Kuchita Mogwirizana ndi Kudzipatulira Kwathu “Tsiku ndi Tsiku”
“Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule [mtengo wake wozunzirapo, NW] tsiku ndi tsiku, nanditsate ine.”—LUKA 9:23.
1. Kodi ndi njira ina iti imene tingapimire chipambano chathu monga Akristu?
“KODI tinalidi anthu odzipatulira?” Yankho la funso limeneli, malinga ndi kunena kwa John F. Kennedy, Pulezidenti wa 35 wa United States, ndilo muyezo wopimira chipambano cha amene ali ndi mathayo m’boma. Funsolo lingakhale ndi tanthauzo lalikulu kwambiri popima chipambano chathu monga atumiki Achikristu.
2. Kodi dikishonale imamasulira motani liwulo “kudzipatulira”?
2 Komabe, kodi kudzipatulira nchiyani? Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary imakumasulira kukhala “mchitidwe kapena dzoma la kupatulira kwa mulungu kapena ku ntchito yopatulika,” “kupereka kapena kuika padera kaamba ka chifuno china,” “kudzipereka kodzimana.” John F. Kennedy mwachionekere anali kugwiritsira ntchito liwulo kutanthauza “kudzipereka kodzimana.” Kwa Mkristu, kudzipatulira kumatanthauza zambiri.
3. Kodi kudzipatulira Kwachikristu nchiyani?
3 Yesu Kristu anauza ophunzira ake kuti: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge [mtengo wake wozunzirapo, NW], nanditsate ine.” (Mateyu 16:24) Kupatulidwa kaamba ka ntchito yaumulungu sikumangophatikizapo kuchita mtundu wina wa kulambira pa Sande kapena pochezera malo ena olambirira. Kumaphatikizapo moyo wonse wa munthu. Kukhala Mkristu kumatanthauza kudzikana kapena kudzilandula potumikira Yehova, Mulungu amene Yesu Kristu anatumikira. Ndiponso, Mkristu amatenga “mtengo wake wozunzirapo” mwa kupirira mavuto alionse amene angadze chifukwa cha kukhala kwake wotsatira Kristu.
Chitsanzo Changwiro
4. Kodi ubatizo wa Yesu unaimira chiyani?
4 Pamene anali pa dziko lapansi, Yesu anasonyeza zimene kudzipatulira kwa munthu mwini kwa Yehova kumaphatikizapo. Malingaliro ake anali akuti: “Nsembe ndi chopereka simunazifuna, koma thupi munandikonzera ine.” Ndiyeno anawonjezera kuti: “Taonani, ndafika, (Pamutu pake pa buku palembedwa za ine) kudzachita chifuniro chanu, Mulungu.” (Ahebri 10:5-7) Monga chiŵalo cha mtundu wodzipatulira, iye anapatulidwira kwa Yehova pa kubadwa. Komabe, kuchiyambi cha utumiki wake wa pa dziko lapansi, iye anadzipereka kuti abatizidwe monga chizindikiro cha kudzionetsera kwake kuti achite chifuniro cha Yehova, chimene kwa iye chinaphatikizapo kupereka moyo wake nsembe ya dipo. Motero anaikira Akristu chitsanzo cha kuchita chilichonse chimene Yehova afuna.
