Mmalo mwake, ayenera kuchita zinthu zolemekeza Mulungu.
Khalani Olingalira Ena
Kuti ‘tichite zonse ku ulemerero wa Mulungu,’ tiyenera kugwiritsira ntchito uphungu wa Paulo wonena za ukwati ndi umbeta. (7:1-40) Awo ogwirizanitsidwa muukwati afunikira kupereka mangawa aukwati molingalirana. Mkristu wokwatira sayenera kulekana ndi mnzake wa muukwati wosakhulupirira, popeza kuti kukhala pamodzi kungathandize ujayo kupeza chipulumutso. Pamene kuli kwakuti ukwati umabweretsa nkhaŵa zowonjezereka, umbeta ungapindulitse munthu wokhumba kuthandiza ena mwauzimu mwa kutumikira Ambuye popanda zocheutsa.
Kusonyeza kulingalira ubwino wauzimu wa ena ndithayo la Akristu onse, kaya akhale mbeta kapena okwatira. (8:1–10:33) Chotero, Akorinto anapatsidwa uphungu kusakhumudwitsa ena mwa kudya zakudya zoperekedwa ku mafano. Kuti apeŵe kutsekereza aliyense kuvomereza mbiri yabwino, Paulo sanagwiritsire ufulu wake kulandira thandizo la chuma chakuthupi. Iye ‘anapumphunthanso thupi lake kotero kuti pambuyo pa kulalikira kwa ena, asakakhale wosavomerezedwa.’ Kukumbukira zokumana nazo za m’chipululu za Israyeli wochimwa kudzatithandiza kupeŵa kulambira mafano ndi kuchita zolakwa. Ndiponso, ‘kuchita zonse ku ulemerero wa Mulungu’ kudzatithandiza kupeŵa kukhumudwitsa aliyense.
Sonyezani Ulemu ndi Kusunga Chilongosoko
‘Kuchita zonse ku ulemerero wa Mulungu’ kumafuna kuti tisonyeze ulemu wabwino. (11:1-34) Mkazi Wachikristu wa m’zaka za zana loyamba anasonyezera ulemu mutu mwa kuvala chophimba kumutu popemphera kapena ponenera mumpingo. Ulemu wofananawo kwa mutu umasonyezedwa ndi akazi opembedza lerolino. Kuwonjezera apa, kuti tipewe kukhala ngati Akorinto amene anafunikira chiwongolero, tonsefe tifunikira kusonyeza ulemu kaamba ka Chakudya Chamadzulo cha Ambuye.
Kuti ‘tichite zonse ku ulemerero wa Mulungu,’ tifunikira kuchititsa misonkhano m’njira yolongosoka. (12:1–14:40) Pamene Akristu oyambirira anakumana, mphatso za mzimu zoterozo zonga mwa kulankhula m’malirime zidagwiritsiridwa ntchito mwaulemu ndi kuyamikira magwero ndi chifuno chake. Chinkana kuti tiribe mphatso zimenezi tsopano, ife timabweretsa ulemerero kwa Mulungu mwa kusonyeza chikondi, chimene chimaposa zonsezo. Timalemekezanso Yehova chifukwa chakuti misonkhano yathu njolinganizidwa bwino, ndipo timagwiritsira ntchito mwaulemu uphungu wa Paulo uwu: ‘Koma zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.’
‘Kuchita zonse ku ulemerero wa Mulungu’ kumatifulumiza kulemekeza chiphunzitso cha Baibulo ndi kuima nji mwauzimu. (15:1–16:24) Mwinamwake mosonkhezeredwa ndi anthanthi Achigiriki, ena mumpingo wa Korinto anati: ‘Kulibe kuuka kwa akufa.’ (Yerekezerani ndi Machitidwe 17:18, 32.) Iwo angakhale adali ndi malingaliro ampatuko akuti sikudzakhala chiukiriro cha mtsogolo koma kuti Akristu amoyo adakumana nako kophiphiritsira, kwauzimu. (2 Timoteo 2:16-18) Paulo anachilikiza chiyembekezo chowona mwa kutchula chiukiriro cha Yesu ndikusonyezanso kuti Akristu odzozedwa adafunikira kufa kotero kuti aukitsidwire ku moyo wosafa wakumwamba. M’njira inanso, mawu ake amatithandiza kupeŵa mpatuko ndi ‘kuchilimika m’chikhulupiriro.’