5. Kodi Yesu anasonyeza motani lingaliro loyenera la zinthu zakuthupi?
5 Pambuyo pa ubatizo wake Yesu anatsatira njira ya moyo imene potsirizira pake inafika ku imfa yansembe. Iye sanafunefune chuma kapena kukhala ndi moyo wapamwamba. M’malo mwake, moyo wake unali pa utumiki wake. Iye analangiza ophunzira ake kuti “muthange mwafuna ufumu ndi chilungamo chake,” ndipo iye mwiniyo anachita mogwirizana ndi mawu ameneŵa. (Mateyu 6:33) Eya, panthaŵi ina ananenadi kuti: “Ankhandwe ali nazo nkhwimba zawo, ndi mbalame za m’mlengalenga zisa zawo, koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu wake.” (Mateyu 8:20) Akanasintha ziphunzitso zake kuti alande ndalama kwa otsatira ake. Pokhala wopala matabwa, akanasiya utumiki wake kwakanthaŵi ndi kukapanga chinthu chabwino kwambiri chamatabwa chogulitsa kotero kuti apeze siliva wowonjezereka. Koma sanagwiritsire ntchito maluso ake kupezera chuma chakuthupi. Monga atumiki odzipatulira a Mulungu, kodi tikutsanzira Yesu mwa kukhala ndi lingaliro loyenera la zinthu zakuthupi?—Mateyu 6:24-34.
6. Kodi ndimotani mmene tingatsanzirire Yesu m’kukhala atumiki odzimana ndi odzipatulira a Mulungu?
6 Poika utumiki wake kwa Mulungu pamalo oyamba, Yesu sanafune zimene iye mwini anakonda. Moyo wake m’zaka zitatu ndi theka za utumiki wake wapoyera unali wa kudzimana. Pachochitika china atagwira ntchito kwambiri, popanda ngakhale kupatula nthaŵi ya chakudya, Yesu anali wofunitsitsa kuphunzitsa anthu amene anali “okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36; Marko 6:31-34) Ngakhale kuti “analema ndi ulendo,” iye anayamba kulankhula ndi mkazi Msamariya amene anadza ku chitsime cha Yakobo ku Sukari. (Yohane 4:6, 7, 13-15) Nthaŵi zonse analingalira za ubwino wa ena kukhala wofunika kuposa wake. (Yohane 11:5-15) Tingatsanzire Yesu mwa kudzimana kwambiri zimene timakonda kuti titumikire Mulungu ndi ena. (Yohane 6:38) Mwa kulingalira za mmene tingakondweretseredi Mulungu kuposa kungochita zimene timafunikira, tidzakhala tikuchita mogwirizana ndi kudzipatulira kwathu.
7. Kodi tingamtsanzire motani Yesu m’kupereka ulemu kwa Yehova nthaŵi zonse?
7 Mwa kuthandiza anthu, Yesu sanali kuyesa kukopera anthu kwa iye mwini. Anali wodzipatulira kwa Mulungu kuchita chifuniro Chake. Choncho nthaŵi zonse anatsimikizira kuti Yehova, Atate wake, analandira ulemerero wonse kaamba ka zilizonse zimene zinachitidwa. Pamene wolamulira wina anamutcha “Mphunzitsi wabwino,” akumagwiritsira ntchito liwulo “wabwino” monga dzina laulemu, Yesu anamuwongolera mwa kunena kuti: “Palibe wabwino, koma mmodzi, ndiye Mulungu.” (Luka 18:18, 19; Yohane 5:19, 30) Kodi ife, monga Yesu, timafulumira kulunjikitsa ulemerero kwa Yehova ndipo osati kwa ife eni?
8. (a) Monga munthu wodzipatulira, kodi Yesu anadzilekanitsa motani ndi dziko? (b) Kodi tiyenera kumtsanzira motani?
8 M’moyo wake wonse wodzipatulira pa dziko lapansi, Yesu anasonyeza kuti anadziika padera kaamba ka utumiki wa Mulungu. Anadzisunga ali woyera kotero kuti anakhoza kudzipereka monga “mwana wa nkhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga” kukhala nsembe ya dipo. (1 Petro 1:19; Ahebri 7:26) Anasunga njira zonse za Chilamulo cha Mose, motero akumakwaniritsa Chilamulocho. (Mateyu 5:17; 2 Akorinto 1:20) Anachita mogwirizana ndi ziphunzitso zake za makhalidwe abwino. (Mateyu 5:27, 28) Panalibe aliyense amene moyenerera anakhoza kumuimba mlandu wa kukhala ndi zolinga zoipa. Ndithudi, ‘anadana nacho choipa.’ (Ahebri 1:9) Monga akapolo a Mulungu, tiyeni titsanzire Yesu mwa kusunga miyoyo yathu ndi zolinga zathu zomwe zili zoyera pamaso pa Yehova.
Zitsanzo Zochenjeza
9. Kodi Paulo anatchula chitsanzo chiti chochenjeza, ndipo nchifukwa ninji tiyenera kupenda chitsanzo chimenechi?
9 Mosiyana ndi chitsanzo cha Yesu, tili ndi chitsanzo chochenjeza cha Aisrayeli. Ngakhale pambuyo polengeza kuti akachita zonse zimene Yehova anawauza, analephera kuchita chifuniro chake. (Danieli 9:11) Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu kutengapo phunziro pa zimene zinagwera Aisrayeli. Tiyeni tipende zochitika zina zimene Paulo anatchula m’kalata yake yoyamba kwa Akorinto ndi kuona mbuna zimene ziyenera kupeŵedwa ndi atumiki odzipatulira a Mulungu m’nthaŵi yathu.—1 Akorinto 10:1-6, 11.
10. (a) Kodi Aisrayeli ‘analakalaka motani zoipa’? (b) Kodi nchifukwa ninji Aisrayeli anali ndi mlandu kwambiri panthaŵi yachiŵiri imene anadandaula za chakudya, ndipo tingaphunzirenji pa chitsanzo chochenjeza chimenechi?
10 Choyamba, Paulo anatichenjeza ‘kusalakalaka zoipa.’ (1 Akorinto 10:6) Zimenezo zingakukumbutseni chochitika china pamene Aisrayeli anadandaula chifukwa cha kudya mana okha. Yehova anawatumizira zinziri. Zofananazo zinali zitachitika m’chipululu cha Sini, patangotsala pafupifupi chaka chimodzi kuti Aisrayeli alengeze kudzipatulira kwawo kwa Yehova. (Eksodo 16:1-3, 12, 13) Koma mkhalidwewo sunali wofanana kwenikweni. Nthaŵi yoyamba imene Yehova anapereka zinziri, sanaimbe mlandu Aisrayeli chifukwa cha kudandaula kwawo. Komabe, panthaŵiyi zinthu zinali zosiyana. “Nyamayi ikali pakati pa mano, asanaitafune, Mulungu anapsa mtima pa anthuwa, ndipo Yehova anawakantha anthu ndi kukantha kwakukulu ndithu.” (Numeri 11:4-6, 31-34) Kodi nchiyani chimene chinasintha? Monga mtundu wodzipatulira, iwo tsopano anaimbidwa mlandu. Kusoŵa kwawo chiyamikiro kaamba ka zogaŵira za Yehova kunawachititsa kudandaulira Yehova, ngakhale kuti anali atalonjeza kuchita zonse zimene Yehova adalankhula! Kudandaula ndi gome la Yehova lerolino kuli kofanana ndi zimenezo. Ena amalephera kuyamikira zogaŵira zauzimu zimene Yehova amapereka mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Komabe, kumbukirani kuti kudzipatulira kwathu kumafuna kuti ife moyamikira tisunge m’maganizo zimene Yehova watichitira ndi kulandira chakudya chauzimu chimene Yehova akupereka.
11. (a) Kodi ndimotani mmene Aisrayeli anaipitsira kulambira kwawo Yehova mwa kupembedza mafano? (b) Kodi tingayambukiridwe motani ndi mtundu wina wa kupembedza mafano?