Nthaŵi Zonse Chitani Zonse ku Ulemerero wa Mulungu
Uphungu wa Paulo m’Akorinto Woyamba ngwopindulitsanso lerolino monga mmene unaliri m’zaka za zana loyamba C.E. Iwo umasonkhezerea Mboni zamakono za Yehova kutumikira Mulungu mogwirizana monga anthu oyera. Mawu a mtumwiwo ayenera kutisonkhezera kulingalira ena ndi kusonyeza ulemu wabwino. Zimene Paulo ananena zingatilimbitsenso kutsutsa mpatuko ndi kuchilimika kaamba ka chikhulupiriro chowona.
Motsimikizirika, n’chikhumbo chapamtima wa mtumiki wokhulupirika aliyense wa Yehova kumudalitsa, kulengeza Ufumu wake, ndi kulemekeza dzina lake loyera. (Salmo 145:1, 2, 10-13) Kwenikweni, kalata yoyamba ya Paulo kwa Akorinto imatithandiza ‘kuchita zonse ku ulemerero wa Mulungu.’
[Bokosi/Chithunzi pamasamba 24, 25]
WOTSIMIKIZIRA KUFA: Kuposa kamodzi m’kalata yake kwa Akorinto, Paulo anatchula imfa yofera m’bwalo. Mwachitsanzo, iye analemba motere: ‘Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife chowonetsedwa ku dziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.’ (1 Akorinto 4:9) Paulo angakhale anali kuganizira za ziwonetsero za bestiarii (amuna amene anamenyana ndi zilombo) ndi zigawenga (amuna amene anamenyana ndi amuna anzawo). Ena anamenyanirana malipiro, koma achifwamba anakakamizidwa kumenyana. Poyamba analoledwa kugwiritsira ntchito zida, pambuyo pake akaidiwa anatulutsidwa opanda kanthu, osadzitetezera, ndipo otsimikizira kufa.
Pokhala ndi “angelo” ndi “anthu” (osati kokha “dziko” la anthu) monga openyerera, atumwiwo anafanana ndi anthu omwe anali pafupi kufa m’chiwonetsero chowopsya chomaliziracho. Paulo anati ‘analimbana ndi zilombo ku Efeso,’ koma ena anakaikira kuti nzika ya Roma ikadaunikiridwa ku ichi ndikuti iye anatanthauza otsutsa ofanana ndi zilombo. (1 Akorinto 15:32) Komabe, ndemanga ya Paulo yakuti Mulungu anampulumutsa ‘ku chinthu chachikulu chonga imfa’ m’chigawo cha Asiya (kumene Efeso inali) imamvana bwino ndi chokumana nachocho kukhala zilombo zenizeni m’bwalo kuposa ndi anthu otsutsa.—2 Akorinto 1:8-10; 11:23; Machitidwe 19:23-41.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 25]
KUMBUKIRANI MPHOTHO: Paulo anagwiritsira ntchito mbali za maseŵera Achigiriki akale pofotokoza mwafanizo mfundo zofunika. (1 Akorinto 9:24-27) M’mipikisano yoteroyo monga ya Maseŵera a Isthmus ochitidwa pambuyo pa zaka ziŵiri zirizonse pafupi ndi Korinto, programu inaphatikizapo kuthamanga, nkhonya, ndi zochitika zina. Pokonzekera mipikisanoyi, othamanga ndi ankhonya anafunikira kudzimana, kudya zakudya zopanda mafuta, ndi kusamwa vinyo kwa miyezi khumi. Komabe, mmalo mwa mphatso ya chisoti chokometseredwa chosakhalitsa chofupidwa kwa opambana m’Maseŵera a Isthmus, Mkristu wodzozedwa amakalamira chisoti chaufumu cha moyo wosatha. Kuti apambane mphotho imeneyo, iye ayenera kusumika maso ake pa iyo ndi kudziletsa. Lamulo limodzimodzili limagwira ntchito kwa Mboni za Yehova zimene ziri ndi chiyembekezo cha moyo wosatha wa padziko lapansi.