11 Ndiyeno, Paulo anachenjeza kuti: “Kapena musakhale opembedza mafano, monga ena a iwo.” (1 Akorinto 10:7) Mwachionekere, mtumwiyo pano anali kunena za kulambira mwana wa ng’ombe kumene kunachitika Aisrayeli atangochita pangano ndi Yehova pa Phiri la Sinai. Mwina munganene kuti, ‘Ine monga mtumiki wodzipatulira wa Yehova, sindingadziphatike ku kupembedza mafano.’ Komabe, taonani kuti malinga ndi kuganiza kwa Aisrayeli, iwo sanaleke kulambira Yehova; komatu anabweretsa machitachita a kulambira mwana wa ng’ombe—chinthu chonyansa kwa Mulungu. Kodi kalambiridwe kameneka kanaphatikizapo chiyani? Anthu anapereka nsembe pamaso pa mwana wa ng’ombe, ndiyeno “anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kuseŵera.” (Eksodo 32:4-6) Lerolino, ena anganene kuti amalambira Yehova. Koma miyoyo yawo ingakhale ili, osati pa kulambira Yehova, koma pa kusangalala ndi zinthu za dzikoli, ndipo amayesa kupezera malo utumiki wawo kwa Yehova pa zinthu zimenezi. Zoona, zimenezi sizonyanya kwambiri monga kugwadira mwana wa ng’ombe wagolidi, koma mzimu wake sunasiyane kwenikweni. Kupanga chikhumbo cha munthuwe kukhala mulungu ndi kosemphana kwambiri ndi kuchita mogwirizana ndi kudzipatulira kwa munthuwe kwa Yehova.—Afilipi 3:19.
12. Kodi chokumana nacho cha Aisrayeli ndi Baala wa ku Peori chimatiphunzitsanji ponena za kudzikana?
12 Mtundu wina wa kusanguluka unaphatikizidwamonso m’chitsanzo chochenjeza chotsatira chimene Paulo anatchula. “Kapena tisachite dama monga ena a iwo anachita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi aŵiri ndi zitatu.” (1 Akorinto 10:8) Aisrayeli, pokopeka ndi zokondweretsa zoipa zoperekedwa ndi ana aakazi a Moabu, analoŵetsedwa m’kulambira Baala wa ku Peori m’Sitimu. (Numeri 25:1-3, 9) Kudzikana kwathu kuti tichite chifuniro cha Yehova kumaphatikizapo kulandira miyezo yake ya makhalidwe oyera. (Mateyu 5:27-30) M’nyengo ino ya kunyonyotsoka kwa makhalidwe, tikukumbutsidwa za kufunika kwake kwa kupeŵeratu mtundu uliwonse wa khalidwe loipa kuti tikhale oyera, tikumagonjera ulamuliro wa Yehova wa kusankha chabwino ndi choipa.—1 Akorinto 6:9-11.
13. Kodi chitsanzo cha Pinehasi chikutithandiza motani kuzindikira zimene kudzipatulira kwa Yehova kumaphatikizapo?
13 Pamene kuli kwakuti ambiri anagwidwa mumsampha wa dama m’Sitimu, ena anachita mogwirizana ndi kudzipatulira kwa mtunduwo kwa Yehova. Mwa iwo, Pinehasi anali ndi changu chapadera. Atangoona kalonga Wachiisrayeli akuloŵetsa mkazi Wachimidyani m’hema wake, Pinehasi nthaŵi yomweyo anatenga nthungo m’dzanja lake nawapyoza. Yehova anati kwa Mose: “Pinehasi . . . wabweza kuzaza kwanga pa ana a Israyeli, popeza anachita nsanje ndi nsanje yanga pakati pawo, kotero kuti sindinawatha ana a Israyeli [m’kuumirira kwanga pa kudzipereka kotheratu, NW].” (Numeri 25:11) Kusalekerera konse kupikisana ndi Yehova—ndi zimene kudzipatulira kumatanthauza. Sitiyenera kulola kalikonse kutenga malo amene kudzipatulira kwa Yehova kuyenera kukhala nawo m’mitima mwathu. Changu chathu kwa Yehova chimatisonkhezeranso kusunga mpingo uli woyera mwa kudziŵitsa akulu za zoipa zazikulu, osazilekerera ayi.
14. (a) Kodi ndimotani mmene Aisrayeli anayesera Yehova? (b) Kodi ndimotani mmene kudzipatulira kotheratu kwa Yehova kumatithandizira ‘kusalema’?
14 Paulo anatchulanso chitsanzo china chochenjeza kuti: “Kapena tisayese Ambuye, monga ena a iwo anayesa, nawonongeka ndi njoka zija.” (1 Akorinto 10:9) Panopa Paulo anali kulankhula za nthaŵi pamene Aisrayeli anadandaulira Mulungu ndi Mose pamene “mtima wa anthu unada chifukwa cha njirayo.” (Numeri 21:4) Kodi inu nthaŵi zonse mumaphophonya mofananamo? Pamene munadzipatulira kwa Yehova, kodi munaganiza kuti Armagedo inali pafupi kwambiri? Kodi kuleza mtima kwa Yehova kwatalika kwambiri kuposa mmene munayembekezera? Kumbukirani kuti kudzipatulira kwathu kwa Yehova si kwanyengo yakutiyakuti yokha kapena kungofikira pa Armagedo. Kudzipatulira kwathu kumapitiriza kosatha. Chifukwa chake, “tisaleme pakuchita zabwino; pakuti panyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.”—Agalatiya 6:9.
15. (a) Kodi Aisrayeli anang’ung’udzira yani? (b) Kodi kudzipatulira kwathu kwa Yehova kumatisonkhezera motani kulemekeza ulamuliro wateokrase?
15 Potsirizira pake, Paulo anachenjeza za kukhala ‘odandaula’ ponena za atumiki oikidwa a Yehova. (1 Akorinto 10:10) Aisrayeli anang’ung’udzira Mose ndi Aroni mwaukali pamene 10 mwa azondi 12 amene anatumizidwa kukazonda dziko la Kanani anabweretsa mauthenga oipa. Ndiponso analankhula za kupeza mtsogoleri wina m’malo mwa Mose ndi za kubwerera ku Igupto. (Numeri 14:1-4) Lerolino, kodi timalandira utsogoleri umene timapatsidwa mwa kugwira ntchito kwa mzimu woyera wa Yehova? Mwa kuona gome la chakudya chauzimu chambiri chimene chikuperekedwa ndi kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, nkosavuta kudziŵa amene Yesu akugwiritsira ntchito kupereka “zakudya panthaŵi yake.” (Mateyu 24:45) Kudzipatulira kwa Yehova ndi mtima wonse kumafuna kuti tisonyeze ulemu kwa atumiki ake oikidwa. Tisakhaletu monga odandaula ena amakono amene atembenukira kwa mtsogoleri watsopano, titero kunena kwake, kuti awabwezere kudziko.
Kodi Chimenechi Ndicho Changu Changa?
16. Kodi ndi mafunso ati amene atumiki odzipatulira a Mulungu angafune kudzifunsa?
16 Aisrayeli sakanagwera m’machimo aakulu amenewo ngati akanakumbukira kuti kudzipatulira kwawo kwa Yehova kunali kotheratu. Mosiyana ndi Aisrayeli opanda chikhulupiriro amenewo, Yesu Kristu anachita mogwirizana ndi kudzipatulira kwake mpaka mapeto. Monga otsatira Kristu, timatsanzira chitsanzo chake cha kudzipereka ndi mtima wonse, tikumakhala ndi moyo ‘wosatsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu.’ (1 Petro 4:2; yerekezerani ndi 2 Akorinto 5:15.) Chifuniro cha Yehova lerolino nchakuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:4) Ndi cholinga chimenecho, tiyenera “kulalikira uthenga uwu wabwino wa Ufumu” mapeto asanadze. (Mateyu 24:14) Kodi ndi kuyesetsa kotani kumene timachita muutumiki umenewu? Mwina tingafune kudzifunsa kuti, ‘Kodi chimenechi ndicho changu changa?’ (2 Timoteo 2:15) Mikhalidwe imasiyana. Yehova amakondwera kutumikiridwa ‘monga momwe munthu ali nacho, si monga chimsoŵa.’ (2 Akorinto 8:12; Luka 21:1-4) Munthu aliyense sayenera kuweruza munthu wina ponena za kuya ndi kuona kwa kudzipatulira kwake. Aliyense payekha ayenera kupenda ukulu wa kudzipereka kwake kwa Yehova. (Agalatiya 6:4) Chikondi chathu pa Yehova chiyenera kutisonkhezera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingamkondweretse motani Yehova?’
17. Kodi kudzipereka ndi chiyamikiro zimagwirizana motani? Perekani chitsanzo.
17 Kudzipereka kwathu kwa Yehova kumakula pamene tikulitsa chiyamikiro chathu kaamba ka iye. Mnyamata wina wa zaka 14 ku Japan anadzipatulira kwa Yehova nasonyeza kudzipatulira kumeneku mwa ubatizo wa m’madzi. Pambuyo pake, anafuna kuchita maphunziro apamwamba kuti akakhale wasayansi. Sanaganizepo za utumiki wanthaŵi yonse, koma monga mtumiki wodzipatulira, sanafune kusiya Yehova ndi gulu lake looneka. Kuti apeze ntchito imene inali chonulirapo chake, anapita ku yunivesite. Kumeneko anaona omaliza maphunziro a yunivesite akukakamizidwa kupatulira moyo wawo wonse ku makampani awo kapena maphunziro awo. Iye anadzifunsa kuti, ‘Kodi ndikuchitanji kuno? Kodi ndingatsatire moyo wawo ndi kudzipatulira ku ntchito yakuthupi? Kodi sindine wodzipatulira kale kwa Yehova?’ Ndi chiyamikiro chatsopano, anakhala mpainiya wokhazikika. Kumvetsetsa kwake kudzipatulira kunazama ndipo kunamsonkhezera kutsimikiza mumtima mwake kupita kulikonse kumene anafunikira. Analoŵa Sukulu Yophunzitsa Utumiki nalandira gawo la kukatumikira monga mmishonale kudziko lachilendo.
18. (a) Kodi kudzipatulira kwathu kwa Yehova kumaphatikizapo chiyani? (b) Kodi ndi mfupo yotani imene tingapeze m’kudzipatulira kwathu kwa Yehova?
18 Kudzipatulira kumaphatikizapo moyo wathu wonse. Tiyenera kudzikana ndi kutsatira chitsanzo chabwino cha Yesu “tsiku ndi tsiku.” (Luka 9:23) Popeza tinadzikana, sitimapempha Yehova tchuthi. Miyoyo yathu imagwirizana ndi malamulo amene Yehova waikira atumiki ake. Ngakhale m’nkhani zimene tingapange chosankha chaumwini, ndi bwino kuona ngati tikuchita zonse zothekera kukhala ndi moyo wa kudzipatulira kwa Yehova. Pamene tikumtumikira tsiku ndi tsiku, tikumachita zomwe tingathe kumkondweretsa, tidzapambana monga Akristu ndipo tidzadalitsidwa ndi chiyanjo cha Yehova, Iye amene ayenerera kudzipereka kwathu kwamtima wonse.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi kwa Yesu Kristu kudzipatulira kunaphatikizapo chiyani?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupeŵa kung’ung’udzira Yehova?
◻ Kodi ndi njira iti imene tingaletsere kupembedza mafano kuloŵa mwamachenjera m’miyoyo yathu?
◻ Kodi ndi kukumbukira chiyani kumene kudzatithandiza ‘kusalema’ pakuchita chifuniro cha Mulungu?
[Chithunzi patsamba 17]
Akristu odzipatulira ‘samalema pakuchita zabwino’